Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 8/8 tsamba 10-12
  • Kodi Ziri Nkanthu Kuti Ndiakanema Otani Amene Ndimawonerera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ziri Nkanthu Kuti Ndiakanema Otani Amene Ndimawonerera?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Akanema—Zikhoterero Zanthaŵi Ino
  • Chiukiro ku Maso ndi Makutu Anu
  • Chiukiro Pamaganizo ndi Makhalidwe Anu
  • Ziyambukiro Zamachenjera
  • Kodi Ndingasankhe Motani Kanema Yabwino?
    Galamukani!—1990
  • Nchiyani Chimene Chiri Chowopsya Motero Ponena Za Makanema Owopsya?
    Galamukani!—1988
  • Kodi Inuyo Muonera Mafilimu Ati?
    Galamukani!—2005
  • Kodi ndingasankhe bwanji mafilimu, mabuku komanso nyimbo zabwino?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 8/8 tsamba 10-12

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ziri Nkanthu Kuti Ndiakanema Otani Amene Ndimawonerera?

‘SINDIMASONKHEZEREDWA kwenikweni ndi akanema,’ akutero wazaka zapakati pa 13 ndi 19 wotchedwa Karen, ‘chifukwa chakuti ndimapita kuakanema kukadabwitsidwa ndi kuwopsezedwa nawo, kungofuna kusangulutsidwa basi.’ Achichepere ambiri amanena zofananazo kuti samayambukiridwa moipa ndi mafilimu. Komabe, Georgia wachichepere, akutsutsa. Pokhala atawona akanema angapo odziŵika kukhala osonyeza chisembwere, iye akuti: “Suumaiŵala konse zisonyezerozo . . . Pamene uzilingalira mowonjezereka, ndipamenenso umasonkhezeredwa mowonjezereka kufuna kuchita zimene unaziwonazo.”a

Akanema ngokondedwa kwambiri ndi achichepere. M’chaka chimodzi chaposachedwapa, 36 peresenti ya oposa 113 miliyoni amene anandanda panyumba zakanema mu United States yonse anali azaka zapakati pa 13 ndi 19. Mamiliyoni owonjezereka akusangalala ndi mafilimu m’zipinda zawo mwanjira zamavidiyo kaseti kapena TV ya nsambo. Ndithudi, tonsefe timafunikira kupuma ndi kusanguluka nthaŵi ndi nthaŵi. Kusintha zochita kotero kungatsitsimule ndi kusonkhezera maganizo. Kwa achichepere ambiri, kuwonerera kanema ndiko njira ina yochitira zimenezi kotero kuti akhale ndi chowasangulutsa masana kapena madzulo osungulumwitsa. Komabe kodi ndiakanema otani amene mudzawonerera? Kodi ziridi nkathu?

Akanema—Zikhoterero Zanthaŵi Ino

“Kusangulutsa maganizo, kugonana, chiwawa, umbombo, dyera.” Mogwirizana ndi katswiri wa nthenda zamaganizo Robert Coles, awa ndiwo makhalidwe ofunga muakanema ambiri opangidwa lerolino. Mofanamo, kufufuza kotsogozedwa ndi Dr. Vince Hammond kunasonyeza kuti “mafilimu ochuluka owonetsedwa m’maiko otsungula amakhala ndi chiwawa chakutichakuti, ambiri akuŵerengeredwa kukhala achiwawa kapena achiwawa chopambanitsa.” Ofufuza a Hammond anapenda mafilimu 1,000 kuchokera kumaiko osiyanasiyana. Kodi anapezanji? “Kupanga mafilimu achiwawa ndiko vuto lapadziko lonse.”

Achichepere amakonda kwambiri mafilimu owopsa, owonetsa kugwidwa ndi ziŵanda, kugwirira chigololo, ndikukhetsa mwazi mwanjira zauchiwanda kotheratu. Monga momwe Dr. Neil Senior, wogwidwa mawu m’magazini a Seventeen, amanenera, mafilimu ameneŵa “amawonetsa chirichonse chimene banja lirilonse sirikanafuna kuti ziwachitikire.” Chikhalirechobe, achichepere ambiri amandanda kuti awaonerere.

Pakhalanso kuwonjezereka kwakukulu m’mafilimu owonetsa kugonana. Ndipo mogwirizana ndi purofesala wina wa pa Yunivesite, “chiŵerengero chachikulu cha owonerera mavidiyo osonyeza kugonana m’Canada ncha achichepere apakati pa 12 ndi 17 ndipo angakhale akuyambukira moipa maganizo awo ponena za kugonana.”

Komabe, bizinesi yopanga akanema iribe nazo kanthu kwambiri. Magazini a Variety akusimba kuti mafilimu owonetsa zithunzi zachiwawa ndi kugonana akuwonjezereka, pamene mafilimu osonyeza mabanja abwino, sakupangidwa konse. Pamenepa, kodi nkotheka kuti kuwonerera mafilimu oipa kungakuyambukireni moipa?

Chiukiro ku Maso ndi Makutu Anu

Akanema amafikira kukhala oukira maganizo mwamphamvu. Yesu anati “diso ndiro nyali yathupi.” (Mateyu 6:22) Ndipo zimene muwona zingakuyambukireni mokulira. Monga momwe encyclopedia ina ikunenera, “maganizo amatsatira maso.” Mwachibadwa, maganizo anu amalamulira zimene maso anu amasankha kuyang’ana ndi kuwona. Koma pamene muyang’ana zithunzithunzi zazikulu zoposa zozoloŵereka zoyenda pachiowonetsero chachikulu, kwakukulukulu maganizo anu amagonjera kwa wopanga kanema imeneyo. Ena amamwerekera kwambiri mu filimuyo mwakuti angafunikire kukhodoledwa mwamphamvu kuti achotse maganizo awo pakanema.

“Khutu lakumva” nalonso limasonkhezera mwamphamvu maganizo anu ndi zochita zanu. (Miyambo 20:12) Zithunzithunzi zogoneka maganizo ndi mawu okambidwa zimachirikizidwa ndi nyimbo zimene zingasonkhezere malingaliro, kuyambitsa mantha, kunyanyuka, mkwiyo, chilakolako. Monga chotulukapo, mafilimu angapereke lingaliro la kuwona zinthu kukhala zenizeni mwakuti ena owonerera amalephera kusiyanitsa pakati pa zenizeni ndi zopeka.

Chiukiro Pamaganizo ndi Makhalidwe Anu

Mawonekedwe akanema nawonso angasonkhezere mokulira mmene mudzachitira nayo. Chifukwa chake opanga akanema amayesayesa kuchititsa owonerera kufuna kumawoneka monga anthu owonetsedwawo—ngakhale ngati ngwaziyo iri munthu waupandu kapena wambanda, kapena wotsendereza.b Ngati susamala, nawenso umayamba kukhala mpandu!

Talingalirani mmene gulu lina linachitira powonerera chithunzi cha munthu wopeka wachiwawa wokhala ndi zala zakuthwa ngati lumo amene anaduladula anthu m’ziwonetsero zotsatizanatsatizana. Anthuwo anakuwirira wakupha wokhetsa mwazi ameneyo! Gululo litatengeka maganizo ndi kamera yokopa maganizoyo, linawonekera kukhala litatayikiridwa luntha lakudziŵa makhalidwe abwino—ndi chifundo chirichonse pa ophedwawo.

Zimenezi nzosiyana motani nanga ndi chilangizo cha Baibulo chotsutsa kukondwera ndi tsoka la mnzako! (Miyambo 17:5) Nzowombana mwachindunji ndi Lamulo Lamakhalidwe Abwino la Yesu—‘lakuchitira ena zimene mufuna iwo kukuchitirani.’ (Mateyu 7:12) Ndiponso, kodi kukuwirira kuchita mbanda kungagwirizane ndi chilangizo cha Baibulo cha kukhala ndi “mtima wachifundo”? (Aefeso 4:32) Kodi sikuli kudzigwirizanitsa ndi “msonkhano wa ochimwa”?—Salmo 26:4, 5.

Ziyambukiro Zamachenjera

Komabe, inu mungalingalire kuti chiyambukiro chakanema nchosakhalitsa, nchakanthaŵi. Ndikuti mwachiwonekere, inu simungayambe kutengula aliyense amene mupeza chifukwa chakuti zimenezo zinawonetsedwa pakanema. Komabe, nyuzipepala yaku New Zealand ikusimba kuti pali “umboni wowonjezereka wogwirizanitsa mafilimu achiwawa ndi mavidiyo ku kudzisungira kwachiwawa kochitidwa ndi anthu amene amawawonerera.” Mofananamo, buku lakuti Adolescence linasonya kumapendedwe ambiri osonyeza kugwirizana kwapakati pa “chiwawa chapa TV ndi kudzisungira kotsendereza” ndipo linavomereza kuti pali “umboni wowonjezereka” wa kugwirizana kwa ziŵirizo.

Pakhalanso malipoti a nkhani zamachitidwe oipitsitsa ochitidwa motsatira zowonereredwa muakanema. Mwachitsanzo, wachichepere wina, anafa atavulala pamene ankayesa kuimirira ndi manja paboneti ya galimoto lothamanga. Iye anali atawona chochitika chimenechi osati kale kwambiri chikuchitidwa m’kanema yotchuka. Chotero sikuli kupanda nzeru kotheratu kulingalira kuti filimu ingayambukire zochita zanu.

Komabe, kaŵirikaŵiri, mafilimu ali ndi chisonkhezero chamachenjera koposa. Mwachitsanzo, kodi mabwenzi anu ambiri samayesayesa kulankhula, kuvala, ndi kupesa mofanana ndi ngwazi zapakanema? Kodi zimenezi siziri umboni wa chisonkhezero champhamvu cha kanema? M’zochitika zina, kuwonerera akanema oipa kumawonekera kukhala ndi chisonkhezero chofooketsa makhalidwe abwino a wachichepere. Motero wofufuza wina Dr. Thomas Radecki akunena kuti kuwonerera akanema achiwawa kwanthaŵi yaitali “kumathetsa mantha owopa chiwawa.”

Baibulo limati: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Kodi kuwonerera mafilimu kosalekeza kungayambukire maganizo anu kulinga kukuchita chiwawa? Kodi mungayambe kupeza chiwawa kukhala chosangulutsa, ngakhale choseketsa? Ndipo kodi kungakhale kotheka kuti mungakhale wokhoterera kuthetsa mavuto ndi zothetsa nzeru mwachiwawa koposa kale? Miyambo 10:23 inanena bwino kuti: “Upandu ndiwo chosangulutsa cha chitsiru.”—New American Bible.

Ndipo bwanji ponena za makhalidwe anu abwino Achikristu? Kodi kupenyerera zithunzi zakugonana ndi umaliseche kungakupangitseni kulingalira zakulakwa ndi zotulukapo zachisoni za kugonana ukwati usanakhale? Kodi kukachepetsa ‘udani wanu wa choipa?’—Salmo 97:10.

Wolemba wotchedwa Jane Burgess-Kohn akusimba za chochitika cha msungwana wotchedwa Jeanie. Pambuyo pa “kuwonerera kanema yoipa yosonyeza kugonana kochititsa manyazi” ali pamodzi ndi wopalana naye ubwenzi, Jeanie anavomereza kuti “anadzutsidwa” kotero kuti anaphatikizidwa m’kugwiranagwirana kodzutsa nyere. Komabe, sanakhoze kuimira pamenepo. “Ndiri wachisoni kunena kuti,” anaulula motero Jeanie, “usikuwo ndinali wosavuta kunyengereredwa ndi kugonedwa. Sindikudziŵabe chomwe chinachitika kotero kuti ndinatayikiridwa maganizo onse. Ndipo sindinali wokondana kwambiri ndi mnyamatayo!”

Pamenepa, mosakayikira, akanema ali ndi mphamvu yosonkhezera mtima wanu, malingaliro anu ndi kudzisungira kwanu. Chotero kodi simuyenera kusankha zimene muyenera kuwonerera? Nkhani yotsatira idzalongosola zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

a Mu United States, bungwe la Motion Picture Association of America silimalola azaka zapansi pa 17 (kusiyapo ngati atsagana ndi kholo kapena wolera) kuloŵa filimu iriyonse yodziŵika kukhala yosonyeza chisembwere, kapena kuti yoletsedwa. Kaŵirikaŵiri mafilimu otero amawonetsa zinthu zachiwawa, kutukwana, kapena zithunzi zowonetsa kugonana ndi umaliseche. Komabe, kaŵirikaŵiri koposa, kuletsako sikumachirikizidwa, ndipo achichepere amaloledwa kuloŵa.

b Kuyesa kosimbidwa mu Science News kunasonyeza kuti owonerera amakhoterera kukuyambukiridwa mokulira ndi zimene amawona “mosasamala kanthu zakuti zithunzizo nzongopeka” malinga ngati iwo ‘awoneka monga munthu wapa TV kapena pakanema.’

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Suumaiŵala konse zisonyezerozo . . . Pamene uzilingalira mowonjezereka, ndipamenenso umasonkhezeredwa mowonjezereka kufuna kuchita zimene unaziwonazo”

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Pali “umboni wowonjezereka wogwirizanitsa mafilimu achiwawa ndi mavidiyo ku kudzisungira kwachiwawa kochitidwa ndi owawonerera”

[Chithunzi patsamba 10]

Atagwidwa ndi mzimu wa kanema, kaŵirikaŵiri magulu amakuwirira kupha mwambanda, kuba, ndi chisembwere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena