Achichepere Akufunsa Kuti
Kodi Ndingapeze Motani Zovala Zoyenera?
ROBERT wasoŵa chochita! Afunikira kupita ku ukwati wa mlongo wake koma alibiretu chovala. Sikuti Robert ali mu “usiŵa” umene Baibulo limanena. (Yakobo 2:15) Koma zovala za Robert za masiku onse zangokhala zosayenera chochitika cholemekezeka chimenechi.
Komabe, Angela wachichepere akupita ku macheza atatu, ndipo alionse akufuna kavalidwe ka sitayelo yosiyana. Koma iye, mosiyana ndi Robert, sakuvutika kwambiri kupeza chovala choyenera. Sikuti Angela ali wolemera. Iye wangokhala ndi zovala zokwanira zimene zimamlola kuvala bwino m’mikhalidwe yosiyanasiyana.
Nkhani ina m’magazini akuti Woman’s Day inati: “Zovala zili zofunika. Zingakuchititseni kupezadi bwino kwambiri.” Zimene mumavala zimayambukiranso kwambiri mmene ena amakuonerani ndi kukuchitirani. Pamenepo, pali chifukwa chabwino chimene Baibulo limatilangizira kuvala “chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso.” (1 Timoteo 2:9) Ngati muli Mkristu, kukhala ndi zovala zoyenera kuyenera kukhala kofunika kwa inu.
Komabe, kodi mwina mumapeza kuti mulibe chovala, mosasamala kanthu kuti muli ndi zovala zochuluka? Kodi vuto lili pati, ndipo kodi mungawongolere motani zinthu?
Kukwera Mtengo kwa Fashoni
Kaŵirikaŵiri vuto silimakhala pa ndalama koma chifukwa cha kukhala mu ukapolo wa masitayelo ndi mafashoni a dziko osintha nthaŵi zonse. Buku lakuti Youthtrends limanena kuti “amalonda amadziŵa kuchuluka kwa ndalama zimene achichepere angawononge pa zovala zokhala ndi maina a wozipanga.” Posonkhezeredwa ndi umbombo wa ndalama, amalonda a zovala amagwiritsira ntchito magazini ndi TV kusatsa malonda mokopa kunyengerera achinyamata kuwononga ndalama zambirimbiri! Pokhala palinso chitsenderezo cha mabwenzi, njirayo imagwira ntchito. Mphunzitsi wina akudandaula kuti: “Aliyense akuwononga ndalama zochuluka kugulira zovala ndipo achichepere amene sakhoza . . . akugwira ntchito ataŵeruka kusukulu kuti angogula jeans yokhala ndi dzina la woipanga.”
Kukhala kapolo wa mafashoni kumatayitsa ndalama zambiri ndipo kungakusiyeni ndi zochepa chabe zogulira zovala zoyenera zimene mufunikiradi. Aroma 12:2 amapereka uphungu wabwino pamene amati: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu.” Zoona, nkovuta nthaŵi zina kukhala wosiyana ndi ena. Charlene wa zaka 16 akuvomereza kuti: “Anzako kusukulu amakuseka ukavala zosiyana ndi zawo.” Komabe, pamene mulola ena kulamulira zochita zanu, mumakhala kapolo wawo. (Yerekezerani ndi Aroma 6:16.) Mtsikana wina wotchedwa Johanna akuvomereza kuti: “Zimandinyansa chifukwa chakuti ndimamva ngati kuti ndimavalira munthu wina nthaŵi zonse.”
Kodi zimenezi ndi zanzeru nthaŵi zonse? Mwachitsanzo, talingalirani mavalidwe a timagulu ta m’makwalala, a hip-hop, ndi a “grunge.” Ambiri amavala masitayelo ameneŵa chabe chifukwa chakuti ali omveka. Koma masitayelowo amasonyeza poyera mkwiyo ndi chipanduko. Kodi kuwavala sikungapereke kwa ena chithunzi cholakwika ponena za inu? (Yohane 15:19; yerekezerani ndi 2 Akorinto 6:4.) Makamaka kuoneka ngati chiŵalo cha kagulu kena kungakuphetseni. Chotero sukulu zina ku United States zaletsa kuvala masitayelo a timagulu. Phunziro lake? Sikwanzeru kulola amsinkhu wanu kukusankhirani zovala, ngakhale kulamulira moyo wanu. M’malo modera nkhaŵa zimene zingawakondweretse, “[pitirizani, NW] kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani”!—Aefeso 5:10.
Kulingalira Zosoŵa Zanu
Mutangomasuka ku ukapolo wa masitayelo ndi mafashoni, mungayambe kupeza zovala zimene zingakwaniritse zosoŵa zanu zenizeni. Mwachitsanzo, nthaŵi yanu yochuluka mumaithera kusukulu. Ngati kusukulu kwanu amafuna yunifomu, kapena ngati pali malamulo amphamvu a kavalidwe, ufulu wanu wa kudzisankhira zovala udzakhala wochepa. Koma m’sukulu zambiri amalola kudzisankhira zovala, ndipo zovala wamba zili zofala.
M’mikhalidwe yotero, sikungakhale kwanzeru kudzionetsera mwa kuvala jekete ndi taye kapena siketi yambambande. Mudzafuna kuoneka mutavala zovala wamba popanda kuoneka wasitayelo kapena wosasamala. Mtsikana wina wotchedwa Millie anachita zimenezo. Pamene anali kusukulu anapeŵa mafashoni opambanitsa. Ngati mkhalidwe wanu uli wofanana ndi umenewu, mwina inu mungafunikirenso kuwonjezera mabuluku wamba angapo, mashati, kapena mabulauzi pa zovala zanu. Ngati ndalama zikusoŵa, kungokhala ndi zinthu zingapo zimenezi kungakhale kokwanira.—Yerekezerani ndi Luka 10:42.
Kukhala ndi zovala za kusukulu zokwanira bwino kungakuchititseni kukhala ndi ndalama zokwanira kusamalira zosoŵa zina. Mwachitsanzo, kodi pali ntchito yapabwalo kapena yam’nyumba imene mufunikira kuchita? Pamenepo mudzafunikira zovala zolimba. Zovala zoyenera zingafunikirenso pa maseŵero ndi zochitachita zina zamaseŵero. Ngakhale kuti kuvala akabudula okhala ndi dzina la wopanga, malaya, ndi ma sneaker kungakhale m’fashoni, mudzapeza kuti zovala zina zosakwera mtengo zingatumikire bwino mofananamo.
Ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, mudzafunikiranso kulingalira za kufunikira kwanu zovala zoyenera pamisonkhano Yachikristu, chifukwa chakuti zovala wamba zopambanitsa zili zosayenera pa kulambira. M’maiko mmene anthu amatsatira mavalidwe Akumadzulo, anyamata kaŵirikaŵiri amavala buluku, shati, taye, ndi jekete. Atsikana kaŵirikaŵiri amavala deresi kapena siketi ndi bulauzi. Zovala zonga zimenezi amazivala m’ntchito yolalikira kukhomo ndi khomo. Unyinji wa zovala zimenezi zimene mungagule umadalira pa ndalama zanu. Mwamwaŵi, zovala zanu sizifunikira kukhala zochulukitsa kapena za fashoni yamakono. Ziyenera kukhala zaudongo ndi zoyera.
Yesu Kristu anapita ku ukwati, ndipo inu mwina mungaitanidwenso kukapezeka ku zochitika zina m’chitaganya. (Yohane 2:1, 2) Ngati kuvalira zochitika zimenezo ndi mwambo wake, pamenepo nkwanzeru kukhala ndi zovala zina zoyenera. “Ndapezeka m’mikhalidwe imene sindinavale bwino pa chochitikacho, ndipo zinali zosakondweretsa,” akuvomereza motero Johanna. Kukhala ndi chovala chimodzi kapena zingapo zabwino kwambiri kungakupeŵetseninso chitsenderezo cha kugula zinthu nthaŵi itatha ndi kuwononga ndalama.
Kuŵerengera
Inu mungachite zimene mlembi Jean Patton akutcha kuŵerengera zovala. (Color to Color) Santhulani zovala zanu, kuphatikizapo zosungidwa padera. Mungapeze zovala zimene munaiŵala. Panthaŵi imodzimodziyo, mukhoza kuchotsa zovala zimene zachepa kapena zimene simuzikondanso.
Ndiyeno, lembani mpambo wa kuŵerengerako, mwinamwake mukumaukonza ndi zovala zazikulu (makhothi, masuti, maderesi, ma blazer, majekete), zovalira pamodzi ndi zazikulu (mabulauzi, majuzi, mashati), ndi zina zowonjezera (masikafu, malamba, magulovu, zipeŵa, nsapato, zola, mataye). Mpambo wotero umakuthandizani kuona zinthu zimene mungafunikire kuti zovala zanu zikhale zokwanira.
Kugula Zinthu Mwanzeru
M’maiko ena zovala zatsopano zili zokwera mtengo kwambiri. Achinyamata kumeneko amayesetsa kusamalira zovala zimene ali nazo ndi kuzisunga zili zaudongo ndithu ndi zoyera. Nanga bwanji ngati mukhoza kugula zovala zatsopano? M’buku lake lakuti Working Wardrobe, Janet Wallach akunena kuti “mkazi angasunge nthaŵi ndi ndalama ngati akonzekera ndipo akhala ndi chifuno pogula zovala zake.” Ndimmenenso ziyenera kukhalira kwa anyamata. Mwina muli ndi ndalama zochepa, chotero mufunikira kuŵerengera mtengo wa chilichonse chimene mukugula. (Yerekezerani ndi Luka 14:28.) Zimenezo zingatanthauze kuchotsapo zina pa mpambo wanu wa zogula, mukumamamatira ku zinthu zofunika kwambiri. Njira yabwino ndiyo kuwonongera ndalama zochuluka pa zovala zimene mudzakhala mukuvala kwambiri.
Buku lakuti The Better Business Bureau A to Z Buying Guide likupereka malangizo aŵa: “Khalani ndi zovala za maonekedwe a m’gulu limodzi lalikulu, monga obiriŵirira ndi otumbuluka kapena ofiirira ndi akuda. Sankhani zovala zazikulu za maonekedwe amenewo, ndipo maonekedwe ena oŵala akhale a mashati, mabulauzi, ndi zina zowonjezera.” Zovala za maonekedwe otumbuluka zimakhala m’sitayelo kwa nthaŵi yotalikirapo. Mwa kumamatira ku maonekedwe aakulu, mukhoza kuyesa mosavuta ndi kudzipangira mavalidwe atsopano.
Miyambo 14:15 imati: “Wochenjera asamalira mayendedwe ake,” ndipo kukonzekera kwanu kotsimikizirika ponena za zogula zanu kungakuthandizeni kupeŵa kagulidwe ka zinthu kosakonzekera kowonongetsa ndalama. “Nthaŵi zonse ndimakhala ndi mpambo wa zogula pamene ndikugula zinthu,” mkazi wina wachichepere akutero. Kumbukiraninso kuti m’kupita kwa nthaŵi, kusankha zovala zolimba, osati zochuluka, kumafupa. Chovala cholimba chingakhale zaka zambiri. “Ndidakali ndi majuzi amene ndinkavala pamene ndinali wachichepere,” mkazi wina wachichepere akutero. Komabe, dzina la wopanga kwenikweni sindilo limene limadziŵikitsa chovala cholimba, koma chimadziŵika bwino mwa kupenda mosamalitsa chovalacho.a
Khalani wosafulumira kusintha masitayelo. Deresi lamwambo kapena suti ya mwamuna nthaŵi zambiri imakhala m’sitayelo. Kutchuka kwa masitayelo amakono kumatha msanga. M’buku lake lakuti Conservative Chic, Amelia Fatt akuti: “Zovala za masitayelo osafulumira kusintha sizimavuta kukometsera, sizimavuta kuwonjezera pa chaka chotsatira, zili chuma chabwino kwambiri.”
Musaiŵale kuti makolo anu ali ndi chidziŵitso cha zaka zambiri cha kugula zovala. Zimene mungakonde zingakhale zosiyana kwambiri ndi zawo, koma mukhoza kugwirizana nawo kwambiri pa zinthu zofunika kuposa ndi mmene mukuganizira. “Amayi anathandiza ineyo ndi mchemwali wanga kukulitsa luso la kusankha zovala zabwino,” Angela akukumbukira motero. M’kupita kwa nthaŵi ndi kuleza mtima, inunso mungakhoze kukhala ndi zovala zoyenera zimene zikhoza kugwiritsiridwa ntchito. Mwinamwake simudzafunikiranso kunena kuti, ‘Ndilibe chovala!’
[Mawu a M’munsi]
a Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chinsinsi cha Kusankha Zovala Zoyenera?” m’kope lathu la October 8, 1989.
[Chithunzi patsamba 26]
Choyamba ŵerengerani zimene muli nazo kale