Luso la Uinjiniya la Chimbalangondo Choyera cha Kumalo Ozizira
MALINGA ndi kunena kwa asayansi ena, chimbalangondo choyera cha kumalo ozizira chingaphunzitse anthu zambiri ponena za kupanga mphamvu ya cheza cha dzuŵa. Katswiri wa physics Richard E. Grojean anakondweretsedwa ndi lingaliro limeneli m’ma 1970, pambuyo pa kupanga kutumbidwa kosangalatsa konena za nyama zoyera za ku Arctic.
Oŵerenga nyama za m’nkhalango a ku Canada anapeza kuti sangakhoze konse kujambula zithunzithunzi zanthaŵi zonse za nyama zimenezi kuchokera m’mwamba, popeza kuti izo zimavunganizikana ndi nthaka yoyera. Mafilimu a infrared, oyenerera kaŵirikaŵiri kujambulira zithunzithunzi za nyama za mwazi wotentha, nawonso analephera. Nyamazo zinali zochinjirizidwa bwino kwambiri kwakuti sizinatulutse kufunda kokwanira kuti filimuyo izindikire. Komabe, pamene mafilimu a ultraviolet anagwiritsidwa ntchito, maseal oyera ndi zimbalangondo zoyera za kumalo ozizira zinawonekera monga zinthu zakuda zozokotedwa pamalo oyera. “Pamene kuli kwakuti chipale chofeŵa chinachezimitsa cheza cha ultraviolet, nyamazo zinatenga chezacho,” ikusimba motero The Toronto Star.
Chifukwa ninji? Mogwirizana ndi akatswiri a physics Grojean ndi Gregory Kowalski profesa mnzake wa luso lopanga makina, chikopa cha chimbalangondo chiri ndi yankho. Kumbali yothera yosakhoza kuwoneka ndi maso ya mbaliŵali ya kuunika ya ultraviolet, ubweya wa chikopacho umagwira 90 peresenti ya kuunika kwa ultraviolet ndi kukutumiza ku ganda lakuda mkati, kumeneko nkumafunditsa chimbalangondocho. Ku Arctic, kumene kuzizira kumatsika kufika -29° C., kukhoza kwa chikopacho kusunga mwiniwake wofunda nkodabwitsa. Mosiyana, ziŵiya zogwira cheza cha dzuŵa zapatsindwi zofala, nzosakhoza kwenikweni. Kwenikweni, Kowalski akuyerekezera kuti mbale zopangidwa ndi anthu za cheza cha dzuŵa zingakhale zokhoza koposa kuŵirikiza 50 peresenti mwakugwiritsira ntchito malamulo a chikopa cha chimbalangondo choyera cha kumalo ozizira.
M’gawo lokhoza kuwoneka ndi maso la mbaliŵali za kuunika, ubweya wa chikopa umachita mosemphana; uwo umachezimitsa 90 peresenti ya kuunika. Ichi chimapatsa chimbalangondocho mawonekedwe ake oyera owala, chinkana kuti ubweya weniweniwo suli konse woyera koma wopenyekera ndi wopanda mtundu. Kuyera kwa chikopacho kumatheketsa chimbalangondocho kusaka nyama mosawoneka pa nthaka yachipale chofeŵa ya ku Arctic. Ofufuza ena awona zimbalangondo zoyera za kumalo ozizira zikubisa mpuno zawo zakuda posaka nyama, ngati kuti zimazindikira kufunika kwa kuvunganizikana ndi chipale chofeŵa.
Chotero chikopa cha chimbalangondo choyera cha kumalo ozizira chimasonyeza zofunika ziŵiri za nyamayo: kuwoneka yoyera ndi kukhala yofunda. Pamenepa, nzosadabwitsa kuti Grojean, katswiri wa physics anatamanda chikopacho kukhala “luso la uinjiniya lodabwitsa kwambiri.” Mwachisawawa, cholengedwa chapadera ndi chachikulu chimenechi chimachitira umboni nzeru ya Mlengi wake.