Lingaliro la Baibulo
Chifukwa Chake Zaumaliseche Ziri Zaupandu
ZAUMALISECHE tsopano sizimapezeka kokha ku mashopu a zamanyazi ndi ziwonetsero za kugonana. Zimakhala zofikirika kwa anthu onse. M’dziko limodzi pambuyo pa linzake, zimasonyezedwa kwa nzika za maganizo abwinopo m’magazini, manyuzipepala, m’mabuku, m’maprogramu a TV, makanema, ndi ma video. Kodi chinthu chofalikira motero chingakhaledi chaupandu kwenikweni?
Komabe, kodi zaumaliseche nchiyani? Zaumaliseche zamasuliridwa kukhala “kusonyeza mkhalidwe wodzutsa nyere (monga ngati m’zithunzithunzi kapena zolembedwa) zolinganizidwira kudzutsa chisangalalo chakugonana.” Kumasulira kumeneko kuli komvekera bwino. Koma pamabuka mikangano ponena za chimene chimadzutsa chisangalalo chakugonana ndi chimene sichimatero. Zowonadi, kumlingo wakutiwakuti, zimene zimalingaliridwa kukhala zaumaliseche zimadalira pa kulingalira kwa munthu payekha. Kunena m’mawu ŵena, zimene zingakhale zodzutsa chilakolako cha kugonana kwa munthu mmodzi sizingakhale zotero kwa munthu wina. Komabe, kupenda kwaposachedwapa kwa ku Jeremani kwa anthu 5,000 kunavumbula kuti kumlingo wakutiwakuti, zinthu zodzutsa nyere zimayambukira pafupifupi aliyense, amuna ndi akazi omwe.
Kodi Kudzutsa Zilakolako Kuli Kolakwa?
Kudzutsa chilakolako choyenera—chamtundu uliwonse—kuli kopanda nzeru ngati palibe njira yochikhutiritsira moyenerera. Mwachitsanzo, ngati palibe chakudya chanu chapamtima, simungakhale wokhutira kumangopenya mosalekeza zithunzithunzi zake m’magazini kapena mabuku. Kumbali ina, ngati inuyo—mwinamwake pazifukwa zaumoyo—simuloledwa kuchidya, kumachilingalira mosalekeza mwachiwonekere kukakutsogolerani kuchita zaupandu. Mofananamo, wosuta yemwe akuyesayesa kuleka chizoloŵezicho sadzawonjezera mpata wakuleka mwakuthera nthaŵi yaitali akupenyerera mokhumbira anthu ena akusuta.
Ponena za zilakolako za kugonana, malinga ndi lingaliro Labaibulo, chimwemwe chimatulukapo mwakuzikhutiritsa moyenera m’chomangira cha ukwati wachikondi. (1 Akorinto 7:2-5; Ahebri 13:4) Chotero kukakhala kupanda nzeru motani nanga kwa munthu wosakwatira kudzutsa zilakolako zomwe sangazikhutiritse! Ichi chimangodzetsa kuipidwa kapena, choipirapo, kuzikhutiritsa mwakutembenukira ku mpsotopsoto kapena dama, mwakutero kulakwira malamulo ndi miyezo yaumulungu.—1 Atesalonika 4:3-7.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti zaumaliseche siziri zaupandu ngati muli wokwatira? Ayi, malamulo Amalemba amenewo onena za mayendedwe amagwiranso ntchito kwa anthu okwatira. Ndiponso, zaumaliseche zimasangalatsa zikhumbo zadyera, kuumirira pakukhutiritsa zilakolako zaumwini, pamene chikondi chimasumika pa kukhutiritsa zofuna za mnzanu. Zaumaliseche zimatsogolera ku kugonana kosalingalira ndi kodzikhutiritsa, kumene, ngakhale mkati mwa ukwati, kumakhala koluluzika ndi kopanda chikondi.—1 Akorinto 13:5.
M’malo molimbitsa chikondi chamuukwati, zaumaliseche zimachipha mwakuchiluluza, ndi kuchipotoza. Kugonana kosonyezedwa m’zaumaliseche kuli maloto oipitsitsa chifukwa chakuti kumapereka uthenga woipa ndi wovulaza ponena za kuyanjana kwa muukwati. Kuwonjezerapo, maunansi enieni amaposa pa kugonana chabe; amazikidwa pa chifundo, kusangalala, kulankhulana, ndi kusamalirana. Mosiyana, zaumaliseche zingakhale chopinga pakati pa anthu okwatirana.
Zaumaliseche zimapangitsa anthu kukhala ngati zinyama zochita zinthu mosalingalira. Sizimalimbikitsa kudziletsa, chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Zingakupangitse kukhala kosavuta kuloŵa m’kugonana koluluzika. Izi nzifukwa zochepa zokha zimene Akristu ayenera kupeŵera zaumaliseche.
Choncho, uphungu wanzeru Wabaibulo uli wakuti: ‘Ukondwere ndi mkazi wokula naye . . . Ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiŵereŵere, ndi kufungatira [m’lingaliro lenileni kapena mwakugwiritsira ntchito zaumaliseche] chifuwa cha mkazi wachilendo?’—Miyambo 5:15-20.
Komabe, kodi ndimotani mmene munthu angapeŵere kapena kumasuka ku zaumaliseche?
Mmene Mungamasukire
Kuti mulimbane ndi kukopa kwa zaumaliseche, Baibulo limalangiza kuti: ‘Chifukwa chake fetsani ziŵalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi.’ (Akolose 3:5) Panopo, liwu lakuti “fetsani” mowonekera bwino limapereka lingaliro lakupha—osati kungotsendereza—chiŵalo chathupi chimene chingagwiritsiridwe ntchito m’zolakwa zimenezo.
Komabe, kuyenera kumvedwa mophiphiritsira, osati m’lingaliro lenileni. Akristu sayenera kudula ziŵalo za matupi awo. Ngati tisankha “kupha” malingaliro oipa akugonana, sitidzagonjera ku kukopa kwa zaumaliseche, mwakutero kugwiritsira ntchito moipa ziŵalo zathupi lathu, monga ngati maso. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:29, 30.) Chifukwa cha ichi, Baibulo limalangiza kuti tiyenera kuloŵa m’malo zilakolako zoipa ndi ‘zirizonse zolungama, zirizonse zoyera,’ ndiyeno “zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.
Kodi nchiyaninso chimene chingathandize? Kukumbukira—mwinamwake kuloŵeza—malemba Abaibulo, monga otsatirawa:
‘Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.’—Salmo 119:37.
‘Chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso . . . sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.’—1 Yohane 2:16.
‘Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.’—Yakobo 1:14, 15.
Chirichonse chimene chingayambitse zochitika zotsogolera ku imfa chinganenedwe moyenerera kukhala chaupandu, ndipo zaumaliseche zimayenerera kulongosola kumeneko! Kumbukirani kuti: ‘Wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera mu mzimu adzatuta moyo wosatha.’ Musalole kuti zaumaliseche zikulandeni moyo wosatha!—Agalatiya 6:8.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
M’malo molimbitsa chikondi chamuukwati, zaumaliseche zimachipha mwakuchiluluza, ndi kuchipotoza