Kodi Ndani Amawaphunzitsa Nkhani za Kugonana?
HA, NCHISANGALALO chotani nanga chimene mwana amabweretsa atabadwa! Makolo amakondwa naye kwadzawoneni, kuseŵera naye, ndi kuuzako mabwenzi awo pafupifupi kalikonse kamene mwanayo amachita. Koma posapita nthaŵi iwo amayamba kuzindikira kuti mwanayo amabweretsanso mathayo aakulu atsopano. Limodzi la iwo nkukhala kufunika kwa kumphunzitsa kudzisungira bwino m’dzikoli lamakhalidwe oipaipirabe.
Kodi ndimotani mmene makolo angathandizire mwana wamng’ono wokondedwa kukula ndi kukhala munthu wamkulu amene adzakhala ndi moyo wabanja wachimwemwe ndipo mwinamwake kulera ana akeake owopa Mulungu? Makolo ena angawone zimenezi kukhala thayo losatheka kwenikweni, chotero tikhulupirira kuti malingaliro operekedwa munomu adzayamikiridwa.
Mwinamwake mumaphunzitsa ana anu mwanjira imene makolo anu anakuphunzitsirani. Koma makolo ambiri anaphunzitsidwa zochepa ponena za kugonana, ngati kuti anaphunzitsidwa nkomwe. Ngakhale ngati munaphunzitsidwa bwino, dziko lasintha, momwenso zosoŵa za ana. Ndiponso, oŵerenga ambiri a magazini ano afikira pakukhala ndi miyezo yapamwamba yakakhalidwe ndi njira yamoyo yabwinopo. Chifukwa chake, muyenera kudzifunsa nokha kuti: ‘Kodi njira imene ndimaphunzitsira ana anga imagwirizana ndi malingaliro anga atsopano ndi zosoŵa zomakulakulabe za ana anga?’
Makolo ena amalola ana awo kudzidziŵira okha zimenezo. Koma kuteroko kumabutsa mafunso owopsa awa: Kodi iwo adzaphunziranji? Liti? Kwa yani, ndipo m’mikhalidwe yotani?
Zimene Sukulu Zimaphunzitsa
Makolo ambiri amanena kuti: “Aaa, munena izo, adzaziphunzira kusukulu!” Nzowona, sukulu zambiri zimaphunzitsa ponena zakugonana, koma ndisukulu zochepa zimene zimaphunzitsa ponena za makhalidwe abwino. Yemwe kale anali mlembi mu Unduna wa Zamaphunziro ku United States William J. Bennett ananena mu 1987 kuti sukulu zimasonyeza “kusafuna dala kusiyanitsa makhalidwe.”
Tom, atate wa asungwana aŵiri okondedwa, anafunsa mmodzi wa aphunzitsi awo kuti: “Bwanji simungonena kuti kugonana kunja kwaukwati nkulakwa? ” Mphunzitsiyo anati akadakonda kunena zimenezo koma sukulu sifuna kukwiitsa amayi osakwatiwa a anawo ndi zitsamwali zimene amakhala nazo m’nyumba. Chotero, ana asukulu amauzidwa kuti ziri kwa iwo kudzisankhira koma samauzidwa kwenikweni chosankha chimne chiri cholondola.
‘Ndidzagula Bukhu’
Makolo ena anganene kuti: “Ndidzawagulira bukhu.” Mwinamwake bukhu labwino lingathandize, koma muyenera kukhala wosamala kutsimikizira kuti mumavomereza zimene limanena. Ndimabuku oŵerengeka ankhani zimenezi amene aphunzitsa makhalidwe ngakhale kutchula cholondola ndi cholakwa. Ena amafikiradi pakuwavomereza machitachita oipa. Ndipo ndibukhu lapaderadi limene limanena kuti kugonana kuyenera kukhalapo kokha muukwati.
Chifukwa chake, thayo lakuphunzitsa ana makhalidwe limabwerera kumene Mulungu analiyika poyamba—kwa makolo awo owakonda. Baibulo limauza atate kuti: ‘Mudziwaphunzitsa [malamulo a Mulungu] mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi powuka inu.’—Deuteronomo 6:7.
Kwenikweni, makolo akhoza kukhala aphunzitsi abwino koposa kwa ana awo. Palibe bukhu kapena sukulu imene ingapose mphamvu ya chikhulupiriro chawo kapena ya chitsanzo chabwino choperekedwa ndi banja. Monga momwe William Bennett ananenera kuti: “Kupenda kumasonyeza kuti pamene makolo akhala magwero aakulu a maphunziro azakugonana, sikwenikweni kuti ana adzadziloŵetsa m’machitachita akugonana. . . . Makolo, kuposa wina aliyense, amachita mbali yaikulu.”
Komabe, makolo ena amawopa kuti ana atadziŵa zimenezi angafune kukayesa. Mwachiwonekere, ichi kwenikweni chimadalira pazimene zikuphunzitsidwa ndi mmene akuziphunzitsira. Chenicheni nchakuti, zivute zitani, tsiku lina achicheperewo adzafikira pakudziŵa zakugonana. Chotero, sikwabwino nanga kuti azidziŵe mwanjira yolondola ndi yolemekezeka kuchokera kwa makolo amakhalidwe abwino ndi owakonda mmalo mwakuphunzitsidwa ndi winawake m’khwalala kapena kusukulu kapena achikulire achisembwere?
Koma funso liripobe: Kodi ndimotani mmene mungaphunzitsire zinthu zimenezi m’njira yaumulungu ndi yolemekezeka? Pamene achichepere amamva kuti “aliyense amachita,” kodi mungawapangitse motani kukhulupirira kuti anthu abwino ndi achimwemwe koposa samatero? Kodi mungawathandize motani kuzindikira kuti kutsatira malamulo a Baibulo ‘akupewa dama’ sikumangotsogolera ku moyo wabwino koposa komanso ndiko njira yokha imene imamkondweretsa Mulungu? Nkhani zotsatira zidzapereka mayankho othandiza a mafunso ofunika kwambiri ameneŵa.—1 Atesalonika 4:3.
[Mawu Otsindika patsamba 3]
“Makhalidwe abwino amene makolo amaphunzitsa ana awo ndiwo ofunika koposa.”—U.S.News & World Report