Kodi Nchiyani Chikuchitika m’Dziko la Maseŵera?
Ndi mlembi wa Galamukani! mu Italy
KODI maripoti amene ali patsamba lapandunjilo akulongosola kugwetsa boma kwaposachedwapa m’dziko la ku Latin-America kapena kuwukira kwina kwa zigaŵenga pa nthaka ya Europe? Ayi, maripotiŵa ndi ena ofanana, monga mmene nyuzipepala ina ya ku Italy inaikira icho, ali a “tsiku la maseŵera la nthaŵi zonse.”
Maseŵera ndi chiwawa zikuwoneka kuyendera limodzi masiku ano. Mwachitsanzo, ambiri adakakumbukirabe madzulo a May 29, 1985, pamene anthu 39 anafa ndipo 200 anavulazidwa m’zochitika za pakati pa ochemerera mpikisano womalizira wa mpira wolimbirana chikho cha European Champions’ Cup usanachitike.
Komabe, zochitika zachiwawa zopangitsidwa ndi otengamo mbali ndi openyerera siziri zolekezera ku maseŵera amodzi okha, onga ngati mpira, koma izo zimabuka m’maseŵera a mitundu yonse—baseball, nkhonya, hockey.
Miyambi yakuti, “Lolani katswiri apambane” ndi, “Nchofunika koposa kutengamo mbali kuposa kupambana,” yakhala zinthu zosoloka m’dziko la maseŵera. Kodi nchifukwa ninji oseŵera ndi openyerera amatulutsa luntha lawo laukali, mkwiyo wosalamulirika, pa zochitika za maseŵera opikisana? Kodi nchiyani chimene chiri kumbuyo kwa chiwawa m’maseŵera? Ndipo kodi vutolo nloipa motani?