Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Cholakwika Nchiyani ndi Nyimbo Zanga?
“Atate amati, ‘Zimitsa nyimboyo! Ikundisokosera!’”—Mnyamata wazaka 13-19.
“Nyimbo zina za rap nzonyansa ndithu.”—Msungwana wazaka 13-19.
“SINKHANI yaikulu,” anadandaula motero Jodie. “Kodi nchifukwa ninji iwo amapanga nyimbo kukhala nkhani yaikulu?” Lisette wazaka khumi ndi zitatu zakubadwa amalingalira mofananamo. “Ndinyimbo chabe,” iye akuumirira kutero.
Kodi inunso mumakangana mosalekeza ndi makolo anu ponena za nyimbo? Ngati ziri choncho, mungakhale mukuyang’anizana ndi madandaulo, ziwopsezo, ndi malamulo nthaŵi iriyonse imene muliza tepi kapena rekodi yanu yapamtima. (“Atate amati, ‘Zimitsa nyimboyo! Ikundisokosera!’” akutero mnyamata wina.) Pokhala wotopa ndi mkanganowo, mwina mungaganize kuti makolo anu akukuza nkhani imene palibe. “Bwanji pamene iwo anali achichepere?” akutsutsa motero msungwana wina. “Kodi makolo awo sanalingalire kuti nyimbo zawo zinali zoipa?”
Msungwanayu wanena kanthu kena kokalingalira. M’mbiri yonse ya anthu, achikulire ndi achichepere alimbana kaŵirikaŵiri pankhani ya zokonda za munthu payekha. Chotero nkulekeranji kumvetsera nyimbo zanu pachifukwa chabe chakuti makolo anu samazikonda? Ndiiko komwe, kodi cholakwika nchiyani ndi nyimbo zanu?
Nyimbo—Malo Ake m’Moyo
Eya, palibe aliyense amene kwenikweni akunena kuti kumvetsera nyimbo nkoipa. Mbali zina za Baibulo lenilenilo—makamaka masalmo—poyamba zinali nyimbo zoimbidwa. M’nthaŵi za Baibulo, nyimbo zinali ndi mbali yaikulu m’kulambira Mulungu. (Salmo 149:3; 150:4) Nyimbo zinalinso njira zosonyezera chimwemwe, chisangalalo, ndi chisoni. (Genesis 31:27; Oweruza 11:34; 1 Samueli 18:6, 7; Mateyu 9:23, 24) M’masiku a Yesu, nyimbo zinali kuimbidwa pamasonkhano amayanjano; zinawonjezera chimwemwe pachochitikacho.—Luka 15:25.
Nyimbo zikupitirizabe kukhala ndi mbali yofunika lerolino—makamaka pakati pa achichepere. The Journal of the American Medical Association ikuti: “Pakati pa amene ali m’giredi lachisanu ndi chiŵiri ndi lakhumi ndi chiŵiri, wachichepere wamba amamvetsera nyimbo za rock kwa maola 10,500, ochepera pang’ono chabe pa chiwonkhetso cha maola otaidwira m’kalasi kuyambira sukulu ya nasale mpaka ya sekondale.”
Kufufuza kwasonyeza kuti achichepere ambiri a ku United States amamvetsera pafupifupi nyimbo za rock ndi pop zokha. (Kuti tipeputse zinthu, tidzagwiritsira ntchito mawu a “rock” ndi “pop” kutchulira pafupifupi mitundu yonse ya nyimbo zofala kwa achichepere—kuyambira nyimbo za soul ndi new wave kufikira za rap ndi heavy metal.) Malinga ndi kunena kwa The World Book Encyclopedia, “nyimbo za rock sizirinso nyimbo za achichepere a ku Amereka okha. Ziri nyimbo za dziko lonse.”
Kukopa kwa Nyimbo za Rock
Kodi nchifukwa ninji nyimbo za rock ziri zotchuka kwambiri? Malinga ndi kunena kwa bukhu lakuti Youth Trends, rock iri monga “chinenero chimodzi cholankhulidwa ndi achichepere onse.” Chotero achichepere ena amalingalira kuti kuyendera limodzi ndi dongosolo la nyimbo—kudziŵa magulu oimba ndi nyimbo zatsopano—kumawathandiza kukhala olandiridwa ndi achichepere anzawo. Nyimbo zimapereka maziko amodzi a unansi pakati pa achichepere ndi mitu ya nkhani zokambitsirana zosatha.
Komabe, achichepere ambiri amasangalala kwambiri ndi nyimbo pamene ali okha. Kodi mumatopa kwambiri kusukulu? Pamenepo mwina ndinu wofanana ndi msungwana wotchedwa Bree amene akuti: “Ndimakakhala m’chipinda mwanga, nkutsegula kwambiri siteriyo ndipo ndimangokhala mmenemo. Kumathetsa kupsinjikako ndi kutopa.” Pamene kuli kwakuti nyimbo za rock kaŵirikaŵiri zimanenedwa kukhala zaphokoso ndi zosamveka bwino, nyimbo zotchuka zambiri ziridi ndi maimbidwe abwino ndi kamvekedwe kosangalatsa.
Komabe, anthu ambiri amakopeka ndi maliridwe ake. “Ndinyimbo zosavuta kuvina,” anafotokoza motero msungwana wina pamene anafunsidwa chifukwa chimene iye amakondera nyimbo za rap. Koma ambiri amakopedwanso ndi mawu. Pokhala olembedwera makamaka achichepere, mawu a nyimbo za pop amasonyeza malingaliro ndi nkhaŵa zosiyanasiyana za achichepere. Nyimbo za rap nzodziŵika kwambiri ndi kusumika kwake pa nkhani zofala, zonga ngati ufuko ndi kupanda chilungamo m’chitaganya. “Ndimatsegula wailesi ndipo nyimbo zambiri ziri zosamveka, zimandikwiitsa,” akudandaula motero wachichepere wotchedwa Dan m’magazini a Newsweek. “Rap iri ndi nkhani zenizeni ndi zinthu zenizeni. Imasangalatsa kumvetsera.”
Komabe, uthenga wa nyimbo ndiwo umene ungakhale wodetsa nkhaŵa kwa makolo anu.
Uthenga wa Rap
Mwachitsanzo, talingalirani nyimbo za rap. M’nyimbo za rap, mawu ake—mawu opotozedwa olembedwa mwandakatulo—amalankhulidwa, osati kuimbidwa, motsagana ndi maliridwe amphamvu. Ndithudi, palibe chirichonse choipa mwachibadwa m’zimenezi. Nyimbo zambiri zomveka m’zaka makumi ambiri zaphatikizapo mawu olankhulidwa. Koma nyimbo za rap zimachita zimenezi mopambanitsa.
Malinga ndi zimene zanenedwa, rap (kapena, hip-hop) inakhala yotchuka kalelo m’ma 1970 m’makalabu ovinira aang’ono mu New York City kumene achichepere a m’makomboni ankapita kaŵirikaŵiri. Pamene madisc jockey anayamba kulankhula (kapena, kuchita rap) mkati mwa kulira kwa zoimbira zojambulidwa, ovinawo anatengeka maganizo. Mwamsanga nyimbo za rap zinafalikira kuchokera m’makalabu a m’makwalala ndi a pansi pa nthaka nizikhala pakati pa nyimbo zolandirika. Ochita rap odzitcha maina achipongwe ngati nyimbo zawo—Public Enemy, M. C. Hammer, ndi Vanilla Ice—mosataya nthaŵi anayamba kumveka ndi mtundu wa nyimbo zawo zaphokoso.
Mosangalatsa, pamene mtola nkhani wa Galamukani! anafunsa kagulu kopangidwa ndi mafuko osiyanasiyana ka achichepere Achikristu ochokera mumlaga kuti, “Kodi ambiri a inu mumamvetsera nyimbo za rap?” modabwitsa ambiri anati inde! “Kodi nchiyani chimene mumakonda m’nyimbo za rap?” iye anafunsanso motero. “Maliridwe ake,” anayankha motero msungwana wina. “Amamveka bwino, ndipo ngosavuta kumvetsera.” “Mungathe kuvina,” anayankha motero wina. Komabe, funso lotsatira linayankhidwa movutirapo: “Kodi nyimbo zina za rap nzoipa kwa Akristu?”
Onse atachita manyazi kwakanthaŵi, msungwana wina anavomera: “Nyimbo zina za rap nzonyansa ndithu.” Ena mokakamizika anavomerezana naye. Ndithudi, panapezeka kuti achichepere ambiri anali ozoloŵerana kwambiri ndi mpambo waukulu wa nyimbo zokaikitsa—nyimbo zimene zinachirikiza uchiwerewere ndi mkhalidwe woluluzika ndi mawu onyansa. Ena anavomereza kuti zambiri za nyimbo zimenezi zinagwiritsira ntchito mawu otukwana momasuka.
Inde, nyimbo za rap zochuluka zimawoneka kukhala zikupereka uthenga wa chipanduko, chiwawa, mkwiyo, ufuko, ndi uchamuna m’kugonana. Wochirikiza rap Daniel Caudeiron, prezidenti wa Black Music Association of Canada, amene amathokoza rap kukhala “yabwino kwambiri,” akuvomereza kuti nyimbo za rap zochuluka ziri “[zotsutsa akazi], zoluluza akazi ndipo nthaŵi zina zotukwana.”—Maclean’s, November 12, 1990.
Makhalidwe a Rap
Kunena zowona, sinyimbo zonse za rap zimene ziri zachisembwere kapena zachiwawa. Malinga ndi kunena kwa The New York Times, zina za izo zimachirikiza zonulirapo zabwino zonga maphunziro, kuletsa kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, ndi kuthetsa mavuto a m’chitaganya. Koma mawu osatukwana angakhale akamodzikamodzi kwambiri, osati anthaŵi zonse. Pamene Newsweek inayesa marekodi khumi opambana a rap, mogwiritsira ntchito muyezo wofanana ndi umene mafilimu amayesedwa nawo ku United States, aŵiri okha ndiwo analingaliridwa kukhala G, kapena oyenera anthu onse. Newsweek inaika marekodi anayi pa R (ya anthu achikulire okha), ndipo aŵiri anaikidwadi pa X chifukwa cha “mawu otukwana” ndi kufotokoza kugonana mwatsatanetsatane.
Ndiponso, uthenga wa rap sumathera m’mawu ake chabe. Rap yachititsa kusintha kwa makhalidwe. Achichepere mamiliyoni ambiri amavala zovala zazikulu koposa, nsapato za tenesi zosamanga malamba ake zofika pamwamba pa akakolo, majini okhuthukira, maunyolo a golide, tizipewa ta baseball, ndi magalasi akuda zimene ziri zovala za rap. Ndiponso ambiri amatsanzira majesichala odziwonetsera ndi kakhalidwe ka oimba nyimbo za rap. Ndipo zodabwitsa kwa makolo ndi kwa aphunzitsi omwe, mawu opanda tanthauzo onga “yo!” ndi “dis”—mawu opotozedwa olankhulidwa ndi achichepere a m’makwalala othokozedwa ndi rap—aloŵerera m’chinenero cha masiku onse.
Kunena zowona nyimbo zina za rap zingatsutsedi chisalungamo. Koma rap yonse irinso njira ya moyo yopandukira miyezo ya Mulungu ya kakhalidwe, kavalidwe, ndi kalankhulidwe. Kodi Mkristu, ndi nyimbo zake zimene amakonda, angafune kudziika paupandu wa kuloŵetsedwa m’khalidwe lokaikitsalo?
Ndithudi, nyimbo za rap sindizo mtundu wokha wa nyimbo zimene zimakhala zoipitsitsa. Magazini a Time akusimba kuti: “Pafupifupi mbali iriyonse ya mtundu wa nyimbo zatsopano za pop za ku Amereka iri yoipa [yonyansa]. Kagulu ka akatswiri a heavy metal ka Motley Crüe kamapembedza zizindikiro za [S]atana ndipo ka Beastie Boys kamatsanzira kuchita psotopsoto kali pasteji.” Baibulo linalosera kuti ‘masiku otsiriza . . . anthu oipa ndi onyenga adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.’ (2 Timoteo 3:1, 13) Pamenepatu, kodi zimenezi ziyenera kukudabwitsani kuti nyimbo zochuluka za lero zimapereka uthenga woipa kwa achichepere Achikristu?
Chotero makolo anu moyenerera angade nkhaŵa kwambiri ngati inu mumakonda rap kapena mitundu ina yopambanitsa ya nyimbo za rock. Iwo angawopere kuti kumvetsera nyimbo zotero nthaŵi zonse kungakuvulazeni. Kodi nkhaŵa zawo zingakhale zotsimikizirika? Kope lathu lotsatira lidzayankha funso limeneli.
[Zithunzi patsamba 17]
Achichepere ambiri tsopano amatsanzira kavalidwe ndi kakhalidwe ka oimba nyimbo za “rap”