Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 4/15 tsamba 19-24
  • Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsira Ntchito Nyimbo Molakwa
  • Kufunika kwa Kuchenjera
  • Nyimbo za Rap​—Nyimbo za Chipanduko
  • Heavy Metal​—Chisembwere, Chiwawa, ndi Kulambira Satana
  • Kututa Chimene Mufesa
  • Chenjerani
  • Kodi Cholakwika Nchiyani ndi Nyimbo Zanga?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Nyimbo Zingandivulazedi?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?
    Galamukani!—2011
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 4/15 tsamba 19-24

Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!

“Penyani bwino umo muyendera, simonga opanda nzeru, koma monga anzeru, akuchita machaŵi, popeza masiku ali oipa.” ​—AEFESO 5:15, 16.

1. Kodi nchifukwa ninji nyimbo zingatchedwe “mphatso yaumulungu”?

“NYIMBO . . . ndimphatso yaumulungu.” Analemba motero Lulu Rumsey Wiley, m’buku lake la Bible Music. Kuyambira nthaŵi zakalekale, amuna ndi akazi owopa Mulungu avomereza mawu ameneŵa. Kupyolera m’nyimbo, munthu wasonyeza za mkati mwa mtima wake​—chisangalalo, chisoni, mkwiyo, ndi chikondi. Chotero nyimbo zinachita mbali yofunika kwambiri m’nthaŵi za m’Baibulo, zotchulidwa m’buku lopatulika lonselo.​—Genesis 4:21; Chivumbulutso 18:22.

2. Kodi nyimbo zinagwiritsiridwa ntchito motani kutamanda Yehova m’nthaŵi za m’Baibulo?

2 Nyimbo zinakhala ndi mbali yolemekezeka kopambana m’kulambira Yehova. Mawu ena olemekezeka koposa achitamando kwa Yehova Mulungu amene ananenedwapo anali m’nyimbo. “Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira,” analemba motero wamasalmo Davide. (Salmo 69:30) Nyimbo zinagwiritsiridwa ntchito ndi munthu ali yekha monga mbali ya kupemphera. “Ndikumbukira nyimbo yanga usiku; ndilingalira mumtima mwanga; mzimu wanga unasanthula,” analemba motero Asafu. (Salmo 77:6) M’kachisi wa Yehova, nyimbo zinalinganizidwa pamlingo waukulu. (1 Mbiri 23:1-5; 2 Mbiri 29:25, 26) Nthaŵi zina, magulu aakulu oimba analinganizidwa, monga ngati pakuperekedwa kwa kachisi, pamene owomba malipenga okwanira 120 anagwiritsiridwa ntchito. (2 Mbiri 5:12, 13) Tilibe cholembedwa chotiuza mmene kuimba kwakukulu kumeneku kunamvekera, koma buku lakuti The Music of the Bible limati: “Sikungakhale kovuta kupeza lingaliro la mmene nyimbo za Pakachisi zinayambukirira anthu onse pa zochitika zapadera . . . Ngati wina wa ife akaperekedwa tsopano pakati pa chochitika choterocho, lingaliro losaletseka la kuchita mantha ndi ulemerero silingapeŵeke.”a

Kugwiritsira Ntchito Nyimbo Molakwa

3, 4. Kodi ndimotani mmene anthu a Mulungu ndi anansi awo akunja anagwiritsirira ntchito molakwa mphatso ya nyimbo?

3 Komabe, sinthaŵi zonse pamene nyimbo zinagwiritsiridwa ntchito molemekezeka chotero. Pa phiri la Sinayi, nyimbo zinagwiritsiridwa ntchito kusonkhezera kulambira fano la mwana wa ng’ombe wagolidi. (Eksodo 32:18) Nyimbo nthaŵi zina, zinagwirizanitsidwa ndi mkhalidwe wauchidakwa ndipo ngakhale uhule. (Salmo 69:12; Yesaya 23:15) Anansi a Israyeli akunjawo sanali opanda liwongo la kugwiritsira ntchito molakwa mphatso yaumulungu imeneyi. “Mu Foinike ndi Suriya,” ikutero The Interpreter’s Dictionary of the Bible, “pafupifupi nyimbo zotchuka zonse zinasonyeza kulambira Ishtar, mulungu wachikazi wakubala. Chotero, nyimbo yotchuka nthaŵi zonse inayamba kuimbidwa pamadzoma akugonana.” Agiriki akale nawonso anagwiritsira ntchito nyimbo pa “kuvina kodzutsa chilakolako chakugonana.”

4 Inde, nyimbo zili ndi mphamvu yosonkhezera, kusangalatsa, ndi kukopa. Zaka makumi ambiri kalelo, buku la John Stainer lakuti The Music of the Bible linafika ngakhale pakunena kuti: “Palibe luso lokhala ndi chisonkhezero champhamvu pa fuko la anthu panthaŵi ino mofanana ndi luso la Nyimbo.” Nyimbo zikupitiriza kupereka chisonkhezero chachikulu lerolino. Chifukwa chake, nyimbo za mtundu wosayenera zingaike ngozi yeniyeni pa achichepere owopa Mulungu.

Kufunika kwa Kuchenjera

5. (a) Kodi nyimbo zili ndi mbali yaikulu motani m’moyo wa achichepere ambiri? (b) Kodi Mulungu amawawona motani achichepere akamasangalala?

5 Ngati ndinu wachichepere, pamenepo mumadziŵa bwino mmene nyimbo​—makamaka mitundu yosiyanasiyana ya nyimbo za pop [zotchuka] kapena za rock​—ziliri zofunika kwa achichepere ambiri. Nyimbo zafika ngakhale pakutchedwa kuti “mbali ya chakudya cha achichepere.” Kukuyerekezeredwa kuti m’zaka zake zisanu ndi chimodzi zomalizira sukulu, wachichepere wamba mu United States amakhala atamvetsera nyimbo za rock kwa maola oposa anayi patsiku! Zimenezo zimasonyezadi kusoŵeka kwa uchikatikati. Sikuti pali cholakwika chilichonse mwakusangalala ndi chinthu chimene chikukhalirani bwino kapena chokusangalatsani. Ndithudi, Yehova, Mlengi wa nyimbo zosangalatsa, sakufuna kuti achichepere akhale achisoni ndi osakondwa. Kwenikweni, iye akulamula anthu ake kuti: “Sekerani mwa Yehova, ndipo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.” (Salmo 32:11) Mawu ake kwa achichepere ngakuti: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako.”​—Mlaliki 11:9.

6. (a) Kodi nchifukwa ninji achichepere afunikira kusamala ndi nyimbo zimene amasankha? (b) Kodi nchifukwa ninji nyimbo zambiri za lerolino zili zosayenera kuposa nyimbo za mibadwo yapitapo?

6 Komabe, pali chifukwa chabwino chokhalira wosamala ndi nyimbo zimene musankha. Mtumwi Paulo anati pa Aefeso 5:15, 16: “Penyani bwino umo muyendera, simonga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machaŵi, popeza masiku ali oipa.” Achichepere ena angatsutse, monga momwe anachitira mtsikana wina kuti: “Makolo athu anamvetsera nyimbo zawo pamene anali achichepere. Nanga ife tidzalekeranji kumvetsera zathu?” Nyimbo zina zimene makolo anu anamvetsera pamene anali pamsinkhu wanu nazonso zingakhale zinali ndi mbali zake zoipa. Mwakupenda mosamalitsa, kwapezeka kuti nyimbo zotchuka zambiri zili ndi mawu obisa otanthauza zachisembwere ndi zamakhalidwe oipa. Koma zimene kale zinali kungotanthauzidwa tsopano zikulongosoledwa poyera. Wolemba wina anati: “Ana tsopano amamva zinthu zonyansa pamlingo waukulu koposa ndi kalelonse m’chitaganya chathu.”

Nyimbo za Rap​—Nyimbo za Chipanduko

7, 8. (a) Kodi nyimbo za rap nzotani, ndipo nchiyani chazipangitsa kukhala zotchuka kwambiri? (b) Kodi munthu wotsatira njira ya moyo ya rap angadziŵike motani?

7 Mwachitsanzo, talingalirani chisonkhezero chatsopanoli cha nyimbo za rap. Malinga nkunena kwa magazini ya Time, nyimbo za rap zakhala “chipanduko cha nyimbo chovomerezedwa cha dziko lonse” ndipo nzotchuka kwambiri mu Brazil, Yuropu, Japan, Russia, ndi United States. Kaŵirikaŵiri zimakhala zopandiratu maimbidwe, mawu ake amakhala olankhula, osati kuimba, akumatsatira kugunda kwamphamvu. Komabe, kuli kugunda kwamphamvu kumeneko kumene kukuchititsa kukula kwa malonda a nyimbo za rap. “Pamene ndimamvetsera nyimbo za rap,” anatero wachichepere wina wa ku Japan, “ndimasangalala, ndiyeno pamene ndivina, ndimamva kukhala waufulu.”

8 Mawu a rap​—kaŵirikaŵiri osanganizikana kwambiri ndi minyozo ndi chilankhulo cha m’khwalala​—akuwoneka kukhala chifukwa china chozikondera. Mosiyana ndi mawu a nyimbo za rock yamwambo, amene kaŵirikaŵiri amaimba nkhani za kukondana kwa achichepere, mawu a nyimbo za rap kaŵirikaŵiri ali ndi mauthenga owopsa kwambiri. Nyimbo zina za rap zimanena zotsutsa chisalungamo, tsankho la fuko, ndi nkhalwe za apolisi. Komabe, nthaŵi zina mang’ombe ake amatchulidwa m’chilankhulo chonyansa kwenikweni ndi chodabwitsa chosalingalirika. Nyimbo za rap zikuwonekanso kukhala zopandukira miyezo ya kavalidwe, kapesedwe, ndi makhalidwe azakugonana. Mosadabwitsa, rap yakhala njira ya moyo payokha. Otsatira njira yake ya moyo amazindikiridwa ndi majesichala opambanitsa, chilankhulo cha m’khwalala, ndi zovala​—zimajini zazikulu, nsapato zotchedwa high-top zimene samanga zingwe zake, unyolo wa golidi, tizipeŵa tonga toseŵerera baseball, ndi mandala akuda.

9, 10. (a) Kodi ndizinthu zotani zimene achichepere ayenera kupenda pofuna kudziŵa ngati nyimbo za rap ndi njira yake ya moyo zili ‘zokondweretsa Ambuye’? (b) Kodi nchiyani chimene achichepere Achikristu ena akuwoneka kukhala akuchiwona mopepuka?

9 Pa Aefeso 5:10, Akristu akuuzidwa “kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani.” Powona mbiri imene nyimbo za rap zapanga, kodi muganiza kuti chingakhale “chokondweretsa Ambuye” kuti inu mudziloŵetsemo? Kodi wachichepere Wachikristu angakonde kukhala ndi njira ya moyo yosavomerezedwa ngakhale ndi anthu akudziko ambiri? Tamverani mmene wopenda wina analongosolera konsati ya rap: “Oimba rap anapikisana wina ndi mnzake m’kuchititsa kakasi mwakutchula mawu otukwana ndi achisembwere. . . . Akazi ndi amuna ovina anayerekezera machitachita akugonana pabwalo lovinira.” Ponena za mutu wa chochitika china, wolipirira konsati wina anati: “Pafupifupi liwu lililonse lochokera pakamwa pawo (nlotukwana).”

10 Ngakhale kulitero, nyimbo zoimbidwa madzulowo sizinalingaliridwe kukhala rap yeniyeni. Woyang’anira holo ya konsati anati: “Zimene mukumvazi ndiyo rap yabwinopo​—yofanana ndi imene amagula m’masitolo.” Nkomvetsa chisoni chotani nanga kunena kuti mwa achichepere okwanira 4,000 ndi kuposapo amene analipo pakonsatipo panali ena odzinenera kukhala Mboni za Yehova! Mwachiwonekere ena akuchiwona mopepuka chenicheni chakuti Satana ali “mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga.” Iye akulamulira “mzimu [kapena, mkhalidwe wamaganizo waukulu] wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Aefeso 2:2) Kodi mungakhale mukukondweretsa yani ngati mudziloŵetsa m’nyimbo za rap kapena njira yamoyo ya rap? Nzowona, nthaŵi zina rap ingakhale yosaipa kwambiri m’mawu ake. Koma kodi nkwanzeru kukulitsa chikondi cha nyimbo iliyonse imene kwakukulukulu imatsutsa miyezo Yachikristu?

Heavy Metal​—Chisembwere, Chiwawa, ndi Kulambira Satana

11, 12. Kodi nyimbo za heavy metal nzotani, ndipo kodi zili ndi mbali zosayenera zotani?

11 Mtundu wina wa nyimbo zotchuka ndiwo heavy metal. Nyimbozi zimaposa hard rock yaphokoso kwambiri. Lipoti lina mu The Journal of the American Medical Association linati: “Nyimbo za heavy metal . . . zimakhala ndi maimbidwe aphokoso kwambiri odukhula mtima ndipo zili ndi mawu ochuluka othokoza chidani, nkhanza, chisembwere, ndi kulambira Satana panthaŵi zina.” Eya, maina enieniwo a ena a magulu oimba otchuka amasonyeza kululuzika kwa mtundu wa nyimbo za rock umenewu. Amaphatikizapo mawu monga “paizoni,” “mfuti,” ndi “imfa.” Chikhalirechobe, heavy metal ikuwoneka kukhala yabwinopo poiyerekezera ndi thrash metal ndi death metal​—mitundu ya nyimbo zoluluzika za heavy metal. Magulu oimba ameneŵa amatchedwa ndi maina onga “odya anthu” ndi “imfa ya munthu.” Achichepere m’maiko ambiri mwina sangadziŵe mmene mainaŵa aliri ochititsa kakasi chifukwa chakuti ali m’Chingelezi kapena chinenero china chachilendo.

12 Nyimbo za heavy metal kaŵirikaŵiri zagwirizanitsidwa ndi kudzipha kwa achichepere, kuchita tondovi, ndi kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa. Kuchititsa kwake mkhalidwe wachiwawa kunapangitsa wofufuza wa pawailesi wina kuzitcha “nyimbo zophera makolo ako.” Kulambira Satana kumene kumaloŵetsedwamo nkumene kumadetsa nkhaŵa makolo ambiri​—ndi apolisi. Wofufuza wina ananena kuti achichepere ena odziloŵetsa m’kulambira Satana analoŵa m’kagulu kachipembedzo kameneko kudzera m’nyimbo zimenezi. Anamaliza ndi mawu akuti: “Samadziŵa kumene zimawapititsa.”

13. Kodi pali ngozi yotani ngati munthu adziloŵetsa m’nyimbo za heavy metal?

13 Komabe, achichepere Achikristu sayenera kukhala “osadziŵa machenjerero [a Satana].” (2 Akorinto 2:11) Ndiiko komwe, tili ndi “kulimbana . . . ndi auzimu a choipa m’zakumwamba.” (Aefeso 6:12) Kukakhala kupusa chotani nanga, kuitanira ziŵanda m’moyo wake munthu, mwa nyimbo zimene amasankha! (1 Akorinto 10:20, 21) Komabe, achichepere Achikristu ambiri mwachiwonekere amakonda nyimbo zimenezi. Ena atembenukira ngakhale ku njira zobisa kuti akhutiritse chikhumbo cha nyimbo zimene amakondazo. Mtsikana wachichepere wina anavomereza kuti: “Ndinali kumamvetsera nyimbo za heavy metal, nthaŵi zina ngakhale usiku wonse. Ndinali kugula magazini [onena] za heavy metal ndi kuwabisa kwa makolo anga m’mabokosi amene kale tinaguliramo nsapato. Ndinanamiza makolo anga. Ndidziŵa kuti Yehova sanakondwere nane.” Iye anasintha maganizo ake pamene anaŵerenga nkhani ya m’magazini ya Galamukani! Kodi ndiachichepere angati ena amene angagwerebe m’mbuna ya nyimbo zoterozo?

Kututa Chimene Mufesa

14, 15. Kodi tingatsimikizire motani kuti kumvetsera nyimbo zosayenera kungakhale ndi chiyambukiro choipa? Perekani chitsanzo.

14 Musachepse ngozi imene nyimbo zingakuikireni. Zowona, inu simungakhale ndi maganizo akufuna kupha munthu kapena kuchita chisembwere kokha chifukwa chakuti munamvetsera nyimbo. Komabe, Agalatiya 6:8, amati: “Wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi.” Kumvetsera nyimbo zaudziko, zankhalwe, ndipo ngakhale zauchiŵanda kungangokuyambukirani moipa. (Yerekezerani ndi Yakobo 3:15.) Profesa wa nyimbo Joseph Stuessy anagwidwa mawu akunena kuti: “Nyimbo za mtundu uliwonse zimayambukira mzimu wathu, mikhalidwe yamtima, mikhalidwe yamaganizo ndi makhalidwe athu otsatirapo . . . Aliyense amene anena kuti, ‘Ndimamvetsera heavy metal, koma siimandiyambukira,’ angonama. Iyo imayambukira anthu osiyanasiyana pamlingo wosiyanasiyana ndi m’njira zosiyanasiyana.”

15 Wachichepere Wachikristu wina anavomereza kuti: “Ndinamwerekera kwambiri m’nyimbo za thrash metal kwakuti umunthu wanga wonse unasintha.” Posapita nthaŵi anayamba kuvutitsidwa ndi ziŵanda. “Ndinafikira pakutaya ma alubamu anga anyimbozo ndipo ziŵandazo zinandisiya.” Wachichepere wina akuulula kuti: “Nyimbo zimene ndinali kumvetsera zinali kuimba za mizimu, mankhwala oledzeretsa, kapena chisembwere. Achichepere ambiri amati sizimawayambukira, koma zimaterodi. Ndinatsala nenene kutulukiratu m’chowonadi.” Mwambi umafunsa kuti: “Kodi mwamuna angatenge moto pachifuŵa chake, osatentha zovala zake?”​—Miyambo 6:27.

Chenjerani

16. Kodi nchiyani chinganenedwe pa olemba ndi oimba nyimbo zambiri zamakono?

16 Paulo analembera Akristu a ku Efeso wakale kuti: “Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo.” (Aefeso 4:17, 18) Kodi mawuŵa sanganenedwe kwa olemba ndi oimba nyimbo zambiri zamakono? Kuposa ndi kalelonse, nyimbo za mitundu yonseyo zimasonyeza chisonkhezero cha “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” Satana Mdyerekezi.​—2 Akorinto 4:4.

17. Kodi ndimotani mmene achichepere angadziŵire pasadakhale, kapena kuyesa nyimbo?

17 Ponena za “masiku otsiriza,” Baibulo linaneneratu kuti: “Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:1, 13) Chotero, kuposa ndi kalelonse, mufunikira kupenya bwino umo muyendera ndi nyimbo zimene musankha. Kaŵirikaŵiri, mutu wake woipa udzakuuzani kuti nyimboyo njosayenera. Yobu 12:11 akufunsa kuti: “M’khutumu simuyesa mawu, monga m’kamwa mulaŵa chakudya chake?” Mofananamo, mukhoza kuyesa nyimbo mwakumvetsera kuimba kwake ndi khutu latcheru. Kodi maimbidwe ake amakuchititsa kumva motani mkati mwanu? Kodi amachilikiza makhalidwe akupulupudza, onyansa​—mzimu wa kusangalala kwaphokoso? (Agalatiya 5:19-21) Bwanji ponena za mawu ake? Kodi amathokoza chisembwere, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa, kapena zolakwa zina zimene “kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi”? (Aefeso 5:12) Baibulo limati zinthu zoterozo “zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe” pakati pa anthu a Mulungu, osati ngakhale kuikidwa m’nyimbo ndi kuzibwerezabwereza mwakuimba. (Aefeso 5:3) Bwanji ponena za zolembedwa pachikuto cha alubamu? Kodi zili ndi mitu yanyimbo ya zamizimu kapena zithunzithunzi zodzutsa chilakolako chakugonana?

18. (a) Kodi ndikusintha kotani kumene achichepere ena ayenera kuchita ponena za nyimbo? (b) Kodi ndimotani mmene achichepere angakulitsire chikhumbo cha nyimbo zoyenera?

18 Mwinamwake mufunikira kusintha nyimbo zimene mumasankha. Ngati muli ndi marekodi, matepi, ndi madiski amene ali ndi mitu yanyimbo yachisembwere ndi yauchiŵanda, muyenera kuzitaya mwamsanga. (Yerekezerani ndi Machitidwe 19:19.) Izi sizitanthauza kuti simuyenera kusangalala ndi nyimbo; sikuti nyimbo zotchuka zonse nzoipa. Achichepere ena aphunziranso kuwonjezera nyimbo zimene amakonda ndipo tsopano amasangalala ndi nyimbo za classic, folk, light jazz, ndi mitundu ina. Matepi a Kingdom Melodies athandiza achichepere ambiri kukulitsa chikhumbo cha nyimbo zotsitsimula za orchestra.

19. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kusunga nyimbo m’malo ake?

19 Nyimbo ndimphatso yaumulungu. Komabe, kwa ambiri zimakhala chotangwanitsa chosayenera. Iwo ali ngati Aisrayeli akale amene anasangalala kuimba ndi “mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, . . . koma iwo sa[na]penyetsa ntchito ya Yehova.” (Yesaya 5:12) Chikhaletu cholinga chanu kusunga nyimbo m’malo ake ndipo lolani ntchito ya Yehova ikhale chosamala chanu chachikulu. Khalani wosankha ndi wosamala m’nyimbo zimene mumasankha. Mukatero mudzakhoza kugwiritsira ntchito bwino​—osati molakwa​—mphatso yaumulungu imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

a Mwachiwonekere, mtundu wa Israyeli unapambana m’luso la kuimba. Chifaniziro chozokota cha Asuri chimasonyeza kuti Mfumu Sanakeribu anafuna oimba Achiisrayeli monga msonkho wochokera kwa Mfumu Hezekiya. Grove’s Dictionary of Music and Musicians imanena kuti: “Kufuna oimba monga msonkho . . . kunali kwachilendo kwambiri.”

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchifukwa ninji nyimbo zingatchedwe mphatso yaumulungu?

◻ Kodi nyimbo zinagwiritsiridwa ntchito molakwa motani m’nthaŵi zakale?

◻ Kodi ndingozi zotani zimene nyimbo za rap ndi heavy metal zimaika kwa achichepere Achikristu?

◻ Kodi ndimotani mmene achichepere Achikristu angakhalire osamala ndi nyimbo zimene amasankha?

[Chithunzi patsamba 23]

M’nthaŵi za m’Baibulo, nyimbo kaŵirikaŵiri zinaimbidwa kutamandira Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena