Madzi Amtengo Wapatali Kwenikweni m’Dziko
Ngakhale ngati kuthira mwazi kutachotsedwa kukhala zotulutsidwa zakaŵirikaŵiri za indasitale yaumbombo, chimenecho sichingalongosolebe chifukwa chimene Mboni za Yehova zimaukanira. Zifukwa zawo nzosiyana kwambiri ndipo nzofunika koposa. Kodi izo nchiyani?
NKOPEPUKA kusalilingalira mosamalitsa dontho lamwazi. Ilo limakha ngati khungu lakhodoledwa kapena litabaidwa, limakhala dontho lochepa lofiirira, ndipo timalifikisa kapena kungolipukuta osalingalira kanthu nkomwe.
Komatu tikadati tidzichepetse kukhala tianthu tating’onong’ono ngati nsonga yasingano kwakuti dontholi nkuwoneka kwa ife lalikulu ngati phiri, mkufiira kwake kwakuyamo tikadaonamo dziko lodzala ndi kucholowanacholowana kodabwitsa ndikwadongosolo. Mkadontho kamodziko, m’makhala modzala ndi makamu amaselo: maselo ofiira a mwazi okwanira 250,000,000, maselo oyera a mwazi okwanira 400,000, ndi magwero othandizira kuumitsa mwazi okwanira 15,000,000, awa ngomwe angatchulidwe okha. Atabalalitsidwira pantchito mumtsempha wamwazi, khamu lirilonse limachita ntchito yakeyake.
Maselo ofiira amathamangathamanga mlukanelukane wocholowanacholowana wa dongosolo ya mitsempha, nanyamula mpweya wa oxygen kuchokera kumapapo nanka nawo ku selo lirilonse mthupimo natulutsanso mpweya wotha ntchito wa carbon dioxide. Timaseloti ntating’onong’onodi kwakuti tutasonkhanitsidwa mumtolo umodzi tokwanira 500 tingatalike masentimita 0.1 okha. Komabe, mutasonkhanitsa mumtolo umodzi maselo ofiira onse mthupi mwanu iwo angafikire pamtunda wa makilomita 50,000! Litapanga pafupifupi ulendo wa masiku 120 kuzungulira thupi nthaŵi zokwanira 1,440 patsiku, selo lofiira limaletsedwa kugwira ntchito. Magwero ake odzala ndi zakudya amazungulutsidwanso mwadongosolo, zotsala zonse zimataidwa. M’kamphindi kalikonse, maselo ofiira mamiliyoni atatu amachotsedwamo, pamenenso atsopano m’chiŵerengero chimodzimodzichi amapangidwa m’mafuta am’fupa. Kodi thupi limadziŵa bwanji kuti selo lofiira lafikira msinkhu woyenerera kuleka kugwira ntchito? Asayansi azizwitsidwa nazo. Komatu mogwirizana ndi katswiri wina wa zamankhwala, popanda dongosololi la kuwalowa mmalo maselo ofiira akale ndi atsopano, “mwazi wathu ukadakhala wouma gwa ngati konkiri m’milungu ingapo.”
Panthawiyi, maselo oyera amamwazikana m’dongosololo, nafunafuna ndikupha adani osafunikiramo. Magwero oumitsa mwazi amasonkhanitsidwa mofulumira patakhala chilonda nayamba ntchito youmitsa mwazi natseka chilondacho. Maselo onsewa ngolenjekeka mmadzi otuwa mopenyeka, otchedwa plasma, yomwe payokha njopangidwa ndi misanganizo mazana ambiri, yambiri ya iyo imachita ndandanda ya ntchito yaikulu ya thupi.
Asayansi ndi nzeru zawo zonse zaluntha kwambirizo samamvetsetsa ntchito zonse zimene mwazi umachita, kusatchula kulephera kwawo kupanga wofanana nawo. Kodi madzi ocholowanacholowana ozizwitsawa angakhale chinthu china choposa kukhala ntchito ya Mpangi Wamkulu? Ndipo kodi kumapanga nzeru kulingalira kuti Mlengi wamkulu woposa munthuyu ali nako kuyenerera kwa kulamulira mmene zolengedwa zake ziyenera kugwiritsiridwa ntchito?
Mboni za Yehova zakhala zikulingalira motero nthaŵi zonse. Iwo amailingaira Baibulo kukhala kalata yochokera kwa Mlengi wathu imene ili ndi zitsogozo zake zonena za mmene tingakhalire ndi moyo wabwino wothekera; ilo ndilo bukhu lomwe silikukhala chete pankhani ya mwaziyi. Levitiko 17:14 ikuti: ‘Moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake’—ndithudi, osati kwenikweni, pakuti Baibulo limanenanso kuti chinthu chamoyo chenichenicho ndicho moyo. Mmalomwake, moyo wa nyama zonse ngwogwirizanitsidwa kwenikweni ndikuchilikizidwa ndi mwazi wokhala mu izo mwazi umenewo umalingaliridwa molunjika kukhala madzi opatulika oimira moyo.
Kwa ena, ichi nchovuta kuchimvetsetsa. Tikukhala m’dziko limene liri ndi zopatulika zochepa. Moyo weniweniwo sumalingaliridwa kukhala wamtengo wapatali monga mmene ufunikira kukhalira. Pamenepo, nkosadabwitsa kuti mwazi umagulidwa ndi kugulitsidwa mofanana ndi katundu wina aliyense. Koma anthu amene amalemekeza zikhumbo za Mlengi samaulingalira mwanjirayo. ‘Musadye mwazi’ ndilo linali lamulo la Mulungu kwa Nowa ndi mbadwa zake—anthu onse. (Genesis 9:4) Zaka mazana asanu ndi atatu pambuyo pake Iye anailemba lamuloli m’Chilamulo chake kwa Aisrayeli. Zaka mazana khumi ndi zisanu pambuyo pake iye analigogomezeranso kumpingo Wachikristu nati: ‘Musale mwazi.’—Machitidwe 15:20.
Mboni za Yehova zimamamatira ku lamulo limenelo kwakukulukulu chifukwa chakuti zimafuna kumvera Mlengi wawo. Kupyolera mu imfa yansembe ya Mwana wake wokondedwa, Mlengi waŵapatsa kale anthu mwazi wopulumutsa moyo. Iwo ungatalikitse moyo osati kwa miyezi kapena zaka zoŵerengeka zokha koma kosatha.—Yohane 3:16; Aefeso 1:7.
Kuwonjezera apa, kupewa kuthiridwa mwazi kwatetezera Mboni kungozi zikwi zambirimbiri. Anthu ambirimbiri pambali pa Mboni za Yehova nawonso akukana kuthiridwa mwazi lerolino. Ziungwe za zamankhwala zikuvomereza mwapang’onopang’ono ndikuchepetsa kugwiritsira ntchito kwawo mwazi. Monga mmene Surgery Annual inanenera motere: “Mwachiwonekere, kuthiridwa mwazi kwachisungiko kwenikweni nkomwe sikukuperekedwa.” Magazine a Pathologist anadziŵitsa kuti Mboni za Yehova zaumirira kwanthaŵi yaitali kuti kuthiridwa mwazi simankhwala ofunikira. Iyo inawonjezera kuti: “Pali umboni wolingalirika wochilikiza chigamulo chawo, mosasamala kanthu za zitsutso zochokera kwa osunga mwazi kutsutsa ichi.”
Kodi inuyo mungakhulupirire yani? Wokhalako wanzeru amene analinganiza mwazi? Kapena anthu amene akupanga kugulitsa mwazi kukhala bizinesi yaikulu?
[Zithunzi patsamba 15]
Dongosolo lamitsempha la anthu, lokhala ndi timinyewa (chithunzi chamkati) tomwe tiri tating’ono kwambiri kwakuti maselo amwazi amakakamizidwa kupyolamo imodzi ndi imodzi