Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 11/8 tsamba 19-21
  • Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutchova Juga—Maupandu Obisika
  • Kutchova Juga Komwereketsa
  • Chinyengo cha Makina Otchovera Juga
  • Kupanga Chosankha Chabwino
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Peŵani Msampha wa Kutchova Njuga
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 11/8 tsamba 19-21

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri?

ANDREW wazaka khumi ndi ziŵiri zakubadwa ndi Julian wazaka khumi zakubadwa potsirizira pake sanali kuwonedwa ndi makolo awo. Banja lawo linali paulendo m’ngalaŵa, ndipo anyamatawo anachititsidwa chidwi ndi makina osiyanasiyana otchovera juga m’ngalaŵamo. Powona chidwi chawo, woseŵera juga wina anapatsa aliyense wa iwo kobili kuchita kuti adziyesere makinawo. Kodi vuto linali lotani? Makolo awo anawaletsa kuyandikira pafupi ndi makinawo.

Mosasamala kanthu za zimenezo, Andrew ndi Julian anasankha kuchitabe mosasamala kanthu za upandu wa kugwidwa ndi makolo. Akukumbukira chenjezo la makolo awo, iwo anaseŵerabe makinawo—ndi kuchulukitsa ndalama zawo mowirikiza kaŵiri! Ndiyeno anaseŵeranso. Nthaŵi ino iwo anadabwa ndi ziŵerengero za zipambano zopezedwa! “Kodi zimenezi zingakhale zaupandu motani?” iwo analingalira motero. “Kupanga ndalama kuli kosavuta kwambiri! Kodi kutchova juga kulidi koipa kwambiri?”

Mofanana ndi achichepere ambiri kumaiko kumene kutchova juga kuli kofala, Andrew ndi Julian sanawone upandu wowopsa. Zimenezi ziri zosavuta kumvetsetsa mutalingalira zitsanzo zimene achikulire ena apereka m’nkhaniyo. Sikokha kuti ambiri amatchova juga komanso amapereka zifukwa zowonekera kukhala zabwino kulungamitsa chizoloŵezi chawo. Mwachitsanzo, iwo amati kutchova juga kumachitadi zabwino zochuluka, akumatchula ndalama zopezedwa m’malotare zimene zimathandiza m’zinthu zofunika. (Koma zimenezi nzopanda nzeru monga momwe kunena kuti chopereka cha wozembetsa anamgoneka wotchuka chothandiza osoŵa chimalungamitsira malonda a anamgoneka!) Komabe ena amanena kuti kutchova juga ndiko kuseŵera ndi kusanguluka kosavulaza, kowonjezera mlingo wa chisangalalo cholandirika kumoyo.

Komabe, ku Britain ndi Ireland, monga kumaiko ena, achichepere zikwi zambiri akhala otchova juga. Ndipo chiyembekezo cha kupanga ndalama zochuluka limodzi ndi kuyesayesa kochepa chingakukopeni.

Kutchova Juga—Maupandu Obisika

Chikhalirechobe, kutchova juga kumakhala ndi upandu wina wowopsa pa achichepere. Malipoti amanena za “omwerekera ndi kutchova juga” ndi “mavuto amene kutchova juga kungadzetse, pamene seŵero losavulaza limakhala chisonkhezero chimene chingasandutse munthu kukhala wakhalidwe loipa.” Malinga ndi The Buzz (programu ya wailesi yakanema Yachibritishi), kutchova juga pakati pa ana “kungachititse kulumpha makalasi, chiwawa, kulanda ndi kuba, kutchova juga komwereketsa ndi uchiwerewere ndipo, m’zochitika zakamodzikamodzi, kudzipha kapena kuyesa kudzipha.” Kuti kutchova juga kulidi ndi kuthekera koteroko kodzetsa ngozi kwatsimikiziridwa ndi zokumana nazo zenizeni.

“Ndinayamba kutchova juga pamena ndinali wazaka 11 zakubadwa,” akutero Adrian. “Ndinapita ndi bambo wanga wamng’ono ndi msuwani kumpikisano wa agalu. Poyamba ndinalidi ndimwaŵi ndi kupambana kaŵirikaŵiri.” Kodi zimenezi zinakhala ndi chiyambukiro chotani pa Adrian? “Sindinazengereze kupeka nthano—kunama—kwa atate wanga kuchitira kuti ndipatsidwe ndalama,” iye akufotokoza motero, “ndipo pamene ndinali wachichepere, ndinalibe mantha ponena za kuba ndalama m’makina osungira ndalama m’sitolo ya atate wanga zolipirira chizoloŵezi changa cha kutchova juga.”

Adrian akutchula chiyambukiro china chosafunika. “Mosavuta ungakhale wosafuna kulembedwa ntchito,” iye akufotokoza motero, “chifukwa ndalama zimene umazipeza mwakugwira ntchito mowona mtima zingawonekere zochepa kukhala poyerekezera ndi zimene muganiza kuti mukhoza kupeza mwa kutchova juga.”—Yerekezerani ndi Miyambo 13:4; Mlaliki 2:24.

Robert (siliri dzina lake lenileni) anayamba kutchova juga pausinkhu wazaka 12. Iye akutchulanso upandu wina: “Ungakhale wokhulupirira malaulo kwambiri.” Iye akulongosola kuti: “Atate wanga anali ndi makina otchovera juga m’sitolo yathu. Ndinadziŵadi mmene makinawo anagwirira ntchito, komano ndinachita zinthu mwamwambo kuyesa kusonkhezera zotulukapo, monga ngati kutabinya batani mumpangidwe wakutiwakuti kapena kusiya ndalama zopezedwazo m’malo a makinawo kumene ndalama zimagaŵidwa kwanthaŵi yotalikirapo. Anthu ena analankhuzanadi ndi makinawo.” Inde, otchova juga ochuluka mosadziŵa amakhala olambira okhulupirira malaulo a mulungu wa mwaŵi—chizoloŵezi chotsutsidwa ndi Mulungu.—Yesaya 65:11.

Kutchova Juga Komwereketsa

Upandu wina wobisika ndiwo chikhoterero chochititsa kutchova juga kukhala komwereketsa kotheratu. “Ana oposa 2,000 osafikira msinkhu wazaka 16 amatengedwa ndi makolo awo kupita ku Gamblers Anonymous (gulu limene limathandiza otchova juga kugonjetsa kumwerekera kwawo) chaka ndi chaka, ndipo zolembedwa zomwe ziripo . . . ku Britain zikulingaliridwa kukhala chabe umboni wa vuto lalikulu.” (The Buzz) Kodi iwo angakhale omwerekera motani? Lipoti lina linati: “Atangomwerekera, iwo ayenera kutchova juga kaya akupambana kapena kulephera.”

Robert akukumbukira kuti anawona mkazi wina akuwawanya £90 ($140, U.S.) kutchovera juga masiku onse. Wotchova juga wachichepere wina analakalaka kwambiri kupeza ndalama zokhutiritsa kumwerekera kwake ku makina otchovera juga kwakuti anayesa kupha amayi ŵake! Paddy, amene anayamba kutchova juga pamsinkhu waung’ono kwambiri, anali ndi vuto lofananalo la kulephera kulamulira chizoloŵezi chake cha kutchova juga. “Ndinaleredwa m’banja lotchova juga,” iye akumbukira. “Ndinkatchova juga pamtengo uliwonse. Pamene ndinakula ndi kukwatira, kutchova juga kunalanda mkazi wanga ndi ana chakudya, ndipo potsirizira pake kunandipangitsa kulingalira kudzipha.”

Chinyengo cha Makina Otchovera Juga

Mtundu uliwonse wa kutchova juga ungatulutse zotulukapo zoipa zoterozo, koma umodzi wa maupandu aakulu kwa achichepere lerolino ndiwo makina otchovera juga. Amenewo “pakali pano akulingaliridwa kukhala vuto lalikulu kwa otchova juga achichepere,” ikutero Journal of Gambling Behavior, Spring 1989. Makina ameneŵo, ofotokozedwa bwino kukhala achifwamba okhala ndi chida chofanana, ali “zipangizo zonyenga ndi zokopa” ikutero The Buzz. “Pamene muwaseŵera mowonjezereka, ndipamene muli wothekera kufuna kuwaseŵeranso.”

Kodi kuli kwanzeru ndithu kuseŵera seŵero, mosasamala kanthu kuti lingakhale lokopa motani, kumene mwaŵi uli wolinganizidwa kutsimikizira kuti inu nthaŵi zonse mudzalephera kotheratu koposa mmene mudzapambanira? Young People Now inafotokoza mipata yanu yakupambana motere: “Osapatsa munthu wopusa mpata wakupambana chirichonse, umatero mwambi. Makina otchovera juga samatero . . . [Ngati] muika £10.00 m’makina mobwerezabwereza idzasunga £7.00 ndi kukubwezerani £3.00.”

Nchifukwa chake Mark Griffiths, wopenda ziyambukiro za kutchova juga pa achichepere, akuti: “Njira yokha yopangira ndalama kuchokera m’makina otchovera juga ndiyo kukhala ndi makina oti anthu ena aseŵere koma osati inuyo.” Kodi kumawonekera kukhala kwanzeru kwa inu kudziloŵetsa m’maseŵera osapindulitsa oterowo?

Ndiponso, makina ameneŵo anapangidwa mwamachenjera kuti akumwerekeretseni kuwaseŵera mowonjezereka. Motani? Mwakusonyeza mizera itatu ya zizindikiro mmalo mwa mzera umodzi chabe! Young People Now ikulongosola kuti: “Mizera yapamwamba ndi yapansi pamizera yopambanira imasonyezedwa kunyenga oseŵerawo kuti ‘kunatsala nenene kupambana’ ndipo motero kuwalimbikitsa kuyesanso.” Chotchedwa kutsala nenene kupambana, zizindikiro ziŵiri za kupambana ndi chachitatu cha kulephera, kaŵirikaŵiri chimawonedwa ndi wotchova jugayo monga “kupambana kwenikweni,” ndipo motero amalimbikitsidwa kuyesanso kachiŵiri—ndi kumangobwerezabwereza.

Koma mmenemu ndimo mmene aliri malonda akutchova juga. Opanga makinawo ndi maseŵera akutchova juga amazilinganiza m’njira yoti ipereke chinyengo kuti mmalo mwa kulephera, inu mwangotsala nenene kupambana! Mukanapambana! Zimenezi zimakusonkhezerani kupitirizabe kuseŵera chifukwa cha nthumanzi imene mumamva potsala nenene “kupambana.” Phatikizani pazimenezi magetsi ong’anima ndi phokoso lochititsa chidwi, ndipo mumayamba kuzindikira zitsenderezo zamphamvu zosonkhezera maganizo zimene zikugwiritsiridwa ntchito kukukopani kuseŵera—kupitirizabe kumaseŵera—ndi kupitirizabe kumalephera.

Kupanga Chosankha Chabwino

Pamenepo, njira yabwino koposa ya kupeŵera kukhala wotchova juga womwerekera ndiyo kupeŵa kutchova juga choyamba. Peŵani mpangidwe uliwonse wa kutchova juga, kuphatikizapo kubetcha ndalama zochepa. Kwa ochuluka chizoloŵezi chakutchova juga chamoyo wonse chinayamba mwakugwiritsira ntchito mapeni otchovera juga. Ndipo ngati mpata wakutchova juga upezeka, kumbukirani lamulo lamakhalidwe abwino limene Yesu Kristu ananena pa Mateyu 7:17: “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.”

Tangolingalirani: Kodi kutchova juga kwenikweni kumatulutsanji m’miyoyo ya anthu? Kodi kumathandiza munthu kukulitsa zipatso za mzimu wa Mulungu, zonga chimwemwe, mtendere, ndi kudziletsa, kapena kumachititsa ndewu, kupsa mtima, ndi umbombo? (Agalatiya 5:19-23) Kumbukirani, umbombo umatsutsidwa ndi Mulungu. Kachitidwe kamodzi chabe kaumbombo kangakupangitseni kukhala wonyansa pamaso pake. Dzifunseni ngati otchova juga ali atsamwali oyenera kwa achichepere Achikristu. (1 Akorinto 15:33) Kumbukirani kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kodi kutchova juga sikumatumikira bwino lomwe chifuno cha Satana Mdyerekezi? Choncho nkukopedweranji kukuphatikizidwamo?

Pamene lotare yadziko lonse la Ireland inayamba, mofulumira inatchedwa dzina lotoleralo msonkho wa zitsiru! Mawu amenewo amafotokoza bwino kutchova juga. Kodi ndani amene amafuna kulingaliridwa kukhala wopusa ndi kuberedwa ndalama zofunikazo mwa kukopedwera m’dziko lamaloto la otchova juga? Mwamwaŵi, Andrew ndi Julian (otchulidwa poyambapo) anawona m’kupita kwanthaŵi kuti kutchova juga kuli maseŵera a zitsiru. Iwo amawona bwino lomwe maupandu ake ndi kuwapeŵa. “Nthaŵi iriyonse,” iwo akutero, “pamakhala zinthu zabwino koposa zoyenera kuchita m’moyo koposa kuwawanya ndalama zanu mukumatchova juga.”

[Chithunzi patsamba 20]

Kutchova juga ngakhale kwa ndalama zochepa kungamwerekeretse munthuwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena