Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 2/8 tsamba 11-13
  • Kodi Pali Chitonthozo Chotani kwa Minkhole?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Chitonthozo Chotani kwa Minkhole?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chomwe Chimafunikiradi Nchiyani?
  • Chitonthozo Kuchokera m’Mawu a Mulungu
  • Mtsogolo Mwabwino
  • Dziko Latsopano Lopanda Mavuto
    Galamukani!—1990
  • Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Kodi Ndizitani Tsoka Likandigwera?
    Galamukani!—2003
  • Pezani Chitonthozo M’nyonga ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 2/8 tsamba 11-13

Kodi Pali Chitonthozo Chotani kwa Minkhole?

KWA anthu oyang’anizana ndi imfa yamwadzidzidzi ya okondedwa awo m’ngozi zochititsidwa ndi zakumwa zoledzeretsa, sipamakhala “nthaŵi . . . yoŵauza kuti ‘Pitani Bwino,’ . . . kapena kuti ‘Ndimakukondani,’” watero Janice Lord, mkonzi wa Survivor Grief Following a Drunk-Driving Crash.

Monga momwe tawonera, opulumuka amakhala ndi zambiri zochita nazo: kuzizwitsidwa, kuvutitsidwa, kukwiitsidwa, ndi kuthedwa nzeru. Kufa kwa okondeka mwanjirayi kumabweretsa malingaliro a kutaikiridwa kosatha. Opulumuka angalingalire kuti kuipidwa kumene avutika nako sikungathetsedwedi.

Pozindikira kupweteka kumene kutaikiridwa koteroko kumabweretsa, akuluakulu ambiri akupanga malamulo kapena mikhalidwe imene ingachepetse ngozi zozizwitsa zambirimbiri chaka chirichonse. Mwachitsanzo, mkulu wina anasonya kumkhalidwe wofooka wopezeka mwa okhala ndi liŵongo la kumwa ndi kuyendetsa galimoto ndipo anapereka lingaliro la kukhazikitsa malikulu oti anthuwa adzipitako komwe, kupyolera m’maphunziro ndi kuŵalangiza zantchito ndi mankhwala ogodomalitsa, iwo ‘angakonzedwe ndi kulimbitsidwa’ kulaka zifooko zawo.

Kodi Chomwe Chimafunikiradi Nchiyani?

Mosasamala kanthu ndi mmene ichi chingakhale chofunikira, palibe munthu kapena chiungwe chaumunthu chimene chingachotsepo kupweteka koikidwa pa minkhole, ndipo anthu sangamuukitsedi wakufayo. Chomwe chikufunikira kuti kuvulaza konseku kuchotsedwe nchoposa chimene munthu angathe kuchichita. Chomwe chikufunikiradi ndicho makonzedwe osiyana kotheratu m’dziko, omwe sakazikidwa pa malingaliro adyera ndi akupha amakono a kufuna ‘zosangulutsa pamtengo uliwonse’ omwe aphetsa anthu ambiri chotero.

Kodi pali maziko abwinopo oyembekezera dziko la mtundu woterowo momwe masoka oterowo akakhala zinthu zakumbuyo? Inde, alipodi. Kwenikweni, pali chiyembekezo chotsimikizirika cha dziko latsopano pano padziko lapansi pomwe masokawa adzatha, dziko lomwe ngakhale minkhole yofa ndi ngozi idzaukitsidwa. Ha, chidzakhala chimwemwe chosafotokozeka chotani nanga pamene awa adzagwirizananso ndi okondedwa awo! Lidzakhala dziko latsopano momwe, m’kupita kwanthaŵi, zikumbukiro zachisoni zakumbuyo zidzathetsedweratu.

Chiyembekezo chimenecho cha dziko latsopano chikupezeka m’Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo, lomwe limati: “[Mulungu] wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” (Yesaya 25:8) Ichi chidzaphatikiza kuwukitsa akufa kuchokera kumanda. Monga mmene mtumwi Paulo analembera motere: ‘Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.’ (Machitidwe 24:15) Yesu ndi atumwi anachisonyeza ichi mwa kuukitsa akufa.—Luka 7:11-16; 8:40-42, 49-56; Yohane 11:1, 14, 38-45; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12.

Moyo padziko lapansi m’dziko latsopano, kuphatikizapo kuukitsidwa kwa akufa kuchokera kumanda, udzakometseredwa mokongola ndiungwiro wa anthu. Mphamvu zochiritsa za Mulungu zidzachiritsa malingaliro ndi matupi a anthu onse amoyo motere: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” ‘Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba.’—Yesaya 33:24; 35:5, 6; onaninso Mateyu 15:30, 31.

Baibulo limaufotokoza mkhalidwe wamtsogolo wa anthu padziko lapansi mwa kunena kuti Mulungu ‘adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’ (Chibvumbulutso 21:4) Mpatsi wa madalitso odabwitsa ndi mikhalidwe yochititsa chimwemwe yomwe ikudzayo akulengeza kuti: ‘Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.’—Yesaya 65:17, 18.

Kodi zonsezi zidzachitika ndi mphamvu za yani? Mwakulamulira kwamphamvu za Mpatsi wamkulu wa chiyembekezo, Mlengi wa chilengedwe chonse, Yehova Mulungu. Iye akutsimikizira m’Mawu ake kuti dongosolo latsopano loterolo mmene ‘mukhalitsa chilungamo’ posachedwapa lidzalowa mmalo dongosolo lamakonoli la zinthu ladyera ndi lachiwawa, dongosolo lomwe liri lozama kale mwakuya “m’masiku otsiriza.”—2 Petro 3:13; 2 Timoteo 3:1-5, 13; Miyambo 2:21, 22.

Chitonthozo Kuchokera m’Mawu a Mulungu

Mboni za Yehova, mofanana ndi anthu ena, sikuti sizikhudzidwa ndi masoka a nthaŵi zathu, ndipotu iwo, m’dziko lowopsali, samayembekezera kuchinjiriza kwaumulungu ku imfa, ngozi kapena zinazake. Iwo amadziŵa kuti ichi sindicho chifuniro cha Mulungu nthaŵi ino. Mlaliki 9:11 imati: ‘Yense angoona zomgwera m’nthaŵi mwake.’ Komabe, Mboni kwanthaŵi yaitali zaika chisamaliro chawo ku Mawu a Mulungu, popeza kuti malonjezo ake amapereka chitonthozo chosatha kwa anthu onse owalabadira.

Mmodzi wa Mboni za Yehova anayambukiridwa kwambiri pamene woyendetsa galimoto wokhuta mowa anapha mlamu wake nasiya mkazi wake (mchemwali wake) wosokonezeka maganizo chifukwa cha kuvulala koipa kwam’mutu, kotero kuti anafunikira kusamaliridwa nthaŵi zonse. Nawonso anali Mboni za Yehova. Iye akusimba motere:

“Kwanthaŵi yochuluka m’chaka, ndinkalira mobwerezabwereza, ndipo ndinakwiyitsidwa. Ndinamkwiyira mnyamata wachichepere amene anachititsa tsokali, kukwiyira makolo ake chifukwa cha kusamuyang’anira mosamalitsa. Nthaŵi zina mkwiyowo unalunjikitsidwadi kwa Mulungu ndi angero kaamba ka kusachinjiriza ichi kuchitika. Kunali kuwawanya chotani nanga anthu aŵiri abwino omwe ankamtumikira!

“Zowonadi, ndinadziŵa kuti Mulungu sanali waliwongo mwachindunji ndipo sanafune kuti zinthuzi zichitike. Koma ndinalingalira kuti iye anatitsogoza kulikonse komwe tinkayenda natitetezera ku zovulaza zoterozo. Tsopano ndinazindikira kuti ndinafunikira kukhala ndi malingaliro olinganizika kwambiri a ichi, ndipo ndinayamba kufunafuna mayankho.

“Panapita nthaŵi ndisanayambe kuiŵala kuipidwa kotero kuti ndilingalire pankhaniyo. Ndinalingalira mofanana ndi Asafu, yemwe ananena mu Salmo 73 kuti zinawoneka ngati kuti oipa ndiwo anayanjidwa kwambiri. Koma m’salmo limodzimodzilo, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti siziri tero, ndikuti Mulungu samayanja oipa, ndikuti m’nthaŵi yake, iwo adzawonongeka.

“Ndinazindikira kuti kuganiza kwanga, osati kwa Mulungu, kunali kolakwika. Ndinali kupotoza malemba. Mulungu samapereka ufulu wa kusayambukiridwa ndi ngozi, matenda, kapena imfa nthaŵi ino koma amalonjeza kuti madalitso oterowo adzakhalako kutsogolo, m’dziko lake latsopano. Nditazindikira kuti Mawu a Mulungu ankanenadi za kutichinjiriza kwa Mulungu m’njira yauzimu panthaŵi ino, osati ya kuthupi, pamenepo mkwiyo wanga unazimiririka pang’onopang’ono. Tsopano ndinakhoza kulunjika pa magwero enieni a masoka, Satana Mdyerekezi, amene anali wakupha anthu ndi wabodza kuchokera panthaŵi imene anaukira Mulungu. Baibulo limachimveketsa kuti wochititsa ndi Satana amene ali mulungu wa dziko lino lodzala ndi kuvutika.—Yohane 8:44; 2 Akorinto 4:4.

“Nditazindikira mokwanira chowonadi cha chifukwa chimene pamakhalira kuvutika, chifukwa chimene Mulungu amakulolera, ndi mmene adzakuthetsera, chinamveketsedwa kuti Mulungu simdani wathu, koma ndimpulumutsi wathu!

“Ndiponso, kunali kotonthoza kwambiri kudziŵa kuti kupyolera mwa mzimu wake woyera, Yehova amachilikiza awo omtumikira. Baibulo limatitsimikizira kuti mzimu woyera udzapereka ‘ukulu woposa wa mphamvu.’ Kupyolera mu uwo amatipatsa nyonga yopirira zinthu zosapiririka. Ndiponso amatitonthoza ndi chiyembekezo chowona okondedwa athu m’chiukiriro. Chotero tingalake nsautso.”—2 Akorinto 4:7.

Mtsogolo Mwabwino

Masoka a mitundu yosiyanasiyana achitikira ambiri, kuphatikizapo Mboni za Yehova, m’zaka zonsezi. Ichi chimatsimikizira kuwona kwa Mawu a Mulungu akuti yense angowona zomgwera m’nthaŵi mwake. (Mlaliki 9:11) Koma zokumana nazo za atumiki a Mulungu zimatsimikiziranso kuwona kwa Mawu a Mulungu kuti Yehova amatonthoza ndi kuchilikiza anthu ake m’nthaŵi yawo ya kusoŵa ndipo zimatsimikiziranso mtsogolo mwabwino m’dziko lake latsopano, mmene masoka oterowo adzakhala zinthu zakale.

Nkotonthozadi kudziŵa kuti m’dziko latsopano lolungama la Mulungu, mudzakhala chikondi chenicheni kwa anthu anzathu ndi kulemekeza mphatso yamtengo wapatali ya moyo. Mikhalidwe yabwinoyi idzaloŵa mmalo dyera ndi kudyerera zifooko za anthu kaamba ka phindu kumene kukufalikira m’dziko lino tsopano. Zakale zidzakhalanso nkhaŵa zadziko lino, zitsenderezo, ndi mantha omwe amachititsa ambiri kufuna kumwa zoledzeretsa mopambanitsa kapena kumwa mankhwala ena.

Ngakhale tsopano, Mboni za Yehova zikupanga ubale wadziko lonse womwe umagwirizanitsidwa pamodzi ndi magwero ogwirizanitsa a chikondi. (Yohane 13:34, 35) Awo omwe ali mbali ya ubalewu amapereka chilikizo lamphamvu lothandiza anthu omwe avutika ndikutaikiridwa. Iwo ngachimwemwe kuthandiza aliyense wofuna kutonthozedwa monga momwe achitira.—2 Akorinto 1:3, 4.

[Chithunzi patsamba 13]

Baibulo limalonjeza kuti padzakhala kuuka kwa akufa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena