Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 183-tsamba 187
  • Kuipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuipa
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Wina Anena Kuti—
  • Ncifukwa Ninji Mulungu Wakulola Kuipa Kupitirizabe Mpaka Lero?
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Masiku a Kulambira Satana Aŵerengedwa
    Galamukani!—1994
  • Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
    Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 183-tsamba 187

Kuipa

Tanthauzo: Choipa kwambiri mwa makhalidwe. Kaŵirikaŵiri chimatanthauza chinthu chovulaza, chakupha, kapena cha chisonkhezero chowononga.

Kodi nchifukwa ninji pali kuipa kochuluka?

Mulungu sangaimbidwe mlandu. Iye anapatsa anthu chiyambi changwiro, koma anthu asankha kunyalanyaza malamulo a Mulungu ndi kudzisankhira chabwino ndi choipa. (Deut. 32:4, 5; Mlal. 7:29; Gen. 3:5, 6) Mwa kuchita izi, adziloŵetsa m’chisonkhezero cha makamu oipa auzimu.—Aef. 6:11, 12.

1 Yoh. 5:19: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”

Chiv. 12:7-12, NW: “Nkhondo inaulika m’mwamba . . . chinjoka ndi angelo ake chinachita nkhondo koma sichinalakika, ngakhale malo sanapezeka konse kaamba ka iwo mmwamba. Chotero chinjoka chachikulucho chinaponyedwa pansi, chinjoka choyambacho, chotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheza dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu; iye anaponyedwa pansi kudziko lapansi ndipo angelo ake anaponyedwa pansi limodzi naye. . . . ‘Kaamba ka chifukwa chimenechi kondwerani, miyamba inu, ndi inu amene mukhalamo! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa chakuti Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala ndi mkwiyo waukulu, podziŵa kuti ali ndi nyengo yaifupi yanthaŵi.’” (Tsoka lowonjezereka iri kudziko lawonekera chiyambire kuponyedwa kwa Satana kuchokera kumwamba pambuyo pa kubadwa kwa Ufumu. Wonani vesi 10.)

2 Tim. 3:1-5: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuŵabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu osati okonda Mulungu; akukhala nawo mawonekedwe achipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” (Izi ndizo zotulukapo za kupatuka pakulambira kowona mkati mwa zaka mazana ambiri. Mikhalidwe imeneyi yabuka chifukwa chakuti anthu amene adzinenera kukhala opembedza anyalanyaza chimene Mawu a Mulungu amanenadi. Iwo atsimikizira kukhala onyenga kumphamvu ya zabwino zimene kudzipatulira kwaumulungu kowona kungakhale nako pamoyo wa munthu.)

Kodi nchifukwa ninji Mulungu amakulola?

Nthaŵi zina kwa ife kungawonekere kuti chinthu chabwino koposa chikanakhala kungochotsa munthu aliyense amene ali woipa. Timalakalaka kutha kwa kuipa, ndipo komabe tavutika ndi kuipa kwazaka zochepa pang’ono poyerekezera ndi nthaŵi imene iko kwakhalako. Kodi ndimotani mmene Yehova ayenera kukhala akulingalirira? Kwazaka zikwi zambiri anthu amuimba mlandu, ngakhale kumtukwana, kaamba ka mikhalidwe yoipa imene avutika nayo. Komabe, imeneyi siimachititsidwa ndi iye, koma ndi Satana ndiponso ndi anthu oipa. Yehova ali ndi mphamvu ya kuwononga oipa. Ndithudi payenera kukhala zifukwa zabwino zimene iye wakulolera motere. Ngati njira ya Mulungu ya kusamalirira mkhalidwewu iri yosiyana ndi imene ife tikanavomereza, kodi zingatidabwitse? Chidziŵitso chake chiri chachikulu kwambiri koposa cha anthu, ndipo lingaliro lake la mkhalidwewo nlotakata kwambiri koposa la munthu wina aliyense.—Yerekezerani ndi Yesaya 55:8, 9; Ezekieli 33:17.

Sipakanakhala kuipa ngati Mulungu sakanapatsa zolengedwa zaluntha ufulu wa kudzisankhira. Koma Mulungu watipatsa mphamvu ya kusankha kumumvera chifukwa chakuti tikumkonda kapena kusamumvera. (Deut. 30:19, 20; Yoswa 24:15) Kodi tikanakonda zikanakhalira mwina? Ngati ife tiri makolo, kodi nziti zimene zimatipangitsa kukhala achimwemwe kwambiri—pamene ana athu atimvera chifukwa chakuti atikonda kapena pamene tiwapangitsa kuti atero? Kodi Mulungu akanafunikira kukhala atakakamiza Adamu kumvera? Kodi tikanakhaladi achimwemwe kwambiri ngati tikanakhala ndi moyo m’dziko limene tinakakamizidwa kumvera Mulungu? Asanawononge dongosolo loipali, Mulungu anapereka mwaŵi kwa anthu kuti iwo asonyeze kuti anafunadi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo ake olungama kapena ayi. Panthaŵi yake yokwanira, mosakakikira iye adzawononga oipa.—2 Ates. 1:9, 10.

Mwanzeru iye waloleza nthaŵi ya kuthetsa nkhani zofunika: (1) Kulungama ndi kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova kunakaikiridwa mu Edene. (Gen. 2:16, 17; 3:1-5) (2) Umphumphu wa atumiki onse a Mulungu kumwamba ndi padziko lapansi unakaikiridwa. (Yobu. 1:6-11; 2:1-5; Luka 22:31) Mulungu akanatha kuwononga opandukawo (Satana, Adamu, ndi Hava) nthaŵi yomweyo, koma kumeneko sikukanathetsa nkhanizo. Mphamvu sizimatsimikizira kuti njira ya munthuyo njolungama. Nkhani zimene zinadzutsidwa zinali zamakhalidwe abwino. Kuloleza nthaŵi kwa Mulungu, sikunali kudzatsimikizira mfundo iriyonse kwa iyemwini, koma kulola zolengedwa zonse zokhala ndi ufulu wodzisankhira kudziwonera zotulukapo zoipa zochititsidwa ndi kupandukira ulamuliro wake, ndiponso kuwapatsa mwaŵi wa kusonyeza pamene iwo eni aima pankhani zofunika zimenezi. Nkhanizi zitakhazikitsidwa, palibenso munthu aliyense amene kachiŵirinso akanaloledwa kudodometsa mtendere. Dongosolo labwino, chigwirizano, ndi ubwino wachilengedwe chonse zimadalira pa kulemekezedwa kwa dzina la Yehova, kuchitiridwa kwake mwaulemu wochokera pansi pamtima woperekedwa ndi zolengedwa zonse zaluntha. (Wonaninso tsamba 354, 355, pamutu wakuti “Satana Mdyerekezi.”)

Fanizo: Ngati munthu wina anakuimbani mlandu pamaso pachitaganya chonse kuti mumagwiritsira ntchito molakwa malo anu antchito monga mutu wa banja, kuti ana anu akachita bwino kwambiri ngati anapanga zosankha zawo mosadalira pa inu, ndi kuti iwo onse anakumverani, osati chifukwa cha chikondi, koma chifukwa chamapindu a zinthu zakuthupi zimene munagaŵira, kodi ndiiti imene ikanakhala njira yabwino yothetsera nkhaniyo? Kodi kuwombera mfuti woneneza wonamayo kukanathetsa zinenezo zimenezo m’maganizo mwa onse a m’chitaganya? Mmalo mwake, ndiyankho labwino kwambiri chotani nanga ngati munapereka mwaŵi kwa ana anu wa kukhala mboni zanu kusonyeza kuti inu muli mutu wa banja wolungama ndi wachikondi ndi kuti iwo akukhala nanu chifukwa cha kukukondani! Ngati ena a ana anu anakhulupirira mdaniyo, nachoka panyumba, naipitsa miyoyo yawo mwa kugwiritsira ntchito njira zawo za moyo, kukachititsa kokha openyerera owona mtima kuzindikira kuti anawo akanakhala bwino kwambiri ngati akanalabadira malangizo anu.

Kodi ife mwa njira iriyonse tapindula mwa chilolezo cha Mulungu cha kuipa kufikira lerolino?

2 Pet. 3:9: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke koma kuti onse afike ku kulapa.” (Chifukwa chakuti kuleza mtima kwake kwafika mpaka kutsiku lathu, tiri ndi mwaŵi wa kusonyeza kuti tikulapa ndi kuti, mmalo mwa kupanga zosankha zathu ponena za chabwino ndi choipa, tifuna kugonjera ku ulamuliro wolungama wa Yehova.)

Aroma 9:14-24: “Ndipo tsono tidzatani? Kodi chiripo chosalungama ndi Mulungu? Musatero ayi. . . . Ngati Mulungu, pofuna iye kuwonetsa mkwiyo wake, ndi kudziŵitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera zamkwiyo zokonzekera chiwonongeko [ndiko kuti, analekerera kukhalako kwa anthu oipa kwa kanthaŵi] ndi kuti iye akadziŵitse ulemerero wake waukulu pazotengera za chifundo, zimene iye anazikonzeratu ku ulemerero [ndiko kuti akagwiritsira ntchito nthaŵiyo kusonyeza chifundo kwa anthu ena, mogwirizana ndi chifuno chake], ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu.” (Motero Mulungu akuchedwetsa chiwonongeko cha oipa kotero kuti alole nthaŵi ya kusankha anthu amene akawalemekeza ndi Kristu monga ziŵalo za Ufumu wakumwamba. Kodi kuchita kwa Mulungu motero kwakhala chisalungumo kwa aliyense? ayi; iri mbali ya kakonzedwe ka Yehova kodalitsira anthu amitundu yonse amene adzapatsidwa mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wa padziko lapansi. Yerekezerani ndi Salmo 37:10, 11.)

Ngati Wina Anena Kuti—

‘Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola kuipa kotere?’

Mungayankhe kuti: ‘Funso lanu nlabwino. Atumiki ambiri okhulupirika a Mulungu avutika maganizo ndi kuipa kowazungulira. (Hab. 1:3, 13)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Sichiri chifukwa chakuti Mulungu ali ndi mphwayi iriyonse. Iye akutitsimikizira kuti wakhazikitsa nthaŵi pamene adzaimba mlandu oipawo. (Hab. 2:3)’ (2) Koma kodi nchiyani chimene chiri chofunika kwa ife ngati titi tikhale pakati pa opulumuka pamene nthaŵiyo idza? (Hab. 2:4b; Zef. 2:3)’

Kapena munganene kuti: ‘Ndakondwera kuti mwafunsa funsoli. Liri limodzi limene limavutitsa maganizo anthu owona mtima ochuluka. Panopa ndiri ndi chidziŵitso chothandiza kwambiri chimene chikuyankha funso lanu. (Ndiyeno ŵerengani naye china cha chidziŵitso patsamba 184-187.)’

‘Pambuyo pa zaka zonsezi, sindimakhulupirira kuti Mulungu adzachita chirichonse kusintha zinthu’

Mungayankhe kuti: ‘Ndakondwera kumva kuti mumakhulupirira mwa Mulungu. Ndithudi nzowona kuti pali kuipa kochuluka, ndipo kunayamba kalekale nthaŵi yathu isanafike. Koma kodi mwalingalira izi . . . ? (Gwiritsirani ntchito mfundo za m’mdime 2 patsamba 184, ponena za utali wanthaŵi imene Mulungu wakulola.)’

Kapena munganene kuti: ‘Ndithudi mudzavomerezana nane pamene ndinena kuti aliyense amene ali ndi mphamvu ya kumanga nyumba alinso woyeneretsedwa kuisesa. . . . Popeza Mulungu analenga dziko lapansi, siikanakhala nkhani yovuta kwa iye kulisesa. Kodi nchifukwa ninji iye wayembekezera nthaŵi yaitali motero? Ndinapeza yankho iri kukhala lokhutiritsa kwambiri. Tandiuzani zimene mukuganiza. (Pamenepo ŵerengani naye mfundo za patsamba 184-187.)’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena