Chithandizo Chabwino Koposa Chikupezeka!
KWA Mkristu chosankha ndi ukulu wa chisamaliro cha odwala mosachiritsika zingadzutse mafunso aakulu. Mwachitsanzo:
Kodi kukakhala kosagwirizana ndi malemba kuchita zochepera koposa zonse zothekera kusungitsa moyo? Ndipo ngati kuli kovomerezedwa kulola munthu wina kufa mwachibadwa, popanda kudodometsa kwaukatswiri kotalikitsa moyo, bwanji ponena za kuphera chifundo—kachitidwe kotsimikizirika, kadala kothetsera kuvutika kwa wodwalayo mwakufupikitsadi kapena kuthetsa moyo wake?
M’tsiku lathu ndi nyengo, ameneŵa ndiwo mafunso ofunika. Komabe, sitiri opanda chithandizo powayankha.
Wolemba wouziridwa moyenerera anati: “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Salmo 46:1) Zimenezo ziridi choncho kwa ife polingalira nkhani yomwe iripo tsopano. Yehova Mulungu ndiye magwero a chithandizo chanzeru koposa ndi chaukatswiri koposa. Iye wawona miyoyo ya anthu zikwi mamiliyoni ambiri. Amadziŵa—bwinopo koposa dokotala aliyense, katswiri wazamakhalidwe, kapena loyala—chimene chiri chabwino koposa. Choncho tiyeni tiwone chithandizo chimene amapangitsa kupezeka kwa ife.—Salmo 25:4, 5; Ahebri 4:16.
Lingaliro Lolungama la Moyo
Tichita bwino kuzindikira kuti lingaliro la kusungitsa moyo pa mtengo uliwonse silolekezera kwa akatswiri azamankhwala. Liri chotulukapo chachibadwa cha lingaliro lofala lamakono. Nchifukwa ninji ziri choncho? Eya, ngati moyo ulipowu ndiwo wokha umene ulipo, pamenepo kungawonekere kuti moyo wathu weniweniwo uyenera kusungidwa mumikhalidwe iriyonse ndi pa mtengo uliwonse. Koma lingaliro lofala ladziko limeneli mumikhalidwe ina lachititsa zochitika zosasangalatsa—anthu okomoka akumakhalitsidwa “amoyo” pamakina kwazaka zambiri.
Ndiponso, pali ena amene amakhulupirira kusafa kwa moyo waumunthu. Malinga ndi lingaliro lawo, moyo uno uli kokha siteshoni yapanjira ya kuchinthu china chabwinopo. Plato, mmodzi wa oyambitsa lingaliroli, anati:
“Kaya imfa ikhale mkhalidwe wa kusakhalako ndi kusazindikira kotheratu, kapena, monga momwe ambiri amanenera, pamakhala kusintha ndi kusamuka kwa moyo kuchokera padziko lino kumka kulina. . . . Ngati imfa iri ulendo womka kumalo ena, . . . kodi ndiubwino wotani, o abwenzi ndi oŵeruza anga, umene ungakhale waukulu koposa umenewu?”
Munthu wokhala ndi kukhulupirira kotero angawone imfa monga bwenzi, yoyenera kulandiridwa ndipo mwinamwake ngakhale kufulumizidwa. Komabe, Baibulo limaphunzitsa kuti moyo ngwopatulika kwa Yehova. “Pakuti chitsime cha moyo chiri ndi inu,” wamasalmo wouziridwa analemba motero. (Salmo 36:9) Pamenepa, kodi Mkristu wowona ayenera kuvomereza kukhala ndi phande m’kuphera chifundo?
Ena amalingalira kuti pali chisonyezero Chamalemba chankhaniyi pamene Mfumu Sauli, wovulazidwa kwambiri, anachonderera wonyamula zida wake kumupha. Iwo alingalira zimenezi kukhala mpangidwe wa kuphera chifundo, kachitidwe kadala kofulumizira imfa ya munthu wina amene anali kale kumafa. Pambuyo pake Mwamaleki anadzinenera kukhala atalolera pempho la Sauli kuti aphedwe. Koma kodi Mwamaleki ameneyo analingaliridwa kukhala atachita bwino kuthetsa kuvutika kwa Sauli? Kutalitali. Davide, wodzozedwa wa Yehova, analamula kuti Mwamaleki ameneyu aphedwe chifukwa cha liwongo lamwazi. (1 Samueli 31:3, 4; 2 Samueli 1:2-16) Pamenepo, chochitika Chabaibulo chimenechi sichimalungamitsa mwanjira ina iriyonse kukhala ndi phande kwa Mkristu m’mbali iriyonse ya kuphera chifundo.a
Komabe, kodi zimenezi zimatanthauza kuti Mkristu ayenera kuchita zirizonse zothekera mwaluso kutalikitsa moyo umene ulinkutha? Kodi munthu ayenera kutalikitsa njira yofera monga momwe kungathekere? Malemba amaphunzitsa kuti imfa, siri bwenzi la munthu, koma mdani. (1 Akorinto 15:26) Ndiponso, akufa sakuvutika ndipo sakusangalala, koma ali mumkhalidwe wofanana ndi tulo. (Yobu 3:11, 13; Mlaliki 9:5, 10; Yohane 11:11-14; Machitidwe 7:60) Ziyembekezo za moyo zamtsogolo za akufa zimadalira kotheratu pa mphamvu ya Mulungu yowaukitsa kupyolera mwa Yesu Kristu. (Yohane 6:39, 40) Motero tikupeza kuti Mulungu watipatsa chidziŵitso chothandizachi: Imfa sichinthu choyenera kulakalakidwa, koma palibenso thayo lakutembenukira kuzoyesayesa zosaphula kanthu zakutalikitsira njira yofera.
Zitsogozo Zachikristu
Kodi Mkristu angagwiritsire ntchito zitsogozo ziti m’chochitika kumene wokondedwa ali mumkhalidwe wakufa?
Choyamba, tiyenera kuzindikira kuti mkhalidwe uliwonse pawokha wophatikiza uthenda wosachiritsika ngwosiyana, wosiyana kwambiri, ndipo palibe malamulo okhudza yonseyo. Ndiponso, Mkristuyo ayenera kusamala kulingalira malamulo adzikolo m’nkhani zoterozo. (Mateyu 22:21) Kumbukiraninso kuti palibe Mkristu wachikondi amene angachirikize kunyalanyazidwa kwa zamankhwala.
Kokha pamene pali nthenda yosachiritsika yotsimikizirika (kumene mkhalidwe watsimikiziridwa bwino lomwe kukhala wopanda chiyembekezo) kulingalira kuyenera kuperekedwa ku kupempha kuti luso lochirikiza moyo liimitsidwe. Mumikhalidwe yotero palibe chifukwa Chamalemba choti nkuumirira paluso lazamankhwala limene likangotalikitsa njira yofera imene iri yopita patsogolo koposa.
Kaŵirikaŵiri imeneyi ndimikhalidwe yovuta kwambiri ndipo ingaphatikizepo zosankha zovutitsa maganizo. Mwachitsanzo, kodi munthu angadziŵe motani pamene mkhalidwe uli wopanda chiyembekezo? Ngakhale kuli kwakuti palibe aliyense amene angakhale wotsimikizira kotheratu, nzeru iyenera kugwiritsiridwa ntchito pamodzi ndi uphungu wosamalitsa. Pepala lina lazamankhwala lolangiza madokotala limati:
“Ngati pali kusamvana ponena za mapendedwe anthenda kapena zizindikiro zake zapasadakhale kapena zonse ziŵiri, njira yochirikizira moyo iyenera kupitirizidwa kufikira kuvomerezana koyenera kutafikiridwa. Komabe, kuumirira pakutsimikizirika kopambana mlingo woyenera kungalefule maganizo a dokotala amene akuchita ndi zosankha zachisamaliro chazamankhwala mwachiwonekere m’zochitika zopanda chiyembekezo. Lipoti lakamodzikamodzi la wodwala wokhala ndi mkhalidwe wofanana amene anapulumuka sindilo chifukwa chachikulu chopitirizira chisamaliro chazamankhwala champhamvu. Kuthekera kwaziŵerengero zazing’ono zoterozo sikumaposa ziyembekezo zoyenera za chotulukapo chimene chidzatsogolera zosankha zachisamaliro chazamankhwala.”
M’vuto lotero, Mkristuyo, kaya wodwala kapena wachibale, moyenerera akayembekezera chithandizo chakutichakuti kuchokera kwa dokotala wake. Pepala lazamankhwala limeneli likumaliza kuti: “Mulimonse mmene zingakhalire, kuli kosalungama kungopereka ziŵerengero za zenizeni zamankhwala ndi zosankha ndi kusiya wodwalayo ali wokaikaika wopanda chitsogozo chirichonse chowonjezereka chonena za njira zina zogwira ntchito ndi zosagwira ntchito.”
Akulu Achikristu amumpingomo, pokhala aminisitala achikulire, angakhalenso othandiza kwambiri. Ndithudi, wodwalayo ndi banja lake lenileni ayenera kupanga chosankha chawochawo cholama mumikhalidwe yogwedeza maganizo imeneyiyo.
Potsirizira, sinkhasinkhani mfundo zimenezi. Akristu amafunitsitsa kukhalabe ndi moyo kotero kuti asangalale ndi kutumikira Mulungu. Komabe, iwo amazindikira kuti m’dongosolo lamakonoli, tonsefe tikufa; m’lingaliro limeneli tonsefe ndife odwala mosachiritsika. Kuli kokha mwa mwazi wansembe wa Yesu Kristu chakuti tiri ndi chiyembekezo chirichonse cha kusintha mkhalidwewo.—Aefeso 1:7.
Ngati imfa ifikiradi wokondedwa, zovuta monga momwe zimenezi ziriri, sitimasiidwa tikuvutika ndi kumva chisoni “monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.” (1 Atesalonika 4:13) Mmalomwake, tingapeze chitonthozo chakuti tinachita bwino koposa moyenerera monga momwe tikanathera kwa wodwala wathu wokondedwa ndi kuti chithandizo chirichonse chazamankhwala chimene tinagwiritsira ntchito chinali kwenikweni chithandizo chakanthaŵi. Komabe, tiri ndi lonjezo losangalatsa la Uyo amene adzatimasula m’mavuto onse oterowo pamene ‘mdani wotsiriza, imfa, adzathedwa.’—1 Akorinto 15:26.
Inde, potsirizira pake chithandizo chabwino koposa cha omafawo chidzachokera kwa Mulungu amene anapereka moyo kwa anthu oyamba ndi amene amalonjeza chiukiriro cha okhulupirira mwa iye ndi Mwana wake, Yesu Kristu.—Yohane 3:16; 5:28, 29.
[Mawu a M’munsi]
a Ponena za ndemanga zowonjezereka zonena za kotchedwa kuphera chifundo, onani Galamukani! wa March 8, 1978, tsamba 4-7, ndi wa May 8, 1974, tsamba 27-8, m’Chingelezi.
[Chithunzi patsamba 29]
Kodi imfa ya Sauli imachirikiza kuphera chifundo?