Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingasiye Motani Kumwa?
“Nthaŵi zonse ndinali mumkhalidwe wowopsa patsiku lotsatira, ponse paŵiri mwamalingaliro ndi mwauzimu!”—Bob.
“Ndinali m’vuto mosalekeza panyumba, kusukulu, ndi mabwenzi ndipo ndi apolisi!”—Jerome.
BOB ndi Jerome onse aŵiri analipilira mtengo wa kumwa zoledzeretsa mopambanitsa ndi mwakaŵirikaŵiri kwambiri. Onse aŵiri anadzamwerekera ndi zoledzeretsa. Ndipo pamene kuli kwakuti Bob potsirizira anali wokhoza kulekeratu kumwa, Jerome adakayesayesabe kugonjetsa uchidakwa.
Kumwerekera ndi zoledzeretsa ndiko vuto lomakulakula pakati pa achichepere m’mbali zambiri zadziko. Ena akuyerekezera kuti mu United States mokha, achichepere pafupifupi mamiliyoni asanu ali ndi vuto lowopsa la kumwa. Komabe, ngati muli wachichepere Wachikristu, mosakaikira mwapewa kuyeseza zoledzeretsa, makamaka ngati kumwa kwa azaka 13-19 kuli kotsutsana ndi lamulo m’chitaganya chakwanu. Komabe, chidziŵitso chotsatirapochi chingatumikire kulimbikitsa chitsimikizo chanu cha kusaphatikizidwa m’kuyamba kumwa—pafupifupi kufikira mutakula ndi kukhala wokonzekera bwinopo kuchita nazo. Koma ngati inu mwamwerekera kale ndi zoledzeretsa, tikhulupirira kuti chidziŵitso chino chidzakuthandizani kugonjetsa vuto limeneli. Mwa kuyesayesa kwanu kwenikweni ndi mwachithandizo cha Yehova Mulungu, kuchira nkotheka.
Kugonjetsa Kukana
Sitepe loyamba ndi lovuta kopambana limene muyenera kutenga ndilo kugonjetsa kukana. Zidakwa mofanana zimakana kukhulupirira kuti ziri ndi vuto lirilonse la kumwa. ‘Ndingathe kuchita nazo,’ ndiko kuwiringula kodzitukumula kwa chidakwa. Mwachitsanzo, talingaliranitu, wazaka 15 zakubadwa wina amene anati: “Ndiribe vuto la kumwa. Ndimamwa kokha mabotolo asanu ndi limodzi a mowa madzulo alionse.” Tikukumbutsidwa za munthu amene ‘adzidyoletsa yekha m’kuwona kwake, kuti asapeze choipa chake ndi kukwiya nacho.’—Salmo 36:2.
Inde, kukana nkwakupha. Chotero ngati muli ndi vuto la kumwa, muyenera kuvomereza chowonadi chopwetekacho.a Musanyalanyaze mabwenzi, abale, kapena makolo amene akukuuzani kuti mumamwa mopambanitsa. Iwo saali adani anu chifukwa chakuti akukuuzani chowonadi. (Yerekezerani ndi Agalatiya 4:16.) Bob (wotchulidwa pachiyambi) ankamwa kwadzawoneni pakutha kwamlungu kulikonse. Pamene bwenzi lake linamuuza zimenezo, Bob anakana lingaliro lirilonse lakuti anali ndi vuto la kumwa, ndipo anathetsa makambitsiranowo. Koma kodi zoledzeretsa zinali kuyambukira motani moyo wa Bob? “Ndinali wamantha ndi wankhaŵa kopambanitsa ngati sindinamwe ndipo ndinali wosalamulirika ngati ndinamwa,” anaulula motero Bob. “Moyo wa banja langa unasweka—monga momwe unachitiranso unansi wanga ndi Mulungu.”
Pachochitika china, Bob potsirizira analeka kutsutsa navomereza kwa bwenzi lake kuti iye analakalakadi zoledzeretsa. Pokhala atagonjetsa vuto la kukana, Bob anali wokhoza kuyamba kuchira.
Kulitsani Chitsimikizo cha Kuleka
Profesala George Vaillant akulemba kuti “uchidakwa . . . ngwochiritsika kotheratu, koma . . . udzafunikira kukhulupirika kwambiri kwa wodwalayo.” Zimenezo zikuphatikizapo kukhala kwanu wotsimikiza kuleka kumwa zoledzeretsa. Kupanda chitsimikizo kungatanthauze kukhalira moyo—ndi kufa—monga chidakwa. Kodi chingathandize nchiyani? Kusumika pa mkhalidwe wovulaza wa uchidakwa kungakuthandizeni “kudana nacho choipa” ndipo kungalimbikitse chitsimikizo chanu cha kulekeratu kumwa.—Salmo 97:10.
Mwachitsanzo, mungalingalire mwamphamvu za chivulazo chachikulu chimene uchidakwa umapangitsa mwakuthupi, mwamalingaliro, ndi mwamakhalidwe. Ndithudi, kumwa kungawonekere kukhala kukumatonthoza kupweteka mtima kwanu kapena malingaliro a kupanda pake kwakanthaŵi. Koma m’kupita kwanthaŵi kudalira pa zoledzeretsa kumatumikira kokha kuyambitsa mavuto owonjezereka; zibwenzi zimatha, ndipo maunansi abanja amaipitsidwa. Ndiponso, chifukwa chakuti zoledzeretsa zimachepetsa kulingalira kwanu molama, zingathe mosavuta ‘kuchotsa cholinga chabwino’ ndi kukuloŵetsani m’tchimo lalikulu.—Hoseya 4:11.
Lingaliraninso, zimene kumwa zoledzeretsa zochuluka kungachitire thupi lanu, kuvulaza mwapang’onopang’ono ziŵalo zanu zofunika. Chifukwa chake Baibulo limanena kuti kumwa mopambanitsa kumachititsa zoposa ‘chisoni, kuipidwa, makangano, nkhaŵa, ndi zilonda.’ (Miyambo 23:29, 30, New English Bible) Kodi chikondwerero chakanthaŵi chirichonse chimene mumapeza nchoyenerera mtengowu?
Kungathandizenso kudzikumbutsa kuti simufunikira zoledzeretsa kuti musangalale. Ndipo simufunikira chisangalalo chachiphamaso kuti mupeze ulemu waumwini, thanzi labwino, mabwenzi okhulupirika, ndi banja lachikondi. Chipambano m’mbali zimenezi za moyo chimachokera m’kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu. (Salmo 1:1-3) Mawu amenewo amakupatsaninso chiyembekezo cha mtsogolo mosangalatsa—moyo wamuyaya wopanda zopweteka zamalingaliro kapena zakuthupi! (Chivumbulutso 21:3, 4) Kukhala ndi chiyembekezo choterocho kumakupatsani chifukwa chinanso cholekera zoledzeretsa.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 6:9, 10.
Pezani Chithandizo
Komabe, kungokhala ndi chikhumbo cha kuchira kokhako kaŵirikaŵiri sikokwanira. Mudzafunikiranso chichirikizo ndi chithandizo cha ena. ‘Aŵiri aposa mmodzi,’ anatero Mfumu Solomo. ‘Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake.’ (Mlaliki 4:9, 10) Kudalira winawake kukuthandizani pavuto lanu sikudzakhala kofeŵa. Koma Katy yemwe anali kuchira kuuchidakwa akupereka uphungu wakuti: “Phunzirani kudalira anthu, makamaka banja lanu.” Inde, m’zochitika zambiri banja lanu ndilo limene liri pamalo abwino kopambana okusonyezani chikondi ndi chichirikizo chimene mufunikira.
Zowona, mkhalidwe wa banja lanu ungakhale umene unasonkhezera kuyamba kwanu kumwa. Koma ngati makolo anu anauzidwa za mkhalidwe wanu, kodi sangawone kufunika kwa kuwongolera zinthu panyumba? Chotero kodi mulekeranji kuyesa kufikira makolo anu, mukumawauza kuti muli ndi vuto lalikulu? Mmalo mwa kuwaimba mlandu kotheratu, pemphani chithandizo chawo ndi chichirikizo. Kukhala wosabisa mawu ndi wowona mtima kwa makolo anu kudzathandiza banja lanu ‘kugwirizana pamodzi mogwirizana’ monga momwe banja la Mulungu liliri. (Aefeso 4:16) Mwanjirayi nonsenu mungayambe kugwirira ntchito pamodzi kukuchira kwachipambano.
Ngati chichirikizo chabanja sichopezeka, ena angathandize.b (Miyambo 17:17) Bob anakhala bwenzi la mkulu Wachikristu amene anawonana naye mlungu uliwonse kwanyengo ya miyezi ingapo kuyang’anira kupita kwake patsogolo. Bob akuti: “Chikondwerero ndi chisamaliro chake zinandipatsa ulemu waumwini zimene ndinafunikira kuti ndileke chizoloŵezi changa choipa.”—Yakobo 5:13, 14.
Koposa zonse, zindikirani kuti mufunikira chithandizo cha Yehova Mulungu. Dalirani pa iye kaamba ka nyonga. Inde, mwachithandizo cha Yehova “osweka mtima” ‘angachiritsidwe ndi kumangidwa mabala awo’ ndi Yehova.—Salmo 147:3; wonaninso Salmo 145:14.
Pezani Mabwenzi Atsopano
Mafufuzidwe a ku New Zealand anasimba kuti mabwenzi ali ndi chisonkhezero chachikulu pa achichepere amene amagwiritsira ntchito molakwa zoledzeretsa. Chifukwa chake mudzakupeza kukhala kovuta kuleka kumwa ngati muyanjana ndi omamwa. Chifukwa cha chimenechi Baibulo limalimbikitsa kuti: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo.” (Miyambo 23:20) Yambitsani zibwenzi zatsopano, zabwino. Monga momwe ziliri zowona kuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma,” mabwenzi abwino ali chisonkhezero chabwino.—1 Akorinto 15:33.
Kim anawona zimenezi kukhala zowona. “Kunali kovuta,” akuvomereza motero, “koma ndinatofunikira kusintha mabwenzi anga . . . Sindinali kufuna kukhala pafupi ndi zoledzeretsa kapena anamgoneka.” Ndithudi, mabwenzi osamwa angawonekere kukhala ovuta kuwapeza. Komabe, mudzapeza kuti, achichepere achitsanzo chabwino pakati pa Mboni za Yehova samaphatikizidwa m’kumwa kosaloleka. Ndipo iwo samadalira pa zoledzeretsa monga magwero a kusanguluka kapena opulumukira. Chotero iwo angathandize—osati kudodometsa—zoyesayesa zanu za ‘kuvula munthu wakale limodzi ndi ntchito zake.’—Akolose 3:9.
Mungathe Kuchira!
Kukhala wopanda zoledzeretsa idzakhala nkhondo yosalekeza kwa inu. Panthaŵi zina kulekeratu kungakhale kovuta kwambiri. “Ndidakali ndi chilakolako champhamvu kwambiri [cha kumwa],” anavomereza motero Ana, “makamaka pamene ndakhumudwa, ndagwiritsidwa mwala, ndatsenderezedwa maganizo kapena ndakwiya.” Chotero sikwachilendo kwa chidakwa chomachira kubwevuka, zikumapangitsa malingaliro amphamvu a liwongo. Ngati zimenezo zichitika, kumbukirani kuti “timakhumudwa tonse pazinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Kumbukiraninso, kuti Yehova ali Mulungu wa chifundo amene amamvetsetsa zofoka zanu.—Salmo 103:14.
Komabe, samalani kuti musagwiritsire ntchito molakwa kukoma mtima kwa Mulungu. Phunzirani m’zophophonya zanu, ndipo tsimikizirani koposa ndi kale lonse kusabwevukanso. Mwa kusonyeza chitsimikizo choterocho, Bob anali wokhoza kusiya kumwa. Chiyambire pamenepo, iye wakhala wokhoza kusangalala ndi maunansi amtendere ponse paŵiri ndi banja lake ndiponso ndi Mulungu. Moyo wake wachimwemwe tsopano umaphatikizapo utumiki monga minisitala wanthaŵi yonse. Chimwemwe ndi mtendere wamaganizo zidzakhala zanunso, ngati mupambana nkhondo yomenyana ndi zoledzeretsa.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Kumwa Kungandimwerekeretsedi?” (Galamukani! ya January 8, 1993) ingakuthandizeni kuzindikira ngati muli ndi vuto pankhaniyi.
b Ambiri apindula ndi chithandizo cha asing’anga ndi aphungu amene anaphunzitsidwa kuchita ndi kumwerekera ndi zoledzeretsa. Akatswiri ena amakhulupirira kuti kufikira pamene mkhalidwe wa kumwerekera weniweniwo walekeka, kugwirira ntchito pa mbali zina za kuchira sikungapambane konse. Chifukwa cha chimenechi ndi zina, ena amavomereza kuti zidakwazo zikhale ndi programu ya kuchotsa ziyambukiro zake m’chipatala kapena m’kiliniki.
[Chithunzi patsamba 13]
Zidakwa zachichepere zimakonda kukana kuti ziri ndi vuto