Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 12/8 tsamba 30
  • Ngalande ya Pont du Gard Ikhalabe kwa Nthaŵi Yaitali

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngalande ya Pont du Gard Ikhalabe kwa Nthaŵi Yaitali
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Ngalande za Madzi za ku Roma Ankazimanga Mwaukadaulo
    Galamukani!—2014
  • Mlatho Umene Unali Kumangidwa Mobwerezabwereza
    Galamukani!—2008
  • Mlatho wa Tower Bridge ndi Njira Yolowera mu London
    Galamukani!—2006
  • Madzi Opatsa Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 12/8 tsamba 30

Ngalande ya Pont du Gard Ikhalabe kwa Nthaŵi Yaitali

“KWA nyengo yaitali pambuyo pa kutha kwa Ufumu Wachiroma, ngalande zake zamadzi zinatsalabe zikugwiritsiridwa ntchito ndipo zinkakhumbiridwa ndi kupereka chisonkhezero kwa omanga a m’nyengo zotsatira,” ikufotokoza tero The New Encyclopædia Britannica. Ngalande ya Pont du Gard inalinso tero. Mwinamwake ndiyo chizindikiro chotchuka kwambiri cha Roma m’Falansa.

Ngalande za Roma sizinangomangidwira kuthirira minda komanso kupereka madzi ku matauni. Matauni ameneŵa anali ndi mitchera ya madzi a onse, madziŵe a madzi otentha, madziŵe osambamo, ndi madziŵe osungiramo madzi; ndipo ina ya mizinda yaikulu inali ndi njira zotaira zonyansa za m’chimbudzi. Inde, matauni a m’Roma ndi maiko ake aang’ono anafunikira madzi—ndipo ambiridi.

Pautali wa mamita 49 pamwamba pa mtsinje wa Gard, pali chimango chonga ulalo chotchedwa Pont du Gard, chachitali koposa chomangidwa ndi Aroma chimene chimachirikiza mfuleni wokumba. Ngakhale kuti nchautali wa mamita 275, icho changokhala mbali yochepa ya ngalande yonse. Utali wonse wa malo opitamo madzi unali makilomita 49. Chinagwiritsiridwa ntchito kupereka madzi m’tauni ya m’Roma ya Nîmes. Mofanana ndi zimango zina za Roma za m’nyengo imodzimodziyo, ngalandeyo yakhalapobe kwa zaka mazana ambiri ndipo imasonyeza ukatswiri wa ntchito ya kumanga kwa Aroma ndi luso la ainjiniya awo. Miyala yaikulu ya njereza, ina yolemera matani asanu ndi imodzi, inadulidwa ndi kusemedwa bwinobwino ku malo ophwanyira miyala apafupi ku Vers. Modabwitsa, palibe msanganizo wa sementi umene unagwiritsiridwa ntchito kumangira miyalayo.

Kumanga makoma okhala ndi mipata osanjikana kunali kofunika kaamba ka zifukwa zingapo. Pamene chimangocho chinafika pautali wakutiwakuti, chinayenera kupeputsidwa m’kulemera kwake, ndipo ndicho chinali chifukwa choikira mipatayo m’makomawo. Koma ngalande ya Pont du Gard inafunikiranso kupanga ulalo pa mtsinje. Kuti ichirimike kukankha kwa madzi amphamvu, omangawo anamanga ulalowo mumpangidwe wokhota.

Ngakhale kuti onse oukhumbira sakudziŵa, mbali zina za ulalowo zinasinthidwa pambuyo pake. Mizati yake yochindikala inanyemedwako kulola magaleta okokedwa ndi akavalo kumadutsa, ndipo m’zaka za zana la 18, malo ake osanja achiŵiri anafutukulidwa. Zaka zana limodzi pambuyo pake, Wolamulira Napoleon III, wosungitsa mwambo ndi wofunitsa kutetezera malowo, anayamba ntchito yokonzanso ulalowo.

Anthu oposa mamiliyoni aŵiri amapita kukauwona chaka chirichonse. Chidwi chachikulu chimenechi chikupereka chiwopsezo cha kuwonongeka kwa ngalande ya Pont du Gard, ndipo maprojekiti osiyanasiyana akuchitidwa kutetezera malowo. Mosasamala kanthu za chimene chidzauchitikira mtsogolo, ulalowu umasonyeza kuti ntchito yochitidwa mwaluso ikhoza kukhalabe kwa nthaŵi yaitali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena