Kupanikizidwa kwa Tchalitchi cha Katolika
“PENTEKOSTE WATSOPANO.” Chimenecho ndicho chinali chiyembekezo chimene Papa John XXIII anachilongosola kaamba ka bungwe la mgwirizano wa matchalitchi loyambika mu 1962 ndipo lomwe linadzafikira pakudziŵika monga Vatican II. Iye anayembekezera kuti ikakhala njira yoyambitsiranso uzimu pakati pa Akatolika ndikuti ikabweretsa masinthidwe amene akatsegula njira yogwirizanitsa Chikristu Chadziko.
Koma malingaliro a aggiornamento (kuzoloŵeretsa) amenewo sanayanjidwe ndi nthumwi zonse za m’Vatican. The New Encyclopædia Britannica ikusimba kuti: “Monga chotulukapo, chosankha cha Papayo chinalandiridwa ndi zikaikiro ndi Gulu lake losafuna masinthidwe, lomwe linatsimikiziridwa kuti tchalitchi chinkayenda bwino pansi pa ulamuliro wa Pius XII ndipo sanawone chifukwa chabwino chopangira masinthidwe amene John anawalingalira. Kwenikweni akadinala ena a Vatican anachita zonse zomwe akanatha kuchedwetsa msonkhanowo kufikira pamene nkhalambayo ikamwalira ndipo ntchitoyo ikanyalanyazidwa mwakachetechete.”
Lamulo la Vatican Ii pa Mgwirizano wa Matchalitchi
Papa John XXIII anakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali mokwanira kukhazikitsa Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican, koma anamwalira mwamsanga pambuyo pake, mu June 1963, msonkhanowo usanatsirizidwe konse mu December 1965. Komabe, Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi linalengezedwa poyera ndi Papa Paul VI pa November 21, 1964. Ilo linafotokoza m’mawu ake oyambirira kuti: “Kubwezeretsedwa kwa umodzi pakati pa Akristu onse ndiko chodera nkhaŵa chachikulu cha Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican.”
Moyenerera, wansembe wa Jesuit wotchedwa Walter M. Abbott analemba motere mu The Documents of Vatican II: “Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi limazindikiritsa kuloŵa kotheratu kwa Tchalitchi cha Roma Katolika m’gulu la mgwirizano wa matchalitchi.” Ndipo mofananamo, pansi pa mutu wakuti “Chiroma Katolika chikutsatira Msonkhano wachiŵiri wa Vatican,” The New Encyclopædia Britannica inanena motsimikiza motere: “Tchalitchi cha Roma Katolika chakana mwalamulo kaimidwe kake ka ‘tchalitchi chimodzi chowona.’”
Koma kodi Tchalitchi cha Katolika chakanadi kaimidwe kameneko? Kodi umodzi umenewo unabweretsedwa pamaziko otani? Pambuyo pofotokoza ukulu umene Akatolika akakhala ndi phande m’zochita za mgwirizano wa matchalitchi, Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchilo linalamula motere: “Msonkhano wopatulikawu ukusonkhezera okhulupirika kusatsatira changu chochepa kapena chosasamala. . . . Ntchito yawo ya mgwirizano wa matchalitchi singakhale yoposa china chirichonse koma mowonadi ndi motsimikiza Njachikatolika, uku ndiko kuti, yokhulupirika ku chowonadi cholandiridwa kuchokera kwa Atumwi ndi Abambo, ndipo njogwirizana ndi chowonadi chimene Tchalitchi cha Katolika chakhala chikuvomereza nthaŵi zonse.”
Zopinga Umodzi
Mfundo njakuti, Tchalitchi cha Roma Katolika sichinaleke kaimidwe kake kakuti ndicho tchalitchi chowona chimodzi chokha. Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi la Vatican II limafotokoza kuti: “Njira yokwanira yachipulumutso ingapezeke kupyolera m’Tchalitchi cha Kristu cha Katolika chokha, chimene chiri thandizo lachilengedwe chonse kulinga ku chipulumutso, chomwe chingatipezetse chipulumutso. Kunali ku gulu la atumwi lokha, lomwe Petro anali mkulu wake, kumene timakhulupirira kuti Ambuye Wathu anaikizira madalitso onse a Pangano Latsopano.”
Bukhu laposachedwapa Lachifrenchi lakuti Théo—Nouvelle Encyclopédie Catholique (1989) likufotokoza kuti: “Kwa Akatolika, papa, monga mloŵa mmalo wa Petro, ali mwa maphunziro azaumulungu maziko a umodzi wa Tchalitchi ndi mabishopu. Komabe, mfundo yeniyeni njakuti, papa ndiye wopangitsa wamkulu wa kugaŵikana pakati pa Akristu.”
Chiphunzitso chogaŵanitsa chimenechi cha ulamuliro wa papa ncholingana kwenikweni ndi ziphunzitso zoikidwiratu za kusalakwa kwa papa ndi kuloŵa mmalo kwa utumwi kwa abishopu Achikatolika, zonse ziŵiri zomwe nzosavomerezedwa ndi matchalitchi a Chikristu Chadziko osakhala Achikatolika. Kodi Vatican II inachita chirichonse kuwongolera kaimidwe Kachikatolika pa ziphunzitso zimenezi?
Vatican II Dogmatic Constitution on the Church ikuyankha motere m’ndime 18: “Sinodi yopatulika imeneyi, potsatira mapazi a Msonkhano Woyamba wa Vatican [umene unalamula chiphunzitso choikidwiratu cha kusalakwa kwa papa], ikuphunzitsa ndi kulengeza kuti Yesu Kristu, pasitala wamuyaya, anakhazikitsa Tchalitchi chopatulika mwakuikizira atumwi ndi ntchito yawo monga momwe iyemwini anatumizidwira ndi Atate (yerekezerani ndi Yoh. 20:21). Iye anafuna kuti aloŵa mmalo awo, abishopu, ayenera kukhala abusa m’Tchalitchi chake kufikira mapeto a dziko. Komabe, ncholinga choti bungwe la abishopulo likhale limodzi losagaŵikana, iye anaika Petro pamwamba pa atumwi ena, ndipo mwa iye anakhazikitsa magwero osatha owoneka ndi maso ndi maziko a umodzi ponse paŵiri wachikhulupiriro ndi chimvano. Chiphunzitso chimenechi chonena za udindo, kukhalitsa, mtundu ndi tanthauzo la ulamuliro wopatulika wa Papa Wachiroma ndi udindo wake wa chiphunzitso cha kusalakwa, sinodi yopatulikayo ikulamulanso kuti chiyenera kukhulupiriridwa zolimba ndi okhulupirika onse, ndipo popitiriza ndi cholinga chosasinthika chimodzimodzichi, ikulingaliranso kulengeza poyera ndikumveketsa bwino chiphunzitso chonena za abishopu, aloŵa mmalo a atumwi, omwe amatsogolera nyumba ya Mulungu wamoyo pamodzi ndi mloŵa mmalo wa Petro, Nthumwi ya Kristu ndi wolamulira wowoneka ndi maso wa Tchalitchi chonse.”
Moyenerera, Dogmatic Constitution on the Church imeneyi inalengezedwa poyera ndi Papa Paul VI patsiku limene anasaina Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi. Ndipo patsiku limodzimodzilo la November 21, 1964, iye anapanga ndemanga yolengeza “Mariya [kukhala] ‘Mayi wa Tchalitchi,’ ndiko kuti, wa okhulupirika onse ndi apasitala onse.” Kodi zinganenedwe motani kuti Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi ‘linazindikiritsa kuloŵa kotheratu kwa Tchalitchi cha Roma Katolika m’gulu la mgwirizano wa matchalitchi’ pamene papa anasankha patsiku lomwelo pamene chinafalitsidwa kutsimikizanso za ziphunzitso zoikidwiratu zimene ziri zosalandirika konse kwa mamembala ambiri a bungwe la WCC (World Council of Churches)?
Kupanikizidwa kwa Tchalitchi
Dr. Samuel McCrea Cavert, yemwe kale anali mlembi wamkulu wa National Council of Churches, amene anachita mbali yaikulu m’kupangidwa kwa bungwe la World Council of Churches, anafotokoza kuti: “Lamulo [la Mgwirizano wa Matchalitchi] silimayanjanitsa kwenikweni kulingalira kwake ndi kunena kwakuti Roma Katolika ndicho Tchalitchi chowona chokha. . . . Kogwirizana nako ndikunena kwa ulamuliro wa Petro ndi ulamuliro wake pa Tchalitchi chonse. Kunena kumeneku kumawoneka kusonyeza kuti kumvetsetsa kwa Roma Katolika kwa mgwirizano wa matchalitchi nkozikidwa mosasunthika pa Roma.”
Dr. Konrad Raiser, wachiŵiri kwa mlembi wamkulu wa bungwe la WCC, analengeza kuti: “Papa [John Paul II] akupanga zilengezo zambiri za mgwirizano wa matchalitchi, koma iye wasonkhezeredwa ndi ntchito yomwe ikumpititsa kumalo osiyana.”
Kusemphana kowonekeratu kumeneku pakati pa chiphimba maso cha mgwirizano wa matchalitchi cha Vatican ndi kumamatira kwake kwathithithi ku malingaliro amwambo kumangovumbula kuti Tchalitchi cha Roma chikudzipeza pampanipani. Ngati nchowonadi ponena za kukhalamo ndi phande kwake m’gulu la mgwirizano wa matchalitchi kaamba ka umodzi Wachikristu, chiyenera kutsutsa zonena zake zakuti ndicho tchalitchi chimodzi chokha chowona. Ngati chikana kutsutsa chonena chimenechi, chiyenera kuvomereza kuti mgwirizano wake wa matchalitchi uli kokha kachitidwe kofuna kunyengerera matchalitchi a Orthodox ndi Protestanti kubwerera kukhola la Katolika.
Kunena mwatchutchutchu, Tchalitchi cha Katolika chiyenera kaya kuvomereza kuti zonena zake za zaka mazana ambiri nzonama kapena kuti kukhalamo ndi phande kwake kwapanthaŵi ino m’gulu la mgwirizano wa matchalitchi kuli chinyengo chabe. Mamembala ambiri owona mtima a matchalitchi a Chikristu Chadziko anazizwitsidwa ndi njira zonse ziŵirizo. Iwo amadabwa kaya ngati umodzi Wachikristu udzafikiridwa konse.
[Mawu Otsindika patsamba 28]
‘Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi limazindikiritsa kuloŵa kotheratu kwa Tchalitchi cha Roma Katolika m’gulu la mgwirizano wa matchaliltchi’
[Chithunzi patsamba 27]
Vatican II inaika Tchalitchi cha Katolika pampanipani
[Mawu a Chithunzi]
UPI/Bettmann Newsphotos