Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 3/8 tsamba 14-16
  • Kodi Nyimbo Zingandivulazedi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nyimbo Zingandivulazedi?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphamvu ya Nyimbo
  • Zosayenera Kumvetsera ndi Kuwonerera
  • Kodi Zingakuvulazeni?
  • Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?
    Galamukani!—2011
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Cholakwika Nchiyani ndi Nyimbo Zanga?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 3/8 tsamba 14-16

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nyimbo Zingandivulazedi?

TOM anali wazaka 14 zakubadwa wabwino—wophunzira wanzeru kwambiri amene anakonda kuchitira anansi ake zinthu zabwino. Koma atagula siteriyo yodula, anayamba kumvetsera nyimbo za heavy metal.

Tom anakhala wodzibindikiritsa weniweni m’chipinda chake. Atate ake akukumbukira kuti: “Ndinkanena kuti, ‘Suyenera kumakhalabe nthaŵi yonse m’chipindamo ndi kumamvetsera siteriyo yako.’” Koma Tom anapitiriza kumamvetsera. Ndiyeno, tsiku lina m’nyengo yachisanu, iye anapha amayi ake mwa kuwabaya ndi mpeni nadzipha. “Uzani makolo kuti asamale ndi nyimbo zimene ana awo amamvetsera,” akuchenjeza motero atate a Tom osweka mtima. M’masiku amene kuphako kunali kusanachitike, Tom mobwerezabwereza anaimba nyimbo yonena za “mwazi ndi kupha amayi ako.”

Kodi imeneyi ndinkhani yonkitsa? Inde ndithu. Ndipo pamene kuli kwakuti zinthu zina mosakaikira zinaloŵetsedwamo kuchititsa tsokali, ilo limaperekadi umboni wa kanthu kena kamene achichepere ambiri amanyalanyaza kaŵirikaŵiri: Nyimbo zingakuyambukireni! Simungakhale wokonda heavy metal, ndipo sikuli kotheka kuti mudzachita chiwawa. Komabe, nyimbo zingakuyambukireni m’njira zimene mwinamwake simungadziŵe konse.

Mphamvu ya Nyimbo

Nyimbo ziri ndi mphamvu. Ndithudi, zingachititse mtundu uliwonse wa mikhalidwe ya mtima wa munthu—kuyambira pa chisoni ndi chifundo mpaka ku chikondi ndi chimwemwe. Nyimbo zingakhazike mtima wa munthu pansi ndi kusonkhezera wina kukwiya. Zingasonkhezere kudzipereka ndi kuchirikiza makhalidwe oipa. Pamenepatu, nzosadabwitsa kuti kuyambira nthaŵi zamakedzana, nyimbo zakhala chida champhamvu cha ‘mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,’ Satana Mdyerekezi.—2 Akorinto 4:4.

Mwachitsanzo: Aisrayeli atangopulumutsidwa kuukapolo mu Igupto, anasiya kulambira Yehova nayanja kwa mwana wa ng’ombe wagolide. Kodi chimene chinatsagana ndi khalidwe lawo lonyansa nchiyani? Nyimbo zaphokoso ndi zoluluzika! (Eksodo 32:1-6, 17, 18) Ndipo pamene Mfumu Nebukadinezara yodzitamandira inalamulira nzika zake kulambira fano lachikunja, kodi ndimotani mmene iyo inayesera kudzutsa kukondetsa dziko la munthuwe ndi changu chachipembedzo cha anthu ake? Mwa kugwiritsira ntchito nyimbo zosonkhezera!—Danieli 3:1-7.

Chotero, tiyenera kuyembekezera Satana kugwiritsira ntchito nyimbo kusokeretsera anthu lerolino. Iye ndiye ‘mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.’ (Aefeso 2:2) Nyimbo zochuluka za lerolino zimasonyeza mzimu wachipanduko wa Satana. Ndipo nzosadabwitsa, pakuti zambiri za izo zimalembedwa ndi awo amene Baibulo limanena za iwo kuti ‘angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.’ Ndithudi, mwa kungowona khalidwe lawo, oimba otchuka, akatswiri a nyimbo, ndi opeka nyimbo ambiri afikira ‘kukhala osazindikiranso makhalidwe onse abwino.’—Aefeso 4:17-19.

Chotero kumvetsera nyimbo zawo kungadzetse upandu waukulu kwa achichepere Achikristu. Sizikutanthauza kuti nyimbo zonse zotchuka nzoipa kapena kuti nyimbo za rock ndizo nyimbo zokha zimene muyenera kusamala nazo.a Nyimbo zosayenera zingapezeke pakati pa nyimbo za classic kudzanso m’maopera. Koma pamene kuli kwakuti kale nyimbo zina zinatchula kapena kupereka lingaliro la makhalidwe oipa, nyimbo zambiri za lerolino zimachirikiza khalidwe loluluzika ndi kulimba mtima koposa kulikonse kumene kunakhalapo.

Zosayenera Kumvetsera ndi Kuwonerera

Tatengani nyimbo za heavy metal—mtundu woipa kwambiri wa hard rock imene imalizidwa mwaphokoso kwambiri. Magulu oimba heavy metal modziwonetsera amagwiritsira ntchito maina onga Poison, Skid Row, Guns N’ Roses, ndi Slayer. Magazini a Time anati: “Maina okha a magulu oimbawo amapereka chithunzi cha chipolowe, chizunzo, ndi imfa.” Zofananazo zinganenedwe ponena za zithunzithunzi zowopsa za pazikuto za marekodi ndi zimene kaŵirikaŵiri zimasonyeza zizindikiro za Satana.

Koma bwanji za nyimbo zenizenizo? Izo zimakhaka ndi mitu yonga ngati “Flesh and Blood” (Mnofu ndi Mwazi) ndi “Appetite for Destruction” (Chikhumbo cha Chiwonongeko) ndipo ziri ndi mawu amene amatama kusangalatsidwa ndi kuvulaza wina kapena kudzivulaza, kugwirira chigololo, ndi mbanda. Chotero nkosadabwitsa kuti bukhu lofotokoza nyimbo za heavy metal la Stairway to Hell limatchula heavy metal kukhala “chilakiko cha mawu otukwana, chiwawa, mawu achindunji, nkhanza.” Nyimbo za heavy metal mobwerezabwereza zagwirizanitsidwanso ndi kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, kulambira Satana, ndi kudzipha kwa ozimvetsera. Komabe, malinga ndi kunena kwa malipoti apanyuzi, nyimbo za heavy metal zikulandiridwa pang’onopang’ono ndi anthu ochuluka.

Nyimbo zambiri za rap (kapena, hip-hop) nazonso zimakhala zonkitsa.b Magazini a Time akuti: “Olemba rap . . . amafuna moto wa nkhondo yolimbana ndi apolisi kapena miyala yamoto ya kugonana . . . koluluzika.” Kunena mosabisa mawu, mawu a nyimbo zambiri za rap zotchuka ngonyansa kwambiri moti sayenera kugwidwa mawu munomo. Ponena za nyimbo ina yotero, msungwana wina anati: “Liwu loyamba linatchulidwa—ndipo ndinachita kakasi!”

Komabe, nyimbo za rock zochuluka zolandiridwa ndi anthu ambiri nzosayenera kwa Akristu kumvetsera. Pamene kuli kwakuti zochuluka za nyimbo Zotchuka 40 kaŵirikaŵiri sizimakhala zachipongwe mofanana ndi rap ndi heavy metal, zambiri mwamachenjera—kapena mowonekera—zimachirikiza chisembwere ndi machitachita ena osakhala Achikristu. Mavidiyo a nyimbo, otchuka kwambiri pakati pa achichepere, amakulitsa chiyambukiro cha nyimbo mwa kuwonjezera zithunzithunzi zosonkhezera. M’kufufuza kwina mavidiyo a nyimbo, 57 peresenti anapezedwa kukhala achiwawa, ndipo 75 peresenti anali ndi zochitika za kugonana. Kavalidwe kosonkhezera ndi kavinidwe kodzutsa nyere kanapezedwanso kukhala kakusonyezedwa mobwerezabwereza m’mavidiyo a nyimbo.

Kodi Zingakuvulazeni?

Mmalo mwa kukhala zosangulutsa ndi zoyenera, nyimbo zambiri zothokozedwa lerolino mwachiwonekere ziri ‘za padziko, zauchinyama, zauchiŵanda.’ (Yakobo 3:15, NW) Komabe, mokopeka, siachichepere onse Achikristu amene amawona vuto lirilonse la kumvetsera nyimbo zonga zimenezi kapena kupenyerera mavidiyo. “Suyenera kuda nkhaŵa ndi mawu a nyimbo za rap,” akutsutsa motero msungwana wina. “Ndiiko komwe sutha kuwamva!” Aliyense amene anayesapo kumasulira mawu a rap angavomereze kuti mwapang’ono zimenezi nzowona.

Sinthaŵi zonse pamene achichepere amazindikira matanthauzo obisika a nyimbo zotchuka. M’kufufuza kwina, achichepere anauzidwa kufotokoza mawu a nyimbo zina zotchuka. Achichepere sanazindikire mitu yamachenjera ya kugonana, chiwawa, anamgoneka, ndi kulambira Satana imene inafala m’nyimbo zawo. Chotero The Journal of the American Medical Association inagamula kuti: “Palibe umboni wakuti nyimbo zimenezi ziri ndi chiyambukiro chirichonse [chovulaza] pa kakhalidwe ka achichepere.”

Komabe, Baibulo limasonyeza zosiyana. Choyamba, limatiuza kuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Tsopano, kodi mungataye maola ochuluka mukuyanjana kapena kumvetsera munthu wina amene amalankhula mawu otukwana kowopsa, amene anakusonkhezerani kugwiritsira ntchito anamgoneka, amene anachirikiza kulambira Satana, kapena amene anafotokoza kugonana koluluzika mwatsatanetsatane kwambiri? Ndithudi ayi! Pamenepatu kodi mawu onga ameneŵa angakhale bwanji osavulaza kwenikweni kokha chifukwa chakuti akuimbidwa kapena kulakatulidwa motsagana ndi zoimbira? Pamene mitu yoluluza yotero iimbidwa mobwerezabwereza, idzakuyambukirani mosakaikira! ‘Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?’ amafunsa motero Miyambo 6:27.

Chifukwa cha chimenechi Baibulo limatilangiza kusatchula konse zinthu zoipa, ngakhale kuzibwerezabwereza. (Aefeso 5:3-5; Afilipi 4:8) Amene amanyalanyaza lamulo la chikhalidwe chabwino limeneli mosakaikira ‘adzatuta chivundi.’ (Agalatiya 6:8) “Nyimbo zimakuchititsa kuganiza,” akuvomereza motero wachichepere wotchedwa Jodie. “Pamene zilakolako zoipa zibuka, nyimbozo zimasonkhezera zilakolakozo.” Pambuyo pomvetsera nyimbo ya rap imene mwatsatanetsatane inafotokoza kugonana koluluzika, wachichepere wina anavomereza kuti: “Sindinathe konse kuitulutsa m’maganizo mwanga.”

Ndipo bwanji za kumvetsera nyimbo za heavy metal zimene zimalengeza imfa, anamgoneka, kapena kulambira Satana? Wachichepere wina Wachikristu anayamba kumvetsera heavy metal ndipo posapita nthaŵi anayamba kumangoganiza za imfa. Kunali kokha mwa zoyesayesa zaphamphu za makolo ake ndi bwenzi Lachikristu lokula msinkhu kuti iye anakhoza kupeŵa ngozi yauzimu ndi yakuthupi.

Nthaŵi zina, malingalirowo amasandulika kukhala kuchitapo kanthu. (Yakobo 1:14, 15) Ndipo nyimbo zochuluka za lerolino mosamalitsa zimakonzedwera kudzaza maganizo anu ndi malingaliro oipa. Zowona, ngati munaleredwa mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo, sikuli kwachiwonekere kuti mudzachita mbanda kapena chisembwere pachifukwa chabe chakuti munadzimva m’nyimbo. Koma pali njira zina zimene mungasonkhezedwere nazo molakwa. Achichepere ena Achikristu ayamba kuvala zovala zachilendo ndi kumeta tsitsi monga momwe amametera oimba nyimbo za rock ndi rap. Kalankhulidwe, majesichala, ndi kakhalidwe ka achichepere otero kamasonyeza bwino lomwe kuti iwo ali kusonkhezeredwa ndi zimene amamva.

“Achichepere amati nyimbo zizimawayambukira,” akutero mnyamata wina wa ku South Africa. “Koma zimapatsa Satana mpata woloŵera m’moyo wanu—kuulamulira.” Iye anadziŵa zimenezi mwa zimene zinamchitikira, monga momwe akufotokozera: “Nyimbo zimene ndinkamvetsera zinali za kukhulupirira mizimu, anamgoneka, ndi kugonana.” Kodi ndimotani mmene anamasukira ku ziyambukiro zovulaza za nyimbo zoipitsazi?

“Ndinataya nyimbo zanga zonse. Kunali kusintha kwakukulu kukhala m’chipinda chabata. Koma kwandichititsa kukhala munthu wabwinopo.” Kodi inu mufunikira kutenga njira zofanana—osati kwenikweni kutaya nyimbo zanu zonse, koma kutaya marekodi anu amene mosakaikira ali oluluza?—Machitidwe 19:19.

Zimenezi zikutanthauza, osati kulekeratu kumvetsera nyimbo, koma kudziŵa kusankha! Njira yochitira zimenezi idzakhala mutu wa nkhani yamtsogolomu.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu akuti “nyimbo za rock” agwiritsiridwa ntchito m’nkhani ino kutanthauza iriyonse ya mitundu yambiri ya nyimbo zotchuka mwa achichepere.

b Wonani nkhani ya “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Cholakwika Nchiyani ndi Nyimbo Zanga?” m’kope la February 8, 1993.

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi kudzaza maganizo anu ndi mauthenga a imfa, chiwonongeko, ndi kululuzika kwa kugonana kungakuthandizeni kapena kukuvulazani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena