Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingasankhe Motani Kanema Yabwino?
AMENE chaka chatha anali katswiri wojambulidwa m’kanema anagwidwa mawu kukhala akumati: “Anthu . . . amandifunsa chifukwa chimene sindikupitiranso kuakanema tsopano. Akanema ambiri ngoluluzika.” Iye anasankha kulekeratu kupita kuakanema monga chosangulutsa.
Msungwana wotchedwa Denise ali ndi maganizo ofananawo, koma iye akulingalira mwanjira yosankhitsa kwambiri. “Nthaŵi zambiri sipamakhala zambiri zowonerera,” akulongosola motero, “chifukwa chakuti mbali yaikulu koposa ndiyo chiwawa. Motero ndimasamala kwambiri zimene ndimawonerera.”
Mosakayikira inunso mumasangalala ndi kanema panthaŵi ndi nthaŵi. Chifukwa chake nzomveka ngati mulibe ganizo lakulekeratu kuwonerera kanema monga mpangidwe wokusangulutsani. Koma monga momwe kwasonyezedwera m’nkhani yanthu yapitayo—ndiponso mwakuyang’ana m’masamba osonyeza zosangulutsa anyuzipepala iriyonse kudzatsimikiziritsa zimenezi—kuti pali mafilimu ochepa opangidwa lerolino amene ali oyenera kuwonereredwa ndi Akristu achichepere.a Iyi sinkhani yoyenera kutengedwa mopepuka, popeza kuti akanema amene mumawonerera amasonyeza mikhalidwe imene mumaikonda. Amavumbulanso zochuluka ponena zamayanjano amene mumakonda, mtundu wachinenero chimene mumalola, ndi makhalidwe azakugonana amene mumafuna.
Baibulo limachichiza kuti “danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) Kodi mungachitedi motero ngati nthaŵi zonse mumakafunafuna kuwona kukhetsa magazi kwauchiwanda, kuvulazana, ndi chiwawa, kapena zithunzi zosonyeza chisembwere? Kutalitali. Wachichepere amene amakondadi malamulo a Mulungu amafunafuna kutsatira uphungu wa Baibulo wapa Afilipi 4:8 wakuti: “Chotsalira, abale, zinthu zirizonse zowona, zirizonse zolemekezeka, zirizonse zolungama, zirizonse zoyera, zirizonse zokongola, zirizonse zomveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” Izi sizikutanthauza kwenikweni kuti muyenera kupeŵeratu akanema onse, koma zitanthauza kuti muyenera kukhala wosankha mosamalitsa zimene mumaziwonerera. Kodi mungachite motani zimenezi?
Kuŵerengera Akanema—Chitsogozo Chosalakwika?
Mu United States, akanema amaŵerengeredwa malinga ndi miyezo yoikidwa ndi bungwe lotchedwa Motion Pictures Association of America. Chizindikiro cha lembo chimasonyeza kuti kaya filimuyo ikuwonedwa kukhala yoyenerera kuwonereredwa ndi aliyense, kapena ngati imafunikira chitsogozo chamakolo, kapena ngati iyenera kuwonereredwa ndi akulu okha. Kuŵerengera kwa kanema kumeneko kaŵirikaŵiri kumazikidwa panjira imene kanemayo imachitira pankhani zakugonana ndi chiwawa, kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa ndi mankhwala ogodomalitsa, chinenero chotukwana, ndi zina zotero.
Pamene kuli kwakuti kuŵerengera koteroko mwachiwonekere kuli ndi zolakwa, ndipo kaŵirikaŵiri nkosagwirizana, iko kumapereka lingaliro kwa woyembekezera kudzawonerera zimene ziri m’filimuyo ndiyeno kuwona kuti kaya iri yoyenerera kuiwonerera kapena ayi. Ngati dongosolo lofananalo lirimo m’dziko lanu, mosakaikira mudzalipeza kukhala lothandiza. Mofananamo makolo anu angagwiritsire ntchito kuŵerengera koteroko popereka zitsogozo zonena zamafilimu amene mungawonerere.
Komabe, kuŵerengera kwa mafilimu kungakhale kosokeretsa. Kumbukirani: Oŵerengera mafilimuwo angakhale osagwirizana ndi makhalidwe abwino ozikidwa pa Baibulo. Ndipo chifukwa cha makhalidwe a dziko lino omanyonyotsoka, mafilimu ambiri amene anawonedwa kukhala ochititsa kakasi kotheratu zaka zoŵerengeka zapitazo tsopano ali ovomerezedwa kuwonereredwa ndi aliyense.
Wachichepere wotchedwa DeMarlo anadziwonera yekha zimenezi pamene anakaloŵa filimu imene anailingalira kuti inaŵerengeredwa kukhala yabwino. Anadzawona kuti inali yodzala ndi “kutukwana ndi chiwawa.” Chotero pamene kuli kwakuti kuŵerengera kwa akanema kofalitsidwa kungakhale kothandiza, sikuyenera kukhala maziko otheratu osankhira zoyenera kuwonereredwa. Baibulo limachenjeza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.
Kufufuza Filimu Pasadakhale
Kodi nzitsogozo zina zotani zimene mungagwiritsire ntchito? Zilengezo za akanema ndi zotsatsa malonda zingakupatseninso lingaliro la zimene kanemayo alinazo. Komano kachiŵirinso, pafunikira kuchenjera. Chilengezo cha kanema chimangopereka lingaliro la munthu wina. Ndipo kutsatsa kungabise dala chenicheni chakuti kanemayo iri ndi ziwonetsero zochititsa manyazi.
Wachichepere wotchedwa Connie anati: “Ndapeza kuti kudziŵa oseŵera mbali zazikulu m’kanema kaŵirikaŵiri kumakupatsa lingaliro la zimene kanameyo idzawonetsa.” Mabwenzi Achikristu okhala ndi mikhalidwe yozikidwa pa Baibulo yofanana ndi yanu angadziŵe ngati filimu yakutiyakuti iri yoyenera. Ndipo mofananamo manijala wanyumba yakanema kapena wogulitsa matikiti angakupatseni chidziŵitso chowona. Komabe, anthu kaŵirikaŵiri amakhotherera kukuuzani zimene zinawasangalatsa m’kanema. Motero bwanji osafunsa zoipa zimene zinalimo? Khalani wolunjika. Funsani ngati iri ndi ziwonetsero zachiwawa chokhetsa magazi, zakugonana kosasankha, kapena kugwidwa ndi ziwanda.
Makolo anu angakhalenso magwero abwino opezako chilangizo. Wachichepere wotchedwa Vanessa akuti: “Ndimafunsa makolo anga. Ngati aganiza kuti kulibwino kwaine kuiwonerera, ndimakailoŵa.”
Zofananazo zingagwire ntchito ponena za kubwereka mavidiyo tepi. Ndiponso, pendani bokosilo kapena chikuto chake mosamalitsa. Kodi pali chithunzithunzi chirichonse kapena mawu amene angasonyeze kuti filimuyo njosayenera? Pamenepo taibwezani! Kungathandizenso kulankhula kwa kalaliki wosunga mavidiyo tepi amene anaiwonapo kale filimuyo. Miyambo 14:16 imati: “Munthu wanzeru amachenjera ndi kufulatira choipa; wopusa salabadira ndipo agweramo chamutu.—The New English Bible.
Kutulukamo, Kuitseka
Komabe, bwanji ngati mwabwereka kale vidiyo tepi, ndiyeno nkupeza kuti iri ndi zithunzi zoipa? Yankho nlosavuta. Taitsekani! Ichi sichingakhale chosavuta. Mungakhale mutatengeka maganizo ndi seŵero losonyezedwa kapena ndi oseŵerawo. Mungakhalenso wolakalaka kufuna kudziŵa mmene filimuyo imathera. Koma kufulatira choipa mwachiwonekere ndiko chinthu chanzeru kuchichita.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:29, 30.
Mkhalidwewo ungakhale wovutirako pang’ono ngati muli kale m’nyumba yowonera kanema ndi mabwenzi anu ndiyeno mungowona kuti kanemayo njoipa. Wachichepere wotchedwa Joseph anayang’anizana kumene ndi mkhalidwe umenewu. Chilengezo cha filimu yapanthaŵiyo chinaisonyeza kukhala “yoyenera kuwonedwa.” Komabe, Joseph akukumbukira kuti: “Mkati mwa mphindi zisanu zoyambirira panali kale ziwonetsero zitatu zachiwawa ndi zaumaliseche.” Mwachifatse, Joseph anauza mabwenzi ake zolinga zake ndikutulukamo. Kodi zimenezi zinamchititsa manyazi? Joseph akuti: “Iyayi, n’mpang’ono ponse. Ndinaganizira Yehova choyamba ndi zakumkondweretsa.”
Indedi, chipsinjo chamabwenzi chotsutsa kutenga kaimidwe koteroko chingakhale champhamvu. Chipsinjo chingachokerenso kwa achichepere oleredwa ndi makolo Achikristu, koma achichepere oterowo ali ndi zikumbumtima zopserera mwakuwonerera mafilimu ambiri okaikitsa. (1 Timoteo 4:2) Iwo angakunenezeni kukhala wonkhitsa kapena kuti ndinu wolungama mopambanitsa. Komabe mmalo mwakugonjera kuchipsinjo chamabwenzi, muyenera “kukhala nacho chikumbumtima chabwino.” (1 Petro 3:16) Chimene kwenikweni chiri kanthu sindicho chimene mabwenzi anu akuganiza ponena za inu koma chimene Yehova akuganiza ponena za inu! Ndipo ngati mwabwenzi anu akukuvutitsani kaamba kotsatira chikumbumtima chanu, ndiyo nthaŵi yakuti mupeze mabwenzi atsopano. (Miyambo 13:20) Inu ndinu mlonda wamkulu wa maso anu, makutu, ndi mtima wophiphiritsira.—Yerekezerani ndi Yobu 12:11; 31:1; Miyambo 4:23.
Kusunga Chikumbumtima Chabwino
Wachichepere wotchedwa Georgia anali ndi chizoloŵezi chakunyonyolokera muakanema oletsedwa kwa amsinkhu wake. Komabe, m’kupita kwanthaŵi, msungwanayo anayamba kulakalaka unansi wabwino ndi Mulungu. Analeka kuwonerera akanema okayikitsa ndikupeza zinthu zina zokondweretsa kuzichita pamodzi ndi mabwenzi ake Achikristu. Georgia akuti: “Tsopano ndiribenso chovutitsa chikumbumtima changa. Ndipo tsopano ndimagonadi bwino chifukwa chakuti ndiri ndi malingaliro oyera mkatimo.”
Kodi mufuna kukhala woyera pamaso pa Wosanthula mitima, Yehova Mulungu? (Miyambo 17:3) Pamenepo samalani zimene muloŵetsa mumtima wanu. Peŵani kuphatikizidwa ndi chiwawa mosayenera, kugonana kosasankha, kapena kutukwana; izi zingagodomalitse lingaliro lanu lachimene chiri chabwino ndi kuipitsa mtima wanu. Khalani monga wamasalmo amene anapemphera kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.”—Salmo 119:37.
Mwakukhala wosamala ndi wosankha, sikokha kuti mungadzitetezere kuzisonkhezero zovulaza koma mungasangalalenso ndi “malingaliro oyera” amene Georgia wachichepereyo analankhula za iwo. Ndipo palibe zosangalatsa zapadera za akanema zimene zingayerekezeredwe ndi malingaliro amenewo!
[Mawu a M’munsi]
a Wonani nkhani yapitayo yakuti “Kodi Ziri Nkanthu Kuti ndi Akanema Otani Amene Ndimawonerera?” m’kope lino.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Mafilimu ambiri amene anawonedwa kukhala ochititsa kakasi kotheratu zaka zoŵerengeka zapitazo tsopano ali ovomerezedwa
[Chithunzi patsamba 13]
Makolo anu angadziŵe ngati kanema yolengezedwayo iri yoyenera