Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 9-12
  • Masiku a Kulambira Satana Aŵerengedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masiku a Kulambira Satana Aŵerengedwa
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Masiku a Dziko Lapansi Laparadaiso Adzakhala Osaŵerengeka!
  • Kodi Zakometsetsa Kwakuti Sizingakhale Zoona?
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Angelo Ena Anaukira Mulungu
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Khalani ndi Moyo Kosatha Padziko Lapansi Laparadaiso
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 9-12

Masiku a Kulambira Satana Aŵerengedwa

YEHOVA MULUNGU analenga Adamu ndi Hava, nawaika m’munda wa paradaiso ndi kuwauza kuti achuluke ndi kudzaza dziko lapansi ndi ana olungama. Iwo anafunikira kusamalira mundawo, kuulima ndi kuuyang’anira, ndi kukhala ndi moyo kosatha, zonsezo zikumadalira pa maziko osavuta amodzi okha: ‘Suyenera kudya mtengo wokhala pakati pa mundawo. Ukadzadya umenewo, udzafa.’​—⁠Genesis 1:​27, 28; 2:​8, 9, 15-17; Yesaya 45:⁠18.

Mngelo wamphamvu anapandukira Mulungu nakhala Satana, kutanthauza “Wotsutsa,” chifukwa iye anafuna kulanda ulamuliro. Iye anafuna kuti kulambira kwa fuko la anthu kukhale kwake. Anasonkhezera Hava kudya chipatso choletsedwa, akumanena kuti chinali chakudya chabwino ndi kuti iye sakafa koma akafanana ndi Mulungu, wokhoza kudzisankhira chabwino ndi choipa. Chosankha chake choyamba chinali choipa; iye anasankha kuti kudya chipatso choletsedwa kukakhala kwabwino. Hava anadya, anapatsa mbali ina ya chipatsocho kwa Adamu nadya, ndipo potsirizira pake onse aŵiri anafa. Motero Adamu anadzetsa uchimo ndi imfa kwa mbadwa zawo, zomwe zakhala zikumafa chiyambire panthaŵiyo. (Genesis 3:​1-6; Aroma 5:12) Anthu aŵiri oyambirirawo anasankha kulondola Satana nakhala otembenuzidwira ku kulambira Satana oyamba. Kufikira lerolino, mamiliyoni asankha kuti chipembedzo cha makolo oyambirira amenewo chinali ndipo chili chabwino kwa iwo. “Kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye.”​—⁠Aroma 6:16; Yohane 17:​15, 16; 1 Yohane 5:⁠19.

Yehova anaweruzira Satana ku chiwonongeko chotheratu, koma anamlola kupitiriza kwa kanthaŵi. Zimenezi zikapatsa Satana mpata wa kutsimikizira chinenezo chimene anapereka, chakuti Mulungu sakakhoza kuika anthu padziko lapansi omwe akakhalabe okhulupirika kwa Iye pansi pa chiyeso​—⁠chinenezo chimene chinasonyezedwa mwamphamvu ndi kuyankhidwa mochirikiza mbali ya Yehova pankhaniyo m’machaputala aŵiri oyambirira a buku la Baibulo la Yobu. Pansi pa ziukiro zankhalwe ndi zosautsa zochokera kwa Satana, Yobu mwiniyo anasankha kusunga umphumphu kwa Mulungu, mwakutero akumatsimikizira Satana kukhala wabodza. (Genesis 3:15; Eksodo 9:16; Yobu 42:7) Ahebri chaputala 11 alinso ndi ndandanda yaitali ya Mboni zomwe zinaima kumbali ya Yehova pankhani ya uchifumu wa chilengedwe chonse.

Kristu Yesu ndiye wapadera koposa amene kwa nthaŵi yonse anapereka yankho lokwanira lochirikiza mbali ya Yehova pankhani ya uchifumu wa chilengedwe chonse ndi umphumphu wa anthu kwa Mulungu. Chimenechi chinali chigonjetso chomgwetseratu Satana. Yesu anakana kwa mtu wagalu chogaŵira cha Satana cha kumpatsa ulamuliro wa dziko lonse mosinthana ndi mchitidwe umodzi wa kulambira Satana. Yesu anapiriranso mosabwevuka nsautso yowopsa pamene anafera pa mtengo wozunzirapo. Iye anagonjetsa Satana ndi dziko la Satana lomwe, akumatipatsa chitsanzo changwiro chochitsatira.​—⁠Mateyu 4:​8-10; 27:50; Yohane 16:33; Ahebri 5:​7-10; 1 Petro 2:⁠21.

Poona nthaŵi zatsoka zimene tikukhalamo, kungaoneke kuti Satana akukhala wamphamvu kuposa ndi kale lonse ndi kuti kulambira Satana kwenikweniko kukuwonjezereka. Komabe, buku la Baibulo la Chivumbulutso limapereka chithunzi chosiyana kotheratu pa chaputala 12, mavesi 7-9, 12:

“Ndipo munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli [Kristu Yesu] ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi. Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthaŵi.”

Masiku a Dziko Lapansi Laparadaiso Adzakhala Osaŵerengeka!

“Podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi,” Satana akuwonjezera ntchito zake zauchiŵanda mu “masiku otsiriza” ano. (Yakobo 5:​1-3) Komabe pali chiyembekezo m’chizimezime cha masiku athu. Chivumbulutso 21:​1, 3-5 chimavumbula chimene icho chili: “Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo ndinamva mawu aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”

Motero, Kristu Yesu adzalamulira kwa zaka chikwi, m’nthaŵi imene Yehova adzachita chifuniro chake choyambirira polenga dziko lapansi ndi kuikapo mtundu wa anthu. (Chivumbulutso 20:​1, 2, 6) Mudzakumbukira kuti mtundu wa anthu poyambirira unafunikira kudzaza dziko lapansi ndi ana olungama, kusamalira dziko lapansi, kusamalira zomera ndi zinyama, kukhala pamtendere, ndi kukondana wina ndi mnzake. Kukwaniritsidwa kwa chifuno chimenecho kunaimitsidwa kulola Satana kuyesa kutsimikizira chinenezo chake chakuti akakhoza kupambutsa anthu onse kuchoka kwa Yehova Mulungu. Iye waika muukapolo anthu mamiliyoni zikwi zambiri, koma walephera kwa mamiliyoni ena a osunga umphumphu.​—⁠Aroma 6:⁠16.

Mkati mwa nthaŵi ya kubwezeretsa, chifundo cha Yehova kupyolera mwa Kristu Yesu chidzafika ndi kumanda komwe kupereka mwaŵi wa moyo wosatha m’dziko lapansi laparadaiso kwa mamiliyoni zikwi zambiri omwe anafa mkati mwa zaka zikwi zapitazo: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”​—⁠Yohane 5:​28, 29.

Aliyense amene panthaŵi imeneyo adzakana kugwirizana ndi mkhalidwe wolungama wa dziko latsopano limenelo sadzaloledwa kukhalapobe ndi kuliipitsa kapena kuliwononga, kuwononga zomera zake ndi zinyama zake, kuwononga mtendere wa mtundu wa anthu, kapena kulambira koona kwa Yehova Mulungu. Salmo 37:​10, 11, 29 limatsimikizira kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”

Mika 4:​2-4 amalonjeza mtendere weniweni ndi chisungiko kuti: “Amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mawu a Yehova. Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”

Mkhalidwe wamtendere umenewu udzafalikira ndi kuphatikizaponso zinyama, monga momwe Hoseya 2:18 akunenera kuti: “Ndipo tsiku lomwelo [ine Yehova] ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m’dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.” Ezekieli 34:25 akulankhulanso za pangano limene limasonyeza kusakhalapo kwa “zilombo zoipa.”

Ndiponso, Yesaya 11:​6-9 amalonjeza mtendere pakati pa zinyama mu Paradaiso kuti: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalungwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzaseŵera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”

Ofatsa adzalandira dziko lapansi. Iwo adzasamalira mpweya, madzi, ndi nthaka. Akasupe ndi mifuleni ya madzi zidzanyoŵetsa nthaka youma. Nkhalango zidzaveka mapiri omwe avulidwa kaamba ka phindu ladyera. Mitengo idzafalikira ndipo zipululu zakale zidzaphuka monga duŵa. Akhungu adzaona, ogontha adzamva, olemala adzayenda, osalankhula adzalankhula. (Yesaya 35:​1-7) Chiyamikiro kaamba ka mapiri aulemerero a Yehova ndi zigwa ndi magombe ake a nyanja zamchere zoŵinduka ndi nyanja zanchere zazikulu sichidzalola dyera laumunthu kubukanso ndi kuwononga dziko lapansi. Kudzakhala kosavuta ndi kwachibadwa, kwa mtundu wa anthu angwiro, odzala ndi zipatso za mzimu wa Yehova, kusangalala, aliyense payekha, ndi kukonda mnansi wake monga iye mwini, ndipo koposa zonse kukonda Yehova ndi mtima wonse, moyo, maganizo ndi nyonga zake zonse. Inde, mtundu wonse wa anthu udzakhala ndi zipatso zauzimu za “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”​—⁠Agalatiya 5:​22, 23.

Kodi Zakometsetsa Kwakuti Sizingakhale Zoona?

Pofika pano oŵerenga ena angakhale akunena kuti, ‘Zonsezo zikumveka kukhala zokometsetsa kwakuti sizingakhale zoona.’ Koma, iyayi, mikhalidwe imene ilipo tsopano njoipititsa kwakuti siingapitirizebe. Tili m’nthaŵi imene Baibulo limaitcha “masiku otsiriza.” Unguzani, ndipo mutha kuona kuti zilidi motero. “Masiku otsiriza,” amatero Mawu a Mulungu, “zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma, olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule. Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”​—⁠2 Timoteo 3:​1-5, 13.

Ngakhale ndi chithunzi choonekera bwino lomwe chimenechi cha nthaŵi zathu, ambiri adzanyodolabe. Zimenezonso ziyenera kuyembekezeredwa. Kunyodola mwa iko kokha kuli mbali ya umboni wakuti tili m’masiku otsiriza: “Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe. . . . Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza. . . . Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.”​—⁠2 Petro 3:​3, 4, 7, 13.

Yehova walonjeza kuti, m’dziko lake latsopano la chilungamo, dongosolo lakale loipali la dziko la Satana silidzakumbukika nkomwe: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.” (Yesaya 65:​17, 18) Masiku a kulambira Satana aŵerengedwa, ndipo panthaŵi yake ya Mulungu, Satana mwiniyo adzawonongedwa kunthaŵi yonse.​—⁠Chivumbulutso 20:​1-3, 7-10.

Ndithudi, mikhalidwe yodalitsika yomwe idzadza padziko lapansi la Paradaiso siili yokoma kuposa pa kukhala yoona; Yehova akuona mikhalidwe yomwe ilipo ya dongosolo ili lolamuliridwa ndi Satana kukhala yoipitsitsa kwakuti siingapitirizebe.

[Chithunzi patsamba 10]

Mikhalidwe yodalitsika ikudzayo m’dziko lapansi la Paradaiso siili yokoma kuposa pa kukhala yoona

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena