Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 10/8 tsamba 25-29
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri?
    Galamukani!—1991
  • Omwerekera ndi Juga Kwawo ndi Kuluza Basi
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 10/8 tsamba 25-29

Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!

KODI mukupukusa mutu chifukwa chosakhulupirira kumwerekera ndi juga kwakukulu kumene, amuna ndi akazi achikulire afikapo? Kodi zimakusokonezani maganizo kuŵerenga za ajuga achikulire omwe alepa ntchito ya moyo wawo ndi zinthu zazikulu zimene apeza—ntchito, malonda, banja, ndipo kwa ena, moyo wawo—chifukwa cha juga? Kodi mungamvetse nzeru za munthu wachikulire wokhwima bwino ndi wophunzira, amene, atawina $1.5 miliyoni pajuga, apitirizabe kuseŵera juga mpaka ataluza $7 miliyoni usiku womwewo? Nthaŵi zambiri chochititsa ndi umbombo, kufunafuna dola yovuta kupezayo. Komabe, choputira kaŵirikaŵiri ndi kusangalatsa kwake kwa juga yeniyeniyo.

Ngati ndinu makolo okhala ndi ana aang’ono, kodi simukuda nkhaŵa chifukwa choganiza kuti juga ndi maseŵero a munthu wokhwima wachikulire? Ganizanipo bwino pamenepo. Talingalirani achichepere okonzeka kukhala oseŵera juga atsopano—kapena amene ayamba kale kuseŵera juga. Maumboni angakudabwitseni.

Mawu otsatira anatuluka m’nkhani zaposachedwapa m’manyuzipepala ndi m’magazini: “Zitheka Kuti Juga Nkukhala Chizoloŵezi Choipa cha Achichepere a m’ma ’90.” “Achichepere Ambiri Akodwa ndi Juga.” “‘Crack wa m’ma ‘90’: Juga Ikoŵa Ana.” “Mwana Wanga Zinamkanika Kusiya Juga.”

Tsopano, taŵerengani nkhani zake. “Akuluakulu a boma akuti choputira kwambiri mliriwo ndi kufalikira kwa juga zochirikizidwa ndi boma ndi tchalitchi,” inatero nyuzipepala ina. “Lerolino, kubetcha nkwapafupi kwambiri kwa achichepere otengekatengeka kuposa ndi kalelonse. Ndipo akatswiri akuchenjeza kuti oposa 90 peresenti ya achikulire omwerekera ndi juga amayamba chizoloŵezicho asanakwanitse zaka 14,” linatero pepalalo. “Kale omwerekera ochuluka anali kuyamba juga ali ndi zaka za ku ma 14. Tsopano tikuona zakazo zikutsika kukhala 9 kapena 10,” wofufuza wina anatero. “Chifukwa? Chifukwa chakuti mwaŵi ulipo,” iye anatero. “Ana . . . amaona zilengezo za juga kulikonse. Yakhala chosangulutsa chovomerezeka kwa anthu.” “Ikuipiraipira mofulumira,” anatero woimira gulu lotchedwa Gamblers Anonymous. “Ana akuyamba pamsinkhu womacheperachepera, ndipo ambiri akukodwa nayo kuposa ndi kalelonse.”

Malinga ndi kufufuza kochitidwa pa achichepere a juga m’boma lina la America, pafupifupi 3.5 peresenti anali okhoza kukhala omwerekera ndi juga; mwachionekere enanso 9 peresenti anali kudzakhala otchova juga “okhoza kubetcha kalikonse.” “Makamaka, ziŵerengero zikusonyeza kuti pali otchova juga ochuluka kwambiri pakati pa achichepere kuposa amene ali pakati pa achikulire onse,” anatero William C. Phillips, mgwirizanitsi wa aphungu pa koleji ina ya America. “Zaka khumi zikudzazo kapena kuposapo tidzakhala ndi mavuto ambiri a achichepere otchova juga kuposa a ogwiritsira ntchito anamgoneka—makamaka anamgoneka osaloledwa,” anatero phungu wina wa za kumwerekera. Profesa Henry Lesieur anafufuza ana a sukulu pa sukulu ya magiredi 7 mpaka 9 ndi ya magiredi 10 mpaka 12. The Los Angeles Times inasimba kuti “zimene iye anapeza nzofanana kwambiri ndi zopezedwa pofufuza ana a sukulu apakoleji: Chiŵerengero cha achichepere ‘odwala’ juga kapena ‘omwerekera’ ndi juga—anthu amene sathanso kulamulira juga—chili pa 5% poyerekezera ndi achichepere onse m’dzikoli.”

Othandiza pa vuto la juga amavomereza kuti zimene zimawadetsa nkhaŵa si ziŵerengero za otchova juga achichepere koma “mzimu umene anawo, makolo ndipo ngakhale aphunzitsi amasonyeza pa juga ya achichepere. . . . Ana ambiri ndi makolo awo amaganiza kuti juga ndi ‘seŵero losavulaza,’ lokhala ndi zotulukapo zake zimene si zoipa kwenikweni poyerekeza ndi zija za ogwiritsira ntchito anamgoneka ndi akumwa moŵa kapena ochita chiwawa kapena uchiwerewere.” Koma phungu wa za khalidwe Durand Jacobs anachenjeza kuti juga imasonkhezera achichepere kuchita upandu, ukamberembere, ndi kukhala ndi chikhumbo chopeza ndalama mosavuta.

Mwachitsanzo, talingalirani za mwana wa sukulu wina pasukulu ya sekondale amene anayamba juga ali wamng’ono. Pamene anali kusukulu anawonongera maola ake ochuluka a m’kalasi pa kutchova juga ndi ana a sukulu ena. Atalephera nataya ndalama zake zonse, anali kuba pa ndalama zimene ana a sukulu anapereka kaamba ka chakudya cha mabanja osoŵa. Mwa kubetchera ndalama zakubazo, iye anaganiza kuti adzakhoza kugulanso wailesi yakanema ya banja lawo ndi mphete ya onyx imene anapereka pinyolo kuti alipire ngongole zoyambirira za juga. Pofika m’giredi lachisanu ndi chinayi, anali atakhalapo kale masiku 20 m’ndende ya ana opulupudza chifukwa cha kuba $1,500 ndipo anali woloŵerera mu dollar-ante poker ndi mu $5-a-rack pool. “Pamene ndinali kukula, ngongolezo zinali kuwonjezereka,” anatero. Posapita nthaŵi anayamba kubera achinansi kuti alipire ngongole zake za juga. Amayi wake anathedwa nzeru. Pofika usinkhu wa zaka 18 iye anakhala womwerekera ndi juga.

Ku England, akatswiri a khalidwe la anthu amati malamulo ofeŵa a juga amalola ana kuseŵera ndi makina a juga. Ana ambiri amachirikiza kumwerekera kwawo pamabwalo a ndege ndi m’malikole mwa kubera makolo awo ndi kuba m’masitolo.

“Pakati pa achichepere, mtundu wa juga yotchuka ndi yomakula mofulumira koposa pasukulu za magiredi 7 mpaka 9, za magiredi 10 mpaka 12 ndi pamakoleji ndiyo kubetchera maseŵero pakati pa [ana a sukulu] okha, nthaŵi zina ochirikizidwa ndi anthu olotera amene adzapambana kwawoko,” anatero Jacobs. “Ndiganiza kuti pali sukulu zoŵerengeka zokha za magiredi 10 mpaka 12 ndi makoleji amene alibe maseŵero obetchera zochuluka.” Ndiponso pali maseŵero a makadi, malotale, ndi makasino kumene achichepere ambiri amawalola kuloŵa chifukwa chakuti amaoneka achikulirepo.

“Mfundo ina yofunika kutchulidwa,” anatero Jacobs, “njakuti anthu ochuluka anafikira kukhala omwerekera ndi juga chifukwa chakuti pamene anayamba ali achichepere, anali kuwina.” “‘Unyinji waukulu’ wa achichepere, iye anatero, amene anawayambitsa kutchova juga ndi makolo awo kapena achibale amene anaiyesa seŵero chabe,” inapitiriza kutero The Los Angeles Times. Phungu winanso pa zinthu zomwerekeretsa anawonjezapo ndemanga yake kuti: “Makolo afunika kupenda nkhani yakale imodzimodzi imene analimbana nayo yokhudza moŵa ndi anamgoneka. Malinga ndi kuganiza kwanga, mukafutukula juga kwambiri, pamakhalanso omwerekera ndi juga atsopano ambiri.” Akatswiri amene amachiritsa omwerekera ndi juga amati monga momwe zimakhalira ndi anamgoneka ndi moŵa, ana ambirimbiri amachirikiza kumwerekera kwawo mwa kuba, kugulitsa anamgoneka, ndi kuchita uchiwerewere atakodwa ndi juga. Makolo angayese juga kukhala “seŵero chabe,” koma apolisi samatero.

“Ana amene anamwerekera ndi makina a juga . . . anali ndi mikhalidwe yoipa ya achikulire omwerekera ndi juga. Achichepere amene anamwerekera ndi makina a juga ameneŵa angakhale atayamba ali ndi zaka 9 kapena 10. Anawononga ndalama zawo zonse, ndalama za kusukulu za chakudya, ndi makobiri amene anatola m’nyumba. Patapita chaka chimodzi kapena ziŵiri, anyamatawo anayamba kuba zinthu. Anali kugulitsa kalikonse m’chipinda chawo, kuyambira ndondo zomenyera mpira, mabuku, ngakhale chuma chonga lekodi puleya: ana ena anali kupeza kuti awabera zoseŵeretsa zawo. Panalibe kanthu kosungika m’nyumba. Moody anauzidwa kuti amayi othedwa nzeru anaunjika katundu wawo m’chipinda chimodzi kuti asungike, mwina anali kubisa zikwama zawo m’mabulangete pokagona. Pokhala ozunguzika mutu, amayi otero sanamvetse zimene zinali kuchitikira ana awo mofanana ndi mbalame zimene cuckoo imabera mazira. Anawo anakhozabe kuba kwina kwake. Pofika zaka 16, apolisi anali kuwafunafuna.”—Easy Money: Inside the Gambler’s Mind, yolembedwa ndi David Spanier.

Monga momwe nkhanizi zasonyezera, achikulire ambiri ndi achichepere anayamba juga kupyolera m’matchalitchi awo—bingo, malotale, ndi zina zambiri. Kodi magulu achipembedzo ndi atsogoleri awo omwe amati ndi otsatira a Kristu ayenera kulimbikitsa, kuchirikiza, ndi kusonkhezera juga ya mtundu uliwonse? Kutalitali! Juga ya mtundu uliwonse imasonkhezera umodzi wa mikhalidwe yoipitsitsa ya munthu, chikhumbo cha kupeza phindu popanda kugwira ntchito, kapena, kunena molunjika, umbombo. Aja amene amaichirikiza amalimbikitsa anthu kukhulupirira kuti kuli bwino kupindulira pa kulephera kwa ena. Kodi Yesu angachirikize mchitidwe wotero umene umaswa mabanja, wonyazitsa, wopatsa matenda, ndi wowononga moyo wanu? Ayi! M’malo mwake, Mawu ouziridwa a Mulungu amafotokoza bwino kuti anthu aumbombo sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9, 10.

Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo akali aang’ono kuti juga ya mtundu uliwonse njoipa. Musaiyese seŵero chabe koma m’malo mwake chiyambi cha ulesi, bodza, kunama, ndi kusaona mtima. M’mizinda yambiri mwakhazikitsidwa maprogramu othandiza onga Gamblers Anonymous. Makamaka, ngati muli ndi vuto, funafunani uphungu wouziridwa wopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Ena amene anaganiza zodzipha amati ali ndi moyo chifukwa cha kutsatira uphungu wouziridwa umenewo.

Chosangalatsa nchakuti Mboni za Yehova zathandiza kumasula ambiri amene anakodwa mumsampha wa kumwerekera ndi juga. Wina yemwe kale anali womwerekera ndi juga analemba kuti atachita zonyansa zaka zambiri, kuphatikizapo kutchova juga kowopsa, “khalidwe mwamsanga linayamba kusintha kwambiri pamene ine ndi tsamwali wanga tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinali womwerekera kwambiri ndi juga, ndipo ndinali ndi vuto kuilamulira. Mwa thandizo la Yehova ndi la tsamwali wanga—limodzi ndi phunziro, pemphero, ndi kusinkhasinkha, makamaka mmene Mulungu amaonera umbombo—kumwerekera ndi jugako ndinakulamulira, ndipo ineyo ndi tsamwali wanga, amene wakhala mkazi wanga kwa zaka 38 tsopano, tinapatulira miyoyo yathu kwa Yehova. Ngakhale kuti tatumikira zaka zambiri kumene kuli kusoŵa kokulirapo ndi mu utumiki wanthaŵi yonse ndipo ndatumikira monga woimira Watchtower Society woyendayenda, kumwerekera kwangako kukalipo ndipo kumangolamuliridwa mwa thandizo ndi chitsogozo cha Yehova.”

Ngati juga ndi vuto lanu, kodi mungawonjoke ku kumwerekerako? Inde, ngati mupitiriza kulandira thandizo la Mulungu ndi kuligaŵira kwa ena amene angalifune.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Posachedwa padzakhala mavuto ochuluka a achichepere otchova juga kuposa a anamgoneka

[Mawu Otsindika patsamba 28]

Anthu aumbombo sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu

[Bokosi patsamba 26]

Makobiri Ajuga Awalandira ndi Manja Aŵiri m’Kachisi Wachikatolika ku Las Vegas

Alendo ku Shrine of the Most Holy Redeemer kaŵirikaŵiri amapempha wansembe kuti: “Bambo, kodi mungandipempherere kuti ndiwine?”

Anthu mamiliyoni amakacheza pachaka ku Las Vegas, Nevada, U.S.A., kuchokera padziko lonse, unyinji wa iwo akumafunitsitsa kulaŵa Mwaŵi. M’kachisi ameneyu wa Tchalitchi cha Roma Katolika wa magetsi ofiirira, amene kuchipupa kwake kuli mafano achitsulo osonyeza Kubadwa kwa Yesu, Mgonero wa Ambuye, ndi Kupachikidwa kwa Yesu, juga imachitikira m’mipando: Olambirawo amaika makobiri ajuga a m’kasino m’mbale za mitulo.

“Nthaŵi ndi nthaŵi timapeza khobiri lajuga la $500 mu imodzi ya mbalezo,” Bambo Leary wa m’kachisiyo anatero ndi matchulidwe amawu Achiairishi pang’ono.

Tchalitchi cha Roma Katolika kumtunda kwa Las Vegas Strip chinatumikira olambira ake zaka makumi ambiri, koma pamene mahotela a kasino anayi aakulu koposa padziko lonse—MGM Grand, Luxor, Excalibur, ndi Tropicana—anamangidwa kumunsi kwa Strip imeneyo, Shrine of the Most Holy Redeemer inamangidwa pafupi kwambiri kulumpha nyumba imodzi yosanja.

Pamene wansembe anafunsidwa chimene anachitira zimenezi, iye anati: “Tikanatani? Ndi kumene kuli anthu.”

Ndi kumenenso kuli ndalama. Choncho akanatani?

[Chithunzi patsamba 25]

Juga imayambitsa mayanjano oipa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena