Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Bwanji Ponena za Makalabu Ausiku?
“TIMAFUNIKIRA zosangulutsa.” “Timangopita kukavina.” “Munthu aliyense akupitako.” “Tikungofuna kusangalala.” Analongosola motero achichepere angapo kwa mtola nkhani wa Galamukani! ponena za chifukwa chimene amapitira mobwerezabwereza ku makalabu ausiku. Malo ausiku oterowo ngotchuka kwambiri pakati pa achichepere ambiri, ndipo ngati alimo m’mudzi mwanu, mungakhale munalingalira zopitako.
Lerolino, achichepere ambiri akuthamangira ku mitundu yotsatirayi ya makalabu, monga momwe yalongosoledwera ndi magazini a Friday: “Nthaŵi ya phwando ndi nthaŵi iriyonse ndipo nthaŵi iriyonse ndi usiku uno. Kwa awo osaletsedwa, phwandolo silimatha konse. Mzimu wa kuvina ukufalikira mumzinda wodzazidwa ndi zakumwa zozizira, magetsi amitundumitundu owala mophanima ndi nyimbo zogwira mtima zomwe sizimakulolani kukhala pansi. ‘Makalabu tsopano akupereka zokonda aliyense. . . . Pali makalabu amene amasamalira akatswiri achichepere, ophunzira pakoleji, ogonana ofanana ziŵalo ndi anthu achikulire.’”
Kwa anthu otsungula, pali makalabu amene amafunikira malipiro apamwamba, malaya odula, ndipo ngakhale mkhalidwe wovomerezeka kuti muloledwe kuloŵa mkati. Kwa awo omwe siolemera kwenikweni, pali makalabu okhala ndi malo osakongola kwenikweni amene amapereka mkhalidwe wa phwando pa mtengo wotsika. Ndipo kwa achichepere aang’ono kwenikweni (kapena osachenjera kwambiri) kuti angathe kuloŵa m’makalabu a achikulire, pali “makalabu a zakumwa zotsekemera” ndi “mabawa a soda,” omwe amalingaliridwa kukhala opanda zakumwa zoledzeretsa.
Nkosavuta kumvetsetsa chifukwa chimene makalabu ausiku aliri okondweretsa kwambiri kwa achichepere ambiri. Pamene muli wachichepere, kufuna kusangalala kumakhala kwachibadwa. (Yerekezerani ndi Mlaliki 11:9.) Usiku wovina ungawoneke kukhala njira yabwino yochotsera chipsinjo cha sukulu ndi ntchito. Koma kodi makalabu ausiku ngabwino motani?
Sonya, mkazi wachichepere yemwe ankapitapita kumakalabu ausiku mobwerezabwereza, akuvomereza motere: “Lingalirolo limawoneka kukhala lopanda liŵongo. Mukupita kukavina ndikusangalala. Koma nthaŵi zambiri zimafikira kukhala zochulukirako. Mumayamba kupita pamene nyimbo ndi khamulo nlokondwera kopambanitsa. Posakhalitsa mumadziŵa akabwerebwere, ndipo nanunso mwakhala kabwerebwere. Lingalirolo nlopita kukavina—ndikukumana ndi winawake. Ndipo kaya chimenecho nchonulirapo chanu kapena ayi, icho nthaŵi zonse chimakhala chonulirapo chawo.” Kodi Sonya akukuza mawu ndi mkamwa?
Makalabu Ausiku Lerolino
Disiko ya zaka khumi zapitazo inakhala malo ofala a chisembwere chakugonana, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, ndipo ngakhale kugonana kwa ofanana ziŵalo.a Ndipo zinthu sizinasinthe kwenikweni chiyambire nthaŵiyo. Ngakhale kuti nyimbozo (mu United States, kaŵirikaŵiri zimatchedwa nyimbo zapanyumba kapena nyimbo zovina) ndipo kavinidwe kasintha, mkhalidwe wa m’malo ambiri ausiku udakali wofanana kwenikweni ndi wa disiko ya chisembwere.
M’nkhani ya m’magazini a Life yonena za nyimbo zapanyumba, wochemerera wina wa ku makalabu ausiku anati: “Nyimbo zovina poyambirira zinkawoneka kukhala zamwambo nthaŵi zonse—kamvekedwe kamphamvu ndi chisonkhezero cha kuutsa chilakolako chakugonana, chikumakula kufikira mkhalidwe wa kutengeka maganizo utabukapo. Chinachake chomwe sichinkapezeka m’mizinda, ndipo nyimbo zapanyumba zikudzaza mpata umenewo.” Woulutsa nyimbo za disiko wa ku New York, David Piccioni akuti: “Cholinga ndicho chakudziloŵetsamo kotheratu usiku wonse.”
Polingalira za msala waposachedwapa wa kavinidwe monga ngati kavinidwe kachisembwere ka lambada, magazini a Mademoiselle analengeza kuti: “Kugonana: Iko kwachoka m’zipinda zosambira ndipo kwabwerera komwe kunali—pabwalo lovinira. M’nthaŵi zakale (m’ma 70), bwalo lovinira linali loutsira chilakolako chakugonana ndipo zipinda zosambira zinali zogonaniranamo ndi kumwa mankhwala ogodomalitsa. Tsopano popeza kuti aliyense akudera nkhaŵa ndi AIDS, zipinda zosambira ndizo zovalira mosamalitsa ndipo pabwalo lovinira mpamene mumapenyerera anthu ena akugonana. Kapena kunyengezera kuti akugonana.” Inde, nyimbo zingadzutse mkhalidwe womwe umathetsa ziletso zamakhalidwe ndikuutsa mkhalidwe wa kugonana.
Kukakumana ndi Yani?
Makalabu ena ngotchuka kukhala malo okumanira ndi munthu wa chiŵalo chosiyana. Komabe, kodi ndi anthu amtundu wanji amene mungakumane nawo? Msungwana wina yemwe kale ankayendera madera osiyanasiyana a makalabu ausiku akuvomereza kuti: “Anthu ambiri kumeneko amatsogoza miyoyo yachisembwere ndipo ngokondweretsedwa nkugonana ndi winawake. Ngati akopeka nawe, amakugulira zakumwa zankhaninkhani, namamatira kwa iwe usiku wonse kukuuza zinthu zabwino, zinthu zosangalatsa akumayembekezera kuti udzagonjera ku zikhumbo zawo.”
Malo ena anakonzedwadi kulola machitachita achisembwere ameneŵa. Doris, mkazi wachichepere yemwenso anali kabwerebwere ku makalabu ausiku akuti: “Pali makalabu omwe ali ndi malo okhalapo okhala ndi makama ndi mipando yogonanirapo kumene anthu ambiri amapita kukapsompsonana ndi kugwirana. Amuna ambiri okwatira amapezeka komweko opanda akazi awo. Ena amakhala komweko akumayembekezera kukumana ndi winawake wokhala naye usikuwo kapena kugonana naye, ndipo ena amafunafuna munthu wodzakwatirana naye.” Doris akutsimikiza motere: “Mkhalidwe wa pa makalabu ausiku ngoyenerera kwenikweni kaamba ka chisembwere. Zakumwa zoledzeretsa zimamwedwa zambiri kufikira m’mamawa, ndipo zinthu zonse zimachitika.”
Malo a makalabu ausiku akhalanso ogwirizana ndi kumwa mankhwala ogodomalitsa. Mwini wa kalabu wina akusimbidwa kuti anati: “Chochitikachi . . . nchogwirizana kotheratu ndi mankhwala ogodomalitsa.” Mankhwala ogodomalitsa ndi zakumwa zoledzeretsa kaŵirikaŵiri zimapezeka ngakhale m’mabawa olingaliridwa kukhala opanda zoledzeretsa. Jesse, munthu wina yemwe kale adali kabwerebwere ku makalabu ausiku, akuwonjezera kuti: “Utsi wa mbanje ndi fodya umadzaza mpweya wonse. Anthu ambiri amavala kuti akhumbiritse thupi: zovala zothina ndi zowonetsa thupi, masitayelo achiŵereŵere, zokometsera zopambanitsa.”
Sonyezani Kuchenjera
Kuyambira nthaŵi zakale, nyimbo ndi kuvina zagwiritsiridwa ntchito kunyenga anthu kuloŵa m’mkhalidwe woipa. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti Aisrayeli panthaŵi ina “anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.” Ichi chinaphatikizapo nyimbo zokwezeka ndi kuvina kosalamulirika. Komabe, “kusewera” kumeneku kunali kalambula bwalo wa kulambira mafano koipa ndi chisembwere chosalamulirika.—Eksodo 32:6, 17-19, 28.
Chotero achichepere Achikristu ayenera kupeŵa kuloŵa m’mkhalidwe uliwonse womwe mofulumira ungakhale ‘kuledzera,’ kapena ‘mchezo.’ (Agalatiya 5:19, 21; Byington) Akorinto Woyamba 15:33 akutikumbutsa kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Kodi munthu angadziloŵetsedi yekha m’phwando la anthu omwe ali ‘odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu’ ndipo nkusayambukiridwa moipa? (Aefeso 4:18) Ndipo monga momwe mkazi wina wachichepere anavomerezera kuti: “Kuyanjana ndi ubwenzi wathithithi kungathe ndipo kaŵirikaŵiri kumachitika [kwa akabwerebwere ena a ku makalabu ausiku].” Kodi ndimotani mmene zimenezi zingakuyambukirireni mwauzimu?
Komabe, ena angalingalire kuti, yankho ndilo kubweretsa gulu la Akristu anzawo. Komabe, chilungamo chingakhalepo kokha pamalo Achikristu. (Yakobo 3:18) Ndipo mkhalidwe wa pamakalabu ausiku ambiri walinganizidwira kudzutsa malingaliro amene ali a ‘padziko, a chifuniro cha chibadwidwe, a ziŵanda,’ osati auzimu.—Yakobo 3:15.
Kunena zowona, simakalabu ausiku onse amene amachita zopambanitsa zomwe zafotokozedwa pano, ndiponso sikolingalirika kutsutsiratu maresitilanti onse omwe amawonetsa kuvina kapena zosangulutsa. Koma Paulo akutipatsa uphungu wa ‘kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani.’ (Aefeso 5:10) Ndipo ngati mwaitanidwa kupita kumalo osadziŵika kapena okhala ndi mbiri yokaikiritsa, muyenera kukhala ochenjera kwambiri povomereza chiitanocho.—Miyambo 14:15.
Mungadzifunse nokha mafunso onga aŵa: Kodi ndani omwe akupitako, ndipo kodi ali ndi mbiri yotani? Kodi makolo anu kapena achikulire ena okhala ndi thayo akudziŵanji za malowo? Kodi ali ndi mkhalidwe wotani? Kodi ndi anthu otani omwe amapitako mobwerezabwereza? Kodi amasamalira achichepere okha? Ngati nditero, kodi nkuthekera kotani komwe kulipo kwa mkhalidwe wabwino? Ngati kuli zosangulutsa, kodi izo nchiyani? Kodi ndinyimbo zamtundu wanji zimene zidzaimbidwa? Kodi malowo amavomereza opezekapowo kukhala pawokha kwa nthaŵi yaitali kapena kwakanthaŵi, kapena kodi ndi malo amayanjano omwe angakukakamizeni kuphatikana ndi ena?
Doris, wogwidwa mawu papitapoyo, akuvomereza kuti: “Satana amawapanga makalabu ausiku kuwoneka osangalatsa, okondweretsa, owala, achiphwete—zonse zimene zimafunikira kuti atinyenge.” Koma musapusitsidwe ndi kuwala kwa makalabu ausiku! Iwo atsimikizira kukhala msampha wakupha kwa achichepere ambiri. Pezani njira zovomerezeka, zopindulitsa zodzisangalatsira.b
[Mawu a M’munsi]
a Onani Awake! ya March 22, 1979.
b Kaamba ka malingaliro ogwirizana ndi zimenezi, onani mutu 37 wa bukhu lakuti Questions Young People Ask—Answers That Work, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 25]
Ambiri amene amapitapita ku makalabu ausiku ngokondweretsedwa ndi kugonana kwachisembwere osati kusanguluka