Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 5/8 tsamba 31
  • Ufulu Wachipembedzo ku Bulgaria

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufulu Wachipembedzo ku Bulgaria
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yapadera ku Bulgaria Inali ndi Zotsatira Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Ndinkafunitsitsa Kudzagwira Ntchito Yoyenda M’madera Osiyanasiyana
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Msonkhano Wamitundu Yonse wa Mboni za Yehova Woyamba mu Russia
    Galamukani!—1993
  • Madalitso Olemerera pa Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 5/8 tsamba 31

Ufulu Wachipembedzo ku Bulgaria

Mabasi asanu ndi imodzi ochokera ku Bulgaria, onyamula nthumwi 300 zopita ku Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu” anafika pamalo a msonkhanowo kunja kwa Thessalonica, Girisi, Lachinayi usiku, pa July 11, 1991. Chifukwa cha nkhondo yachiweniweni m’Yugoslavia wapafupiyo ndi chipwirikiti chomwe inachititsa m’deralo, nthumwi zimenezi sizinakhoze kupeza zilolezo zawo kufikira mphindi yomalizira yeniyeni.

Lachitatu masana ogwira ntchito pa ofesi ya kazembe mu Sofia, Bulgaria, anagwira ntchito kwa maola owonjezereka kuti akonze zilolezozo. Chotero, mabasiwo anakhoza kunyamula nthumwizo m’mbali zosiyanasiyana za Bulgaria panthaŵi yake kupita nawo kumalo a msonkhanowo usiku wotsatizana ndi tsiku limene msonkhanowo umayamba pa Lachisanu, July 12.

Panthaŵiyo, Mboni za Yehova zinali zoletsedwa mu Bulgaria, choncho zinali zosangalatsa chotani nanga kwa iwo kukhala ndi mayanjano Achikristu momasuka m’dziko loyandikana nalo la Girisi! Holo ina pa malo a msonkhanopo, yokhala ndi pulatifomu yokongoletsedwa bwino (yomwe ikuwonekera pachithunzipa), inakonzedwera alendo ochokera ku Bulgaria. Ha, alendowo anali osangalala ndi oyamikira chotani nanga kuti programu yonse inaperekedwa m’chinenero chawo! Drama Yabaibulo yokha sinali m’chinenero chawo. Nkhani ya mphindi 15 yofotokoza dramayo mwachidule inaperekedwa m’chinenero cha ku Bulgaria, ndiyeno nthumwizo zinakumana ndi abale awo olankhula Chigiriki kuwonerera kuseŵeredwa kwake.

Mfundo yaikulu ya msonkhano wa chinenero cha ku Bulgaria inali nkhani ya ubatizo pa Loŵeruka m’maŵa. Chiŵerengero chapamwamba cha anthu 342 anapezekapo, ndipo 39 anabatizidwa (ena a iwo akuwoneka ataimirira pamwambapa). Nthumwizo zinasangalalanso ndi kutulutsidwa kwa brosha ya Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo m’chinenero chawo.

Koma chosangalatsa chachikulu kwambiri chinayembekezera nthumwizo mwamsanga pambuyo pobwerera kwawo ku Bulgaria. Pa July 17, mlungu umodzi usanakwanire kuchokera pamene msonkhanowo unatha, ntchito ya Mboni za Yehova inavomerezedwa mwalamulo mu Bulgaria! Mosangalatsa, mwezi wotsatira ofalitsa a mpingo mu Bulgaria anachita avareji ya maola 21.2 muuminisitala wawo. Tiyenera kukhala achimwemwe chotani nanga kuti m’dziko lina la Kum’maŵa kwa Yuropu anthu akusangalala ndi ufulu wachipembedzo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena