Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 11/8 tsamba 12-13
  • Kodi Kuthiridwa Mwazi Ndiko Mfungulo Yopulumukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuthiridwa Mwazi Ndiko Mfungulo Yopulumukira?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Unyinji wa Zolowa Mmalo
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Zoloŵa M’malo mwa Kuthiriridwa Mwazi Zabwino
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
  • Kodi Kuika Magazi Anthu Odwala Kudzapitirirabe?
    Galamukani!—2006
  • Mafunso Ophunzirira Brosha ya Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 11/8 tsamba 12-13

Kodi Kuthiridwa Mwazi Ndiko Mfungulo Yopulumukira?

MU 1941 Dr. John S. Lundy anaika miyezo yothirira mwazi. Mwachiwonekere popanda kuchirikizidwa ndi ukatswiri wa zamankhwala uliwonse, iye anati ngati mwazi wamtengatenga mthupi la wodwala (hemoglobin), womwe uli magwero onyamula mpweya wa oxygen m’mwazimo, uchepa kufikira pachiŵerengero cha magramu khumi kapena kucheperapo ndi nusu yokha ya mwazi, pamenepo wodwalayo afunikira kuthiridwa mwazi. Pambuyo pake chiŵerengero chimenechi ndicho chinakhala muyezo kwa adokotala.

Muyezo wa magramu khumiwu watokosedwa pafupifupi kwa zaka 30. Mu 1988 The Journal of the American Medical Association inanena mwagogogo kuti umboniwo sumachilikiza chitsogozo. Katswiri wotsimikizira kuti munthu sakumva kuwawa potumbulidwa wotchedwa Howard L. Zauder akuti iwo “waikidwa kukhala chinsinsi m’mwambo, wosaululidwa m’mabwalo, ndi wosafotokozedwa momvekera ndi ukatswiri wa zamankhwala kapena umboni wotumbidwawo.” Ena amangoutcha kukhala nthano.

Mosasamala kanthu za kuchivumbula mwamphamvu chinsinsichi, nthanoyi ikukondedwabe padziko lonse kukhala chitsogozo chabwino. Kwa akatswiri ambiri otsimikizira kuti munthu sakumva kuwawa potumbulidwa ndi adokotala ena, kuperewera kufika pamlingo wa chiŵerengero chakhumi kwa mwazi wamtengatenga mthupi nkomwe kumachititsa kuthiridwa mwazi kuti mwazi wochepawo uchulukitsidwe. Zimachitika zokha.

Mosakaikira, ichi nchimene chimachititsa kugwiritsiridwa ntchito mopambanitsa kwa mwazi ndi zam’mwazi lerolino. Dr. Theresa L. Crenshaw, amene anatumikira Pantchito Yotumidwa ndi Prezidenti Kufufuza Mliri wa Kachirombo Kosaululidwa Msanga ndi Zotetezera Thupi Lamunthu, anayerekeza kuti mu United States mokha, mamiliyoni aŵiri a kuthiridwa mwazi kosayenerera amachitidwa chaka chirichonse ndikuti pafupifupi theka la kuthiridwa mwazi wosungidwawo konse kukadapewedwa. Unduna wa Zaumoyo ndi Makhalidwe Abwino m’Japan unatsutsa “kugwiritsiridwa ntchito kosasankha kwa kuthira mwazi” m’Japan, limodzinso ndi “chikhulupiriro chawo cholakwika m’mankhwala awowo.”

Vuto la kuyesa kuwonjezera mwazi woperewera mwa kuthira mwazi njakuti kuthiridwa mwaziko kungakhale kwakupha kwenikweni kuposa kuperewera kwa mwaziko. Mboni za Yehova, zimene zimakana kuthiridwa mwazi kwakukulukulu pamaziko a chipembedzo, zathandiza kutsimikizira mfundoyi.

Inu mungakhale munawonapo mitu yankhani ya m’nyuzipepala yosimba kuti mmodzi wa Mboni za Yehova anafa chifukwa cha kukana kuthiridwa mwazi. Mwachisoni, nkhanizo kaŵirikaŵiri sizimasimba nkhani yonse yomwe inachitika. Mobwerezabwereza, kumakhala kukana kwa dokotalayo kutumbula, kapena kutumbula mofulumira kwambiri, kumene kumaphetsa Mboni. Adokotala ena otumbula amakana kugwira ntchitoyo atamanidwa ufulu wa kuthira mwazi ngati mwazi wamtengatenga uperewera kufika pamlingo wa chiŵerengero chakhumi. Komabe, adokotala otumbula ambiri atumbula Mboni mwachipambano pamene mwazi wamtengatenga uli pamlingo wa chiŵerengero cha zisanu, ziŵiri, kapena ngakhale wochepera wokha. Dokotala wotumbula wotchedwa Richard K. Spence akuti: “Chomwe ndapeza kwa Mboni nchakuti kuchepa kwa mwazi wamtengatenga sikumabweretsa imfa nkomwe.”

Unyinji wa Zolowa Mmalo

‘Mwazi kapena imfa.’ Umu ndimo mmene adokotala ena amafotokozera zolowa mmalo zoyang’anizana ndi odwala omwe ali Mboni. Komabe, kunena mwantheradi, pali zosankha zolowa mmalo kuthira mwazi zambiri. Mboni za Yehova sizimakondwera nako kufa. Izo zimakondweretsedwa ndi mankhwala olowa mmalo. Popeza kuti Baibulo limaletsa kudya mwazi, izo mopepuka sizimalingalira kuthiridwa mwazi kukhala cholowa mmalo.

M’June wa 1988, Lipoti Lantchito Yotumidwa ndi Prezidenti Kufufuza Mliri wa Kachirombo Kosaululidwa Msanga ndi Zotetezera Thupi Lamunthu linapereka malingaliro akuti odwala onse adzipatsidwadi chimene Mboni zinakhala zikuchipempha kwa zaka zambiri, chakuti: “Chikalata cha kumvana kaamba ka kuthiridwa mwazi kapena mbale zake chiyenera kuphatikiza mawu olongosola ngozi zophatikizidwa . . . ndi mawu onena za zoyenerera zolowa mmalo mankhwala a kuthiridwa mwazi wochokera mwa munthu wina.”

Kufotokoza m’mawu ena, odwala ayenera kupatsidwa chosankha. Chimodzi cha chosankhacho ndicho kuthiridwa mwazi wochokera mwa munthu mwiniyo. Mwazi wa wodwala mwiniyo umasungidwira kwina pamene akutumbulidwa ndikubwezeretsedwanso m’misempha ya wodwalayo pambuyo pake. Pamene kachitidweka kangokhala chabe magwero apambali komwe mwazi wozungulira mdongosolo la thupi la wodwalayo umangopitira, iko kamakhala kovomerezedwa ndi Mboni zambiri. Adokotala otumbula amagogomezeranso phindu la kuwonjezera mwazi wambiri mwa wodwalayo ndi mankhwala opanda mwazi ndikuleka thupi kudzipangira maselo ake ofiira amwazi. Malusowa agwiritsiridwa ntchito mmalo mwa kuthiridwa mwazi popanda kuwonjezera ngozi ya imfa. Kwenikweni, iwo angawonjezere chisungiko.

Mankhwala odzetsako lonjezo otchedwa recombinant erythropoietin avomerezedwa kugwiritsiridwa ntchito pamlingo wokhala ndi polekezera posachedwapa. Iwo amafulumizitsa thupi kudzipangira maselo ake ofiira am’mwazi, nathandizira kwenikweni munthu kudzipangira mwazi wake.

Asayansi adakafufuzabe cholowa mmalo mwazi chotsimikizirika chomwe chingatsanzire ntchito yochitidwa ndi magwero ake ozizwitsa onyamulira mpweya wa oxygen. Mu United States, nkosapepuka kwa opanga zolowa mmalozi kuti zopangidwa zawo zivomerezedwe. Komabe, monga momwe wopanga wina anatsutsira motere: “Ngati munalingalirapo kupereka mwazi ku FDA [Food and Drug Administration] kuti ukavomerezedwe, simukanaupempherera nkomwe kuti upimidwe pakuti nkwapaizonidi.” Chikhalirechobe, ziyembekezo nzazikulu zakuti mankhwala otsimikizirika adzapezedwa omwe adzavomerezedwa kukhala chinthu cholowa mmalo kunyamulira mpweya wa oxygen kaamba ka mwazi.

Chotero ziripo zosankha. Zomwe zatchulidwazo nzochepa pa zomwe ziripo. Monga mmene Dr. Horace Herbsman, profesa wa kutumbula kwamchipatala, analembera motere m’magazine a Emergency Medicine: “Nkwachiwonekere . . . kuti zosankha zolowa mmalo mwazi tiri nazo. Ndithudi, mwinamwake chokumana nacho chathu ndi Mboni za Yehova chingafotokozedwe kutanthauza kuti sitimafunikira kudalira pa kuthiridwa mwazi, wokhala ndi kucholowanacholowana kwake konseko, monga mmene tinazilingalira kalelo.” Ndithudi, palibe nchimodzi chomwe cha izi chomwe chiri chatsopano. Monga mmene The American Surgeon inafotokozera motere: “Mfundo yakuti kutumbula kowopsa kwambiri kungachitidwe mwachisungiko popandadi kuthiridwa mwazi yafotokozedwa kwambiri m’zaka 25 zapitazo.”

Koma ngati mwazi ngwangozi, ndipo zosankha zolowa mmalo mwake zakuugwiritsira ntchito mwachisungiko zilipo, pamenepo kodi nchifukwa ninji anthu mamiliyoni ambiri akuthiridwa nawo mosayenerera—ambiri a awa popanda nkudziŵa komwe, pamenenso ena motsutsana ndi zofuna zawo? Lipoti la ntchito yotumidwa ndi prezidenti kufufuza AIDS mwapang’ono ikunena kuti chiri kulephera kuphunzitsa adokotala ndi ogwira ntchito m’zipatala ponena za zolowa mmalo mwakezo. Ilo limaperekanso liwongo pa mfundo inanso iyi: “Malikulu a mwazi a mmadera ena akhala onyumwa kupititsa patsogolo njira zimene zimachepetsa kugwiritsira ntchito mankhwala a kuthiridwa mwazi, popeza kuti malipilo antchito yawo amachokera m’kugulitsa mwazi ndi zam’mwazi.”

Kuzifotokoza m’mawu ena tingangoti: Kugulitsa mwazi ndi bizinesi yaikulu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena