Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 10/8 tsamba 16-18
  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chinsinsi cha Kusankha Zovala Zoyenera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chinsinsi cha Kusankha Zovala Zoyenera?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusankha “Zovala” Zoyenera
  • Phindu la Kuvala Mosasintha
  • Kugula Kwanzeru
  • Zinthu Zofunika Koposa
  • Kodi Ndingapeze Motani Zovala Zoyenera?
    Galamukani!—1995
  • Zovala Zolembedwa Dzina la Ozipanga Kodi Nzanga?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Zovala Zimene Timavala Zilidi N’kanthu?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 10/8 tsamba 16-18

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chinsinsi cha Kusankha Zovala Zoyenera?

MIKE amadziŵa kusankha zovala zabwino—ndi mmene angazipezere izo pa mtengo wabwino. Nthaŵi zina ziŵalo za banja lake zimafikiradi pa kumpempha iye kukazigulira! Paulendo wina wokagula, iye anasankha madelesi a amayi wake, mlongo wake wokwatiwa, ndi mwana wamkazi wa mlongo wake wa zaka zisanu ndi zitatu zakubadwa—masaizi oyenerera ndi masitayelo omwe anafuna! Pamene iye anali paulendowo, iye anadzisankhira malaya ovala pokasamba ochepa mtengo kuchepera nthaŵi zinayi pa mtengo wake wa nthaŵi zonse. Kwa Mike, ichi sichinali chozizwitsa koma chisangalatso chenicheni.

Mwinamwake mulibe changu cha Mike cha kugula. Koma mofanana ndi anthu ambiri achichepere, inu mwinamwake mumafuna kuwoneka bwino koposa ku sukulu, ku ntchito, ndi poseŵera. Vuto liri lakuti, chenicheni chakuti sitayelo inayake ikulingaliridwa kukhala ya fashoni pakati pa achichepere sichimatanthauza kuti chiri chinthu choyenera kuvala, ndiponso kugula chinthu “chamakono” sikuli kugwiritsira ntchito kwabwino koposa kwa ndalama zanu. Chotero, kulingalira kuti makolo anu amakupatsani ufulu wa kusankha zovala zanu, pano pali nsonga zina za mmene mungasankhire ndi kugula zovala zoyenera.

Kusankha “Zovala” Zoyenera

Choyamba, tiyeni tichotse lingaliro lakuti chirichonse chimayenda bwino pamene tikamba za zovala. Inu mukukula, ndipo ziyembekezo za kupanga umoyo ndipo mwinamwake kuchirikiza banja ziri kutsogolo kwanu. Kavalidwe kanu kadzayambukira osati kokha ziyembekezo zanu za kupeza ntchito komanso njira mu imene mudzawonedwera ndi kuchitiridwa ndi ena. Chofunika koposa, ife Akristu “sitiyenera kudzikondweretsa ife eni,” koma tiyenera kudera nkhaŵa za mmene zimene timachita—kapena kuvala—zimayambukirira ena.—Aroma 15:1.

Miyambo 25:20 ikulankhula za “kuvula malaya tsiku la mphepo.” Nchosayenerera chotani nanga! Nchosayenera mofananamo kuvala malaya a sitayelo omwe sali oyenerana ndi chochitika. Wochita chitsanzo pa seŵero la pa pulatifomu amasankha moyenerera chovala choyenerana ndi mbali yake. Ndipo m’moyo weniweni, mbali zomwe timachita kaŵirikaŵiri zimafunikira “zovala” zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kodi mukupita kukafunsidwa za ntchito? Pamenepo suti ya ku ntchito ingakhale chovala choyenerera. Kodi mukupita ku sukulu? Pamenepo kawonekedwe komwe mufuna kangakhale kachisawawa koma kaudongo.

Millie, mmodzi wa Mboni za Yehova, anapezeka ku sukulu imene chiwawa chinali chofalikira. Kuvala ngati kuti akupita ku msonkhano Wachikristu kukanampanga iye kukhala wowonekera mopambanitsa. Chotero iye anavala jeans yowoneka bwino mkati mwa maola a ku sukulu, popeza chimenecho chinali cholandirika pa sukulu yake. Koma popeza kuti anadziloŵetsa m’ntchito yophunzitsa Baibulo pambuyo pa makalasi, iye anatenganso delesi. Kusintha chochita, kusinthanso chovala.

Achichepere pakati pa Mboni za Yehova amapereka lingaliro lapadera ku chimene amavala pa misonkhano Yachikristu ndi m’ntchito yawo yolalikira mwapoyera. Mwachitsanzo, jeans ndi masneaker, zomwe zingatumikire bwino ku sukulu, siziri zoyenerera mkati mwa kulambira; izo zimachotsa wina pa kudzinenera kwa kukhala minisitala wa Mulungu.—Yerekezani ndi 2 Akorinto 6:3.

Phindu la Kuvala Mosasintha

Nthanthi ya Rudy wachichepere pa kuvala ingakudabwitseni. Iye akunena kuti: “Ndimakonda mtundu wa zovala zomwe anthu akhala akuvala kwa zaka 50 zapita.” Kodi ndi wachikale momvetsa chifundo? Kutalitali. Rudy waphunzira kuti ngakhale kuti ‘dziko likusintha,’ masitayelo enieni samasintha konse. (1 Akorinto 7:31) Lamulo lake liri lakuti: Usavale chirichonse chamakono chomwe mosakhalitsa chidzakhala chachikale! “Mwanjira imeneyi, nthaŵi zonse mumakhala m’masitayelo,” akulangiza choncho Rudy.

Akatswiri akuvomereza. Mwachitsanzo, phungu Amelia Fatt, akunena kuti zinthu zosasintha ziri “zosungidwa zabwino.” Izo sizimakhala zachikale chifukwa chakuti mawonekedwe ake siali odziŵikiratu. Monga phindu lapadera, nthaŵi zonse chimakhala chopepuka kugwirizanitsa masitayelo osasintha ndi zinthu zina m’chipinda chanu chosungira zovala.

Masitayelo ena amakono sali oyenerera kwa Akristu. Ena ndi abwino. Tikumalingalira kuti makolo anu amavomereza, ngati mupeza kuti chinthu china cha sitayelo pambali powoneka bwino kwa inu chimayenderananso bwino ndi zinthu zina m’chipinda chanu chosungira zovala, mungafune kulingalira kuchivala icho. Koma chenjerani ndi kukhala kapolo wa fashoni! Phungu wa fashoni Carole Jackson akunena kuti: “Ngati mumatsatira zikhoterero za fashoni kuti mukhale ‘wamakono,’ ngakhale pamene chikhotero cha panthaŵiyo sichikuyenerani, mukungodzinyenga nokha.”

Pali mwaŵi wina wa kukhala wosasintha m’kavalidwe. Akazi ena achichepere apeza kuti ichi sichimalimbikitsa kuvutitsidwa kwa zakugonana ku sukulu ndi pamalo a ntchito. Kuwonjezerapo, wachichepere yemwe amamamatira ku masitayelo a mwambo mwachidziŵikire adzawonedwa ndi ena kukhala wachikulire, wokhazikika, osati monga wina wokokedwakokedwa ndi mkuntho uliwonse wa zikhoterero ndi fashoni.

Mwachitsanzo, Tammy ali mkazi wachichepere wotumikira monga mlengezi wa nthaŵi zonse. Ngakhale kuti zovala zazifupi ziri zofala kumene iye amakhala, iye akunena kuti, “Kwa ine, chovala chopitirira mawondo pang’ono chiri chautali woyenera.” Ichi chimagwirizana ndi kudekha Kwachikristu. (1 Timoteo 2:9) Ndithudi, miyezo ya kudekha imasiyanasiyana m’dziko. Ndipo ngati mukukaikira ngati sitayelo ina iri yoyenerera kapena ayi, lankhulani ndi kholo kapena bwenzi lachikulire.

Kugula Kwanzeru

‘Ndi chitsogozo chaluntha chitani nkhondo yanu,’ likulangiza motero Baibulo pa Miyambo 20:18. Chitsogozo chaluntha chimafunikira ngakhale m’nkhani zochepera zonga kugula. Mwachitsanzo, kodi muli ndi vuto m’kupeza zovala zomwe zimakusangalatsani? Mungapeze chitsogozo chaluntha mwa kungopanga ulendo ku laibulale yaunyinji ndi kufufuza! Kumeneko kuli mabukhu ndi nkhani zomwe zingakuthandizeni kugwiritsira ntchito zovala zosiyana, mitundu, ndi masitayelo a zovala kuti muthetse mavuto a nkhope, utali wa khosi, kawonekedwe ka thupi, ndi zina zotero.

Bwanji ponena za mtundu wa zovala zomwe mumagula? Ngakhale kuti Yesu Kristu anali wosauka mwakuthupi pamene anali padziko lapansi, iye mwachiwonekere anavala zovala za mtundu wapamwamba kotero kuti omupha ake anachita mayere pa yemwe akazitenga izo! (Yohane 19:23, 24) Mofananamo, muyenera kukalamira kumamatira ku zovala za mtundu wabwino, ngakhale ngati ndalama zanu nzochepa ndipo mungayenere kusunga ndalama musanagule. M’kupita kwa nthaŵi, chovala cha mtengo wodulirako cha mtundu wabwino chomwe chidzakutengerani zaka mukuchigwiritsira ntchito chingakhale cha mtengo wotsika kuposa “chogulidwa pa mtengo wotsika” koma chosakhalitsa.

Kodi ndimotani mmene mungakulitsire luso la kusankha cha mtundu wolimba? Yesani kuyang’ana m’masitolo odula koposa omwe ali akatswiri mu zovala zolimba. Dziŵani mmene zovala zabwino zimawonekera ndi kumvekera m’manja. Bukhu lakuti Elegance likunena kuti: “Musatengeke ndi dzina; chovala chiyenera kudziimira pachokha . . . Chovala chosalimba, mosasamala kanthu za mitundumitundu, sichiri cha mtengo wotsika.” Igwireni nsaluyo. Fufuzani kolala, nsalu ya mkati, ndi ziboo za mabutawo. Yang’anani kusoka kolimbitsa.

Mike (wotchulidwa poyambapo) wakulitsa luso lakudziŵa mtundu wolimba. Chotero, iye anazindikira kuti chovala chopitira kosambacho chinalidi chotsitsidwa mtengo! Komabe, “musanyengedwe ndi ‘kutsitsa mtengo,’” akuchenjeza tero Amelia Fatt. Juzi ya mtengo waukulu yomwe ingavalidwe ndi zinthu zina zokhala m’chipinda chanu choika zovala ingakutumikireni mokulira kuposa juzi “yotsika mtengo” yomwe sifanana ndi chirichonse. Miyambo 21:5 ikunena kuti: “Wansontho angopeza umphawi.” Peŵani kugula pamene muli otanganitsidwa. Gulani pamene masitolo sali odzazidwa ndi anthu. Dziŵani pasadakhale chomwe mukufuna. Ukulu umene mumasunga wa nsalu m’maganizo, sitayelo, mtundu, ndi mtengo womwe mukufuna, umakhala kuchepera kumene mudzasokeretsedwa m’kugula chinachake chomwe simukuchifunadi.

Ogulitsa m’masitolo angakhale othandiza kwambiri ngati muwawuza zofuna zanu zachindunji. (Ndithudi, linali thandizo la mkazi wogulitsa kuti Mike anali wokhoza kugula zovala za ziŵalo zazikazi za banja lake.) Koma musalole anthu ogulitsa kukunyengani m’kuchita chosiyana ndi chosankha chanu chabwino. “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.

Valani ndi kupesa moyenerera pamene mupita kukagula. Kodi ndimotani mmene mungadziŵire ngati jekete ya suti ikuwoneka bwino pamene muyesera iyo pamwamba pa sikipa? Kapena ndimotani mmene mungadziŵire ngati malaya kapena delesi liri lokondweretsa ngati mwavala masneaker? Wolemba wina akunenanso kuti ngati mwavala mosawoneka bwino, anthu ogulitsa amakhoterera “kulingalira kuti muli munthu wokhala ndi polekezera m’zokonda ndi/kapena mulibe ndalama zowononga,” ndipo angasumike maganizo pa ogula ena.

Pomalizira pake, mungapeze kuti nthaŵi zambiri “aŵiri aposa mmodzi” pamene mukugula. (Mlaliki 4:9) Bwenzi kapena kholo lingakuwuzeni mmene chovala chikuwonekera kumbuyo, kaya ndi chokhwepa kwambiri, kapena chothina, kapena ngati m’njira zina zake chiri chosadekha.

Zinthu Zofunika Koposa

Pa Afilipi 1:10, Akristu akuchenjezedwa ‘kutsimikizira zinthu zofunika koposa.’ Zinthu zofunika koposa zenizeni m’moyo zimazikidwa pa kukhala ndi chidziŵitso cha Mulungu—osati zovala. Nchomvetsa chisoni kunena kuti, achichepere ena angakhale ovala mowoneka bwino koma osasamala m’kukhoza kwawo kwa kupanga chilengezo chapoyera cha chikhulupiriro chawo.

Chotero pamene kuli kwakuti nkwabwino kukhala wogula wanzeru ndi kuwoneka bwino monga mmene ndalama zanu zingalolere, sumikani maganizo pa kukhala Mkristu wachikulire. Phunzirani kukhala ndi mbali imeneyo, ndipo kavalidwe koyenerera kadzabwera mwachibadwa.

[Chithunzi patsamba 16]

Zovala zachikhoterero zimachoka m’sitayelo mofulumira. Masitayelo osasintha a zochitika zosiyanasiyana amakhalitsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena