Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 1/8 tsamba 9-11
  • Kodi Ndingakonzekere Motani Kukagwira Ntchito m’Dziko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingakonzekere Motani Kukagwira Ntchito m’Dziko?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Lingaliro Labwino la Ntchito
  • Sankhani Maphunziro Oyenerera
  • Pamene Zosankha Ziri Zochepa
  • Kudzimana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuika Nzeru Kumaphunziro Pasukulu?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Ndiyenera Kugwira Ntchito Pamene Ndidakali Pasukulu?
    Galamukani!—1991
  • Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • “Kodi Ndichite Chiyani?”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 1/8 tsamba 9-11

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingakonzekere Motani Kukagwira Ntchito m’Dziko?

“NDIMAKHALA wamantha ndi wachimwemwe panthaŵi imodzimodzi!” Anatero Maureen wazaka 16 pamene anafunsidwa mmene anamverera ponena za kukagwira ntchito tsiku lina m’dziko. Nkwachibadwa kumva wamantha pamene mulingalira zakuyamba ntchito—ngakhale ngati mukukalimira chonulirapo chimenecho. Pamene René wachichepere anali pafupi kumaliza sukulu, anati: “Pambuyo povutika ndi maphunziro kwa zaka 12, ntchito idzakhala chinthu chosangalatsa.”

Mosasamala kanthu za malingaliro anu, mwina tsiku lina mudzakhala pantchito m’dziko. Kodi mungakonzekere motani kaamba ka tsiku limenelo? Kupita kusukulu kumakupatsani mwaŵi wakukulitsa zizoloŵezi zabwino, monga ngati kusunga nthaŵi. Ndiponso, achichepere amene adakali pasukulu akhoza kupeza chidziŵitso mwakugwira ntchito zaganyu. Komabe, kuti mukonzekere bwino kukagwira ntchito m’dziko, nkofunika kwambiri kulingalira mosamalitsa makosi amene mumasankha pasukulu.

Lingaliro Labwino la Ntchito

Choyamba, muyenera kudziŵa chimene mumafunira kugwira ntchito. Achichepere ena samalingalira zinthu zina koma unyinji wamalipiro basi. Kunena zowona, ‘ndalama zichinjiriza’ ndipo nzofunika m’moyo. (Mlaliki 7:12) Koma Baibulo nlowona pamene limanena kuti ‘moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.’ (Luka 12:15) M’bukhu lakuti Yes—I Can!, lolembedwa ndi Barkai, Barkai ndi Yeo, akonziwo akupereka uphungu uwu: ‘Musagwere mumsampha wakungofuna malipiro apamwamba.’ Iwo akuwonjezera kuti: “Kukhutiritsidwa ndi ntchito kuli kofunika kaamba ka chimwemwe chanu chamtsogolo.” Paulo wazaka khumi ndi zisanu mphambu ziŵiri anasonyeza lingaliro labwino pamene ananena kuti: “Ndingangofuna malipiro okwanira malinga ngati ndikusangalala ndi ntchito yanga.”

Komabe, ngati ndinu Mkristu, palinso zina zofunika kuzilingalira. Ngakhale ntchito yosangalatsa, yapamwamba koposa sidzakhutiritsa chosoŵa chanu chauzimu. Ndiiko komwe, ‘choyenera anthu onse’ ndicho ‘kuwopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake.’ (Mlaliki 12:13) Popeza kuti lamulo la Mulungu kwa Akristu nlakuti ‘apange ophunzira,’ Mboni za Yehova zambiri zachichepere zimapanga makonzedwe akuyamba ntchito yakukhala apainiya, kapena alaliki anthaŵi zonse. (Mateyu 28:19, 20) Msungwana wa ku South Africa wotchedwa Shulamite anachita zimenezo. Ndipo iye akunena kuti “amapeza chikhutiro chachikulu cha kuthandiza anthu m’kusoŵa kwawo kwauzimu.”

Mwinamwake nanunso mumakhumba kukhala ndi phande muuminisitala wanthaŵi zonse. Komabe, mwachiwonekere mudzafunikira kugwira ntchito kuti mudzisamalire. Tsiku lina mudzafunikira kusamalira banja. Kumbali ina, mikhalidwe singakuloleni kukhala mpainiya, ndipo mungafunikire kufuna ntchito yanthaŵi zonse. Mulimonse mmene zingakhalire, kodi simungakonde kupeza ntchito imene ingakuloleni kukhala ndi phande lokwanira muutumiki wa Mulungu monga momwe kungathekere? Zambiri zidzadalira pakosi imene muisankha pasukulu.

Sankhani Maphunziro Oyenerera

M’maiko ena wachichepere akhoza kusankha pakati pa maphunziro akuphunzitsa, amalonda, aukatswiri wazopangapanga, ndi aumisiri. Kaŵirikaŵiri nkwanzeru kulingalira mtundu wa ntchito zimene zimapezeka m’dziko mwanu. Panthaŵi imodzimodziyo, mutha kupenda nzeru zanu ndi zofuna zanu. Motani? Mwakupanga ndandanda ya zinthu zonse zimene mumakonda kapena zimene mumazichita bwino. Kodi ndimasamu? Sayansi yamakompyuta? Umakanika? Phatikizanipo zochita zakukhosi kwanu ndi zinthu wamba zimene mumakonda. Ichi chingakupatseni lingaliro la mtundu wa ntchito imene ingakulingeni bwino koposa ndi kosi imene ingakutsogolereni kuntchito imeneyo. Kukambirana ndi makolo anu kapena achikulire ofikapo kungakuthandizeninso kupenda maluso anu ndi zikhoterero zanu mowona mtima.—Yerekezerani ndi Miyambo 15:22.

Mwachitsanzo, kodi ndinu wodziŵa kuyanjana ndi anthu? Pamenepo mwina mungakonde kulingalira maphunziro amene angakupezetseni ntchito zakugulitsa kapena ntchito zina zofunikira kuyanjana ndi anthu. Kumbali ina, ngati muli ndi luso lakugwira ntchito ndi manja anu, mungalingalire kutenga kosi yaumisiri. Mulimonse mmene zingakhalire, alaliki ambiri anthaŵi zonse amadzichirikiza ndi maluso amene anawaphunzira ku sukulu yasekondale. Ena apeza ntchito zaganyu m’ntchito zomanga, kukonza zamagetsi, kupala matabwa, kusula ziŵiya panyumba, ntchito zakompyuta, kapena ukalaliki.

Kwa Damaris, mkazi wachichepere wa ku Colombia, South America, kuphunzira typing ndi bookkeeping kunamthandiza. Iye anapeza ntchito yaukalaliki ya theka latsiku imene inachirikiza ntchito yake yakulalikira. Akristu ena akwaniritsa zosoŵa zawo mwantchito yakuyeretsa maofesi, kukongoletsa pabwalo, ndi zina zotero.

Pamene Zosankha Ziri Zochepa

Komabe, sisukulu zonse zimene zimapereka maphunziro antchito okwanira; ena amalephera ngakhale kupereka maluso oyambirira akuŵerenga ndi kulemba kwa ana. M’malo ena maphunziro owonjezereka angakhale ofunikira kaamba ka kupeza pafupifupi mtundu uliwonse wa ntchito. Pansi pa mikhalidwe yoteroyo, mungafune kudziŵa ngati pali maphunziro ochitira pantchito kapena zigwirizano zakumaloko zophunzitsa ntchito. Chosankha china chingakhale kosi yaifupi pasukulu yophunzitsa ntchito zimene zimapezeka. Mokondweretsa, ena atenga maphunziro oterowo kuwonjezera pa ntchito yawo monga alaliki anthaŵi zonse.

Achichepere a m’maiko osatukuka angapeze kuti zosankha za maphunziro ndi sukulu nzochepa kwambiri. Katiti, mwamuna wachichepere wokhala m’tauni ya kumalo akumidzi kum’mwera kwa Afirika, analibe chosankha koma kuphunzira Chilatini, masamu, ndi physical science, ngakhale kuti maphunziroŵa sanali aphindu kwenikweni m’kupeze ntchito m’dzikolo. Komabe, Katiti anachita mwaŵi wakupeza ntchito. Motani? Mwakugwiritsira ntchito maluso ake m’zosoŵa zakumaloko. Pamene Katiti anamaliza sukulu, anadzichirikiza mwakulima ndi kugulitsa ndiwo zamasamba, kuluka ndi kugulitsa nduŵira ndi zipewa zaubweya, ndipo ngakhale kugulitsa mankhwala ololedwa mwalamulo m’malo akumidzi. Chifukwa chakuti sukulu inamphunzitsa maluso akukambitsirana ndi anthu, iye anakhoza kuchita bwino lomwe ntchito zosiyanasiyana zimenezi.

Bukhu lakuti Choosing Your Career and Your Higher Education limanena kuti luso la “kulankhulana, kumvetsetsa ndi kumvedwa nlofunika kwambiri” pantchito. M’ntchito zambiri, kaya ikhale luso lazopangapanga, malonda, kapena yakuphunzitsa, imafunikira maluso akulankhulana. Chotero, ngakhale ngati sukulu yanu simapereka maphunziro antchito yakutiyakuti, gwirani ntchito zolimba kuti mukhale aluso m’kulemba, kulankhula, ndi kumvetsera. Chithunzi chimene mumapereka kwa amene angakulembeni ntchito chidzadalira kwakukulukulu pa luso lanu lakulankhula; ndilo lingakupangitseni kupeza ntchito imene mumaifuna. Pakati pa Mboni za Yehova, achichepere ambiri akulitsa maluso awo akulankhulana mwakukhala ndi phande mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki mumpingo Wachikristu.

Kudzimana

Bukhu lakuti Your Child at School limanena kuti: “Sitinapangidwe tonse ofanana.” Achichepere ena amachita bwino m’zaumakanika, pamene kuli kwakuti ena ali ndi mphatso ya zamaphunziro. Komanso ena anadalitsidwa ndi maluso ndi kukhoza m’mbali zina za kuimba, umisiri, kapena za maseŵera anyonga. Kumadzichirikiza monga katswiri wa zamalonda kapena wophunzitsa kuimba kuli bwino, koma kulondola chuma kapena kutchuka m’mbali zimenezi kungabweretse maupandu auzimu kwa Mkristu. Kuwonjezerapo, popeza ntchito zimenezi zingakulandeni nthaŵi yochuluka ya zochita Zachikristu, monga ngati kupezeka pamisonkhano ndi kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira, kodi kukakhala kwanzeru kuthera zaka m’maphunziro ndi kupeza maluso okukhozetsani kupambana m’zimenezi?—1 Akorinto 7:29.

Mboni yachichepere yotchedwa Philip inayesa kulondola ntchito ya kuseŵera tennis. “Pomalizira pake,” akuvomereza tero Philip, “ndinafunikira kupanga chosankha pakati pa Chikristu ndi tennis. Ndinalibiretu nthaŵi yokwanira yakuti ndilondole zonse ziŵirizo mokwanira. Ndinasankha kuleka tennis, ndipo ngakhale kuti kunali kovuta panthaŵiyo, sindinachitepo chisoni kuti ndinaleka.”

Mtumwi Paulo anapanga chosankha chofananacho. Ngakhale kuti anaphunzira zamalamulo, iye anasankha kulondola uminisitala Wachikristu, akumadzichirikiza ndi malonda akupanga mahema. (Machitidwe 18:3; 22:3) Koma Paulo sanachite chisoni ndi chosankha chake. Iye anati: ‘Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitaiko chifukwa cha Kristu. . . . Ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.’—Afilipi 3:7, 8.

Mwinamwake mudzasonkhezeredwa kupanga zosankha zofananazo. Mmalo mokulitsa maluso anu m’zamaphunziro, zakuimba, kapena umisiri, mukhoza kusankha kukulitsa maluso anu auzimu. Izi zingatanthauze kuphunzira ntchito yowoneka kukhala yotsika kwa anthu ambiri. Nthaŵi zina wachichepere angaphunzire ntchito mwakugwirira pamodzi ndi makolo ŵake, kapena kuphunzira kupala matabwa, kuika mipopi, kapena ntchito zina zoterozo.

Chirichonse chimene mungasankhe m’zimenezi, lingalirani ponena za mtsogolo mwanu. Sankhani maphunziro anu mwanzeru ndipo mosamalitsa. Ndi chithandizo cha Mulungu, mudzakhala wokonzekera mokwanira kukagwira ntchito m’dziko!

[Chithunzi patsamba 10]

Ambiri amadzichirikiza okha ndi maluso ophunziridwa kusukulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena