Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 5/8 tsamba 26-29
  • Kodi Mitala Njolakwika Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mitala Njolakwika Motani?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mitala m’Baibulo
  • Muyezo Woyambirira wa Mulungu
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Banja / Kodi Mulungu Amaloleza Mitala?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Anauza Mulungu Zakukhosi Kwake
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 5/8 tsamba 26-29

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mitala Njolakwika Motani?

Mavuto a Jane anayamba pamene abambo ake anapeza ntchito m’mzinda.a Pokhala kutali ndi nyumba yawo ya kumudzi m’Afirika, iwo anayamba kukhala ndi mkazi wina kumeneko. “Moyo sunali wokhweka kwa ife,” akufotokoza motero Jane, “chifukwa chakuti abambo sanali kutichirikiza m’zachuma; iwo anali kuchirikiza akazi awo achiŵiri ndi ana awo. M’zaka zanga zomaliza sukulu, ndinkagona ndi njala kaŵirikaŵiri. Banja lathu linali m’mkhalidwe wovutika kwadzawoneni. Kumapeto a milungu ndinayesayesa kuthandiza amayi kugulitsa zipatso, koma sitinkakhoza kukwaniritsa zofunikira za moyo. Ndinkalira usiku uliwonse.”

CHOKUMANA nacho cha Jane chimaunikira mavuto omwe ukwati wamitala umadzetsa pa ziŵalo zopanda liŵongo. Anthu olankhula Chivenda kum’mwera kwa Afirika ali ndi dzina lakuti muhadzinga, limene mkazi wokwatiwa angatche mkazi wokwatiwa mnzake m’banja lamitala. Ilo linatengedwa ku mawu otanthauza “kukazinga,” amene mwinamwake amafotokoza bwino lomwe vuto limene mitala imadzetsa kaŵirikaŵiri pakati pa akazi okwatiwa.

‘Koma,’ inu mungafunse, ‘kodi mitala njolakwika? Ngati nditero, nchifukwa ninji anthu ena otchuka otchulidwa m’Baibulo anali amitala?’

Mitala m’Baibulo

Mulungu analola mitala kwanthaŵi yakutiyakuti, popeza kuti inatheketsa kukwaniritsidwa kwa lonjezo lake kwa Abrahamu lakuti: ‘Ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu.’ (Genesis 12:2; Eksodo 1:7) Panthaŵiyo, mkazi wa Abrahamu Sara, anali wopanda mwana. M’kupita kwanthaŵi, iye anamchonderera Abrahamu kubala mwana mwa mdzakazi wake, Hagara. Chokondweretsa nchakuti, Baibulo limafotokoza bwino mavuto amene zimenezi zinadzetsa pa banja la Abrahamu.—Genesis 16:5, 6; 21:8-10.

Ponena za Yakobo, mdzukulu wa Abrahamu, iye anafuna kukwatira mkazi mmodzi yekha, Rakele. (Genesis 44:27) Anali Labani, mpongozi wa Yakobo, yemwe anampusitsa kukwatira ana ake aakazi onse aŵiri, Rakele ndi Leya. (Genesis 29:21-28) Ndipo kunali atakakamizidwa ndi akazi ake ameneŵa kuti Yakobo anabala ana mwakugonana ndi adzakazi awo, Biliha ndi Zilipa. Panonso, Baibulo silimabisa mavuto ambiri odzetsedwa ndi mitala pa banja lalikulu la Yakobo.—Genesis 29:30, 31; 30:1-3, 15, 16, 20; 37:2-4; 44:20-29.

Baibulo limasimbanso nkhani ya Elikana, abambo a mneneri Samueli, ndi akazi a Elikana aŵiri, Hana ndi Penina. Hana ankavutidwa kwambiri ndi Penina kwakuti iye ankalira kaŵirikaŵiri ndi kusala kudya. Penina, kumbali ina, anali wansanje mwachiwonekere chifukwa chakuti Elikana anasonyeza chikondi chachikulu kwa Hana.—1 Samueli 1:4-7.

Ndithudi, mwambo wa mitala wadzetsa mavuto. Pamene kulikwakuti unalekereredwa pakati pa anthu a Mulungu akale, Baibulo limasonyeza momvekera bwino ngati Mulungu poyambirira anafuna kuti mwamuna akhale wamitala.

Muyezo Woyambirira wa Mulungu

Kuti timvetsetse muyezo wa Mulungu wa ukwati, tifunikira kubwerera m’mbuyo kuchiyambi cha mbiri yakale ya anthu. Mawu a Mulungu amafotokoza kukopeka mtima komwe Adamu anamva popatsidwa mkazi wake yekhayo, Hava, wolengedwa chatsopanoyo. Iye anati: ‘Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.’ Baibulo likupitiriza kuti: ‘Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.’—Genesis 2:21-24.

Ku maukwati Achikristu, Yesu anabwezeretsa muyezo woyambirira wa Mulungu—kukwatira mmodzi. (Mateyu 19:4, 5) Kuwonjezerapo, iye anasonyeza kuti tsopano anthu okwatirana ayenera kumamatira ku muyezo waumulungu umenewu. Monga momwe anafotokozera kuti: ‘Salinso aŵiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.’ (Mateyu 19:6) Chotero, Mkristu wokwatira ayenera kutetezera unansi wa “thupi limodzi” umene umakhala pakati pa iye ndi mnzake wamuukwati walamulo.b Kugonana ndi munthu wachitatu m’mitala kukanyozera makonzedwe aumulungu amenewo. Kachitidwe kotero nkoletsedwa mumpingo Wachikristu.—1 Akorinto 5:11; 6:9, 16, 18; Ahebri 13:4.

Pamenepo nzosadabwitsa kuti, Malemba amatchula moyanja Akristu okwatira amene ali ndi mkazi mmodzi yekha. (1 Akorinto 9:5; 1 Timoteo 3:2) Baibulo limafotokoza kuti: “Munthu yense akhale naye mkazi [osati akazi] wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna [osati mwamuna yemwe ali kale ndi mkazi wake walamulo] wa iye yekha.”—1 Akorinto 7:2; Miyambo 5:18.

Pophunzira za chiletso cha Baibulo cha mitala, ambiri atenga masitepe molimba mtima kugwirizanitsa miyoyo yawo ndi chifuniro cha Mulungu. Talingalirani John, amene amakhala m’mzinda wa pakati pa Afirika.c Iye ankakhala ndi akazi atatu. Koma ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, John anapanga chosankha chaumwini mwakukambitsirana ndi akazi ake. Pambuyo popanga makonzedwe a chisamaliro cha mtsogolo cha mkazi wake wachiŵiri ndi wachitatu limodzi ndi ana awo a muukwati wamitala wakalewo, iwo anabwerera ku midzi yawo. Mwanjirayi John anayeneretsedwa kaamba ka mwaŵi wa kutumikira Mulungu moyanjana ndi mpingo wakumaloko. Iye anasangalalanso ndi madalitso ena.

“Usiku uliwonse,” iye akufotokoza motero, “ndinkabwera kunyumba ya mavuto ochuluka. Mwachitsanzo, mkazi mmodzi akapeza chifukwa kwa mwana wa mkazi wina, ndipo anawo ankapatukana. Choyamba chomwe ndidafunikira kuchita chinali kuwongolera chisokonezocho. Tsopano popeza ndaphunzira kukhala ndi mkazi mmodzi, nyumba yanga yakhala malo a mpumulo ndi mtendere.”

Ndithudi, mtendere ndi dalitso la Mulungu nzoyenerera kuyesayesa kumeneko.—Aroma 12:1, 2.

[Mawu a M’munsi]

a Dzina lenileni silinagwiritsiridwe ntchito.

b The New International Dictionary of New Testament Theology limanena kuti mawu Achigiriki otembenuzidwa kukhala “thupi limodzi” pa Mateyu 19:5b ali ndi tanthauzo lapadera monga matembenuzidwe a mawu Achihebri pa Genesis 2:24 ndipo amasonyeza “chigwirizano chotheratu cha mwamuna ndi mkazi chimene sichingaswedwe popanda kuvulaza awo ogwirizana mu icho.”

c Dzina lenileni silinagwiritsiridwe ntchito.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Nsanje ya zakugonana ndi kulongolola ndi mavuto ofala m’banja [lamitala]; ndipo mwamuna ayenera kukhala wanzeru, wolimba, waluso, ndi waluntha kuti asungitse chimvano.”—The New Encyclopædia Britannica

[Chithunzi patsamba 28]

Chifanizo cha banja la Chiafirika; mwamuna wa Chiigbo ndi akazi ake

[Mawu a Chithunzi]

Mwachilolezo cha The British Museum

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena