Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 12/8 tsamba 3-4
  • Kodi Ndife Aumoyo Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndife Aumoyo Motani?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chithunzicho Lerolino
  • Kuyang’ana Kutsogolo
  • Umoyo Wabwino—Kodi Mungachitenji Ponena za Iwo?
    Galamukani!—1989
  • Zimene Zimakupatsani Thanzi—Zimene Mungachite
    Galamukani!—1995
  • Kodi Umoyo Nchiyani?
    Galamukani!—1989
  • Mmene Mungatetezere Thanzi Lanu
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 12/8 tsamba 3-4

Kodi Ndife Aumoyo Motani?

MADOLA miliyoni chikwi chimodzi! Uwu ndi unyinji umene anthu mu United States akuwononga pa kusamalira umoyo. Nzika za ku Federal Republic of Germany zimawononga zoposa pa mbali zisanu za zopangidwa za chuma chawo cha dzikolo, kapena zoposa zikwi 340 miliyoni za ndalama za deutsche marks pachaka, kusamalira zosoŵa za umoyo wawo. Mkhalidwewo uli wofanana m’maiko ena okhupuka ndi maindasitale kapena otukuka.

Palibe kukaikira kuti nzika iriyonse m’maiko amenewa ikukhaladi yodera nkhawa umoyo moposerapo. Mabukhu ndi mavideo onena za kadyedwe ndi maseŵera akutenga malo okulira mokhazikika pa ndandanda ya zogulidwa koposa. Zakudya zaumoyo, zotetezera ku matenda, zolimbitsa thupi, ndi maseŵera zakhala malonda a amponda matiki. Ndipo masiku ano chodziŵitsa munthu wopambana sichirinso kunyada kwa wokhupuka wotafuna ndudu koma thupi lowoneka mwaudongo, lathanzi labwino.

Pokhala ndi chisamaliro ndi chikondwerero zonsezi zikuperekedwa ku umoyo ndi thanzi labwino, kodi ndifedi aumoyo kuposa anthu a mibadwo yapita? Kodi ndalama zochulukira zowonongeredwa pa mankhwala ndi kusamalira umoyo zatulukapo ubwino wakuthupi kwa tonsefe? Zowonadi, kodi ndife aumoyo motani?

Chithunzicho Lerolino

Mosiyana ndi zimene tingayembekezere, maripoti ochokera kwa ponse paŵiri maiko olemera ndi osauka kuzungulira dziko lonse amasonyeza kuti anthu lerolino ali kutalitali ndi chithunzi chaumoyo. Polankhula za kunyonyotsoka kwaumoyo wa dziko lonse, ripoti lokonzekeredwa ndi Worldwatch Institute likunena kuti: “Ngakhale kuti kusamalira kwaumoyo wawo kumasiyana kwadzawoneni, olemera ndi osauka ali ndi chinthu chimodzi chofanana: onse amafa mosayenerera. Olemera amafa ndi matenda a mtima ndi kansa, osauka amafa ndi kutseguka m’mimba, chibayo, ndi chikuku.”

Mosasamala kanthu za kupita patsogolo m’kufufuza kwa zamankhwala, matenda a mtima ndi kansa akupitirizabe kukhala mliri wa maiko olemera. M’chenicheni, ripoti la mu The New England Journal of Medicine likunena kuti: “Sitikuwona chifukwa chirichonse chokhalira ndi chiyembekezo cha kupita patsogolo konseko m’zaka zaposachedwapa. Palibe chifukwa choganizira kuti, m’zonsezo, kansa ikunka nizimiririka.” Ponena za kukambapo kofala kwa thanzi labwino, mkhalidwewo waikidwa mofupikira ndi Dr. Michael McGinnis wa U.S. Department of Health and Human Services: “Unyinji wokulira ukudziŵa kufunika kwa thanzi labwino. Koma sanachitepo kanthu iwo eni. Anthu a ku America sali athanzi labwino monga m’mene amadziganizira kukhala.”

Ku mbali ina ya nkhaniyo, “nusu la anthu adziko lonse alibe madzi audongo akumwa ndi zimbudzi zabwino,” likunena tero ripoti la Worldwatch. “Monga chotulukapo, matenda akutseguka m’mimba ali m’liri kuzungulira Maiko Osatukuka onse ndipo chirinso chochititsa chachikulu cha dziko cha imfa zamakanda.” Kutseguka m’mimba, chibayo, chikuku, diphtheria, chifuwa chachikulu, ndi matenda ena, amapha miyoyo ya ana 15 miliyoni okhala pansi pa msinkhu wa zaka zisanu chaka chirichonse ndi kupinimbiritsa kakulidwe kachibadwa ka mamiliyoni owonjezereka. Komabe, vuto lenileni liri lakuti akatswiri amalingalira kuti ochulukira a awa angachinjirizidwe mosavuta.

Pamene kuli kwakuti ana m’maiko otukuka angapulumutsidwe ku masoka oterewa, pali zizindikiro zowopsya zakuti umoyo wachisawawa wa achichepere amakono ukunyonyotsokanyonyotsoka m’malo mowongokera. Mwachitsanzo, The Guardian ya ku London, pansi pa mutu wakuti “Children ‘Healthier 35 Years Ago’” (Ana Anali Aumoyo Kwenikweni Zaka 35 Zapitazo), ikusimba kuti kufufuza kochitidwa ndi Medical Research Council kwapeza “chiwonjezeko chapadera m’kudwalira m’chipatala kwa ana kufika pa msinkhu wa zaka zinayi, kuwirikiza katatu kwa matenda a mphumu, ndi chiwonjezeko cha kuwirikiza kasanu ndi chimodzi kwa matenda otupa thupi pakati pa mbadwo watsopanowo.” Zopezedwanso zinali ziwonjezeko zodetsa nkhaŵa m’matenda a suga, kunenepetsa, kupsyinjika, ndi matenda a maganizo mwa achichepere.

Kufufuza kozungulira dziko la United States kunavumbulanso kuti mkhalidwe wakuthupi wa ana opita kusukulu lerolino suli mmene ufunikira kukhalira. “Chiri chinsinsi chosungidwa kwenikweni mu America lerolino—kupanda thanzi labwino kwa achichepere,” akutero George Allen, wapampando wa President’s Council on Physical Fitness and Sports. Ziŵerengero zaposachedwapa zotulutsidwa ndi bungwelo zikusonyeza kuti 40 peresenti ya anyamata ndi 70 peresenti ya atsikana a zaka 6 kufika ku 17 zakubadwa samachita maseŵera ndi amodzi omwe. Kufufuza kwina kunapeza kuti a zaka zapakati pa 13 ndi 19 lerolino ali ndi kuyenda kopambanitsa kwa mwazi, milingo yopanda umoyo ya cholesterol (zonyamula zothandizira thupi m’mitsempha ya mwazi) ndi mafuta a m’thupi, kusatchulapo mavuto oipitsitsa a maganizo, limodzinso ndi mavuto a kugwiritsira molakwa mankhwala ogodomalitsa ndi zakumwa zoledzeretsa.

Kuyang’ana Kutsogolo

Ambiri aife timazindikira kuti mkhalidwe wathu waumoyo m’moyo wonse umadalira ku mlingo winawake, pa mkhalidwe waumoyo wa m’nthaŵi yathu yaubwana. Chotero, nchosadabwitsa kuti George Allen ananena kuti: “Chimene ndikuda nacho nkhaŵa nchakuti ngati mulibe achichepere amene akuphunzira thanzi labwino tsopano, iwo sadzaphunzira nkomwe atakula.” Zofananazo nzowona ponena za maiko otukuka kumene, kusiyapo kokha kuti kumeneko ana ambiri samapatsidwa mwaŵi wa kukula kukhala achikulire aumoyo.

Ngakhale kuti ali otsendereza chotero, mavutowo sali osalakika. Inu panokha, kulikonse kumene mumakhala, pali chinachake chimene mungachite ponena za umoyo wanu ndi wabanja lanu. Komabe, zambiri zimadalira pa kulingalira kwanu kwa umoyo wanu ndi inumwini. Ndithudi, mafunso angafunsidwe akuti: Kodi umoyo nchiyani? Kodi nchiyani chimene mungachite ponena za kusungabe umoyo wabwino? Mafunso ameneŵa adzalingaliridwa m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena