Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 1/8 tsamba 22-24
  • Kodi Ndiyenera Kugwira Ntchito Pamene Ndidakali Pasukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiyenera Kugwira Ntchito Pamene Ndidakali Pasukulu?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chimene Amagwirira Ntchito
  • Kuŵerengera Mtengo
  • Kusungabe Kulinganizika Kwanu
  • Kodi Ndiyenera Kupeza Ntchito Yogwira Pambuyo Poŵeruka Kusukulu?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Ndingakonzekere Motani Kukagwira Ntchito m’Dziko?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Ntchito Yapambuyo Poŵeruka Kusukulu Idzandithandiza Kukula?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuika Nzeru Kumaphunziro Pasukulu?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 1/8 tsamba 22-24

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiyenera Kugwira Ntchito Pamene Ndidakali Pasukulu?

MASIKU asukulu ngotanganitsa kwa achichepere ambiri. Malangizo a m’kalasi amatenga mbali yaikulu ndithu ya tsiku lirilonse la mlungu. Homuweki ndi kuphunzira zimatenga madzulo. Ndipo pakatipo pamakhala ntchito zambiri zapanyumba zolira chisamaliro.a

M’maiko a Kumadzulo achichepere amsinkhu wopita kusukulu angamayembekezere mapeto a mlungu monga nthaŵi yosangalala ndi kupumula. Koma m’mbali zambiri zadziko, mapeto a mlungu sali konse nthaŵi yopumula. Mwachitsanzo, m’madera akumidzi a Afirika, achichepere kaŵirikaŵiri amathera masiku akumapeto kwa mlungu akuthandiza makolo awo kumunda, kukwaniritsa nthaŵi yomwe anaiwononga mkati mwa mlungu wawo wopita kusukulu. Ndipo pakati pa Mboni za Yehova, achichepere ali ndi thayo lowonjezereka la kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira kukhomo ndi khomo ndikupita kumisonkhano Yachikristu.—Ahebri 10:23-25.

Chotero kungawoneke kukhala kosayenerera kuti achichepere aku Afirika angafune kusenza mtolo wowonjezereka wa ntchito yakuthupi. Koma achichepere ambiri oterowo akugwira ntchito ndipo akutero m’njira zambiri: kulima minda yawo ndikugulitsa mbewuzo, kuluka nsalu ndi zolukira zakumanja, kapena kuluka mitanga ndikuigulitsa pamsika. Ndipo enabe amasodza, kugulitsa manyuzipepala, ndikutchola kapena kugulitsa zipatso.

Komabe, kodi nchifukwa ninji achichepere ameneŵa akutenga ntchito yakuthupi? Kodi zimatanthauzadi kuti nanunso mufunikira kuchita zofananazo?

Chifukwa Chimene Amagwirira Ntchito

Achichepere ena amakakamizika kotheratu kugwira ntchito chifukwa cha mikhalidwe yomwe sangathe kuilamulira, monga ngati imfa ya kholo. (Ichi chingasiye wachichepere wopanda winawake wolipirira sukulu yake.) Kumbali ina, achichepere ena amagwira ntchito kuti akhale osadalira pa makolo awo.

Talingalirani za Kofi, mwamuna wachichepere wa ku Ghana. Pamene anali kusukulu ya ukatswiri wa zopangapanga, ankagwira ntchito pafamu kwa maola aŵiri tsiku lirilonse pambuyo poŵeruka kusukulu.b Kofi akulongosola kuti: “Makolo anga anapereka zosoŵa zanga pamene ndinali pasukulu yapulaimale. Koma sindinafune kupitiriza kudalira pa iwo kaamba ka chosoŵa changa chirichonse. Chotero ndinayamba ntchito yakuthupi. Ndinadzimva kukhala wachimwemwe kwenikweni kukhala wokhoza kudzigulira mabuku ndi zolembera ndikudzilipirira basi popita kusukulu.”

Mchimwene wake wa Kofi, Moses mofananamo adali ndi ntchito. Pamene anali kusukulu ya sekondale, Moses ankaphunzitsa payekha ana asukulu achichepere. Koma pamene kuli kwakuti ndalama za Kofi moyenerera zinkalipirira zosoŵa zake, ndalama zina za Moses zinkaperekedwa kuchilikiza banja lake. Chifukwa ninji? Pokhala wochokera ku banja la ana asanu ndi atatu, iye analingalira motere: “Kugwira kwanga ntchito yaganyu kunapatsa makolo anga mpumulo winawake m’kusamalira zosoŵa zanga ndi za azichimwene ndi azichemwali anga.” Iye akuvomerezanso kuti amadzimva wokhutira chifukwa chokhala wokhoza kudzigulira zinthu.

Kuthandiza makolo anu pamene kulidi kofunika kutero kungakhale njira imodzi yowalemekezera. (Aefeso 6:1, 2) Komabe, panthaŵi imodzimodziyo, palibe cholakwika kwenikweni nkugwira ntchito kotero kuti mukhale ndi ndalama zanu zanu zoziwononga.

Kukhala ndi ntchito kungakupangitseninso kudzimva kukhala wachichepere wathayo. Kungathandize wachichepere kuzoloŵera maluso amene pambuyo pake angagwiritsiridwe ntchito kuchilikiza banja. Mwachitsanzo, Yesu Kristu iyemwini anaphunzira ntchito yopala matabwa mwakugwira ntchito ndi atate wake omlera monga wachichepere. (Mateyu 13:55; Marko 6:3) Komabe, ‘yafupika nthaŵi yotsalako’ ya dziko lino, ndipo wachichepere wanzeru amatsimikizira kuti nthaŵi yake ikugwiritsiridwa ntchito mopindulitsa. (1 Akorinto 7:29; Aefeso 5:16) Choncho musanayambe ntchito, muyenera kupenda nsonga zonse zoloŵetsedwamo—kuphatikizapo zolinga zanu zenizenizo.

Kuŵerengera Mtengo

Nawa mafunso ena omwe mungaŵalingalire: Kodi makolo anga amafunikiradi kapena kukhumba thandizo langa landalama? Kapena kodi ngofunitsitsa kupirira ndizochepa kotero kuti ndingalimbikire ntchito yakusukulu ndi kukula kwauzimu? Kodi ndikuzifunikiradi ndalama zowonjezerekazo, kapena kodi ndikuvomereza ‘chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo’?—1 Yohane 2:16.

Mwamuna wanzeru Solomo anafotokoza motere: “Ndaphunziranso chifukwa chimene anthu amagwirira ntchito zolimba kuti apambane: nchifukwa chakuti amasirira zinthu zimene anansi awo ali nazo. Koma nzopanda pake. Nkofanana ndi kuthamangitsa mphepo. . . . Nkwabwino kukhala ndi zochepa, ndi mtendere wamaganizo, kuposa kukhala wotanganitsidwa nthaŵi zonse ndi manja onse aŵiri, kuyesayesa kugwira mphepo.”—Mlaliki 4:4-6, Today’s English Version.

Mfundo ina imene ingafunikire kuilingalira ndiyo chiyambukiro chimene kugwira ntchito kungakhale nacho pakuphunzira kwanu. Kofi, wotchulidwa koyambirirayo, akukumbukira motere: “Pamene ndinali m’chaka choyamba kusukulu ya ukatswiri wa zopangapanga pamene sindinkagwira ntchito yakuthupi, ndinkachita bwino m’maphunziro. Kenaka chinafika chaka chachiŵiri pamene ndinayamba ntchito yakuthupi, ndipo magiredi anga anabwerera m’mbuyo. Komabe ndinakhozabe kuchita bwino, koma zonsezo zidali zotopetsa.” Mosangalatsa, phunziro lofufuza lina lochitidwa mu United States linapeza kuti “kugwira ntchito kumatsogolera ku kutsika kwa kuchita bwino m’sukulu ndi kuchepetsa kudziloŵetsamo m’sukulu kwa wachichepere.”

Kodi mukumkumbukira Moses, mchimwene wake wa Kofi, amene adali ndi ntchito yophunzitsa? Iye akuvomereza kuti: “Ngati susamala, ungayambe kutenga ophunzira ambiri kuposa omwe angaphunzitsidwe m’nthaŵi yochepa yomwe ilipoyo.” Mawuli, mwamuna wina waku Afirika, ankagwira ntchito yaganyu monga msodzi. Iye akuti: “Padali chiyeso chachikulu pamene nsomba zinkafa zambiri pagombepo. Chisonkhezero chidali chakuleka sukulu ndikupita kukapanga ndalama zowonjezereka. Anyamata ambiri m’mudzimo anachita chimenecho naleka sukulu.”

Sukulu kuphatikizapo ntchito zingatherenso wachichepere nyonga kufikira pakumufooketsa mwauzimu. Chingakhale chovuta kwa iye kupezeka pamisonkhano Yachikristu kapena kutchera khutu pamene ali kumeneko. Phunziro laumwini la Baibulo ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo zingakankhidwire pambali.

Kusungabe Kulinganizika Kwanu

Komabe, pambuyo posanthula mfundo zonsezi, inu ndi makolo anu mungalingalire kuti kugwira kwanu ntchito inayake kungakhale kopindulitsa. Kodi mungaugwiritsire ntchito bwino motani mkhalidwewo?

Kudzilanga nkofunika koposa. Mtumwi Paulo analankhula za zoyesayesa zake, nati: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo.” (1 Akorinto 9:27) Mukafunikira kudzilanga kuti musunge—osati kuwononga—ndalama zimene mumalandira. Mudzafunikiranso kudzilanga kuti mugwiritsire ntchito moyenerera nthaŵi yotsala. Ndithudi, kusanguluka ndi kupumula kokwanira ziri ndi malo ake ndipo zingapititse patsogolo ntchito yopindulitsa. Koma samalirani kuti zizoloŵezi ndi zosangulutsa sizikulanda malo a homuweki ndipo ngakhale zinthu zauzimu.

Chotero mufunikira kupanga ndandanda yotsimikizirika ya nyengo zakuphunzira—ndipo mamatirani ku iyo. Mwachitsanzo, chingakhale chabwino koposa kuyamba homuweki yanu mwamsanga mutaŵeruka kuntchito, osadikira kufikira mutatha kudya chakudya chamadzulo pamene mumayamba kuwodzera. Ena amakonda kugona mofulumira ndikusamalira maphunziro awo mmamawa. Mulimonse mmene zingakhalire, pangani nyengo zakuphunzira kwanu kukhala zopindulitsa kwenikweni. Peŵani kuseŵera nyimbo kapena kudziloŵetsa m’zocheutsa zina. Homuweki yanu ingayendenso bwino ngati mupereka chisamaliro chachikulu ku kumvetsera kwanu m’kalasi, kulemba nsonga zazikulu ndi tsatanetsatane wochilikiza nsongazo.—Yerekezerani ndi Luka 8:18.

Komabe, zofunika koposa zonse ndizo zosoŵa zanu zauzimu. (Mateyu 5:3) Kuti zimenezi zikwaniritsidwe, muyeneranso kuika pambali nthaŵi ya phunziro Labaibulo laumwini, misonkhano Yachikristu, ndi kukhala ndi phande muuminisitala wapoyera. Zowonadi, kugwira ntchito ndikupita kusukulu nzolira nthaŵi. Koma ngati mufunikira kuchita zonse ziŵirizo, patsani zinthu zauzimu malo oyamba. Pempherani mosalekeza kwa Yehova Mulungu kuti akuthandizeni kusungabe kulinganizika kwanu. Ngati musankha ntchito kuwonjezera pa sukulu, iye angakulimbikitseni kuchilimika ndi zitsenderezo za mkhalidwewo.—Yesaya 40:29-31.

[Mawu a M’munsi]

a Nkhaniyi ikufotokoza mkhalidwe woyang’anizana ndi achichepere akumaiko otukuka kumene. Komabe, malingaliro olembedwa munomu ngozikidwa pa malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo ndipo chotero adzatsimikizira kukhala othandiza kwa achichepere padziko lonse.

b M’maiko ena, pambuyo pa sukulu ya pulaimale wachichepere amasankha kaya kupita ku sukulu ya sekondale, kapena yapamwamba, (imene imaphunzitsa maphunziro osiyanasiyana) kapena kusukulu ya ukatswiri wa zopangapanga.

[Chithunzi patsamba 24]

Achichepere ena aku Afirika amagwira ntchito pambuyo poŵeruka kusukulu. Koma kodi ndiati omwe ali maubwino ndi kuipa kwakuchita motero?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena