Mpira Wachitanyu Wolimbirana Chikho Chapadziko Lonse—Maseŵera Kapena Nkhondo?
Ndi mlembi wa Galamukani! m’Italiya
CHIDWI cha dziko lonse chinasumikidwa pa mpira wachitanyu. Kuchokera pa June 8 mpaka July 8, 1990, maso a anthu mamiliyoni mazanamazana anali dwii kuzisonyezero za mawailesi awo akanema kutsatira chochitika cha chakacho—maseŵera a mpira wachitanyu olimbirana Chikho Chapadziko Lonse ochitidwira m’Italiya. Anthu okwanira chiwonkhetso cha padziko lonse cha 30,000,000,000 openyerera wailesi yakanema anawonerera pakutha maseŵera 52—kuŵirikiza kasanu ndi kamodzi chiŵerengero cha anthu onse padziko!
Chochitika cha pa wailesi yakanema chimenechi chinatheka ndi kulinganiza kwa maluso a zopangapanga apamwamba oposa akale alionse—malo apakati owulutsira TV otumikira lukanelukane wa malo 147 oimira maiko 118, ndi makamera a wailesi yakanema okwanira 180, magulu okonza zithunzithunzi 38, ndi akatswiri amaluso a zopangapanga 1,500. Opezekakonso ku maseŵerawo, ochitidwira m’mabwalo 12 ampira wachitanyu a ku Italiya, ndiwo owonerera 2,515,000 ndi amtola nkhani 6,000 ochokera kumbali zonse za dziko. Komabe, ziŵerengerozo sizimasimba nkhani yonseyo. Kuti afotokoze chochitika chachikulu chimenechi chomwe ena achitcha “loto lalikulu,” olemba, akatswiri a zamayanjano, akatswiri a zamaganizo, amisiri, ndipo ngakhale akatswiri a maphunziro a zaumulungu anathirira ndemanga pa chochitikacho.
Komabe, kodi mpira wachitanyu wolimbirana Chikho Chapadziko Lonse unalimbitsa kugwirizana kwa mitundu yonse ndi zamaseŵera? Pogwirizana mwa chilakolako chawo cha maseŵera ameneŵa, kodi anthu okwanira mamiliyoni omwe anapenyerera maseŵerawo kupyolera m’masetilaiti anakhoza kulaka mikangano yawo yautundu mkati mwa masiku 30 amenewo? Kodi mpira wachitanyu unakhala mphamvu ya chigwirizano?
Maseŵera Kapena Nkhondo?
Tiyeni tilingalire mbali imodzi yokha yokhala m’zochitika zamaseŵera zambiri zalerolino—chiwawa. Vuto limeneli limachitika mobwerezabwereza pa maseŵera a mpira wachitanyu—pabwalo loseŵerera, m’malo okhalamo ochemerera, ndi kunja kwa bwalo lamaseŵera. Akatswiri amaganizo, akatswiri a zamayanjano, ndi amtola nkhani akuvomereza kuti m’dziko lachiwawa chachikulu motero, ngakhale m’maseŵera sichimatsala. Makhalidwe ofunika kwambiri akululuzidwa mosalekeza. Kugwiritsira ntchito mawu onga akuti “maseŵera ali chokumana nacho chabwino,” “mzimu wa ubwenzi,” kapena “ubale,” poyesa kuphimba zochitika zachiwawa za m’maseŵera amakono sikukugwira ntchito.
Maseŵera olimbirana Chikho Chapadziko Lonse anali motero. Pamene anali asanayambe, panamveka malipoti ochititsa mantha. “Mzimu Wachiwawa wa Maseŵera Ampira Wachitanyu Ukupereka Chiwopsezo ndipo Alendo Akuchoka m’Italiya,” ndiwo unali mutu m’magazini a La Repubblica apo nkuti kutatsala masiku 18 kuti maseŵera oyamba achitike. Owopsa koposa anali mahooligan (anthu ankhalwe) oipitsitsawo, iri ndi gulu la ochemerera mpira wachitanyu Achizungu odziŵika m’Yuropu monse kaamba ka mkhalidwe wawo wa kusakaza asanayambe, mkati, ndi pambuyo pa maseŵera alionse.a
Kope la La Stampa lamasiku onse la ku Turin la June 1, 1990, linapenda zochititsa chiwawa m’mabwalo a zamaseŵera ndi kudzisungira kosalingalira kwa mahooligan, likuthirira ndemanga kuti: “M’fuko la mpira wachitanyu, tsopano mulibe zochitidwa mwatheka. Olimbana nawo salinso kokha olimbana nawo koma ‘adani’; kukanthana sikwakamodzikamodzi koma ndiwo mkhalidwe, ndipo kuyenera kukhala kwamphamvu, kwamphamvudi monga momwe kungathekere.” Koma nchifukwa ninji? “‘Chifukwa chakuti timadana,’ anayankha motero mahooligan ena ampira wachitanyu a ku Bologna.” Poyesa kulongosola nzeru yokhala m’chidani choterocho, katswiri wa zamayanjano Antonio Roversi anati: “Anyamata a m’bwalo la mpira ali ndi vuto la ‘mzimu wa chibedouin.’ Awo okhala ndi vuto limeneli amawona adani a bwenzi lawo kukhala adani awo, mabwenzi a mdani wawo kukhala adani awo, ndiponso, mwanjira ina, bwenzi la bwenzi ndi bwenzi ndipo mdani wa mdani ndi bwenzi.”
Panali udani, chiwawa, kukangana, kusakaza, “mzimu wa chibedouin”—maseŵera a mpira wachitanyu wolimbirana Chikho Chapadziko Lonse anali pafupi kuyamba, ndipo mkhalidwe unali kale uja wa chilengezo cha nkhondo. Mosasamala kanthu za zimenezi, Italiya anakonzekera kaamba ka chochitikacho mwamzimu wadzoma.
Dalitso la Papa
Ngakhale papa, yemwe sangaphonye chochitika cha unyinji choterocho, anafika ku “kachisi” wa maseŵera a Chikho Chapadziko Lonse, Bwalo Lamaseŵera la Olympic lokometseredwa mokongola m’Roma, ndi kulidalitsa. Iye anati: “Pambali pakukhala dzoma la maseŵera, maseŵera a Mpira Wachitanyu Adziko Lonse angakhale dzoma la chigwirizano pakati pa mitundu.” Iye anawonjezera kuti maseŵera amakono ayenera kupeŵa maupandu oipitsitsa, monga ngati chikhumbo choipa chofuna phindu la zinthu zakuthupi, chigogomezero chopambanitsa pa chopenyereredwacho, mankhwala ogodomalitsa, chinyengo, ndi chiwawa. Iye anayembekezera “kuti zoyesayesa ndi nsembe zimene zinaperekedwa zidzapanga ‘Italiya ’90’ kukhala mphindi ya kukula kwa ubale pakati pa nzika zinzanu ndi pakati pa anthu onse.” Wansembe Paride Di Luca, yemwe kale ankaseŵera mpira wachitanyu, anamveketsa malingaliro a papa mu ‘Pemphero la Ochemerera Mpira Wachitanyu’ pamene anati: “Idzani, O Mulungu wanga, mudzawone maseŵera a Chikho Chapadziko Lonse.”
Koma kodi maseŵera a Chikho Chapadziko Lonse analidi dzoma lofunika koposa? Kodi Mulungu wa chilengedwe chonse akadziloŵetsamo? Tiyeni tisumike chisamaliro pa maseŵera monga momwe iwo aliridi, pa makhalidwe amene iwo amachirikiza.
Mahooligan a m’Maseŵera
Chifukwa cha mahooligan, mizinda yonga ngati Cagliari ndi Turin inakhala mumkhalidwe wa kulaliridwa mkati mwa chigawo choyamba chonse cha maseŵerawo. Nayi ina ya mitu ya m’manyuzipepala: “Rimini Wagwedezeka ndi Nkhondo”; “Cagliari, Nkhondo Yaulika”; “Chiwawa m’Turin: Mjeremani ndi Mbritish Agwazidwa ndi Mpeni”; “Tsiku la Chipolowe Pakati pa Ochemerera Achizungu, Achijeremani, ndi Achitaliyana”; “Tipulumutseni kwa ochemerera Achizungu—Meya wa ku Turin Akuchonderera”; “Kukanthana Kwausiku Pakati pa Ochirikiza Matimu. Meya: Ochokera ku Turin Ndiwo Mahooligan Enieni.” Nachi chitsanzo china chochititsa mantha: “‘Mmene Mungabaire Wochemerera wa Mbali Ina’—Yofalitsidwa m’Mangalande, Malangizo aHooligan Wokhoza.” Mitu yankhani imeneyi njokwanira kupereka chithunzi cha mkhalidwewo. Koma zinthu zoterozo ziri kokha chochitika chozoloŵereka m’chitaganya chokhalira chiwawa.
Chochitika cha maseŵera chachikulucho sichinathe ndi chimwemwe. Kuliza miluzu konyodola kwa ochemerera Achitaliyana kulinga kwa timu ya ku Argentina ndi ngwazi yawo, Maradona, kaamba kogonjetsa timu Yachitaliyana, kunaphimba chisangalalo cha maseŵera omalizira ndikuwononga kuseŵera kothera. Madzulo a July amenewo, panalibe “ubale weniweni wochilikizana” m’Bwalo Lamaseŵera la Olympic; “kachisi” wa maseŵera a Chikho Chapadziko Lonse anatonzedwa. Il Tempo ya July 10, 1990, inati: “Pabwalopo, anaipsa maseŵerawo—m’malo okhalamo ochemerera, anawononga dzina la maseŵera.”
Awa ndi mapeto ochititsa chisoni a chochitika chimene ena anayembekezera kuti chikapanga dziko kukhala “mudzi wa dziko lonse” popanda zopinga kwa masiku 30 okha. Koma ngati mpira wachitanyu sungathe kukhazikitsa mtendere ndi chigwirizano mkati kapena kunja kwa bwalo lamaseŵera, kodi nkowona kulingalira kuti uwo ungasonkhezere mtendere wadziko lonse?
Lingaliro Lachikatikati la Mpira Wachitanyu
La Stampa inathokoza mpira wachitanyu, kuulongosola kukhala “chotsalira chopatulika cha kulimbana kwa makolo akale, mpira kukhala chizindikiro chakusakhoza kulosera zakutsogolo, mfundo yeniyeni ya mipikisano yonse ya maseŵera.” Kupenda lingaliro limeneli, kodi ndimotani mmene Mkristu wowona mtima ayenera kuuwonera mpira wachitanyu? Ndithudi, kodi ndimotani mmene Mkristu ayenera kuwonera maseŵera onse aukatswiri?
‘Awo amene samakonda mpira wachitanyu akuphonya chinthu chabwino m’moyo,’ kukunenedwa kuti Bertrand Russell ananena zimenezo. Indedi, kuseŵera mpira wachitanyu kapena maseŵera ena alionse kungakhale ponse paŵiri kosangalatsa ndi kopatsa thanzi, makamaka pamene anthu ambiri motero akukhala ndi moyo wosayendayenda. Koma kodi izi zikutanthauza kuti palibe maupandu oloŵetsedwamo?
Baibulo limati: ‘Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.’ (Agalatiya 5:26) Maseŵera olimbirana Chikho Chapadziko Lonse anasonyeza kotheratu mmene chiwawa ndi mzimu wa kufuna kupambana pamtengo uliwonse kaŵirikaŵiri zimayendera pamodzi. Iyi ndiyo mbali yoipa ya maseŵera aukatswiri. Kuti apeŵe ‘ntchito za thupi’ zoterozo, Akristu, ponse paŵiri otenga mbali ndi openyerera, ayenera kulamulira mzimu wawo, makamaka ponena za chikhumbo chakufuna kukhala woyamba. (Agalatiya 5:19-21) Kumbukirani mawu a wolemba ndakatulo akuti: “Pamene Wopereka Mfupo alemba pa dzina lako, iye amalemba—osati kuti unapambana kapena unalephera—koma mmene unaseŵerera maseŵerawo.”
Mbali ina imene siiyenera kunyalanyazidwa ndiyo mfundo ya nthaŵi. Kodi muli pakati pa mamiliyoni openyerera wailesi yakanema omwerekera omwe amawononga maola osaŵerengeka akuwonerera maseŵera? Mosiyana, kodi mumawononga nthaŵi yanu yochuluka motani mukuchita maseŵera olimbitsa thupi? Chikatikati—ndilo liwu la mfungulo. Limatanthauza kupeza nthaŵi ya maseŵera olimbitsa thupi ndi zosangulutsa, popanda kunyalanyaza zochitachita zauzimu zofunika koposa. Mtumwi Paulo anapereka uphungu kwa Timoteo wachichepere umene umagwira ntchito koposadi lerolino: ‘Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8.
[Mawu a M’munsi]
a Malongosoledwe ena onena za chiyambi cha liwu lakuti “hooligan” amati: “Mwamuna wotchedwa Patrick Hooligan, yemwe ankayendayenda uku ndi uku pakati pa anzake, akumawalanda ndipo nthaŵi zina kumawakantha.”—A Dictionary of Slang and Unconventional English, yolembedwa ndi Eric Partridge.
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Chithunzithunzi cha Agenzia Giuliani