Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 8/8 tsamba 25-26
  • Aids Zimene Makolo ndi Ana Ayenera Kudziŵa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aids Zimene Makolo ndi Ana Ayenera Kudziŵa
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Muyenera Kudziŵa
  • Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS
    Galamukani!—1994
  • Kodi Ndani Amene Ali Pangozi?
    Galamukani!—1986
  • AIDS—Vuto la Azaka Zapakati pa 13 ndi 19
    Galamukani!—1991
  • AIDS—Kodi Ndili Paupandu?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 8/8 tsamba 25-26

Aids Zimene Makolo ndi Ana Ayenera Kudziŵa

MWATSOKA minkhole yachichepere yambiri imene iri ndi AIDS, mavuto awo kaŵirikaŵiri amakulitsidwa ndi kulingalira kopanda nzeru kwa achikulire ambiri amene amadziŵa zochepa ponena za AIDS. M’zochitika zambiri makolo apangitsa ana awo kukhala ndi malingaliro oipa ponena za matendawo. Ngakhale pambuyo pakuti adokotala anena kuti palibe upandu, oyang’anira sukulu ndi aphunzitsi aakulu ena akana kuloŵetsa ana amene ali oyambukiridwa ndi kachirombo ka AIDS. Chotero chinsinsi ndicho liwu limene makolo okhala ndi ana oyambukiridwa ndi HIV amagwiritsira ntchito. Iwo amawopa, nthaŵi zina pamakhala chifukwa chabwino, kuti ana awo adzavutitsidwa, kuchitiridwa nkhanza, kapena zoipa zina.

Mwachitsanzo, nakubala wokhala ndi mwana wamkazi woyambukiridwa ndi AIDS anachita mantha kuti akaloŵa m’vuto ndi anansi ake kotero kuti anamletsa mwana wakeyo kuseŵera ndi ana awo. “Sumafuna kuti anthu okhala pafupi nawe adziŵe kuti mwana wako ali ndi AIDS, chifukwa chakuti anthu amachita zinthu zachilendo.” Mogwirizana ndi malipoti, ukutu sikunena kosinjirira. Makolo akanidwa ndi mabwenzi ndi anansi awo abwino koposa. Mabwenzi anathaŵa m’khwalala m’malo mwakuvomereza kukhalapo kwawo kapena kuwapatsa moni. Kuchititsa manyazi kwa AIDS kumazama m’kuthengera kwake kotero kuti ochilikiza mabanja amatuluka m’malesitilanti, akumatukwana pamene banja lokhala ndi mwana woyambukiridwa ndi AIDS linalowa. Atate ataikiridwa ntchito zawo. Ena awopsezedwa ndi kuphulitsidwira mabomba. Enabe anaotcheredwa nyumba zawo.

Ana odwala AIDS akhala minkhole ya njerengo zankhanza ndi anzawo akusukulu. Mnkhole wina wa AIDS woteroyo, yemwe anatenga matendawo chifukwa chakuthiridwa mwazi, anapatsidwa mlandu mobwerezabwereza ndi anzake akusukulu wakukhala wogonana wofanana ziŵalo. Iwo ankatonza kuti: “Timadziŵa mmene unaitengeradi AIDS.” Banjalo linapeŵedwa ndi ziŵalo zakutchalitchi kwawo. Makalata oipa opanda maina analandiridwa. Miulu ya zinyalala inataidwa pabwalo pawo. Wina analasa chipolopolo pazenera.

“Ndinkhani yachinsinsi kwenikweni,” anatero nakubala wina wa mwana woyambukiridwa ndi AIDS, “ndipo nchimene chimaipangitsa kukhala yosungulumwitsa.” The New York Times ikuwonjezera kuti: “Ambiri a ana Achimereka 1,736 a zaka zochepera pa 13 opimidwa kukhala ndi AIDS apatulidwa chifukwa cha matenda awo, kukakamizidwa kubisa mkhalidwe wawo kwa mabwenzi kapena anzawo akusukulu athanzi omwe angawathawe.” Ndipo potsirizira pake, panali ndemanga iyi ya mu The Toronto Star: “Ngakhale pambuyo pakufa kwa wachichepereyo, mabanja ambiri amawopa kuvumbula chowonadi, chomwe chimawonjezera kupweteka ndi kudzipatula komwe kumatsagana ndi kutaika kwa mwana.”

Zimene Muyenera Kudziŵa

Kuyenera kuvomerezedwa kuti AIDS simalemekeza anthu. Iyo ingayambukire achuma, osauka, achichepere, makanda enieni, ndi nkhalamba. M’maiko ena, achichepere amadziŵa zochepa kwenikweni ponena za AIDS. Anthu ambiri “samalingalira konse kuti AIDS ili upandu waukulu chotani kwa azaka zapakati pa 13 ndi 19,” anatero katswiri wa AIDS wa ku New York City.

Mwachitsanzo, kufufuza kwa achichepere mumzinda waukulu wa ku Amereka kunavumbula kuti 30 peresenti ya awo ofufuzidwa anakhulupirira kuti AIDS ingachiritsidwe ngati mankhwala aperekedwa mofulumira. Palibe mankhwala ochiritsa AIDS omwe apezeka. Chigawo chimodzi mwa zitatu sanadziŵe kuti munthu sangatenge AIDS mwakungokhudza kapena kugwiritsira ntchito chipeso cha munthu wodwala matendawo. Kufufuza kowonjezereka kwa achichepere 860, a zaka 16 mpaka 19, m’mbali ina ya United States kunapeza kuti 22 peresenti sanadziŵe kuti kachirombo ka AIDS kangapatsiridwe mwa ubwamuna ndikuti 29 peresenti sanadziŵe kuti kangapatsiridwe mwa madzi a m’mpheto ya akazi.

Mkati mwa nthaŵi yonse imene matendawo amabindikira ndiponso pamene AIDS imawonekera kwenikweni, minkhole yake imakhala yoyambukiritsa ndipo ingapatsire kachirombo ka AIDS kwa ena. Komabe, sikangapatsiridwe mwakugwirana chanza kapena kukupatirana ndi mnkhole wa AIDS, popeza kuti kachiromboko kamafa mofulumira pamene kali kunja kwa thupi. Mofananamo, kachiromboko sikangakhale pachimbudzi, chimene anthu ena amawopa. Kodi aphunzitsi aakulu apasukulu ndi oyang’anira anawopa kuti ophunzira opanda AIDS angatengere matendawo mwakumwa pakasupe amene wangogwiritsiridwa ntchito ndi mnkhole wa AIDS? Akatswiri amanena kuti mantha ameneŵa ngopanda maziko popeza kuti kachiromboko sikangakhale ndi njira yoloŵera m’mwazi wa munthu wosayambukiridwa.

Kaŵirikaŵiri adokotala amafunsidwa za upandu wakuboola makutu, popeza kuti singano zimagwiritsiridwa ntchito. Akatswiri akuvomereza kuti ngati chiŵiya choipitsidwa chigwiritsiridwa ntchito, imeneyi ingakhale njira yotengera kachirombo ka AIDS. Nanga bwanji ponena za kumpsompsonana? “Ngati winawake wodwala AIDS kapena woyambukiridwa ndi HIV akumpsompsonani, ndipo muli ndi chironda chotulutsa mwazi pamilomo yanu kapena mkamwa, zingachitike, koma sizothekera kwenikweni,” anatero katswiri wina. Komabe, kuli kotheka.

Njira yokha imene mungadziŵire ngati ndinu woyambukiridwa, ngakhale pambuyo pakuti pangawonekere zizindikiro zina zokaikiritsa, ndiyo kupyolera m’kufufuza kosamalitsa kwa dokotala ndi kupimidwa kwa mwazi.

Ndipo pomalizira pake, ngati ndinu mwana, khalani wowona kwa makolo anu. Pamene ena onse adzakukanani, iwo ndiwo okha amene adzamamatira kwa inu ndikukupatsani chitonthozo ndi chithandizo chimene mudzachifunikira. Khalani wanzeru ndikukana mankhwala ogodomalitsa ndi kugonana ukwati usanakhale. Kungapulumutse moyo wanu. Achichepere ambiri amene anatenga kachirombo ka AIDS kupyolera m’kugonana kapena kugwiritsira ntchito singano zoipitsidwa avomereza kuti anasonkhezeredwa ndi mayanjano oipa. Ndithudi, mawu a mtumwi Paulo ali ndi tanthauzo lalikulu kwa iwo tsopano. “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma”—ndipo nthaŵi zina, angakutengereni moyo wanu.—1 Akorinto 15:33.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena