Lingaliro la Baibulo
Masoka Kodi Ali Zilango Zochokera kwa Mulungu?
KU Philippines, dziko lokanthidwa mobwerezabwereza ndi masoka achilengedwe, anthu ambiri amafunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amayesa anthu ndi masoka otero?’ Mu 1991, pambuyo pa kuphulika kwa phiri kosakaza koposa m’zaka za zana lino, mutu wankhani m’nyuzipepala ina ya ku Philippines unafunsa kuti: “Kuphulikako: Kodi Nchilango Chochokera kwa Mulungu?”
Nelly Favis-Villafuerte, wolemba m’danga la nyuzipepala anasonyeza lingaliro lotero pamene analemba kuti: “Komabe kwa Akristu okhulupirira Baibulo—pali malongosoledwe amodzi okha akuti: Kuphulika kwa phiri la Pinatubo ndichilango cha Mulungu chotikumbutsanso kuti pali Mulungu, mfumu yaikulu, amene ali ndi mphamvu yolamulira zochita ndi mtsogolo mwa anthu ndi mitundu.” Polingalira chigomeko chimenechi, tingafunse kuti:
Kodi Mulungu Wamphamvuyonse Amaweruza Zitaganya Lerolino?
Chenicheni chakuti Mulungu anatero kalelo sichingakanike. Zitsanzo zolembedwa m’Malemba za Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa, kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora, ndipo kusakazidwa kaŵiri kwa Yerusalemu, mzinda wochita ndi dzina lake lalikulu, zimasonyeza kuti Mulungu Wamphamvuyonse angadzetse mwadala chiweruzo pa anthu amene mobwerezabwereza amalephera kutsatira miyezo yake.—Genesis 7:11, 17-24; 19:24, 25; 2 Mbiri 36:17-21; Mateyu 24:1, 2.
Koma bwanji ponena za lerolino? Chenicheni chakuti kukakhala nthaŵi yatsoka lapadziko lonse chinanenedweratu ndi Kristu Yesu mu Mateyu mutu 24, Marko mutu 13, ndi Luka mutu 21. M’mitu imeneyi, iye anapereka machenjezo aulosi a zochitika ndi mikhalidwe imene ikasonyeza chimaliziro cha dongosolo ili la zinthu kotero kuti anthu olingalira bwino akakhoza kuzindikira kuti iye anali kulamulira mosawoneka kumwamba. Maulosi ameneŵa akukwaniritsidwa lerolino. Ngakhale nditero, muyenera kudziŵa kuti m’ziweruzo zonse zotchulidwa pamwamba, Yehova Mulungu anapereka machenjezo omvekera bwino obwerezabwereza chiwonongeko chisanadze. (Amosi 3:7) Komabe, ponena za masoka achilengedwe ochitika m’nthaŵi yathu, machenjezo amaperekedwa ndi olamulira adziko, malinga ndi umboni wa sayansi.
Ndiponso, wophunzira Yakobo akutidziŵitsa m’mutu woyamba wa kalata yake, vesi 13 kuti: “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iye mwini sayesa munthu.” Pokhala ndi chiŵerengero cha anthu chomakulakulabe padziko lonse, anthu afikira pakukhala pafupi ndi malo othekera kuchitika ngozi. Kufunika kwa malo okhala ndi olima chakudya kumachititsa kusenga madera amene kale anali nkhalango, nthaŵi zina ngakhale kuwonjezera masoka ena achilengedwe ochititsidwa ndi kugwa kopambanitsa kwa mvula ndi chigumula.
Chotero, sikukakhala kolondola kunena kuti masoka achilengedwe amatumizidwa mwachindunji ndi Mulungu Wamphamvuyonse monga chilango pa anthu okhala m’madera okanthidwawo. Kwenikweni, timawona kuti anthu ambiri opanda liŵongo, monga ana aang’ono, ndiwo amavutika kwambiri m’nthaŵi ya tsoka. Komabe, ngakhale kuti Mulungu Wamphamvuyonse samadzetsa masoka oterowo, tingafunsebe kuti:
Kodi Pali Zimene Tingaphunzirepo?
Inde. Kwa okhala m’madera okanthidwa, pali chiyeso cha ukulu wa mtengo umene amaika pachuma chawo chakuthupi poyerekezera ndi moyo weniweniwo. Anthu adziika mosayenerera paupandu woika moyo pachiswe panthaŵi zotero kokha kuti apulumutseko katundu wawo wina. Tifunikira kukumbukira kuti Yesu anati: ‘Moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.’ (Luka 12:15) Zinthu zakuthupi zingapezedwenso, koma palibe munthu amene akhoza kubwezeretsa moyo wake.—Mateyu 6:19, 20, 25-34.
Masoka achilengedwe amachititsanso anthu kusinkhasinkha pa mmene amatsogozera moyo wawo. Mtumwi Paulo anafulumiza Akristu kukhala osamala m’mayendedwe awo kuti: “Chotero penyani mosamalitsa mmene muyendera, osati monga opusa koma monga anzeru, mukumagwiritsira ntchito bwino tsoka mmene mungathere, chifukwa masiku ngoipa.” (Aefeso 5:15, 16, Byington) Chiyeso chirichonse chimene munthu ayang’anizana nacho m’moyo wake chiri chikumbutso cha mmene kuliri kofunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.
Phunziro lachitatu limene titengapo pa masoka achilengedwe nlakuti timafunikira kukulitsa kukoma mtima kochuluka, kapena chifundo, pa ena. M’dera lokanthidwa ndi tsoka, chisamaliro chachikondi chiyenera kusonyezedwa kwa ovutika anzathu mmalo mokhala ndi lingaliro lakuti aliyense adzaziwonera. Kwenikweni zimenezi ziri choncho kwa oikiziridwa mathayo a kuyang’anira ena. Mneneri Yesaya anafotokoza amene anatcha “akalonga” kukhala ‘pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.’—Yesaya 32:1, 2.
Posonyeza chifundo m’nthaŵi yatsoka, pangakhale nthaŵi yogaŵana ndi ena zimene wina ali nazo, ponse paŵiri m’mawu ndi zochita. Mwachitsanzo, kuphulika kwa phiri la Pinatubo ndi masoka ake otsatira kunapereka mipata yosaŵerengeka yakukhala ndi phande m’kuthandiza amene anathaŵa tsokalo. Ambiri analibe ndalama zogulira ngakhale chakudya chawo chatsiku ndi tsiku. Chotero, anthu anali okhoza kusonyeza kupanda dyera kwawo mwakuthandiza ena. Komabe, ambiri amafunabe kudziŵa kuti:
Kodi Kudzakhala Chiweruzo Chomalizira cha Anthu?
Inde, chidzakhalako, monga momwe kwasonyezedwera bwino m’Mawu a Mulungu. (Mateyu 24:37-42; 2 Petro 3:5-7) Chiweruzocho chisanadze, ntchito yakuchenjeza yapadziko lonse iyenera kuchitidwa, monga momwe Yesu analoserera mowonjezera kuti: “Ndiponso, mbiri yabwino iyenera choyamba ilalikidwe m’mitundu yonse.”—Marko 13:10, NW.
Chotero, aliyense wa ife ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzachitanji?’ Tikukufulumizani kupeza nthaŵi yofufuza zimene Baibulo limalimbikitsa aliyense wa ife kuchita kotero kuti mukapulumuke tsoka lapadziko lonse limenelo.