Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Mkristu ayenera kupewa kofi ndi tiyi chifukwa chakuti ziri ndi mankhwala omwerereketsa otchedwa kafeini?
Baibulo silimatchula kofi kapena tiyi. Koma chimene limanena chingathandize Mkristu kupanga chosankha chakuti kaya adzamwa kofi kapena tiyi.
Mankhwala a kafeini angayambukire maganizo ndi thupi. Mamiliyoni a makapu a kofi ndi tiyi amamwedwa tsiku lirilonse, kukumachititsa Dr. Melvin Konner kunena kuti: “M’chenicheni, [Kafeini] angakhale mankhwala ogalamutsa maganizo ogwiritsiridwa ntchito koposa padziko lonse.” Iwo angawonjezere kugalamuka, kuwonjezera mlingo wochangamula mauthenga m’thupi, ndi kufulumizitsa kuyenda kwa mwazi ndi kupukusa zakudya. Chenicheni chakuti iwo ndimankhwala mwa icho chokha sichimatsimikizira kuti kaya Mkristu ayenera kuleka zakumwa zokhala ndi Kafeini (kofi, tiyi, kokokola, maté) kapena zakudya (zonga chokoleti).
Zoledzeretsa zirinso mankhwala amene angayambukire maganizo ndi thupi, komabe kodi Malemba amanenanji ponena za izo? Baibulo limavomereza kuti vinyo (kapena zakumwa zina zoledzeretsa) “zingakondweretse mtima wa munthu” kapena kutsitsimula munthu wopsinjika mtima. (Salmo 104:15; Miyambo 31:6, 7) Komabe, Mawu a Mulungu, samasonyeza kuti alambiri owona ayenera kupewa zakumwa zonse zokhala ndi zoledzeretsa. Chimene Baibulo limatsutsa ndicho kugwiritsiridwa ntchito kwa zoledzeretsa kopambanitsa—uchidakwa.—Deuteronomo 21:18-21; Miyambo 20:1; Hoseya 4:11; 1 Akorinto 5:11-13; 1 Petro 4:3.
Komabe, bwanji ponena za kunena kwakuti munthu angakhale womwerekera ndi kafeini? Ambiri amene ali ndi chizolowezi cha kumwa kofi, tiyi, kapena maté amakhala ndi mlingo wakutiwakuti wa kudalira pa izo, ngakhale kuli kwakuti nkosatsimikizirika kuti kumeneku ndikumwererekeradi kwa zamankhwala. Kwenikweni iwo amakhala ndi zizindikiro zamasire, monga ngati kupweteka kwa mutu kapena mseru, akapanda kumwa mlingo wozolowereka wa kafeini. Komabe, panopa kachiwirinso, pamatikumbutsa lingaliro Labaibulo la zakumwa zoledzeretsa. Ngakhale kuti anthu ambiri amwererekera ndi zoledzeretsa, izo ziri zosaletsedwa kwa Akristu zitamwedwa mwachikatikati. Yesu anamwa vinyo; iye adapangadi vinyo mozizwitsa paphwando laukwati.—Mateyu 26:29; Yohane 2:3-11.
Chikhalirechobe, Mkristu angalingalire kuti akasankha kusadziika pangozi ya kukhala wodalira pa kafeini. Ngati kusamwa kwake kokhazikika kwa kafeini kumpangitsa kusapeza bwino (“kunjenjemera akasowa kofi”), iye angalingalire kuleka kumwa kafeini kukhala chisonyezero cha “kudziletsa.” (Agalatiya 5:22, 23) Popeza kuti Baibulo silimatchula za kupewa zakumwa zokhala ndi kafeini, chosankha ponena za kofi kapena tiyi chiyenera kupangidwa ndi aliyense payekha. Chikatikati nchoyenera ngati Mristu akumwa chirichonse.—Yerekezerani ndi Tito 2:2.
Chikatikati chirinso yankho pankhani ya maupandu ena othekera a thanzi. Pali maupandu ambiri onenedwa ochititsidwa ndi kumwa kafeini wochuluka (kaya m’kofi, m’tiyi, m’kokokola, kapena zakumwa zina kapena zakudya). Komabe, pamafufuzidwe alionse ogwirizanitsa upandu wathanzi uliwonse ndi kafeini, ena amawonekera kukhala osonyeza zosiyana.
Nzeru ya kuchita mwachikatikati imatsimikiziridwa ndi chimene Baibulo limanena ponena za uchi. Ndiwo chakudya chozolowereka, ndipo kuudya monga chakudya chosonkhezera thanzi nkwachibadwa (mosiyana ndi kukokera utsi m’mapapu). (1 Samueli 14:26, 27; Mateyu 3:4) Komabe, mungasanze mutaudya wochulukitsitsa. Baibulo limachenjeza kuti: “Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze.”—Miyambo 25:16, 27.
Anthu ena samadya uchi uliwonse mpang’ono pomwe. Mofananamo, kaamba ka zifukwa zathanzi ena angafunikire kupewa zoledzeretsa, kafeini, zakudya zopangidwa ndi mkaka, kapena zakudya zina ndi zakumwa. Ena angapewe zinthu zoterozo modzifunira kapena chifukwa cha lingaliro losayanja lofalikira m’malowo, mosafuna kukhumudwitsa aliyense. Ichi chimatikumbutsa za ndemanga ya mtumwi Paulo yakuti: “Ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.”—1 Akorinto 8:13.
Chotero, munthu aliyense achitetu mogwirizana ndi chitsimikizo chake popanda kulingalira kuti chosankha chake chifunikira kukakamizidwa pa ena. Paulo analemba kuti: “Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wodyayo; pakuti Mulungu wamlandira. Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake?”—Aroma 14:3, 4.