Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/99 tsamba 8
  • “Kodi Ndichite Chiyani?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Ndichite Chiyani?”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingakonzekere Motani Kukagwira Ntchito m’Dziko?
    Galamukani!—1992
  • Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?
    Galamukani!—1998
  • Maphunziro Okhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 4/99 tsamba 8

“Kodi Ndichite Chiyani?”

1 Monga wachinyamata amene akupita kuuchikulire, mungafunse kuti, ‘Kodi ndichite chiyani ndi moyo wanga?’ Achinyamata achikristu akufuna kufutukula utumiki wawo kwa Yehova. Koma kodi mungachite bwanji zimenezi pamene mukusamaliranso maudindo auchikulire, amene amaphatikizapo kusamalira zosoŵa zanu zakuthupi? Si kwapafupi kupeza yankho.

2 Achinyamata ena amada nkhaŵa atayang’ana mkhalidwe wazachuma wa dzikoli ndi zomwe zidzachitike m’tsogolo. Angafunse kuti: ‘Kodi ndiwonjezere maphunziro anga akusukulu? Kodi ndiloŵe mu utumiki wanthaŵi zonse tsopano lino?’ Kuti munthu asankhe bwino, ayenera kuyankha funso ili moona mtima, ‘Kodi chofunika kwambiri m’moyo wanga n’chiyani?’ Ayenera kupenda zolinga zake.

3 Kodi paunyamata wanuwo n’chiyani chimene mwazindikira kukhala chofunika kwambiri? Kodi kwenikweni mukufuna kukhala wolemera, kapena mukufunitsitsa kugwiritsa ntchito moyo wanu kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu? Kukhala ndi digiri ya kuyunivesite sizitanthauza kuti mudzapeza ntchito mosavuta. M’malo mwake, anthu ambiri aphunzira maluso oti akhoza kupeza nawo ntchito mwa kupangana ndi owalemba ntchito kuti agwire kwanthaŵi yakutiyakuti, ena achita maphunziro akusukulu owaphunzitsa ntchito zina kapenanso maluso ena a manja, kapena kupita kukoleji kukachita maphunziro amene amafuna nthaŵi yochepa kwambiri ndi amene salira zambiri.

4 Khulupirirani Mawu a Yehova: Mfundo yofunika kuilingalira ndi lonjezo la Yehova Mulungu lakuti adzasamalira amene amaika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wawo. (Mat. 6:33) Limeneli si lonjezo lonama ayi. Abale ambiri amene amapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki anapeza madigiri kukoleji asanaphunzire choonadi. Koma kodi anali kuchita ntchito yanji yakuthupi? Anthu oŵerengeka okha ndiwo anali kugwira ntchito yomwe anaphunzirayo. Koma ambiri anali kugwira ntchito zing’onozing’ono za manja monga maganyu, ndipo anali okhoza kupeza ndalama ndi kudzisamalira bwino mwakuthupi kwinaku akuchita upainiya. Mwa kufutukula ntchito yawo mu utumiki, akulandira madalitso aakulu oposa mapindu alionse amene ndalama zikanawapatsa.

5 Posankha chimene muyenera kuchita mukatha maphunziro akusekondale, pendani mfundo zonse zofunika komanso pendani zolinga zanu mosamalitsa. Kuti musankhe bwino, pendani nkhani zonga ija ili mu Galamukani! ya March 8, 1998, masamba 26-28. Lankhulani ndi makolo anu, akulu, woyang’anira dera wanu, ndi apainiya achipambano am’dera lanu. Zimenezi zidzakuthandizani kusankha mwanzeru zomwe muyenera kuchita ndi moyo wanu.—Mlal. 12:1, 13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena