Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 2/8 tsamba 21-23
  • Kodi Ndingakhale Motani m’Banja Logaŵikana Mwachipembedzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingakhale Motani m’Banja Logaŵikana Mwachipembedzo?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbuna Zoti Zipeŵedwe
  • Kupanga Chosankha Chanuchanu Chachipembedzo
  • Kukopa Kholo Lanu Losakhulupirira
  • Kodi Ndingachite Nalo Motani Kholo Langa Limene Linachoka Panyumba?
    Galamukani!—1990
  • Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • N’chiyani Chingandithandize Kupirira Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Anamwalira?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Ndingathandize Motani Kholo Langa Limodzi?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 2/8 tsamba 21-23

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingakhale Motani m’Banja Logaŵikana Mwachipembedzo?

“Kukula kwathu kunali kovutikira. Abambo ŵanga anatsutsa chipembedzo chathu. Munali mkangano wosatha m’banja.”—Terry.

KODI mumakhala m’banja logaŵikana mwachipembedzo? Ngati nditero, mumadziŵa mmene zinthu zingakhalire zoipa ndi zovuta. Mayi ndi Bambo angavomerezane bwino lomwe kulondola zikhulupiriro zawo mosiyana, molingana ndi mmene ananenera S. Sandmel m’bukhu lake lakuti When a Jew and Christian Marry: “Kodi kuvomereza kwa munthu chipembedzo cha mnzake wamuukwati kumaphatikizapo kulola ana kuleredwera m’chipembedzo chimenecho? Yankho lowona mtima kaŵirikaŵiri nlakuti ayi.”

Mwachitsanzo, talingalirani zimene zingamachitike ngati mmodzi wa makolo anu ali mboni ya Yehova. Kholo limenelo limadzimva kukhala ndi thayo lalikulu la kukulerani ‘m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova,’ ndipo lingakhale ndi malingaliro amphamvu pa kupita kocheza, makhalidwe, kukhalamo ndi phande m’maseŵera akusukulu, kugwiritsira ntchito nthaŵi yopuma, ndi zonulirapo za ntchito yophunziridwa. (Aefeso 6:4) Komabe, kholo lanu losakhala Mboni lingakhale ndi lingaliro loyanja kumwerekera nazo zinthuzi.

Pa Sande masana Amayi angafune kuti mupite nawo ku msonkhano Wachikristu. Bambo angafune kuti mutsale nawo panyumba ndi kupenyerera maseŵera ampira pa TV. “Nthaŵi zina ndinkawachitira chisoni pang’ono abambo ŵanga,” akukumbukira motero Doug. “Iwo ankakhala kumalonda, chotero sitinkawawona mkati mwa mlungu, ndipo kumapeto a mlungu nakonso, ziŵalo zabanja zinkawasiya pamene zinanka kumisonkhano yawo. Kamodzikamodzi, ndinkaphonya misonkhano ndikutsala nawo.”

Yesu anawoneratu kuti mikhalidwe yoteroyo ikakhalako. Iye anati: ‘Ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate ŵake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi apongozi ŵake: ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.’ (Mateyu 10:35, 36) Sikuti ndiko kunali chikhumbo cha Yesu kugaŵanitsa mabanja, koma iye anadziŵa kuti mavuto akabuka ziŵalo zina zabanja zitavomereza kulambira kowona ndipo zinazo nkusatero. Funso nlakuti: Kodi muyenera kuchitanji ngati muli mumkhalidwe woterowo?

Mbuna Zoti Zipeŵedwe

Choyamba, zindikirani kuti chonulirapo ndicho kukondweretsa, osati mmodzi wa makolo anu yekha, koma Mulungu iyemwini! Iye ndiye amafuna ‘kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:24) Koma kuti muchite choncho m’banja logaŵikana mwachipembedzo, pali mbuna zoyenera kupeŵedwa.

Kulolera molakwa—Mnyamata wina amene makolo ake anasudzulana akunena motere za kukachezetsa atate ŵake osakhulupirira: “Iwo amayesayesa kundipangitsa kuchimwira chowonadi ndi Mulungu.” Iwo amachita zimenezi mwakukakamiza mwana wawo kukhalamo ndi phande m’mapwando a maholide osakhala Achikristu. “Izi zimandivutitsa maganizo,” akuvomereza motero mnyamatayo. Koma Yesu akutikumbutsa kuti: ‘Iye wakukonda atate ake, kapena amake koposa ine, sayenera ine.’ (Mateyu 10:37) Chotero limbikani nazo mtima zimene mumakhulupirira! Ngati kupempha mwamachenjera kuti musaloŵe m’machitachita okaikiritsa sikuthandiza, lidziŵitseni kholo lanu mwaulemu koma molimba kuti mukukana kulolera molakwa. Pamene kholo lanu liwona kutsimikiza mtima kwanu kosagwedezeka, chipsinjocho mwapang’onopang’ono chingachepetsedwe.

Komabe, pamafunikira kukhala wachikatikati. Afilipi 4:5 imati: “Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.” Kufatsa kumaphatikizamo kukhala wogonjera, wokonzekera kusintha. Mwinamwake mungapange makonzedwe akuthera nthaŵi yokwanira ndi kholo lanu losakhulupirira ngati limalingalira kuti likunyalanyazidwa. Kumbukiraninso kuti, muli ndi thayo kwa makolo anu onse aŵiriwo.—Aefeso 6:1.

Kukhala ‘wolinganizitsa’—Chifukwa cha lingaliro lolakwika lakukhala wopanda tsankhu, inu mungayesedwe kutsatira chipembedzo cha Amayi ŵanu chifukwa chakuti mchimwene wanu akutsata cha Bambo—kapena mosiyana. Koma kodi amenewo ndiwo maziko olimba osankhira mmene mungalambirire Mulungu? Bwanji ngati malingaliro a chipembedzo cha Amayi ngolakwika, osakhala am’malemba? “Gula ntheradi, osaigulitsa,” ikulangiza motero Miyambo 23:23.

Kutsatira mtsogoleri—Mwinamwake mumakonda kwambiri mchimwene kapena mchemwali wanu kuposa aliyense wa makolo anu. Chotero mungakhoterere kutsatira njira yachipembedzo iriyonse imene iye angasankhe kuitenga. “Ndinalingalira choncho, popeza kuti ndimachokera m’banja lalikulu,” akutero Roberto. Chotero iye anabwerera m’mbuyo mwauzimu pamene mchimwene wake wamkulu anakana kotheratu kulambira kowona ndikuchoka panyumba. “Kunandilefula kwambiri,” iye akuvomereza motero. Mosasamala kanthu kuti mchimwene wanu ngwapamtima chotani, kodi sikukakhala kupusa kumlola iyeyo kukupatutsani pakulambira Mulungu?

‘Kulekanitsa ndi kulaka’—“Pamene ndinali pafupifupi wazaka 19, abambo ŵanga anayamba kundilimbikitsa kupita kocheza,” akukumbukira motero Doug. “Amayi, omwe adali Mkristu wobatizidwa, anatsutsa lingalirolo kwamtu wagalu. Mwamsanga ndinayamba kutsatira zokonda Bambo, ngakhale kuti pansi pamtima ndinadziŵa kuti Amayi anali olondola.” Pamene makolo ali ndi miyezo yosiyana yamakhalidwe, pamakhala mpata waukulu wakuchita mwaumdyera kuŵiri kwa makolo. Mungayesedwe kugonjera kwa kholo lopatsa ufulu kwambiri.

Komabe, kupikitsanitsa makolo sikumachita kanthu mpang’ono ponse kusiyapo kungowonjezera kukangana m’banja. Ndipo kupatsidwa chilolezo chakuchita chinachake chimene mukudziŵa kuti sichanzeru kapena ncholakwa sikumakulungamitsani kwa Mulungu. ‘Kwa iye amene adziŵa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.’ (Yakobo 4:17) Mmalo mokondweretsa kholo limene limakupatsani ufulu waukulu koposa, bwanji osayesa kulabadira kholo limene likukutsogozani ‘m’njira ya moyo’?—Miyambo 6:23.

Kupanga Chosankha Chanuchanu Chachipembedzo

Komabe, achichepere ena angasokonezeke osadziŵa yemwe akakhala kholo limenelo. Kodi mungalisankhe motani? Baibulo limatiuza za mwamuna wachichepere wotchedwa Timoteo yemwe anakulira m’nyumba yogaŵikana mwachipembedzo. Iye akufotokozedwa kuti ‘amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mhelene.’ (Machitidwe 16:1) Nthaŵi zina Timoteo ayenera kukhala anadzimva wogaŵikana pakati pa makolo ake. Komabe, iye anakupatira chikhulupiriro cha chipembedzo cha amayi ŵake nakhala woyenda naye wa mtumwi Paulo. (Machitidwe 16:2, 3) Kodi uku kunali kuŵakonda kwambiri amayi ŵake kuposa abambo ŵake? Kutalitali.

Mtumwi Paulo analembera Timoteo kuti: ‘Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene anakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.’ (2 Timoteo 3:14, 15) Mwazimenezi tingagamule kuti chosankha chimene Timoteo anapanga chinali chozikidwa pa phunziro losamalitsa la Mawu a Mulungu! Iye ‘anatsimikizika mtima,’ kugomekedwa maganizo kuti akhulupirire.

Mmalo mopanga chosankha chozikidwa pa njerengo kapena malingaliro, santhulani zikhulupiriro za makolo anu m’chidziŵitso cha “malembo opatulika.”a Inuyo, osati Amayi kapena Abambo ŵanu, ndinu muli ndi thayo lonse lakukonza chipulumutso chanu!—Afilipi 2:12.

Kukopa Kholo Lanu Losakhulupirira

Mutatsimikiza mumtima mwanu kutsatira chipembedzo chowona, pamenepo, kodi ndimotani mmene muyenera kulingalira kholo lanu losakhulupirira? Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuyesayesa kukopa anzawo amuukwati osakhulupirira kuti: “Tachilingalirani: monga mkazi mungapulumutse mwamuna wanu; monga mwamuna mungapulumutse mkazi wanu.” (1 Akorinto 7:12-16, The New English Bible) Kodi izi sizingagwire ntchito kwenikweni, kwa ana a osakhulupirira?

Mayendedwe anu oyera ndi ulemu wakuya kwa kholo lanu zingalithandize mokulira kuti likhale ndi chithunzi chabwino cha Chikristu chowona. (Yerekezerani ndi 1 Petro 3:1, 2.) Kumbukiraninso kuti, kutenga kaimidwe ka chowonadi sikumatanthauza kuti inu mukuchita motsutsana ndi kholo lanu losakhulupirira. Ndithudi, mwakupitiriza kukhala wokoma mtima, womvera, ndi wogwirizanika, mungasonyeze kholo linalo chikondi chanu chosalekeza.

Pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Ngati pabuka mwaŵi wa kulankhula ndi kholo lanu ponena za zikhulupiriro zanu, chitanidi motero! “Oyenera kulandira zabwino usawamane,” ikutikumbutsa motero Miyambo 3:27. Koma khalani wokoma mtima, wochenjera. Peŵani kulisuliza khololo chifukwa chakuti mumadziŵa zochuluka za m’Baibulo. Mudziŵa bwanji, mwinamwake zoyesayesa zanu zidzabala zipatso. “Abambo ŵanga adali otsutsa mwamphamvu kwa zaka zambiri,” akukumbukira motero Jay. “Kunawonekera kuti iwo sakasintha, koma potsirizira pake tinawakopa.” Pamene Abambo ŵa Jay anamwalira zaka zingapo zapitazo, iwo ankatumikira monga mkulu Wachikristu.

Ngati sipakupezeka chivomerezo, kumbukirani mawu a Davide aŵa pa Salmo 27:10: ‘Wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.’ Inunso muli ndi chilikizo la mabwenzi anu okhulupirika mumpingo Wachikristu, amene ‘angamamatire kwa inu kupambana ndi mbale.’ (Miyambo 18:24) Ndithandizo lawo ndi la kholo lanu lokhulupirira, mungakhale olimba kaamba ka chowonadi.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yokhala ndi mitu yakuti “Why Should I Accept My Parents’ Religion?” ndi “Is the Bible Really True?” zopezeka m’makope a Awake! a November 22, 1986, ndi June 8, 1987.

[Chithunzi patsamba 23]

Kuchita umdyera kuŵiri kwa makolo anu kungakuthandizeni, koma m’kupita kwanthaŵi, kumawonjezera mkangano m’banja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena