Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 12/8 tsamba 12-13
  • Chifukwa Chake Krisimasi Siiri ya Akristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Krisimasi Siiri ya Akristu
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkuti Kwenikweni Kumene Krisimasi Inachokera?
  • Kodi Anatembenuza Akunja Kukhala Akristu?
  • Kodi Ndimotani Mmene Yesu Kristu Amaiwonera Krisimasi?
  • Krisimasi—kodi Nchifukwa Ninji Iri Yotchuka Kwambiri M’japani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chiyambi cha Krisimasi Yamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Miyambo ya Krisimasi—Kodi Ziyambi Zake Nzotani?
    Galamukani!—1989
  • Khirisimasi—N’chifukwa Chiyani Imachitikanso M’mayiko a Kummaŵa?
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 12/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Chifukwa Chake Krisimasi Siiri ya Akristu

‘KRISIMASI yaletsedwa! Aliyense amene adzapezedwa akuikondwerera kapena ngakhale kulova kuntchito pa Tsiku la Krisimasi adzapatsidwa chilango! ’

Zimenezi zikumveka zachilendo, koma zinakhaladi lamulo kumbuyoko m’zaka za zana la 17. Opatulika Achiprotestanti analetsa phwandolo m’Mangalande. Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kutsutsa Krisimasi kwamphamvu koteroko? Ndipo nchifukwa ninji pali mamiliyoni ambiri lerolino okhala ndi lingaliro lakuti Krisimasi siiri ya Akristu?

Kodi Nkuti Kwenikweni Kumene Krisimasi Inachokera?

Mwina mungadabwe kudziŵa kuti Krisimasi sinayambidwe ndi Yesu Kristu ndipo iye ngakhale ophunzira ake a m’zaka za zana loyamba sanaikondwerere. Kwenikweni, panalibe cholembedwa chirichonse cha Krisimasi kufikira zaka 300 pambuyo pa imfa ya Kristu.

Anthu ambiri okhalako panthaŵiyo analambira dzuŵa, popeza analingalira kuti anadalira kwambiri pa kuzungulira kwake kwa chaka ndi chaka. Madzoma aakulu olambira dzuŵa ankachitidwa mu Ulaya, Igupto, ndi Peresiya. Mfundo yaikulu m’maphwando ameneŵa inali kubweranso kwa kuunika. Popeza kuti likawonekera ngati latha mphamvu m’nyengo yachisanu, dzuŵalo linali kupemphedwa kubwera kuchokera ‘kukayendayenda kumalo akutali.’ Madzomawo anaphatikizapo kusekerera, madyerero, kuvina, kukongoletsa nyumba ndi nyali ndi zokometsera, ndi kupatsana mphatso. Kodi machitachita ameneŵa akumveka ofala?

Olambira dzuŵa anakhulupirira kuti nkhuni yosapsa ndi moto ya yule inali ndi mphamvu zamatsenga, kuti kuyatsa chimoto pabwalo kukapatsa mulungu-dzuŵa nyonga ndi kumpatsanso moyo, kuti kukongoletsa nyumba ndi zitsamba zobiriŵira kukaingitsa ziŵanda, kuti mtengo wa holly unayenera kulambiridwa monga chizindikiro cha kubweranso kwa dzuŵa, ndi kuti mphukira za mtengo wa mistletoe zikadzetsa mwaŵi zitavalidwa monga njirisi. Kodi ndiphwando liti limene zinthuzi zimachitidwa lerolino?

December unali kale mwezi wadzoma lalikulu m’Roma wachikunja kwa nthaŵi yaitali Krisimasi isanayambidwe kumeneko. Dzoma la Saturnalia lotha mlungu (lotamanda Saturn, mlungu wa ulimi) ndi la Dies Natalis Solis Invicti (Tsiku Lakubadwa kwa Dzuŵa Losalakidwa) anachitika panthaŵi imodzimodzi imeneyi. Ndiponso, December 25 inalingaliridwa kukhala tsiku lakubadwa kwa Mithras, mulungu wa kuunika Wachiperesiya.

Kodi Anatembenuza Akunja Kukhala Akristu?

Poyesa kutembenuza akunja ameneŵa, anayamba kusakaniza ziphunzitso Zachikristu ndi zachikunja motsutsana ndi malemba, choncho tchalitchi chinasankha deti la Krisimasi limene likakhala patsiku limodzimodzi la dzoma lofunika koposa lachikunja. Ndipo bwanji ponena za miyambo ya Krisimasi? Encyclopedia of Religion and Ethics imavomereza kuti miyambo yambiri ya Krisimasi “siri miyambo yeniyeni Yachikristu, koma yachikunja imene inatengedwa kapena kuloledwa ndi Tchalitchi.” Mwachiwonekere iwo analingalira kuti kungoiveka dzina Lachikristu miyambo imeneyi kukapangitsa awo oitsatira kukhala Akristu.

Komabe, mmalo motembenuza achikunja kukhala Achikristu, miyambo imeneyi inatembenuza Zachikristu kukhala zachikunja. Mkati mwa ma 1600, Opatulika Achiprotestantiwo anavutitsidwa maganizo kwambiri ndi mkhalidwe wachikunja wa Krisimasi kwakuti tchuthicho chinaletsedwa m’Mangalande ndi m’maiko ena olamuliridwa ndi Amereka. Zilango zinaperekedwa kwa amene anakondwerera Krisimasi kapena kungolova kuntchito pa Tsiku la Krisimasi. Ku New England (U.S.), Krisimasi sinaloledwe kufikira mu 1856.

Koma pali mfundo yofunika kwambiri ponena za Krisimasi kuposa mmene tchalitchi, akunja, kapena Opatulika Achiprotestantiwo anaiwonera kalelo. Chachikulu kwenikweni kwa Akristu nchakuti . . .

Kodi Ndimotani Mmene Yesu Kristu Amaiwonera Krisimasi?

Ngati anthu akuchitirani phwando lokulemekezani, kodi kuvomereza kwanu mkhalidwe wake sikukakhala kofunika kwambiri? Chotero, tiyenera kufunsa kuti: Kodi Baibulo limasonyeza mmene Yesu amaiwonera miyambo yachikunja?

Yesu anatsutsa atsogoleri achipembedzo amene analolera molakwa kulambira koyera kuti atembenuze anthu. Iye anati kwa atsogoleri oterowo: “Inu [mumayenda] panyanja ndi pamtunda kuti mutembenuze munthu mmodzi, komano mumamluluza moŵirikiza kumyeneretsa chiwonongeko kuposa inu eni.”—Mateyu 23:15, Phillips.

Kutembenuza anthu sikunayenera kuchitidwa mwakusakaniza ziphunzitso zachikunja ndi Zachikristu. Paulo, mtumwi wa Yesu, analembera Akristu okhala mu Korinto kuti: ‘Simungathe kumwera chikho cha [Yehova, NW] ndi chikho cha ziŵanda.’ (1 Akorinto 10:21) Ndipo m’kalata yake yotsatira kwa iwo, Paulo anawonjezera kuti: “Musagwirizane ndi osakhulupirira ndi kuyesa kugwirira nawo pamodzi. . . . Kodi pangakhale bwanji kugwirizana pakati pa Kristu ndi mdyerekezi?”—2 Akorinto 6:14, 15, Phillips.

Ngati mayi wosamala anawona mwana wake akutola siwiti pamchera wa zonyansa, iye akamutaitsa mwamsanga. Kungoganizira za mwana wake kuidya—ndipo ngakhale kungoigwira—kumamnyansa. Krisimasi, ngakhale kuti njokoma kwa ambiri, inatoledwa m’malo onyansa. Mawu a Yesu amagwirizana ndi a mneneri Yesaya, amene anachichiza olambira owona a m’nthaŵi yake kuti: ‘Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa.’—Yesaya 52:11.

Chifukwa chake, Akristu owona lerolino samakondwerera Krisimasi. Pamene kuli kwakuti kaimidwe kawo kangawoneke kachilendo kwa ena, iwo amawona miyambo monga momwe Yesu anachitira. Pamene anafunsidwa kuti: ‘Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? ’ iye anayankha kuti: ‘Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?’ Ndipo anawonjezera kuti: ‘Inu mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.’—Mateyu 15:2, 3, 6.

Akristu owona lerolino amasonyeza chigwirizano ndi Yesu mwakulondola ‘mapembedzedwe oyera ndi osadetsa,’ osaipitsidwa ndi miyambo yachikunja ya anthu.—Yakobo 1:27.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

‘Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?’—Mateyu 15:3

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena