Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 12/8 tsamba 9-11
  • Pamene Kusweka Mtima Kudzatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Kusweka Mtima Kudzatha
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yamtendere
  • Mmene Nkhondo Zonse Zidzathera
  • Nkhondo Yothetsa Ndhondo
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhondo
    Galamukani!—2017
  • “Sitifunanso Mahiroshima Ena!”
    Galamukani!—1991
  • Dziko Lopanda Nkhondo Posachedwa
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 12/8 tsamba 9-11

Pamene Kusweka Mtima Kudzatha

ADELINE NAKO wachichepere, wotchulidwa kuchiyambi kwa mpambo uno, anakulitsa udani waukulu ndi dziko la makolo ake, Japani. Pamene ana ena anatcha nzika za Japani zokhala ku Hawaii kukhala “Japs,” iye ankayankha mwaukali kuti, “Ndife nzika za Amereka.” Iye analemba zikwangwani zonena kuti, “Chotsani Maulamuliro Aakulu Ogwirizana Amenewo” ndipo anali mtsogoleri wa ndawala yogula masitampa ogulitsidwa kuti apeze ndalama za nkhondo. Adeline anati: “Ndinanyadira kwambiri magulu ankhondo otchedwa 100 ndi 442 opangidwa ndi nisei, kapena mbadwo wachiŵiri wa nzika za Japani zokhala ku Amereka, zimene zinamenyera nkhondo Amereka molimba mtima.”

Komabe, pamene anakula, iye anayamba kudabwa kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji anthu amaphana? ’ Zonse zinawonekera kukhala zolakwa. ‘Abuda anamenya nkhondo. Akristu anamenya nkhondo. Onse ali onyenga,’ analingalira motero. Pamene anayamba kuphunzira Baibulo mothandizidwa ndi Mboni za Yehova, iye anatokosa Mboni yomwe inali kumphunzitsayo ndi funso lakuti, “Kodi inu Mboni za Yehova mumamenya nkhondo?”

Iye anauzidwa kuti sizimanyamula zida kukapha munthu aliyense. Panthaŵiyo nkhondo inali kuchitikabe ku Ulaya limodzinso ndi ku Asia. Adeline anaphunzira kuti Mboni za ku Jeremani zinali kutumizidwa kumisasa yachibalo ndipo za ku United States zinaponyedwa m’ndende chifukwa chosamenya nkhondo. Iye analingalira kuti, ‘Ichi chiyenera kukhala chipembedzo chowona.’

Ntchito Yamtendere

Pamene chidziŵitso chake cha Baibulo chinawonjezereka, iye anasonkhezeredwa kupatulira moyo wake kwa Yehova, Mulungu wa Baibulo. Kudzipereka kwake kwa “Mulungu wa mtendere” kunamsonkhezera kufutukula chikondi chake mwakutsatira mapazi a nzika za Japani zokhala ku Hawaii zisanu zimene zinadzipereka modzifunira kupita ku Japani mwamsanga pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya II. (Afilipi 4:9) Izo zinali zofunitsitsa kuthandiza anthu a m’dziko la makolo awo, omwe kale anali adani, mwakulalikira monga amishonale mbiri yabwino yotonthoza ya Ufumu kuchokera m’Baibulo.—Mateyu 24:14.

Mmodzi amene anadzipereka modzifunira kukathandiza m’dziko lokanthidwa ndi nkhondo la Japani, Shinichi Tohara, akukumbukira mmene anamverera za ntchito yake. “Ndinalingalira za kukhulupirika kwa anthu a ku Japani pamene anali kutumikira ambuye aumunthu ndi wolamulira,” iye anatero. “Ndinalingalira za oulutsa ndege za kamikaze, amene anapereka miyoyo yawo kwa wolamulira mwakuulutsira dala ndege zawo m’zombo zankhondo za adani. Ndinaganiza kuti, ngati nzika za Japani ziri zokhulupirika motero kwa anthu, kodi zikachitanji zitapeza Ambuye wowona, Yehova?”

Pokhala ndi malingaliro abwino amenewo, odzipereka modzifunira ameneŵa analoŵa m’Tokyo mu 1949, yomwe inasandutsidwa bwinja ndi kuukiridwa ndi ndege zoponya mabomba za B-29. Kodi iwo anapezanji m’misasa ya m’mabwinjawo? Anapeza anthu ofatsa omwe anali ogwira ntchito akhama. Ndithudi, munali anthu omwe anali ndi chidani ndi utundu. Komabe, ambiri anavomereza moyanja uthenga wamtendere wa Baibulo.

Mu 1953, Adeline anagwirizana ndi amishonale oyamba amenewo. Iye anathandiza mwamphamphu awo amene anali ndi njala ndi ludzu la uthenga wotonthoza wopezeka m’Baibulo. Anakumanadi ndi anthu otsutsa m’ntchito yake yolalikira. Iwo ankamuuza kuti: “Anthu inu munaponya mabomba a atomu pa Hiroshima ndi Nagasaki! ”

Iye ankayankha kuti, “Eya, mukudziŵa kuti ndine wochokera ku Hawaii. Ndipo anali Japani amene anayamba kuukira Pearl Harbor ndikupha anthu ambiri kumeneko. Koma zimenezo sizinandiletse kubwera kuno ku Japani kudzauza anthu mbiri yabwino imeneyi.” Kaŵirikaŵiri zimenezo zinawatontholetsa, ndipo ankalandira mabuku ofotokoza Baibulo.

Timayamikira maziko abwino okhazikitsidwa ndi amishonale oyambirira amenewo ochokera ku Hawaii ndi maiko ena, tsopano nzika za Japani zoposa 150,000 ziri mbali ya gulu la abale amene ‘saphunziranso nkhondo.’—Yesaya 2:4; 1 Petro 2:17.

Mmene Nkhondo Zonse Zidzathera

Ndithudi, kudziŵana ndi kukulitsa chikondi chopanda dyera kwa wina ndi mnzake kuli kofunika koposa ku mtendere wadziko. Komabe, zimenezo sizokwanira. Anthu amene anakonda mtendere ndipo anali ndi mabwenzi kutsidya linalo anasonkhezeredwanso kuloŵa m’nkhondo ya ku Pacific pansi pa chikakamizo cha zochititsa “zolungamitsidwa.” Mfuu zautundu zinagonjetsa zikhoterero zawo zachibadwa. Ngakhale kuti ena anakana kupita kunkhondo mosasamala kanthu kuti kuteroko kukachititsa kutumizidwa kumisasa yachibalo kapena kundende, zochita zawo, ngakhale kuti zinali zoyamikirika, zinalibe chiyambukiro m’kuthetsa mzimu wa nkhondo.

Pamene dziko lonse laloŵetsedwa m’nkhondo, oposa manja a anthu okha amakhala akutsogolera. Kaŵirikaŵiri onse oloŵetsedwamo amaumirira kuti analakalaka kuti akanapeŵa nkhondoyo. Komabe, chisonkhezero china champhamvu chimawafulumiza kuchita mosemphana ndi zokhumba zawo. Baibulo limazindikiritsa chisonkhezero champhamvu chimenechi kukhala “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (2 Akorinto 4:4, NW) Ndithudi, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi.—1 Yohane 5:19; onaninso Yohane 12:31; 14:30.

Komabe, Baibulo limalonjeza kuti “Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana.” (Aroma 16:20) Chiyambi cha kuphwanya kumeneku chinachitika kumwamba zaka 77 zapitazo. Tamverani malongosoledwe a zimene mtumwi Yohane anawona m’masomphenya osangalatsa zaka mazana 18 kukwaniritsidwa kwake kusanachitike mu 1914: ‘Munali nkhondo m’mwamba. . . . Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.’—Chibvumbulutso 12:7-9.

Chiyambire nthaŵi imeneyo Satana Mdyerekezi wabindikiritsidwa pafupi ndi dziko lapansi. Mwakuyendetsa andale zadziko ndi ankhondo monga zidole, iye wachititsa kuvutika kosaneneka m’nkhondo za zaka za zana lino. Komabe, kusakhazika mtima kwake kumangosonyeza kukhala kwake ndi mkwiyo waukulu, ‘podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’ (Chibvumbulutso 12:12) Kudzera m’manja amphamvu a ‘Kalonga wa Mtendere,’ Yesu Kristu, Mulungu adzalanda mphamvu Satana pambuyo pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse’ pa “Harmagedo.”—Yesaya 9:6; Chibvumbulutso 16:14, 16.

Mosiyana ndi nkhondo zonse zimene zamenyedwa ndi anthu, muyezo wa chiweruzo cholungama umene udzakhala m’nkhondo ya Mulungu ikudzayo uli wotsimikizirika. Uli muyezo wa Mlengi wa anthu, amene ali wofunitsitsa kuchitira anthu zabwino. Mosiyana ndi atsogoleri andale zadziko amene amakakamiza anthu awo kuloŵa m’nkhondo, Yehova, Mlengi wathu, adzauza anthu ake monga momwe anauzira mtundu wa Israyeli m’masiku a Yehosafati wa Yuda m’zaka za zana lakhumi B.C.E. kuti: ‘Si kwanu kuchita nkhondo kuno ayi; chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu.’—2 Mbiri 20:17.

Pamene chisonkhezero choipa cha Satana chidzachotsedwa, anthu a mitundu yonse adzasangalala ndi mtendere weniweni ndi chisungiko padziko lonse lapansi. Ndiyeno mikhalidwe yotsatirayi yonenedweratu ndi Yesaya idzakhala yeniyeni. “Tawonani, ndilenga miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukiridwa konse ndiponso sizidzabwera m’maganizo.”—Yesaya 65:17, The New English Bible.

Chotero, zimene zinachitika pa Pearl Harbor sizidzakumbukiridwa movutitsa maganizo, ndiponso minkhole ya kuphulitsa mabomba a atomu pa Hiroshima ndi Nagasaki sidzafuulanso kuti “Sitifunanso Mahiroshima Ena!” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mawu otsatirawa a ulosi wa Yesaya adzakhalanso owona kwa munthu aliyense padziko lapansi: ‘Iye [Mulungu] adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.’—Yesaya 2:4.

Kukwaniritsidwa kwa maulosi ameneŵa kukuwoneka kale pakati pa Mboni za Yehova, zomwe tsopano zimapanga gulu lalikulu la ubale wapadziko lonse lokwanira mamiliyoni ambiri. Ichi chimawonekera bwino lomwe pamisonkhano yamitundu yonse ya Mboni za Yehova yochitidwira m’mbali zosiyanasiyana za dziko. Nanunso mungakhale mbali ya umodzi ndi mtendere wamitundu yonse umenewo. Bwerani nimuphunzire mmene mungakhalire mmodzi wa anthu amene ‘asula [kale] malupanga awo kukhala zolimira ndi nthungo zawo kukhala anangwape,’ amene ‘samaphunziranso nkhondo,’ ndi amene amayembekezera paradaiso amene adzabwera padziko lapansi posachedwapa, kumene nkhondo sizidzachitikanso.—Salmo 46:8, 9.

[Chithunzi patsamba 9]

Jerry ndi Yoshi Toma, Shinichi ndi Masako Tohara, ndi Elsie Tanigawa anadzipereka modzifunira kukathandiza omwe kale anali adani awo

[Chithunzi patsamba 10]

Lerolino, gulu la abale amitundu yonse limalambira Mulungu muumodzi ndi mumtendere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena