Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 4/8 tsamba 10-11
  • Kuipa Kodi Ndani Ali ndi Thayo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuipa Kodi Ndani Ali ndi Thayo?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Saali ndi Thayo
  • Wochititsa Weniweni Avumbulidwa
  • Kodi Mulungu Adzathetsa Kuipa?
  • Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
    Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
  • Ncifukwa Ninji Mulungu Wakulola Kuipa Kupitirizabe Mpaka Lero?
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kuipa
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 4/8 tsamba 10-11

Lingaliro la Baibulo

Kuipa Kodi Ndani Ali ndi Thayo?

PAMENE anangoloŵa m’nyumba mwake, mkaziyo anazindikira kuti simunali bwino. Kungomwaza maso m’nyumbamo kunakhutiritsa chikaikiro chake chachikulucho—wailesi yakanema, sitiriyo, zovala zina, ndi zinthu zina munalibemo. Ndiyeno, lingaliro lowopsa linabwera m’maganizo mwake, ‘Bwanji ngati mbalazo zikali m’nyumba muno?’ Mkaziyo anabwerera nathaŵira kunyumba ya mnansi wake wapafupi kuti akaitane apolisi. Inde, anali mkole wina wa upandu.

Ngati inuyo simunayang’anizanepo ndi upandu, mwachiwonekere mumadziŵa munthu wina amene anatero. Umachitidwa kaŵirikaŵiri padziko lonse ndi anthu osafuna kuuchita. Malinga ndi kufufuza kwa Komiti ya UN Yochinjiriza ndi Kuletsa Upandu, kuchuluka kwa upandu wochitidwa lipoti kukuwonjezereka kwambiri kuposa chuma cha dziko ndi chiŵerengero cha anthu.

Kulikonse anthu owona mtima amawopa upandu, kupha kwachiŵembu, chisalungamo, ndi kuipa komwe kukukantha dziko lonse ndipo agwidwa ndi mantha a chiwawa chamwadzidzidzi. Choncho ambiri amafunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji Mulungu sathetsa zimenezi?’

Limenelo ndifunso labwino, ndipo Baibulo limayankha. Komabe, kuti tilimvetse yankholo, nkofunika kuzindikira magwero, wochititsa weniweni, wa kuipako.

Mulungu Saali ndi Thayo

‘Kodi chiripo chosalungama ndi Mulungu?’ anafunsa tero Paulo, wolemba Baibulo. ‘Msatero ayi,’ anayankha motero. (Aroma 9:14) Koma ena angaganize kuti popeza kuti Mulungu ali wamphamvuyonse, pamenepo ali ndi thayo la zonse zimene zikuchitika. Koma siziri choncho ayi. Talingalirani: Wopanga mapulani a nyumba alinganiza nyumba yokongola yokhoza kukhalidwamo. Kamangidwe kake kali kamtengo wapatali, ndipo milimo yogwiritsiridwa ntchito njabwino koposa. Komabe, okhalamo aiwononga naigwiritsira ntchito moipa nyumbayo. Posapita nthaŵi ifunikira kukonzanso kwakukulu. Ndithudi mukuvomereza kuti okhalamowo, osati wolinganiza kapena womanga, ndiwo ali ndi thayo la mkhalidwe woipa wa nyumbayo! Zilinso choncho ndi anthu ndi dziko lapansi lerolino. Monga momwe Deuteronomo 32:4, 5 amalongosolera, ntchito za Yehova nzangwiro. ‘Njira zake zonse ndichiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo.’ Pamenepa, kodi ndani ali ndi thayo la mavuto otero padziko lapansi lerolino?

Lembalo limapitiriza kuti: ‘Anamchitira zovunda . . . chilema nchawo.’ Indedi, unyinji wa mavuto omwe ali m’dziko lerolino uli chotulukapo chachindunji cha chifooko kapena, kusasamala kwa anthu. Komabe, pali magwero ena aakulu ndi ochititsa kuipaku.

Wochititsa Weniweni Avumbulidwa

Pa Chivumbulutso 12:9, timaŵerenga kuti Satana Mdyerekezi, “wonyenga wa dziko lonse,” aponyedwa pansi pafupi ndi dziko lapansi. Kodi pakhala chotulukapo chotani? Vesi 12 la mutu umodzimodziwo lipitiriza kuti: ‘Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’ Chotero ali yemweyo, Mdani wamkuluyo, yemwe amayambitsa chisalungamo chomwe chadzaza dziko lapansi. Kunena zowona, pali anthu amene amagwirizana ndi zoyesayesa zake; koma iye ndamene walongosoledwa kukhala ‘wambanda kuyambira pachiyambi.’ (Yohane 8:44) Malemba amatisonyeza kuti Satana Mdyerekezi ali wochititsa wamkulu wa mavuto a anthu. Saali chabe wochititsa koma wapitirizabe kusonkhezera kuipa, kuwonjezera zoyesayesa zake ‘m’masiku ano otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-5, 13) Chotero Yehova Mulungu saali wochititsa kuipa. Koma kodi amasamala kwambiri kotero kuti afuna kuthetsa kuvutika kwa anthu?

Kodi Mulungu Adzathetsa Kuipa?

Inde, amasamala, ndipo adzathetsa kuipa ndi kuvutika. Iye ndi Mulungu wachikondi, ndipo pokhala Atate wachikondi, amadziŵa ndipo akufuna kukhutiritsa zosoŵa ndi zikhumbo za ana ake. (Salmo 145:16; 1 Yohane 4:8-10) Chenicheni chakuti Mulungu sanaterobe sichizindikiro chakuti ali wamphwayi. Mmalomwake, kudziletsa kwake ndi kuleza mtima kuli umboni wa ukulu wake ndi mphamvu. Iye adziŵa nthaŵi yabwino koposa yothetsera dongosolo loipa ili la zinthu, ndipo panthaŵi yeniyeni yoyenera, adzatero.

Mkhalidwewo ungayerekezeredwe ndi nakubala yemwe ali ndi pathupi. Pamene kuli kwakuti amakhala wolakalaka kubadwa kwa khandalo, amadziŵa kuti palibe chifukwa chokhalira wodera nkhaŵa mopambanitsa. Amazindikira kuti kumatenga nthaŵi yaitali kuti khandalo likule m’mimbamo. Mosakaikira, adzakhala ndi nkhaŵa zina ndi kusakhazikika m’nthaŵiyo, koma kubadwa kwa khanda lokhwima, lathanzi, ndi lamiyezi yokwanira kumapangitsa nkhaŵa zonse ndi kuyembekezerako kukhala zophula kanthu.

Ndimo mmene ziliri ndi dziko latsopano la mtendere laulemerero lofotokozedwa m’Baibulo. Lidzafika mwamsanga Ufumu wa Mulungu utaloŵerera m’zochita za anthu, kuchotsa dziko losalungama liripoli. Pamenepo, kuipa konse kudzakhala mbiri yakale. Kuvutika, ululu, nthenda, ndi imfa—zonsezo zidzapita. (Chivumbulutso 21:3, 4) Amene ali ndi thayo lodzetsa kuvutika nawonso adzachotsedwa. Satana ndi ziŵanda zake, limodzi ndi anthu amene akhala ziŵalo za dongosolo la zinthu, adzawonongedwa.—Malaki 4:1; Chivumbulutso 20:1-4.

Anthu onga mkazi yemwe watchulidwa poyamba nkhaniyi sadzafunikiranso kuchita mantha kubwera kunyumba ali okha. Monga momwe mkaziyo ndi mwamuna wake ananenera: “Nyumba yathu itathyoledwa, tinaika belu la alamu. Papita zaka zambiri tsopano kuchokera pamene tinaberedwa, choncho sikumatidetsanso nkhaŵa kwambiri. Koma tidziŵa kuti tidzasangalala ndi mtendere weniweni ndi chisungiko mtsogolo m’dongosolo la Ufumu wa Mulungu.”

Kufikira tsiku lomadza mofulumiralo litafika, tifunikira kugwiritsira ntchito mwanzeru nthaŵi yomwe tiri nayo tsopano. Petro akutiuza kuyesa ‘kulekerera kwa Ambuye . . . chipulumutso [chathu, NW].’ (2 Petro 3:15) Ndiponso chipulumutso cha ena, pakuti pamene tiuzako anthu za chiyembekezo chodabwitsa chimenechi, ‘tidzadzipulumutsa ife eni ndi iwo akutimva.’ (1 Timoteo 4:16) Tsopano ndiyo nthaŵi yakukalimira kukulitsa mikhalidwe imene idzatipanga kukhala mtundu wa anthu amene adzakhala ndi moyo m’dziko latsopano, m’mene kuipa kudzakhala mbiri yakale. (Salmo 37:9-11) Tifunikira kulifufuza Baibulo kuti tipeze osati kokha mayankho a mafunso athu komanso chitsogozo chomwe timafunikira chogwirizanitsira miyoyo yathu ndi chifuniro cha Mulungu.

[Chithunzi patsamba 10]

Chifaniziro cha Lusifa chojambulidwa ndi Doré mu Divine Comedy ya Dante

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena