Msonkhano Wamitundu Yonse wa Mboni za Yehova Woyamba mu Russia
ST. PETERSBURG, Russia, ndiwotchuka kwambiri chifukwa cha zimene nzika zake zimatcha “mausiku oyera”—nyengo ya pafupifupi masabata atatu m’June pamene thambo silimakhala lakuda kotheratu. Koma June 26 mpaka 28 wa 1992 anali wapadera.
Pamasiku amenewo, Mboni za Yehova zinali ndi msonkhano umene unagogomezera, osati kuunika kwenikweni kwamaola makumi aŵiri mphambu anayi koŵalira pamzinda wa St. Petersburg, koma kuunika kwauzimu kumene Akristu owona amaŵalitsa. Nchifukwa chake mutu wa msonkhanowo unali wakuti: “Onyamula Kuunika.”
Umenewu unali msonkhano wamitundu yonse wa Mboni woyamba m’dziko limene kale linali Soviet Union. Kunali nthumwi zochokera kumaiko pafupifupi 30 kuzungulira dziko lonse, kuphatikizapo Briteni, Canada, Denmark, Finland, Italiya, Japan, Jeremani, Netherlands, Norway, Sweden, Switzerland, ndi United States.
Ndiponso, panali pafupifupi Mboni 29,000 za m’dziko limene kale linali Soviet Union. Zina zinachokera ku Estonia, Georgia, Latvia, Lithuania, Moldova, ndi Ukraine. Opezekapo anali ochuluka kwambiri polingalira kuti Russia anali kupanga masinthidwe ovuta azachuma. Kwapadera kunali kukhalapo kwa nthumwi za Russia zimene zinayenda mtunda wamakilomita 8,000 kuchokera ku Vladivostok ndi malo ena kugombe la kummaŵa kwa Russia.
Nthumwi zochuluka zakunja kwa dziko zinachokera ku Finland wapafupi, ndi oimira oposa 10,000. Bwalo lamaseŵera linagaŵidwa paŵiri—mbali ya olankhula Chirussia ndi ya olankhula Chifinnish, iriyonse ndi pulatifomu yake pamene nkhani zonse zinakambidwira.
Kukonzekera
Malo a msonkhano anali Kirov Stadium ya zaka 42, yapachisumbu cha Krestovsky, makilomita angapo chabe kuchokera pakati pa St. Petersburg. Iri ndi mipando yokhala anthu pafupifupi 60,000 ndipo ndiyo bwalo lamaseŵera lachiŵiri kukula kwake m’dziko limene kale linali Soviet Union. Chakumbuyo kwake madzi a Mtsinje wa Neva amawoneka akutsira mu Gulf of Finland.
Komabe, bwalo lamaseŵeralo linafunikira kukonzedwa. Mapaipi a zimbudzi anayeretsedwa, ndipo zimbudzi zowonjezereka zinamangidwa. Pafupifupi makilomita 30 a mizera ya malo okhala anayenera kupakidwa utoto. Ndiponso, zitsamba zozungulira bwalo lamaseŵera zinadulidwa, ndipo udzu unamwetedwa. Ntchito imeneyi inatenga masabata ambiri kuti imalizidwe.
Kayendedwe ndi Malo Ogona
Pokhala ndi nthumwi za maiko akunja zoitanidwa pafupifupi 17,000, makonzedwe a kayendedwe ndi malo ogona anakhaladi ntchito yaikulu. Akuluakulu a Russia anali ogwirizanika kwambiri osati pamaofesi osiyanasiyana a akazembe okha komanso kumalire oloŵera m’dzikolo ndi pabwalo la ndege lalikulu mu St. Petersburg.
Makonzedwe anapangidwa ku mahotela 32 kuti apereke malo ogona ochuluka a nthumwi zakunja kwa dziko 17,000. Nthumwi zina 29,000 zochokera kumbali zosiyanasiyana za dziko limene kale linali Soviet Union zinapatsidwa malo ogona m’masukulu ndi m’malo osamalira ana a makolo ogwira ntchito 132. Nthumwizo zinafunikiranso zoyendera tsiku lirilonse popita kumalo a msonkhano, ndipo mabasi pafupifupi 390 anahaidwira zimenezi.
Nthumwi zakunja kwa dziko zambiri zinali kudyera m’mahotela awo. Komabe, miyezi ingapo msonkhanowo usanayambe, akuluakulu a boma mu St. Petersburg anadera nkhaŵa vuto la kudyetsa nthumwi zikwi zambiri zochokera kumadera osiyanasiyana a dziko limene kale linali Soviet Union. Iwo anati simukakhala chakudya chokwanira mumzinda ndi kuti Mboni zikayenera kubweretsa chakudya kuchokera kwina.
Ndipo iwo anachita zimenezo. Nthambi zingapo za Watch Tower Society zinapereka chopereka cha mitokoma yaikulu ya chakudya. Nthambi ya Finland yokha inapereka matani 200 a chakudya cha pamsonkhano! Ndiponso, nthumwi zambiri zakunja kwa dziko zinabweretsa mitokoma yaing’ono ya nyama ya m’zitini, zipatso ndi mtedza wouma, mkate, ndi zakudya zina zofunika. Patsiku lomalizira la msonkhano, chakudya chochuluka chodzala malole chinagaŵiridwa pabwalo lamaseŵera kwa nthumwi za m’dziko limene kale linali Soviet Union kuti zikhale ndi kamba wa paulendo popita kwawo.
Mkupiti Waukulu wa Kulengeza
St. Petersburg ndiwo mzinda wachiŵiri kukula kwake m’Russia, wokhala ndi nzika pafupifupi mamiliyoni asanu. Kwa nthaŵi yoyamba, Mboni za Yehova m’Russia zinaloledwa kuchita mkupiti waukulu wa kulengeza.
Mkupiti umenewu wosayerekezereka unayamba masabata angapo msonkhanowo usanayambe. Pafupifupi mahandibilu miliyoni imodzi anasindikizidwa m’Chirussia ndi kugaŵiridwa. Pachikuto choyamba cha handibilu panali chiitano cha kufika pankhani yapoyera pa Loŵeruka masana. Pachikuto chotsirizira, panali ndandanda ya programu ya pa Sande. Ndiponso, pafupifupi makope 750,000 a trakiti lakuti Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani? anagaŵiridwa kwa nzika za St. Petersburg. Limeneli linawadziŵitsa ziphunzitso za Mboni.
Nthumwi zochuluka zinafika m’St. Petersburg pakati pa tsiku limodzi kapena anayi msonkhano usanayambe. M’masiku amenewo, nthumwi zikwi zambiri zinali m’makwalala zikumagaŵira mahandibilu ndi matrakiti ndi mabuku ena a m’Chirussia. Ndiponso, zikwangwani zazikulu zingapo zinakonzedwa ndi kuikidwa m’mbali mwa makwalala oyenda anthu ochuluka a m’tauni la St. Petersburg. Zinali pafupifupi zamamita atatu muutali ndi mita imodzi ndi theka m’bwambi mwake, ndi chiitano chamawonekedwe okongola chokapezeka pankhani yapoyera, kutsogolo ndi kumbuyo kwake. Zina zinaikidwa pamakhomo penipeni pamasteshoni otanganidwa a sitima zapansi panthaka.
Programu
Tsopano, tsiku loyamba la msonkhano linafika, ndi opezekapo oposa 45,000! Programuyo inasinthidwa kuti nthumwi zambiri zipindule zimene sizinalankhule Chirussia kapena Chifinnish. Mwachitsanzo, nkhani zingapo zinakambidwa m’Chingelezi ndi kumasulidwira m’Chifinnish ndi Chirussia. Ziŵalo zisanu ndi chimodzi za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova zinakamba zingapo za nkhani zimenezi.
Patsiku lirilonse la msonkhano, panali kuperekedwa malipoti ndi zokumana nazo za kumaiko ena zosonyeza mmene Yehova akudalitsira ntchito yolalikira m’maikowo. Mofananamo, malipoti ameneŵa, pamodzi ndi zokumana nazo zambiri, anasimbidwa m’Chingelezi ndi kumasulidwira m’Chirussia ndi Chifinnish.
Nkhani yapoyera ya chigawo cha olankhula Chirussia inayankha funso lofunika kwambiri kwa nzika za Russia lerolino. Mutu wake unali wakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” Pambuyo pa nkhaniyo nthumwi zinasangalala kulandira brosha latsopano lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? m’Chirussia ndi Chifinnish.
Bukhu la nyimbo logwiritsiridwa ntchito ndi Mboni za Yehova pamisonkhano yawo silinatulukebe m’Chirussia. Chotero, Watch Tower Society inakonza brosha lapadera lokhala ndi mawu a nyimbo zonse zokaimbidwa pamsonkhano. Nthumwi za Russia zinatenga makope awo poloŵa m’bwalo lamaseŵera. Kunali kosangalatsa chotani nanga kumvetsera anthu 46,000 ochokera kumaiko osiyanasiyana 30 akuimba zitamando kwa Yehova Mulungu m’zinenero zawozawo, kuphatikizapo Chirussia!
Kwazaka makumi ambiri nthanthi ya chisinthiko yakhala ikuphunzitsidwa m’madera ambiri a dziko, kuphatikizapo m’zigawo za dziko limene kale linali Soviet Union. Mboni za Yehova m’maiko ameneŵa ziri zokonzeka bwino kwambiri tsopano kuvumbula zinyengo za nthanthi imeneyi ndi kuwanditsa chowonadi cha Mlengi wa moyo. Nthumwizo zinakondwera chotani nanga pamapeto a programu ya m’maŵa pa Sande pamene chiŵalo cha Bungwe Lolamulira chinatulutsa bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? m’Chirussia! Onse anapatsidwa kope laulere.
Nthumwi za kumaiko akunja zinauzidwa pasadakhale kuti Mboni zambiri m’Russia zinalibe Mabaibulo. Choncho Mabaibulo zikwi zambiri m’Chirussia anabweretsedwa monga mphatso. Mabaibulowo anaikidwa pamalo amodzi otengera kuti atengeredwe kumipingo ya Mboni za Yehova ndi kukagaŵiridwa kwa ofunikira kope.
Anadabwa!
Loŵeruka, m’maŵa monse ndi kuchiyambi kwa masana, panali namtindi wa alendo osakhala Mboni omadza mosalekeza m’bwalo lamaseŵera. Iwo anakopeka mtima nafuna kudziwonera okha zimene zinali kuchitika. Ambiri anadabwa. Ochuluka a iwo anali asanamvepo za Mboni za Yehova asanalandire chiitano cha kupezeka pa nkhani yapoyera. Ena anamva za msonkhanowo pankhani zoulutsidwa pa wailesi yakanema. Chiŵerengero chapamwamba cha opezeka pamsonkhano chinali 46,214.
Mkazi wina wachichepere amene ali wa Tchalitchi cha Russian Orthodox anati: “Ndachita chidwi kwambiri ndi Mboni. Ziri anthu amtendere, aulemu, ndi akhalidwe labwino.” Mlendo wina anati: “Tikhulupirira kuti Mboni za Yehova zidzakhala ndi misonkhano ina yambiri muno mu St. Petersburg.” Mkulu wa apolisi a Russia, kapena gulu losungitsa mtendere, amene anapatsidwa ntchito yoyang’anira malo a msonkhano ananena kuti kunali “kosangalatsa kupezeka pano pamsonkhano.”
Mkulu wa boma wakomweko anati ‘Mboni za Yehova zimawonedwa ndi ena monga kagulu ka mpatuko kachizembera komachitira zinthu mumdima ndi kochitira nkhalwe ana ndi iwo eni. Koma ndikuwona anthu abwino, achimwemwe, ndipo abwino koposa anthu ambiri amene ndidziŵa. Ali a mtendere ndi ofatsa, ndipo amakondana kwambiri.’ Anawonjezera kuti: “Sindimamvetsetsa konse chifukwa chimene anthu amakunamizirani motero.”
Pa Loŵeruka masana, otsutsa anayesa kudodometsa msonkhanowo. Ananyamula zikwangwani zazikulu zolembedwapo mawu osemerera Mboni. Pamene gulu la otsutsalo linayamba kukulakula ndi kuchita phokoso kwambiri, apolisi anaitana magulu ena apolisi owachirikiza kutetezera nthumwi za msonkhano. Otsutsawo sanakhoze kuloŵa pazipata zakutsogolo. Potsirizira pake, anangochoka, ali ogwiritsidwa mwala.
Mmodzi wa nthumwi za msonkhano amene anawona zimene zinachitika anachita chidwi ndi mkhalidwe wakugwirizanika wa gulu la apolisi osungitsa mtendere. “Ndadabwa kuwona gulu la apolisi osungitsa mtendere likuyesayesa mwaphamvu kutitetezera. Zaka zingapo zokha zapitazo, Mboni za Yehova zinalingaliridwa kukhala adani a Boma. Koma tsopano gulu la apolisi osungitsa mtendere likutitetezera!” Nduna ya gulu la apolisi osungitsa mtendere inapereka malingaliro ake pamene inauza nthumwi zingapo kuti: “Sitifuna kuti inu mudzitiwopa ayi. Tiri pano kukutetezerani ndi kutsimikizira kuti zonse zikuyenda bwino.”
Zonse zinayendadi bwino. Ngakhale masikuwo anacha bwino. Patsiku lirilonse la msonkhano, kunalibe mvula, kunali kofunda, ndipo kunalibe mitambo.
Zikwi Zambiri Zibatizidwa
Kwa ambiri chochitika chachikulu pamsonkhanowo chinali ubatizo wa zikwi zambiri. Mpingo wina m’St. Petersburg, wa ofalitsa 254, unapereka lipoti la obatizidwa 108! Nkovuta kulongosola chimwemwe chachikulu chimene nthumwi zinakhala nacho pamene zinawona oyembekezera kubatizidwa 3,256 akuimirira. Wokamba nkhani anafunsa mafunso aŵiri onena za kudzipatulira kwawo kwa Yehova, ndipo iwo anayankha mofuula kuti “da” (inde).
Pambuyo pa pemphero, akazi okabatizidwa anatsogozedwa kunjira ina ya kuzipinda zawo zosinthira, ndi amuna okabatizidwa kunjira ina ya kuzipinda zawo zosinthira. Pamene mazana ambiri a iwo anali kutuluka m’bwalolo, iwowo ndi omvetsera analonjerana mwa kuweyula manja.
Ambiri mwa omvetsera analira ndi chimwemwe. Ena anawomba m’manja molekezalekeza kwa mphindi zoposa 45. Nthumwi ina ya ku Finland inalephera kugwira mtima niyamba kulira. Iye akufotokoza kuti: “Mu 1943, ndinalembedwa usirikali m’gulu la nkhondo la Finland lokamenyana ndi la Russia. Inali nkhondo yowopsa imeneyo. Koma tsopano, pamsonkhano uno, ndawona nzika za Russia zikwi zambiri zikupatulira miyoyo yawo kwa Yehova! Pamene ndawona ena ali pamipando yamagudumu ndi ena akutsimphina, ndalira kwambiri. Ndinadzifunsa ndekha kuti: ‘Kodi nawonso anamenyako nkhondo ija? Kodi anavulazidwa ndi asirikali a Finland?’ Mwinamwake Yehova angandithandize tsopano kuti ndithandize abale anga a ku Russia.”
Kodi abale olankhula Chirussia anayamikira makonzedwe a Yehova a phwando limeneli la masiku atatu limene anawakonzera iwo, msonkhano waukulu umenewu woyamba m’St. Petersburg? Pamene wokamba nkhani wothera anali kumaliza ndemanga zake, anati: “Koposa zonse tikuyamika Yehova Mulungu kaamba ka msonkhano wabwino kwambiri umenewu.” Omvetsera anaimirira nawomba m’manja mwamphamvu kwa mphindi zoposa zisanu. Anali kuthokoza Yehova ali chiimire!
Yehova Mulungu, Magwero a kuunika, akuchirikizadi zikwi zambiri za onyamula kuunika m’maiko ameneŵa amene kale anali mbali ya Soviet Union. Pambuyo pa zaka zoposa 70 za ziletso ndi chizunzo, tsopano kuli kwachiwonekere kuti m’nthaŵi yonseyo Yehova anali kukwaniritsa lonjezo lake la pa Yesaya 60:22, pamene akuti: ‘Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.’
Mboni za Yehova ndizo gulu la m’mitundu yonse la ophunzira Baibulo oposa mamiliyoni anayi amene ali odzipereka kuthandiza anthu kuphunzira zowonjezereka ponena za dziko loŵazungulira ndi ponena za Mawu a Mulungu ndi mmene akukwaniritsidwira. Ngati mungakonde kudziŵa zowonjezereka kapena phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena keyala yoyenerera pa ondandalitsidwa pa tsamba 5.
[Bokosi patsamba 31]
Misonkhano Ina
Yonse pamodzi, misonkhano isanu ndi umodzi inachitidwa chilimwe chathachi m’dziko lonse lomwe kale linali Soviet Union. Chiwonkhetso cha anthu 91,673 anapezekapo, ndipo 8,562 anabatizidwa. Zimenezi zikutanthauza kuti 9.3 peresenti ya chiŵerengero cha opezekapo anabatizidwa pamisonkhano imeneyi. Ndithudi, peresenti imeneyi ikanaposerapo ngati nthumwi zakunja kwa dziko pafupifupi 17,000 sizinalipo pamsonkhano wamitundu yonse ku St. Petersburg.
Visoki Zamok, yofalitsidwa mu Lviv (mzinda umene kale unali Lvov), inati: “Kukoma mtima ndi kuwona mtima zinafungadi m’bwalo lamaseŵera pamasiku atatu a msonkhano. Mosasamala kanthu za kuchuluka kwa opezekapo, malowo akali audongo monga momwe analiri msonkhanowo usanayambe. Chitsanzo cha bata ndi mtendere chinali ponseponse.”
Tsopano popeza kuti Mboni za Yehova ziri ndi ufulu wa kulambira Mulungu poyera m’dziko lomwe kale linali Soviet Union, ambiri kumeneko ali ndi mwaŵi wa kudziwonera okha mmenedi Mboni ziliri. Krasnoyarskii Komsomolets, nyuzipepala ya Chirussia, inati: “Iwo ali anthu abwino, aubwenzi kwambiri, ndipo saali konse andale za dziko; amalimbikitsa kugwira ntchito zolimba, osati kulondola njira zopezera ‘ndalama mosavuta.’”
Misonkhano m’Dziko Lomwe Kale Linali Soviet Union
CHIŴER. CHAPA-
DETI MZINDA MWAMBA CHA OPEZ. OBATIZIDWA
June 26-28 St. Petersburg, Russia 46,214 3,256
July 10-12 Lviv, Ukraine 15,011 1,326
Alma-Ata, Kazakhstan6, 605 829
July 17-19 Kharkov, Ukraine 17,425 2,577
July 24-26 Irkutsk, Siberia 5,051 536
Tallinn, Estonia 1,367 38
CHIWON. 91,673 8,562
[Chithunzi patsamba 28]
Zikwangwani zinalengeza msonkhanowo
[Zithunzi patsamba 29]
Nthumwi ya Russia ikulandira kope lake la Baibulo
Mabrosha a nyimbo apadera anagwiritsiridwa ntchito
[Zithunzi patsamba 30]
Anthu ochuluka okwanira 3,256 anabatizidwa