Kukulira Mumzinda wa mu Afirika
Kukula kwa ziŵerengero za anthu m’maiko a mu Afirika apafupi ndi Sahara kuli pakati pa ziŵerengero zapamwamba kopambana zadziko. Kumeneko mkazi aliyense, paavareji, amabala ana oposa asanu ndi mmodzi. Umphaŵi, mkhalidwe womaipa wa malo okhala, ndi kuchepa kwa zochirikiza moyo, zimangokulitsa kokha vutolo. Nayi nkhani yonena za mmene moyo uliri m’mbali ya dzikolo.
NDINAKULIRA muno, mumzinda waukulu wa ku Kumadzulo kwa Afirika. Tinali ana asanu ndi aŵiri m’banja, koma aŵiri anamwalira adakali achichepere. Nyumba yathu inali chipinda chogona ndi chochezera zalendi. Amayi ndi atate anali kugona m’chipinda chogona ndipo anafe tinali kugona pamphasa m’chipinda chochezera, anyamata kumbali ina m’chipindacho ndipo asungwana kumbali inayo.
Mofanana ndi anthu ambiri m’chitaganya chathu, tinalibe ndalama zambiri, ndipo sinthaŵi zonse pamene tinali ndi zonse zimene tinafuna. Nthaŵi zina panalibe ngakhale chakudya chokwanira. Mmaŵa, kaŵirikaŵiri tinalibe choti tidye kusiyapo mpunga wofunditsidwanso wosiidwa dzulo. Panthaŵi zina ngakhale zimenezo zinali zosapezeka. Mosiyana ndi ena amene amalingalira kuti mwamuna, monga wopeza ndalama, ayenera kukhala ndi mbali yaikulu, mkazi mbali yachiŵiri, ndi kuti ana adzipeza zosiidwa, makolo athu ankagona ndi njala ndi kulola anafe kuti tigaŵane zochepa zimene zinalipo. Ndinayamikira kwambiri kulepa kwawo.
Kupita Kusukulu
Anthu ena mu Afirika amakhulupirira kuti anyamata okha ndiwo amene ayenera kupita kusukulu. Iwo amalingalira kuti sikuli kofunikira kuti asungwana adzipita chifukwa chakuti amakwatibwa ndipo amuna awo amaŵasamalira. Makolo athu analibe lingaliro limenelo. Asanu tonsefe tinatumizidwa kusukulu. Koma kunali kutsenderezedwa m’zandalama kwa makolo athu. Zinthu zonga pensulo ndi pepala sizinali vuto lalikulu, koma mabukhu oŵerenga anali okwera mtengo, ndipo choteronso ndi yunifolomu yasukulu inali yokakamiza.
Pamene ndinayamba kupita kusukulu, ndinalibe nsapato. Ndinalibe kufikira m’chaka changa chachiŵiri cha sukulu ya sekondale, pamene ndinali wazaka 14, kuti makolo anga anali okhoza kundigulira nsapato. Komatu, zimenezi sizikutanthauza kuti ndinalibiretu nsapato. Nsapato zokha zimene ndinali nazo zinali za ku tchalitchi, ndipo sindinaloledwe kuzivala popita kusukulu kapena kumalo ena alionse. Ndinafunikira kupita wosavala nsapato. Nthaŵi zina atate wanga anali wokhoza kupeza matikiti okwerera basi, koma pamene anali wosakhoza, tinatofunikira kuyenda pansi popita kusukulu ndi kubwerako. Inali pautali wa pafupifupi makilomitala atatu.
Tsiku Lochapa ndi Kutunga Madzi
Tinkachapa zovala zathu mumfuleni. Ndikukumbukira tikumapitako limodzi ndi amayi, amene adanyamula mtsuko, sopo, ndi zovala. Kumfuleniko, ankadzaza mtsukowo ndi madzi, ndi kuviikamo zovala, ndi kutikitira sopo. Pamenepo ankamenyetsa zovalazo pamatanthwe ndi kuzisukuluza mumfulenimo. Pambuyo pake ankaziyanika pamatanthwe ena kuti ziume chifukwa chakuti zinali zolemera kwambiri kosakhoza kupita nazo kunyumba zili zamadzi. Ndinali wachichepere panthaŵiyo, chotero ndinapatsidwa thayo la kulindilira zovalazo kufikira zitauma kotero kuti palibe aliyense amene anali kudzaziba. Amayi anachita yambiri ya ntchitoyo.
Anthu ochepa kwambiri anali ndi madzi a m’mipope m’nyumba zawo, chotero imodzi ya ntchito zanga inali kupita ndi chitini kukatunga madzi pampope wapanja, wotchedwa kuti mpope woimirira. Vuto linali lakuti m’nyengo yotentha, mipope yambiri yoimirira inali kutsekedwa kusungitsa madzi. Pachochitika china, tinatha tsiku lonse lathunthu popanda madzi akumwa. Popandiratu ngakhale dontho limodzi! Nthaŵi zina ndinatofunikira kuyenda makilomitala ambiri kukafunafuna madzi odzaza chitini chimodzi chokha. Kunyamula madzi pamutu kwaulendo wautali wotero kunali kusosola tsitsi langa pamutu pamene chitinicho chinali kuikidwa. Ndinali wadazi pausinkhu wazaka khumi! Ndiri wachimwemwe kunena kuti tsitsilo linameranso.
Ana Monga Chisungiko
Poyang’ana kumbuyo, ndingathe kunena kuti mkhalidwe wathu wa moyo unali wachikatikati, mwinamwake wabwinopo koposa wachikatikati kumbali yathu ya Afirika. Ndikudziŵa za mabanja ena ambiri amene mkhalidwe wawo wa moyo unali woipa kwambiri koposa wathu. Ambiri a mabwenzi anga a pasukulu anafunikira kukagulitsa pamitsika asanapite kusukulu ndi pambuyo pake kotero kuti abweretsere mabanja awo ndalama. Ena sanali okhoza kupeza kanthu kena kakudya mamaŵa asanapite kusukulu, ndipo ankachoka panyumba ali anjala ndi kukhala kusukuluko tsiku lonse lathunthu opanda chakudya. Ndingakumbukire nthaŵi zambiri pamene ndinadya buledi wanga pasukulu kuti mmodzi wa ana ameneŵa ankadza ndi kundichonderera kuti ndimpatseko. Chotero ndinkanyema ndi kugaŵana naye.
Mosasamala kanthu za mavuto ndi zopinga zoterozo, anthu ambiri adakafunabe kukhala ndi mabanja aakulu. “Mwana mmodzi simwana ayi,” anthu ambiri amatero kunoko. “Ana aŵiri ndimmodzi, ana anayi ndiaŵiri.” Zimenezo ziri chifukwa chakuti mlingo wa imfa zamakanda uli pakati pa waukulu kopambana m’dziko lonse. Makolo amadziŵa kuti ngakhale kuti ena a ana awo adzafa, enawo adzakhalabe ndi moyo, kukula, kupeza ntchito, ndi kubweretsa ndalama panyumba. Pamenepo adzakhala okhoza kusamalira makolo awo amene akalamba. M’dziko lopanda mapindu achitetezo cha anthu onse, zimenezo ziri ndi tanthauzo lalikulu.—Monga momwe yasimbidwira ndi Donald Vincent.