Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/15 tsamba 4-6
  • Baibulo—Buku Loyenera Kuŵerengedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Baibulo—Buku Loyenera Kuŵerengedwa
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Chake Linapulumuka!
  • Chizoloŵezi cha Kuŵerenga Baibulo
  • Liŵerengeni Mokhazikika
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuŵerenga Baibulo—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mmene Tingaŵerengere ndi Kukumbukira
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kondwerani ndi Mawu a Mulungu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/15 tsamba 4-6

Baibulo​—Buku Loyenera Kuŵerengedwa

NKOSAVUTA kusoŵa mawu osonyeza kupambana pamene munthu akulankhula za Baibulo. Kwakukulukulu ilo lili buku lofalitsidwa kopambana m’mbiri yonse. Baibulo ndi buku lakale koposa, lotembenuzidwa kopambana, logwidwa mawu kopambana, losonkhezera kopambana, ndi lolemekezedwa kopambana. Mwinamwake lilinso buku lodzetsa mkangano kopambana. Ndipo ndithudi lili buku limene lapulumuka ziletso, kuwotcha, ndi zitsutso zachiwawa zochuluka kopambana. Komabe, momvetsa chisoni, pali liwu losonyeza kupambana limodzi limene silimagwiranso ntchito ku Baibulo. Mwinamwake sililinso buku loŵerengedwa kopambana m’dziko.

Ngakhale kuti anthu angakhale ndi Baibulo pamalo ena m’nyumba, ambiri amaganiza kuti ali otanganidwa kwambiri kwakuti alibe nthaŵi ya kuliŵerenga. Kuŵerenga kunali chosangulutsa chofala pa nthaŵi ina. Komabe, tsopano, ochuluka amakonda kuthera nthaŵi yawo yopuma akuonerera wailesi yakanema kapena kuchita chinthu china. Awo amene amaŵerengabe pang’ono kaŵirikaŵiri amakonda kuŵerenga zinthu zosafunikira kuyesayesa ndi zosavuta. Kuŵerenga Baibulo kumafunikira kusumika maganizo, ndipo anthu ochuluka samasumikanso maganizo mwakuya pa zimene akuŵerenga.

Komabe, Baibulo silinapulumuke kuti lingokhala pa mashelufu athu a mabuku. Pali zifukwa zabwino zimene liyenera kuŵerengedwera. Talingalirani mfundo zina zonena za ilo.

Nchifukwa Chake Linapulumuka!

Liwu lakuti “Baibulo” likuchokera ku liwu Lachigiriki lakuti bi·bliʹa, kutanthauza “timabuku.” Zimenezi zimatikumbutsa kuti Baibulo lapangidwa ndi mabuku ambiri​—ena si aang’ono kwambiri! Iwo analembedwa pa nyengo ya zaka mazana khumi ndi asanu ndi limodzi. Ngakhale kuti olembawo anali anthu, iwo anauziridwa ndi Magwero apamwamba. Wolemba Baibulo wina anati: “Pakuti kalelonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.” (2 Petro 1:21) Zimene zili zoona ponena za ulosi wa Malemba zilinso zoona ponena za Baibulo lonse. “Timabuku” touziridwa ndi Mulungu timeneti ntodzaza ndi malingaliro apamwamba a Yehova Mulungu. (Yesaya 55:9) Nzosadabwitsa kuti Baibulo lakhalako kwa nthaŵi yaitali motero!

Kwa atumiki a Mulungu, Baibulo nthaŵi zonse lakhala buku lofunika koposa. Iwo amagwirizana ndi mtumwi Paulo, yemwe anali mmodzi wa olemba Baibulo. Iye anati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso.” (2 Timoteo 3:16) Motero, Baibulo lili maziko a chikhulupiriro cha Mboni za Yehova lerolino. Limakhazikitsa ziphunzitso zawo ndi kulamulira khalidwe lawo. Zimavomereza ndi mtima wonse kuti aliyense aŵerengeko mbali ina ya Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndi kusinkhasinkha moyamikira za mkati mwake.​—Salmo 1:1-3.

Chizoloŵezi cha Kuŵerenga Baibulo

Chizoloŵezi cha kuŵerenga Baibulo chinali chopindulitsa m’nthaŵi zakale. Mafumu a Israyeli analamuliridwa kulemba pamanja kope lawolawo la Chilamulo​—chomwe tsopano chili mbali yofunika ya Baibulo​—ndi kuchiŵerenga tsiku ndi tsiku monga chikumbutso chosalekeza cha chifuniro cha Mulungu kwa iwo. (Deuteronomo 17:18-20) Kulephera kuchita zimenezi kunachititsa mafumu ambiri kugwa.

Phindu la kuphunzira Malemba lasonyezedwa m’nkhani ya mneneri Danieli wokalambayo. Chifukwa cha kuphunzira kwake mbali za Baibulo zomwe zinalipo m’nthaŵi yake, pamene anali muukapolo ku Babulo, Danieli anali wokhoza ‘kuzindikira mwa mabuku’ kuti ulosi wofunika wolembedwa ndi Yeremiya unali pafupi kukwaniritsidwa.​—Danieli 9:2.

Panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu, munthu “wolungama mtima ndi wopemphera” Simeoni anali kuyembekezera mwachidaliro kuona amene akakhala Kristu, kapena Mesiya. Simeoni anali atalonjezedwa kuti sadzafa asanaone Kristu. Kutchula kwake mawu a ulosi wa Yesaya pamene ananyamula khandalo Yesu m’manja mwake kumasonyeza kuti Simeoni anali woŵerenga wosamalitsa wa mabuku a Baibulo amene anali atalembedwa kale m’nthaŵi yake.​—Luka 2:25-32; Yesaya 42:6.

Pamene Yohane Mbatizi anali kulalikira, “anthu anali kuyembekezera” Mesiya. Kodi zimenezi zimasonyeza chiyani? Zimapereka lingaliro lakuti ochuluka mwa Ayuda anali kudziŵa za maulosi a Mesiya amene analembedwa m’Malemba. (Luka 3:15) Zimenezi nzokondweretsa, popeza kuti m’masiku amenewo mabuku sanali kupezeka mosavuta. Makope a mabuku a Baibulo anafunikira kulembedwa mosamalitsa ndi manja, ndipo motero anali okwera mtengo ndi ovuta kupeza. Kodi anthuwo anadziŵa bwanji za mkati mwake?

M’zochitika zambiri, mwa kuŵerenga poyera. Mwachitsanzo, Mose analamula kuti pa nthaŵi zakutizakuti zoikika, Chilamulo chonse choperekedwa ndi Mulungu chiŵerengedwe kwa Aisrayeli onse osonkhana. (Deuteronomo 31:10-13) Pofika zaka za zana loyamba C.E., kuŵerenga poyera mabuku a Baibulo kunali kofala. Wophunzira Yakobo anapereka ndemanga yakuti: “Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nawo m’midzi yonse amene amlalikira, akuŵerenga mawu ake m’masunagoge masabata onse.”​—Machitidwe 15:21.

Lerolino, nkosavuta kukhala ndi kope laumwini la Baibulo. Pafupifupi tina ta “timabuku” timeneti timapezeka m’zinenero 98 peresenti za anthu a m’dziko. Motero nzomvetsa chisoni kuti ena alibe chidwi cha kudziŵa zimene Baibulo likufuna kuwauza. Ino ingakhale nyengo ya sayansi, koma Mawu a Mulungu, Baibulo, mwapadera adakali ‘opindulitsa pa chiphunzitso.’ Amapereka uphungu wanzeru pa makhalidwe, maunansi a anthu, ndi nkhani zina zambiri. Ndiponso, Baibulo limapereka chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo mwamtendere.

Liŵerengeni Mokhazikika

Chifukwa chake Mboni za Yehova zapanga kukhala mbali yofunika ya ntchito yawo kulimbikitsa kuŵerenga Baibulo mokhazikika. Pa fakitale yawo ku malikulu a dziko ku Brooklyn, New York, pali mawu olembedwa ndi zilembo zazikulu zooneka bwino amene amasonkhezera anthu kuti: “READ GOD’S WORD THE HOLY BIBLE DAILY (Ŵerengani Mawu a Mulungu Baibulo Lopatulika Tsiku ndi Tsiku).” Anthu odutsapo mamiliyoni ambiri aona mawu ameneŵa, ndipo tikhulupirira kuti ambiri awalabadira.

M’mipingo yoposa 73,000 ya Mboni za Yehova pa dziko lonse, zigawo za Sukulu Yautumiki Wateokratiki zimachitidwa mlungu uliwonse. Mbali ina ya kosiyo ili kuŵerenga poyera mbali zosankhidwa za Baibulo. Onse opezekapo amakhalanso ndi gawo la kuŵerenga machaputala angapo a Baibulo mlungu uliwonse m’nyumba zawo. Awo amene amatsatira ndandanda imeneyi potsirizira pake amaŵerenga Baibulo lonse.

Kakonzedwe kameneka kali kogwirizana ndi limodzi la mabuku ophunziridwa ogwiritsiridwa ntchito m’sukuluyi. Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki limati: “Programu yanu ya inu nokha iyenera kuphatikizamo nthaŵi ya kuŵerenga Baibulo lenilenilo. Pali phindu lalikulu m’kuŵerenga lonse kuyambira ku chikuto kufikira ku chikuto. . . . Komabe, chonulirapo chanu m’kuŵerenga sichiyenera konse kungokhala kutsiriza zoti ziŵerengedwezo, koma kupeza lingaliro lake lathunthu limodzi ndi cholinga cha kukumbukira. Khalani ndi nthaŵi ya kusinkhasinkha zimene likunena.”

Zofalitsidwa zina zotulutsidwa ndi Mboni za Yehova zimalimbikitsanso kuŵerenga Baibulo. Mwachitsanzo, m’magazini anzake a magazini ano, Galamukani!, munali chilimbikitso chotsatirachi kwa achichepere: “Kodi mwamaliza kuliŵerenga . . . Baibulo lonse? Inde, Baibulo ndi bukhu lalikuludi, koma bwanji osaligawa m’zigawo zochepa m’kuliŵerenga kwake? . . . ‘Mfulu’ za ku Bereya ‘zinasanthula malemba masiku onse.’ (Machitidwe 17:11) Ngati inu mutsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku ya kuŵerenga mphindi 15 zokha patsiku . . . , mungamalize kuŵerenga Baibulo m’chaka chimodzi.” Inde, Mboni za Yehova zimalingalira kuti Akristu amakono ayenera kukhala odziŵa Malemba, monga momwe analiri atumiki a Mulungu m’nthaŵi zakale.

Polingalira zimenezi, Mboni zachirikiza njira ya m’zaka za zana la 20 ya kuŵerenga poyera Baibulo. M’zinenero zingapo, zatulutsa makaseti ojambulidwa a kuŵerengedwa kwa Baibulo lonse. Kwa ambiri chimenechi chakhala chithandizo chabwino m’kulaka zopinga zina za kuŵerenga Baibulo. Ena amamvetsera zojambulidwa zimenezi pamene akugwira ntchito m’nyumba, kuyendetsa galimoto lawo, kapena kuchita zinthu zina zambiri. Kukhala pansi ndi kumvetsera mwakachetechete ku kuŵerengedwa kwa mbali za Baibulo pamene mukutsatira m’kope lanu kuli chinthu chokondweretsa.

Ngati simunayambebe kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, bwanji osapanga chizoloŵezi cha kuchita motero? Zimenezi sizitofunikira kutenga nthaŵi yaitali tsiku lililonse, koma mapindu ake adzakhala aakulu, popeza kuti kugwiritsira ntchito Malemba kudzakutheketsani kuchita mwanzeru ndi kukhala ndi moyo wofupa mwauzimu. Mudzakhalanso mukuchita zinthu mogwirizana ndi lamulo ili loperekedwa kalekale kwa Yoswa mtsogoleri wa Israyeli: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.”​—Yoswa 1:8.

Masamba a Baibulo amasonyeza chifuno chachikondi cha Yehova kwa anthu omvera. Chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ake ouziridwa chimachititsa chimwemwe chenicheni ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’Paradaiso m’dziko latsopano labwino koposa la madalitso osatha. (Luka 23:43; 2 Petro 3:13) Tenganitu mwaŵi wanu wa kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo kuti mupeze moyo wabwino koposa umenewu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena