Nkhalango Zomazimiririka, Kutentha Komawonjezereka
KULIKHA nkhalango za kumalo otentha. Chiyambukiro cha kutentha kopambanitsa. Ngozi ziŵirizi kaŵirikaŵiri zimatchulidwa panthaŵi imodzi. Ndipo pali chifukwa chabwino chakuti: Yoyambayo imapangitsa yomalizirayo. Pamene anthu awotcha, kulambula, ndikupasula magawo aakulu a nkhalango kuti apange malo a ulimi wa ng’ombe, misewu, ndi madamu a mphamvu ya magetsi, nkhalango zimatulutsa nkhokwe zawo zazikulu za carbon m’mlengalenga. Carbon dioxide imene imatulukapo ili kokha umodzi wa mpweya umene umapangitsa mlengalenga kusunga chitungu, numatenthetsa pang’onopang’ono dziko lonse.
Malipoti aposachedwapa a Mitundu Yogwirizana akuvumbula kuti ngozi zonse ziŵirizo zingakhale zoipitsitsa kuposa mmene zinalingaliridwa. Mwachitsanzo, akatswiri achitungu oposa 300 ochokera padziko lonse anapereka chenjezo mu May 1990 kuti kutentha kwa paavareji kwa dziko lonse kudzakwera ndi 2° Celsius m’zaka 35 zotsatira ndi 6° Celsius pofika kumapeto kwa zaka zana ngati munthu sasintha chikhotererochi.
Ichi chikaimira kusintha kowopsa kwa avereji ya kutentha imene dziko lapansi lakhala nako m’zaka zikwi khumi, akutero asayansi. Pamene kuli kwakuti chiyambukiro cha kutentha kopambanitsa chakhala nkhani ya mkangano pakati pa asayansi, The Washington Post ikudziŵitsa kuti: “Asayansi amene analemba lipotilo . . . ananena kuti linaimira kugwirizana kodabwitsa pakati pa mazana ambiri a asayansi amene kaŵirikaŵiri amakangana.”
Pakali pano, lipoti lokhala ndi mutu wakuti World Resources 1990-91, linayerekezera kuti dziko likutaya nkhalango zake zakumalo otentha pa liŵiro lowirikiza ndi 50 peresenti kuposa mmene kuyerekeza koyambirira kunasonyezera. Liŵiro lakulikha nkhalango zakumalo otentha lophatikizidwa la maiko asanu ndi anayi—mu Asia, Afirika, ndi Kum’mwera kwa Amereka—linawirikiza kuposa katatu m’ma 1980! Chiwonkhetso cha dziko lonse, mogwirizana ndi lipotilo, chiri pakati pa mahekitala mamiliyoni 16 ndi 20 a nkhalango zakumalo otentha zimene zimawonongedwa chaka chirichonse.
Kulikha nkhalango kukutenga kale mbali yake. Mwachitsanzo, International Wildlife ikudziŵitsa kuti, nkhalango zamvula zapadziko ndizo mudzi wa pafupifupi mamiliyoni 5 ndipo mwinamwake mamiliyoni okwanira 30 a mitundu ya zomera ndi zinyama—“kuposa zimene zimakhala mmalo ena apamtunda zitaikidwa pamodzi.” Mitundu imeneyi ikunka ku kusoloka. Kalekale anthu openyerera mbalame ena kumbali yakumpoto ayamba kuwona kuti mbalame zimene zimasamuka nyengo iriyonse sizikuwonekawoneka.
Ku Madagascar mitundu yokwanira 80 peresenti ya zomera zochita maluŵa sizimapezeka kwina kulikonse papulaneti lino; chimodzi cha izo, rosy periwinkle, ndiwo maziko a ena a mankhwala apadziko lonse ofunika koposa oletsa kansa. Komabe, loposa theka la nkhalango za Madagascar zachepetsedwa kale kapena kugululidwiratu.
Munthu ‘akuwonongadi dziko’ m’masiku ano omalizira, monga momwe Baibulo linasonyezera kalelo kuti akatero.—Chibvumbulutso 11:18.
[Mawu a Chithunzi patsamba 27]
Abril Imagens/João Ramid