Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 10/8 tsamba 12-13
  • Kodi Nkuphunziriranji Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkuphunziriranji Baibulo?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumatsegula Malingaliro Akuya a Kumvetsetsa
  • Magwero a Mapindu Enieni ndi Ulosi
  • “Anakambirana Nawo Mfundo za M’Malemba”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi Kumtumikira M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Baibulo—Buku Loyenera Kuŵerengedwa
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 10/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Kodi Nkuphunziriranji Baibulo?

KUŴERENGA Baibulo lonse sikuli chinthu chopepuka. Kodi munayamba machitapo zimenezo kamodzi kapena mwinamwake nthaŵi zambiri? Anthu ambiri amanyadira kuchita zimenezo. Kupeza nthaŵi yoŵerenga Baibulo kuyenera kukhala koyambirira pa zinthu zathu zofunika koposa. Chifukwa ninji? Kuti mudziŵe zamkati mwa bukhu lofalitsidwa koposa m’mbiri yonse, bukhu lokha lomwe moyenerera limanena kuti linauziridwa ndi Mulungu.—2 Timoteo 3:16.

Komabe, munthu angachite zambiri kuposa kungoŵerenga Baibulo ndikudziŵa mfundo zake zazikulu. Kodi muli ndi chilakolako chakukondweretsa Mulungu ndikusangalala ndi mapindu okwanira a ziphunzitso za bukhu lopatulika limenelo? Pamenepo tsatirani uphungu umene mtumwi Paulo anapereka kwa Timoteo wachichepere kuti: ‘Usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.’—1 Timoteo 4:13, 15, 16.

Kusinkhasinkha koteroko pa ziphunzitso za Baibulo ndikukhala wokutidwa nazo kumaphatikizapo zoposa kuŵerenga Malemba okha. Kuŵerenga Baibulo mwa iko kokha sikumatsimikizira kuti munthu angagwiritsire ntchito moyenerera chidziŵitso chopezedwa, monga momwedi kuŵerenga bukhu lonena za ubongo wa munthu sikumamyeneretsa kukhala dokotala wopanga opareshoni ya ubongo. Chifukwa chake, mvetserani uphungu wowonjezereka wa Paulo kwa Timoteo: ‘Uchite changu kudziwonetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa chakuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a chowonadi.’—2 Timoteo 2:15.

Kumatsegula Malingaliro Akuya a Kumvetsetsa

Kuphunzira kulunjika nawo Mawu a Mulungu mwaluso kumafunikira kuphunzira. Pamene munthu aphunzira Baibulo mosamalitsa, kulingalira zimene limanena, kulimvetsetsa, kuŵerenga ndime mogwirizana ndi mawu apatsogolo ndi apambuyo, kumvetsetsa mbiri yake, pamenepo malingaliro akuya osayembekezereka angayambe kumtsegukira. Iye tsopano amayamba kupindula mwaumwini ndi Mawu a Mulungu.

Tatiyeni titenge chitsanzo chosonyeza chimenecho mwakungoŵerenga mbali imodzi ya Lemba, sitingathe kumvetsetsa tanthauzo la zimene zanenedwa kusiyapo kokha ngati tiŵerenga mawu apatsogolo ndi apambuyo. Pa Machitidwe 17:11 timaŵerenga ponena za anthu a mzinda Wachigiriki wa Bereya, wokhala osati kutali ndi Tesalonika: ‘Ameneŵa anali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.’

Kungopenya kamodzi kokha tingagamule kuti Akristu a m’Bereya anali ophunzira kwambiri kuposa a m’Tesalonika. Komabe, tawonani vesi 10 la Machitidwe mutu 17 kuti pamene Paulo ndi Sila anafika ku Bereya analoŵa “m’sunagoge wa Ayuda” kukalalikira Mawu a Mulungu. Ndipo vesi 12 likunena kuti “ambiri a iwo [Ayuda] anakhulupira.” Vesi limenelo limatithandiza kugamula mosiyana. Cholembedwa chopatulikacho chikutiuza kuti sanali Akristu omwe anali kuyerekezeredwa wina ndi mnzake m’mizinda iŵiri imeneyi, koma, m’malo mwake, anali Ayuda a m’malo amenewo.

Ndiponso, kodi mwawona zimene zinapangitsa Abereya kukhala mfulu? Iwo anasanthula Malemba mofunitsitsa mtima. Profesa Archibald Thomas Robertson, pothirira ndemanga pa mawu amenewo m’bukhu la Word Pictures in the New Testament, analemba kuti: “Paulo anafotokoza Malemba mwatsatanetsatane tsiku ndi tsiku monga momwe anachitira ku Tesalonika, koma Abereya, mmalo motsutsa kumasulira kwake kwatsopano, anasanthula (anakrinō kutanthauza kuti anasefa, anafufuza mosamalitsa ndi motsimikiza monga momwe amachitira m’nkhani zalamulo . . . ) Malemba.” Kusanthula kwawo sikunali kwachiphamaso. Ayuda a ku Bereya amenewo anafufuza mosamalitsa kuti apeze chitsimikizo chakuti zimene Paulo ndi Sila anali kuphunzitsa kuchokera m’Malemba ponena za Yesu monga Mesiya wolonjezedwa kalekale zinali zowona.

Chotero, mwakutsatira chitsanzo cha Abereya akale, kuli kofunika kuti tisamangoŵerenga kokha Mawu a Mulungu komanso kuwaphunzira—“kusanthula Malemba mosamalitsa” (NW)—kuti timvetsetse tanthauzo la zimene zikunenedwa. Mwanjirayi tingazamitse chiyamikiro chathu cha Baibulo, ndipo nafenso, mofanana ndi Timoteo, timakhala anthu okhoza ‘kupulumutsa ife eni ndi iwo akumva ife.’ Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, kuwonjezera pa kuŵerenga Malemba, tawaphunzira kotero kuti tilabadire zimene taphunzira.—Miyambo 3:1-6.

Magwero a Mapindu Enieni ndi Ulosi

Tiyeni tipende zifukwa zina ziŵiri zophunzirira Baibulo. Baibulo liposa mabuku onse m’kupereka mapindu amakhalidwe ndi mwambo. Zaka zambiri zapitazo, mlangizi wa ku Amereka anapanga ndemanga iyi: “Ndikhulupirira kuti chidziŵitso cha Baibulo popanda maphunziro a ku koleji chiri chaphindu kuposa maphunziro a ku koleji popanda Baibulo.” Kuti chidziŵitso cha Baibulo chikhale chuma chanu, cholinga chanu chophunzirira Malemba chiyenera kukhala kugwiritsira ntchito miyezo yake ndi ziphunzitso m’moyo wanu watsiku ndi tsiku kotero kuti zikupangeni kukhala munthu wabwinopo, ‘amene angalunjike nawo bwino mawu a chowonadi.’—2 Timoteo 2:15; Miyambo 2:1-22.

Kuwonjezerapo, mkati mwake mumapezeka maulosi ouziridwa ndi Mulungu amene akwaniritsidwa kale m’mbiri ndipo ena akukwaniritsidwa m’zaka za zana lathu. Kuphunzira maulosi a Baibulo kumathandiza munthu kumvetsetsa tanthauzo la mikhalidwe yadziko—nkhondo, njala, kusweka kwa mabanja, maupandu achiwawa—ndi mmene angapeŵere kugwidwa ndi nkhaŵa chifukwa cha izo. (Luka 21:10, 11, 25-28) Chotero, timawunikiridwa ndi mayankho a Mulungu ku mavuto amakono, mayankho amene amavumbula kumene tiri m’nyengo ya nthaŵi ndi mmene tingakonzekerere mwachipambano kaamba ka mtsogolo. Mayankho amenewo amadza kwa ife kupyolera m’ngalande ya kagulu ka ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wodzozedwa,’ kamene kamagwiritsira ntchito Watchtower Society monga chiŵiya chake chofalitsira.—Mateyu 24:45-47; 2 Petro 1:19.

Salmo 119:105 limati: ‘Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.’ Chotero, anthu amene amaphunzira mokhazikika mawu anzeru opezeka m’Baibulo ndi kuwagwiritsira ntchito adzakhala pakati pa awo amene adzamvetsetsa chifuniro ndi cholinga cha Mulungu ndipo, kwenikwenidi, adzakhala ndi njira younikiridwa imene imatsogolera moyo wawo watsiku ndi tsiku mkati mwa tsoka lamakhalidwe lalerolino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena