Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 12/1 tsamba 4-10
  • Masoka Achilengedwe—Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masoka Achilengedwe—Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi “Tsoka Lachilengedwe” Nchiyani?
  • Kodi Ndani Amene Amazichititsa?
  • Kodi Mankhwala Ake Nchiyani?
  • Zochita za Mulungu Mtsogolomu
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Masoka Achilengedwe Achuluka Chonchi?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mulungu Amalanga Anthu Pogwiritsa Ntchito Masoka Achilengedwe?
    Galamukani!—2012
  • Pamene Kugwa Masoka Achilengedwe
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 12/1 tsamba 4-10

Masoka Achilengedwe​—Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?

“KALANGA ine, Mulungu wanga, mwatichitiranji?”

Amenewo anali mawu osimbidwa kukhala atanenedwa ndi munthu wopulumuka amene anakaona chiwonongeko cha kuphulika kwa phiri la chipale la Nevado del Ruiz mu Colombia pa November 13, 1985. Thope lake linakwirira mzinda wonse wa Armero ndi kupha anthu oposa 20,000 muusiku umodzi.

Nkomvekera bwino kuti wopulumuka anganene zimenezo. Pokhala opanda thandizo pakuwopsa kwa mphamvu zochititsa mantha zachilengedwe, kuyambira m’nthaŵi zakale anthu anagwirizanitsa zochitika zotero ndi Mulungu. Anthu osatsungula anapereka nsembe, ngakhale za anthu, kuti atonthoze milungu yawo ya kunyanja, ya kuthambo, ya padziko lapansi, ya phiri, ya kuphulika kwa mapiri, ndi magwero ena a ngozi. Ngakhale lerolino, anthu ena amangovomereza zochitika za masoka achilengedwe kukhala choikidwiratu kapena chinthu chochitidwa ndi Mulungu.

Kodi Mulungu ndiyedi amachititsa masoka amene amadzetsa mavuto ochuluka kwa anthu ndi kutayikiridwa ndi zinthu padziko lonse? Kodi iye ayenera kuimbidwa mlandu? Kuti tipeze mayankho ake, tifunikira kuyang’anitsitsa pazinthu zimene zimaloŵetsedwa m’masoka otero. Kwenikweni, tifunikira kupendanso maumboni ozoloŵereka.

Kodi “Tsoka Lachilengedwe” Nchiyani?

Pamene chivomezi chinakantha Tangshan, mu China, ndipo malinga nkunena kwa malipoti a boma la China chinapha anthu 242,000, ndipo pamene mkuntho wa Hurricane Andrew unasakaza mu South Florida ndi Louisiana mu United States ndi kuwonongetsa katundu wa madola mamiliyoni zikwi zambiri, masoka achilengedwe otero anali nkhani zazikulu za padziko lonse. Komabe, bwanji ngati chivomezicho chikanakantha kumalo osakhalidwa ndi anthu a Gobi Desert, makilomita 1,100 kumpoto koma chakumadzulo kwa Tangshan, kapena bwanji ngati mkuntho wa Hurricane Andrew ukanadzera mbali ina nuchitikira panyanja, ndi kusafika kumtunda? Izo sizikanakumbukiridwa tsopano.

Pamenepo, mwachionekere, pamene tinena za masoka achilengedwe, sitikungonena za zochitika zazikulu za mphamvu zachilengedwe. Chaka chilichonse pamakhala zikwi zambiri za zivomezi, zazikulu ndi zazing’ono, ndiponso anamondwe ambiri, akavumvulu, mikuntho, kuphulika kwa mapiri, ndi zochitika zina zowopsa kwambiri zimene zimangolembedwa m’mabuku. Komabe, pamene zochitika zoterozo ziwononga kwambiri miyoyo ndi katundu ndi kudodometsa njira ya moyo yozolowereka, zimakhala masoka.

Tiyenera kudziŵa kuti sinthaŵi zonse pamene chiwonongeko ndi kutayikiridwa kumene chimakuchititsa zimakhala zolingana mu ukulu wake ndi mphamvu zachilengedwe zochitikazo. Sikuti tsoka lalikulu koposa nthaŵi zonse limachititsidwa ndi mphamvu zachilengedwe zazikulu koposa. Mwachitsanzo, mu 1971 chivomezi chofikira 6.6 pasikelo ya Richter chinakantha San Fernando, ku California, United States, ndi kupha anthu 65. Chaka chimodzi pambuyo pake chivomezi chofikira 6.2 pasikelo ku Managua, Nicaragua, chinapha anthu 5,000!

Motero, pamene tinena za kuwonjezereka kwa kuwononga kwa masoka achilengedwe, tiyenera kufunsa kuti, Kodi mphamvu za chilengedwe zawonjezereka m’kusakaza kwake? Kapena kodi anthu awonjezera vutolo?

Kodi Ndani Amene Amazichititsa?

Baibulo limadziŵikitsa Yehova Mulungu monga Mlengi Wamkulu wa zinthu zonse, kuphatikizapo mphamvu zachilengedwe za dziko lapansili. (Genesis 1:1; Nehemiya 9:6; Ahebri 3:4; Chivumbulutso 4:11) Zimenezi sizimatanthauza kuti iye amachititsa kayendedwe kalikonse ka mphepo kapena kuvumba kulikonse kwa mvula. Mmalo mwake, iye anayambitsa kugwira ntchito kwa malamulo amene amalamulira dziko lapansi ndi malo ake. Mwachitsanzo, pa Mlaliki 1:5-7, timaŵerenga za kayendedwe ka zinthu zitatu zofunika zimene zimatheketsa moyo kukhalapo padziko lapansi​—kutuluka ndi kuloŵa kwadzuŵa kwa tsiku ndi tsiku, kusasintha kwa mayendedwe a mphepo, ndi kayendedwe ka madzi. Kaya anthu amadziŵa zimenezi kapena ayi, kwa zaka zikwi zambiri madongosolo achilengedwe ameneŵa, ndi ena ofanana nawo, ophatikizapo mkhalidwe wakunja, malo, ndi zolengedwa za padziko lapansi akhala akugwira ntchito. Kwenikweni, wolemba Mlaliki anali kusonyeza kusiyana kwakukulu kumene kulipo pakati pa njira zosasinthika ndi zosatha za chilengedwe ndi mkhalidwe wosintha ndi wakanthaŵi wa moyo wa munthu.

Yehova sali kokha Mlengi wa mphamvu zachilengedwe komanso iye ali ndi mphamvu ya kuzilamulira. M’Baibulo lonse timapezamo zochitika za kulamulira kwa Yehova kapena kugwiritsira ntchito mphamvu zotero kuti akwaniritse chifuno chake. Zimenezi zimaphatikizapo kugaŵanitsa madzi a Nyanja Yofiira m’tsiku la Mose ndi kuimitsa dzuŵa ndi mwezi m’njira zawo kuthambo m’nthaŵi ya Yoswa. (Eksodo 14:21-28; Yoswa 10:12, 13) Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu ndi Mesiya wolonjezedwayo, nayenso anasonyeza mphamvu yake pamphamvu zachilengedwe, mwachitsanzo, pamene analetsa namondwe pa Nyanja ya Galileya. (Marko 4:37-39) Zochitika zonga zimenezi zimatsimikiziritsa kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, angalamuliredi mokwanira zinthu zonse zimene zimayambukira moyo padziko lapansi pano.​—2 Mbiri 20:6; Yeremiya 32:17; Mateyu 19:26.

Popeza izi zili choncho, kodi tiyenera kuimba mlandu Mulungu wa kuwonjezereka kwa kusokonezeka kwa zinthu ndi chiwonongeko zimene zachititsidwa ndi masoka achilengedwe munthaŵi yaposachedwapa? Kuti tiyankhe funso limeneli, choyamba tiyenera kupenda kuti tione ngati pali umboni wakuti kuwopsa kwa mphamvu zachilengedwe kwawonjezereka posachedwapa mwamphamvu, mwinamwake ngakhale kusalamulirika.

Ponena za nkhaniyi, onani zimene buku lakuti Natural Disasters​—Acts of God or Acts of Man? likunena: “Palibe umboni wakuti mchitidwe wa mkhalidwe wakunja wogwirizanitsidwa ndi zilala, kusefukira kwa madzi ndi akavumvulu ukusintha. Ndipo palibe katswiri wodziŵa za malo amene akunena kuti kayendedwe ka dziko lapansi mogwirizana ndi zivomezi, kuphulika kwa mapiri ndi tsunami (kugwedeza kwa chivomezi) zikukhala zowopsa kwambiri.” Mofananamo, buku lotchedwa Earthshock likunena kuti: “Matanthwe a dziko lililonse amasonyeza zochitika za malo zazikulu ndi zazing’ono zosaŵerengeka, chochitika chilichonsecho chikanakhala tsoka lalikulu kumtundu wa anthu ngati chikanachitika lerolino​—ndipo nkotsimikizirika mwausayansi kuti zochitika zotero zidzachitika mobwerezabwereza mtsogolo.” M’mawu ena, dziko lapansi ndi mphamvu zake zazikulu sizinasinthe kwa nyengo zonse. Chifukwa chake, ngakhale kaya zopendedwa zina zikusonyeza chiwonjezeko cha mitundu ya zochitika za malo kapena zochitika zina, sikuti dziko lapansi lakhala losakaza mosalamulirika m’nthaŵi zaposachedwapa.

Pamenepo, kodi nchiyani chimene chimachititsa kuwonjezereka kwa kukantha kobwerezabwereza ndi kuwononga kwa masoka achilengedwe amene timaŵerenga? Ngati mphamvu zachilengedwe zilibe mlandu, mlanduwo ukuwonekera kukhala ukumaikidwa pa anthu. Ndipo, ndithudi maboma azindikira kuti zochita za anthu zachititsa malo athu okhala kukhala okanthidwa mosavuta ndi masoka achilengedwe ndi osatetezereka. M’maiko osatukuka, kusoŵa chakudya komawonjezereka kumaumiriza alimi kulima munda wawo mopambanitsa kapena kukulitsa munda mwa kulambula mitengo yofunika kwambiri ya malo a thengolo. Zimenezi zimachititsa kukokoloka kwa nthaka kwakukulu. Kuchuluka kwa anthu nakonso kumafulumizitsa kukula kwa zithando zomangidwa mochititsa ngozi m’madera osatetezereka. Ngakhale m’maiko otukuka kwambiri, anthu, onga mamiliyoni ambiri amene amakhala m’mbali mwa San Andreas Fault ku California, adziika paupandu mosasamala kanthu za machenjezo operekedwa momvekera bwino. M’mikhalidwe yotero, pamene zochitika zamwadzidzidzi​—namondwe, kusefukira kwa madzi, kapena chivomezi​—zichitika, kodi kuwonongeka kwa zinthuko kungatchedwedi “kwachilengedwe”?

Chitsanzo chabwino ndicho cha chilala cha ku Sahel wa Afrika. Kaŵirikaŵiri timaganiza kuti chilala chimachititsidwa ndi kusoŵa kwa mvula kapena madzi, kukumachititsa njala, ndi imfa. Koma kodi njala yaikulu m’chigawo chimenechi njochititsidwa ndi kusoŵa kwa madzi kokha? Buku lakuti Nature on the Rampage limati: “Umboni wosonkhanitsidwa ndi asayansi ndi nthumwi zopereka chithandizo ukusonyeza kuti njala ya masiku ano ikupitirizabe osati kwenikweni chifukwa cha chilala chotenga nthaŵi yaitali koma chifukwa cha kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa minda ndi madzi. . . . Kukula kwa chipululu cha Sahel komapitirizabe kwakukulukulu nkochititsidwa ndi anthu.” Nyuzipepala ya ku South Africa, yotchewa The Natal Witness, ikunena kuti: “Njala simakhalapo chifukwa cha kusoŵa chakudya; imakhalapo chifukwa cha kusoŵa njira yopezera chakudya. Mwa mawu ena, imakhalapo chifukwa cha umphaŵi.”

Zofananazo zinganenedwe ponena za kuwonongeka kwa zinthu kochititsidwa ndi masoka ena. Zofufuzidwa zasonyeza kuti maiko osauka kwambiri amakanthidwa kwambiri ndi imfa zochititsidwa ndi masoka achilengedwe koposa maiko amene ali okhupukirapo a dzikoli. Mwachitsanzo, kuyambira 1960 kufika mu 1981, malinga nkufufuza kwina, Japan anakanthidwa ndi zivomezi 43 ndi masoka ena ndipo anthu 2,700 anafa, akumakhala ndi avareji ya imfa 63 patsoka lililonse. M’nyengo imodzimodziyo, Peru anakanthidwa ndi masoka 31, ndipo anthu 91,000 anafa, kapena 2,900 patsoka lililonse. Kodi nchifukwa ninji pali kusiyana? Mphamvu zachilengedwe zingakhale zitachititsa tsokalo, komatu ali machitachita a anthu​—achitaganya, achuma, andale zadziko​—amene anachititsa kusiyana kwakukuluko kwa kutayikiridwa ndi miyoyo ndi kuwonongeka kwa katundu kumene kunachitika.

Kodi Mankhwala Ake Nchiyani?

Asayansi ndi akatswiri ena ayesayesa kwa zaka zambiri kulinganiza njira zolimbanirana ndi masoka achilengedwe. Iwo amapenda mwakuya pansi pa dziko lapansi akumafunafuna kudziŵa mmene zivomezi ndi kuphulika kwa mapiri kumachitikira. Mwa kugwiritsira ntchito masetilaiti a m’mlengalenga amapenda njira za kayendedwe ka mphepo kuti adziŵe njira za akavumvulu aakulu ndi mikuntho kapena kudziŵiratu za kusefukira kwa madzi ndi chilala. Kufufuza konseku kwawapatsa chidziŵitso chimene akuyembekezera kuti chidzawakhozetsa kuchepetsa kusakaza kwa mphamvu zachilengedwe zimenezi.

Kodi zoyesayesa zimenezo zathandiza? Ponena za mtundu wa zoyesayesa umenewu wa maluso apamwamba ndi wokwera mtengo kwambiri, gulu lina loyang’anira malo adziko likunena kuti: “Zimenezi zili nkufunika kwake. Koma ngati zimadya ndalama zambiri kwambiri ndi kuyesayesa​—ngati zigwiritsiridwa ntchito monga chodzikhululukira chonyalanyazira maupandu amene amachititsidwa m’zitaganya za mikholeyo kumene kumachititsa masokawo kukhala oipa kwambiri​—pamenepo zikhoza kuchititsa ngozi kwambiri kuposa kuchitira anthu zabwino.” Mwachitsanzo, pamene kuli kwakuti nkothandiza kudziŵa kuti malo a m’gombe la Bangladesh nthaŵi zonse amakhala pangozi ya kusefukira kwa madzi ndi mafunde, kudziŵa zimenezo sikumaletsa anthu mamiliyoni ambiri a ku Bangladesh kukakamizika kukhala komweko. Chotulukapo chake ndicho masoka obwerezabwereza ndi anthu zikwi mazana ambiri akumafa.

Mwachionekere, chidziŵitso cha luso lazopangapanga chingakhale chothandiza pamlingo wochepa chabe. Chinthu china chimene chikufunika ndicho luso la kuchepetsa zitsenderezo zimene zimasiya anthu alibe chochita chenicheni koma kungokhala m’madera omwewo amene ali pangozi kapena kukhala ndi moyo m’njira zimene zimawononga malo okhala. Mwa mawu ena, kuti achepetse kuwononga kochitidwa ndi anthu kukafunikira kusintha njira za kakhalidwe ka anthu, zachuma, ndi za ndale zadziko zimene tilimo. Kodi ndani amene angakwaniritse ntchito yotero? Ali Uyo yekha amene angakhoze kulamulira ngakhale mphamvu zimene zimachititsa masoka achilengedwe.

Zochita za Mulungu Mtsogolomu

Yehova Mulungu sadzangothetsa zizindikiro zake chabe koma adzafikira muzu weniweniwo wa mavuto a anthu. Adzachotsa madongosolo aumbombo ndi otsendereza andale zadziko, amalonda, ndi achipembedzo amene ‘apweteka anzawo powalamulira.’ (Mlaliki 8:9) Aliyense amene ali wozoloŵerana ndi Baibulo sadzalephera kuona kuti m’masamba ake onse muli maulosi ambiri osonyeza nthaŵi imene Mulungu adzachitapo kanthu kuchotsa zoipa ndi mavuto padziko lapansi ndi kubwezeretsa paradaiso wamtendere ndi chilungamo wa padziko lapansi.​—Salmo 37:9-11, 29; Yesaya 13:9; 65:17, 20-25; Yeremiya 25:31-33; 2 Petro 3:7; Chivumbulutso 11:18.

Ndithudi, zimenezo ndizo zimene Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake onse kupempherera, kuti, “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu Waumesiya udzachotsa ndi kuloŵa mmalo ulamuliro wopanda ungwiro wa anthu, monga momwe mneneri Danieli ananeneratu kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44.

Kodi nchiyani chimene Ufumu wa Mulungu udzachita chimene sichingachitidwe ndi mitundu ya anthu lerolino? Baibulo limasonyezeratu zinthu zokondweretsa zimene zizadza. Mmalo mwa mikhalidwe yosonyezedwa pamasamba ameneŵa, yonga ngati njala ndi umphaŵi, “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri,” ndipo “mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.” (Salmo 72:16; Ezekieli 34:27) Ponena za malo achilengedwe, Baibulo limatiuza kuti: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. . . . Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se. Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi.” (Yesaya 35:1, 6, 7) Ndipo sipadzakhalanso nkhondo.​—Salmo 46:9.

Mmene Yehova Mulungu adzachitira zonsezo, ndi mmene adzachitira ndi mphamvu zonse zachilengedwe kotero kuti sizidzawononganso, Baibulo silimanena. Komabe, chinthu chotsimikizira nchakuti, onse amene adzakhala m’boma lolungama limenelo “sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.”​—Yesaya 65:23.

M’masamba a magazini ano, ndiponso m’zofalitsidwa zina za Watch Tower Society, Mboni za Yehova zasonyeza mobwerezabwereza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’chaka cha 1914. Pansi pa chitsogozo cha Ufumu umenewo, umboni wa padziko lonse wakhala ukuperekedwa kwa pafupifupi zaka 80, ndipo lerolino tili pakhomo pa “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” zolonjezedwazo. Anthu adzamasulidwa osati kokha kukukanthidwa ndi masoka achilengedwe komanso zoŵaŵa zonse ndi mavuto amene akhala akukantha mtundu wa anthu kwazaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapitazo. Ponena za nthaŵiyo kunganenedwedi kuti, “zoyambazo zapita.”​—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:4.

Komabe, bwanji nanga ponena za tsopano lino? Kodi Mulungu wakhala akuchitapo kanthu kuthandiza awo ovutitsidwa ndi mikhalidwe yachilengedwe kapena mikhalidwe ina? Ndithudi iye watero komatu osati mwanjira imene anthu ochuluka angayembekezere.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Zochita za anthu zachititsa malo athu okhala kukhala okanthidwa mosavuta ndi masoka achilengedwe

[Mawu a Chithunzi]

Laif/​Sipa Press

Chamussy/​Sipa Press

Wesley Bocxe/​Sipa Press

Jose Nicolas/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena