Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 5/8 tsamba 30
  • Vuto la Khofi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vuto la Khofi
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nthanga Imene Inazungulira Dziko
    Galamukani!—2006
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Luso Lopanga Khofi
    Galamukani!—2009
Galamukani!—1991
g91 5/8 tsamba 30

Vuto la Khofi

MAKAPU oposa 1,500,000,000 patsiku! Mogwirizana ndi kuŵerengera kwaposachedwapa, ndiko kuchuluka kwa khofi womwedwa padziko lonse. Kumwedwa kwakukulu kumeneku kwapitirizabe mosasamala kanthu za machenjezo ochokera kwa asayansi m’zaka zaposachedwapa kuti anthu omwa khofi akuyang’anizana ndi nakatande wokulira wa maupandu, kuyambira nthenda za mtima, nthenda ya suga ndipo ngakhale mitundu yosiyanasiyana ya kansa. Pamenepa, nchifukwa ninji kulikwakuti anthu omwa khofi oŵerengeka okha ndiwo asiya ndipo amapeŵa kuimwa?

Zaka zoposa 40 zapitazo, asayansi afalitsa malipoti oposa mazana asanu onena za ziyambukiro za kumwa khofi. Koma chikhalirechobe zigamulo zawo zakhala kwenikweni, zosatsimikiza. Chifukwa ninji? Chifukwa chimodzi ndi ichi, khofi ngocholoŵana kwambiri kuposa mmene amawonekera. Kapu ya khofi ingakhale ndi makemiko achibadwa oposa mazana asanu. Komabe, mafufuzidwe ambiri amapereka chisamaliro pa nsanganizo imodzi yokha, mankhwala otsitsimula a caffeine.

Mwa anthu ena, caffeine ingachititse kusoŵa tulo ndi kukwiya msanga kapena kuchipangitsa chovuta kupereka chisamaliro. Nanga bwanji ponena za kansa? Magazini otchedwa Which? akusimba kuti: “Kwakukulukulu kufufuza kulikonse kosonyeza kugwirizana kothekera [pakati pa caffeine ndi kansa], pali kwina kokhala ndi zotumbidwa zosemphana nako.” Pamenepa, nzosadabwitsa kuti katswiri wofufuza khofi wa ku London akusimba kuti pakati pa anthu wamba, pakhala palibe “kachitidwe kathanzi koipeŵeratu khofi.” Kuwonjezerapo, ambiri amadziŵa kuti tii, koko, ndi zakumwa za cola nazonso ziri ndi caffeine. Kwenikweni, magazini a Which? akufotokoza kuti “poyerekezera, tii iri ndi caffeine yochuluka koposa khofi, koma mwachisawawa njochepa imene imagwiritsiridwa ntchito popanga kapu ya tii.”

Chikhalirechobe, pali machenjezo angapo amene womwa khofi ayenera kuwasamalira. Magazini a The Times a ku London posachedwapa anagwira mawu mfundo yotumbidwa yochokera m’lipoti Lachidatchi lakuti: “Kusakaniza mwachindunji khofi ndi madzi oŵira kungawonjezere unyinji wa cholesterol (maselo onyamula mafuta m’thupi) ndi 10 peresenti, poyerekezera ndi kumwa khofi wosuzidwa kapena ndi kusamwa aliyense.” Cholesterol ndiyo chochititsa chodziŵika cha nthenda ya mtima. M’kope la pambuyo pake, The Times inagwira mawu katswiri wa zakadyedwe wa ku Briteni akumati: ‘Omwa khofi okhazikika ayenera nthaŵi zonse kumwa watsopano ndi kupeŵa uja wokhala nthaŵi yaitali kapena woŵira.’

Ngati pali chirichonse chimene akatswiri amavomerezana ponena za khofi, ndicho kumwa mwachikatikati. Adokotala mwachisawawa amavomereza kuti anthu ayenera kumwa makapu a khofi osaposa pa asanu ndi imodzi (kapena makapu aakulu anayi) patsiku. Awo omwe ali ndi matenda a mtima ndi impso kapena kuthamanga kwa mwazi ayenera kumwa wocheperapo. Akazi apathupi kapena oyamwitsa ana sayenera kumwa yoposa kapu imodzi patsiku.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena