Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 5/8 tsamba 28-30
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kufika Msanga Panyumba?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kufika Msanga Panyumba?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthaŵi Zausiku Zoyenera Kufika Panyumba—Lingaliro la Makolo
  • Zimatanthauza Kuti Amasamala
  • Kodi Nchifukwa Ninji Makolo Anga Amayesayesa Kulamulira Moyo Wanga?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Nchifukwa Ninji Chiletso Chofika Usiku Panyumba Chiri Chopambanitsa pa Ine?
    Galamukani!—1992
  • N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Anandiikira Malamulo Ambirimbiri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 5/8 tsamba 28-30

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kufika Msanga Panyumba?

“KODI aliyense wa inu ali ndi nthaŵi yausiku yoyenera kufika panyumba yoikidwa ndi makolo?” atola nkhani a Galamukani! anafunsa gulu la achichepere. Onse anapereka yankho limodzi lakuti inde! Komabe, funso lotsatira linayankhidwa mosiyanasiyana. Tinafunsa kuti: “Kodi muganiza kuti ayenera kukulolani kukhala kunja kufikira nthaŵi yanji usiku?”

“Ndiganiza kuti uyenera kuchita zirizonse zimene makolo anena,” anatero Monica wachichepere.a Bill wachichepere sanavomereze. Iye anatsutsa nati: “Ndiganiza kuti sayenera kukuuza nthaŵi imene uyenera kufika panyumba. Ndiiko komwe, mwina iwo ankafika panyumba usiku kwambiri pamene anali ana.” Wachichepere wotchedwa Sally anayesa kukhala pakati mwakumati: “Ndiganiza kuti uyenera kufika panyumba panthaŵi iriyonse imene makolo afuna—malinga ngati itapyola pa 8:00 p.m.” Potsirizira, panali Jerry, yemwe anawoneka kukhala ndi malingaliro amphamvu pa onse. Iye anati: “Mmalo motiuza nthaŵi yeniyeni yofika panyumba, nchifukwa ninji sitingangowaimbira foni ndi kuwauza kumene tiri? Ayenera kumvetsera.”

Mosasamala kanthu ndi malingaliro anu, nkothekera kwambiri kuti makolo anu anakuikirani nthaŵi yakutiyakuti yausiku yoyenera kufika panyumba. Lingakhale lamulo losasintha lakuti: ‘Uyenera kumafika panyumba itakwana 10:00 p.m., ukapanda kumatero udzachiwona! ’ Kapena makolo anu amaika nthaŵi yausiku yoyenera kufika panyumba molingana ndi mkhalidwe uliwonse. “Atadziŵa amene ndidzapita naye ndi kumene tidzapita,” anatero msungwana wazaka 16 wogwidwa mawu m’magazini a ’Teen, “amaika nthaŵi imene ndiyenera kufika panyumba. Zimangodalira pa anthu amene ndimapita nawo ndi malo amene timapitako.” Ngakhale wachichepere amene angawonekere kukhala ndi ufulu wokulirapo ayenera kudziŵitsa makolo ake za kumene adzakhala ndi nthaŵi imene adzabwerako.

Achichepere ambiri amawoneka kukhala osavutika kwambiri ndi ziletso zoterozo. Koma ena amawona kuikiridwa nthaŵi yobwera panyumba kukhala chododometsa chachikulu kapena chopinga chokwiitsa cha zochita zaumwini. Bukhu lakuti Teens Speak Out, lolembedwa ndi Jane Rinzler, linagwira mawu msungwana wina wazaka 16 yemwe anadandaula kuti: “Ndimadziwona ngati khanda ndikuti ndilibe ufulu wakudzisankhira.” Ena amaipidwa kwambiri ndi kuikiridwa nthaŵi yausiku yoyenera kufika panyumba chifukwa cha zokwiitsa zimene nthaŵiyo imadzetsa m’miyoyo yawo. Wachichepere wina anati: “Ndisanachoke panyumba ndiyenera kuuza amayi kumene ndikupita, amene ndikupita naye, mmene ndidzapitira ndi kubwerera.”

Nthaŵi Zausiku Zoyenera Kufika Panyumba—Lingaliro la Makolo

Kodi nchifukwa ninji makolo anu sangangokulolani kubwera ndi kupita pamene mufunira? Eya, talingalirani chiletso chimene Mulungu anaika pamtundu wa Israyeli. Pausiku wakuchita phwando loyamba la Paskha mu 1513 B.C.E., Mulungu analangiza Aisrayeli kuti: ‘Asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m’maŵa.’ (Eksodo 12:12, 22) Kodi Mulungu anachita mopambanitsa? Ayi. Chimenechi chinali chitetezo kuti asaphedwe ndi mngelo wa Yehova!

Ngakhale kuti mkhalidwe lerolino sungakhale wofulumira chotero, makolo ambiri ali ndi zifukwa zabwino zoyesera kutetezera ana awo. Ndiiko komwe, nkwachibadwa kwa makolo kudera nkhaŵa za ana awo. Makolo a Yesu Kristu ‘anada nkhaŵa’ pamene sanadziŵe kumene iye anali—ndipotu iye anali mwana wangwiro! (Luka 2:41-48) Makolo anu amadziŵa kuti sindinu wangwiro. Choncho iwo adzadadi nkhaŵa nthaŵi ndi nthaŵi ponena za inu, ngakhale kuti sindinu mwana wosamvera. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho?

Chifukwa chakuti makolo anu amadziŵa mmene “zilakolako za unyamata” zingakhalire zamphamvu. (2 Timoteo 2:22) Pokhala kuti anakhalapo achichepere amadziŵanso kuti ‘mwana womlekerera achititsa amake manyazi.’ (Miyambo 29:15) Kholo lina linavomereza kuti: “Ndinali wachichepere wopulupudza kwambiri. Ndidziŵa zimene ungabisire makolo ako.” Chotero pamene makolo amva za uchiwerewere wa achichepere, kumwa zakumwa zoledzeretsa ndi anamgoneka, kapena mapwando osalamulirika akwanuko, angagamule moyenerera kuti ziletso zakutizakuti nzofunika.

Makolo anu angakhalenso ndi nkhaŵa zoyenera za chisungiko chanu. Baibulo limatiuza kuti pamene ana a kholo Yakobo anachedwa kubwerako kumalo apafupi ndi Sekemu, Yakobo anauza Yosefe mwana wake wamwamuna kuti: ‘Pita tsopano, nukawone ngati abale ako ali bwino, . . . nundibwezere ine mawu.’ (Genesis 37:13, 14) Kumeneku sikunali kusawakhulupirira anawo. Chifukwa cha zochitika zaka zakumbuyo, Sekemu anali malo aupandu kwa ana a Yakobo!—Genesis, mutu 34.

Lerolino dziko nlaupandu kwambiri kuposa mmene linaliri m’nthaŵi za Baibulo—kapena ngakhale pamene makolo anu anali achichepere. Tiri mkati mwenimweni mwa “masiku otsiriza,” nyengo imene Baibulo linalosera kuti ikazindikiridwa ndi ‘nthaŵi zoŵaŵitsa.’ Liwu Lachigiriki lomasuliridwa ‘zoŵaŵitsa’ lingamasuliridwenso monga “zowopsa,” “zaupandu,” “zochititsa chisoni,” ndi “zovuta.” (King James Version, Douay, English Revised Version, Moffatt) Anthu ambiri lerolino ali “osakhoza kudziletsa,” kapena “achiwawa.” (2 Timoteo 3:1-5; Today’s English Version) Nchifukwa chake maupandu achiwawa, kuphatikizapo kugwirira chigololo ndi mbanda, ziri zoipa zenizeni zomwe zimachitika lerolino.

Makolo anu amadziŵanso kuti kuthekera kwanu kugwera m’mavuto kumakula pamene kwada kwambiri. “Zoipa zimachitika usiku kwambiri,” msungwana wina anauza Galamukani!, “ndipo makolo amayesa kukutetezera.” Wachichepere wina anafotokoza kuti: “Nthaŵi itapyola pakati pa usiku, misewu imadzala magalimoto oyendetsedwa ndi anthu oledzera, ndipo sikwabwino kukhala kunja usiku kwambiri pamene zidakwa zikuyendetsa magalimoto.”

Koma palinso upandu wa makhalidwe. Pamene usiku umka nukhwima, kudziletsa kumachepa, ndipo kudzisungira kosalamulirika kumawonjezereka. Pamenepo, pokhala ndi chifukwa chabwino, Baibulo limagwirizanitsa khalidwe loluluzika ndi usiku. Pa Yesaya 5:11, Mulungu analengeza “tsoka” kwa amene ‘achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa!’ (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:7.) Chotero makolo anu angawope kuti mutakhala kunja kufikira usiku kwambiri, upandu umakulirako wakuloŵetsedwa m’mapwando osalamulirika, kumwa zakumwa zoledzeretsa, kapena chisembwere chakugonana. Choncho ngati simuli panyumba panthaŵi imene makolo ailingalira, mwachiwonekere adzada nkhaŵa. Ndipo ayenera kudziŵa chifukwa.

Msungwana wina akukumbukira kuti: “Tsiku lina ndinali kucheza kunyumba ya tsamwali wanga wamkazi kufikira usiku kwambiri. Amayi sanadziŵe kumene ndinali, choncho anadza kudzandifunafuna. Anayamba kuyendayenda m’dera lathu akuitana dzina langa!” Kodi zinali zomvetsa manyazi? Mosakaikira zinalidi tero. Koma monga momwe amayi ŵena analongosolera, “Nthaŵi iriyonse imene [ana anga aakazi] afika panyumba kutada, ndimaganiza za zinthu zoipitsitsa zimene angakhale azichita.”

Zimatanthauza Kuti Amasamala

Koma bwanji ngati simuganizirako za khalidwe loluluzika? Bwanji ngati mungofuna kucheza ndi mabwenzi anu kwanthaŵi yakutiyakuti? Kunena zowona, kungakhale kogwetsa ulesi kukhala panyumba pamene ausinkhu wanu aloledwa kupita kokayenda. Kungakhalenso kochititsa manyazi kufotokozera mabwenzi anu kuti simungapite nawo chifukwa chakuti muyenera kufika panyumba mofulumira. Koma mutalingalira, mudzapeza kuti mawu a Leslie wachichepere ali owona kwambiri. Iye anati: “Kodi nchiyani chimene mungachite pa 12 [koloko yausiku] chimene simungachite pa 8 koloko?” M’mawu ŵena, kodi simungasanguluke moyenerera pamene anthu kaŵirikaŵiri amakhala maso? Chotero nkudziikiranji paupandu wa kuyenda usiku kwambiri?

Nayi mfundo ina yoyenera kuilingalira: Kodi kufika panyumba usiku kwambiri ndiko kugwiritsira ntchito mwanzeru nthaŵi yanu? Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti: ‘Potero, penyani bwino umo muyendera, simonga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machaŵi, popeza masiku ali oipa.’ (Aefeso 5:15, 16) Ndiponso, kodi kufika panyumba usiku kwambiri kungawongolere ntchito yanu yakusukulu kapena kukuthandizani kumaliza ntchito zapanyumba? Kodi kungafooketse luso lanu lakusumika maganizo pamisonkhano Yachikristu?

Potsiriza, muyenera kuwona chiletso chakufika panyumba mochedwa monga chisonyezero cha chikondi cha makolo. M’bukhu lake lakuti How to Raise Parents, wolemba Clayton Barbeau anafunsa kuti: “Kodi ungaganizirenji ngati ineyo, monga kholo lako, ndingakuuze kuti, ‘Ndilibe nazo kanthu ngati ungamwe anamgoneka kapena zakumwa zoledzeretsa kapena kusuta. Ndilibe nazo kanthu ngati uthamangitsa galimoto mopambanitsa. Zilibe kanthu kwa ine ngati ufika usiku panyumba. . . . ’ Kodi ungati ndikukuuzanji? Ndithudi: Ungati ndikukuuza kuti, ‘Sindimakukonda. Sindimakusamalira. Ndilibe nawe ntchito.’” Zowona, nthaŵi zina mungakhumbire achichepere amene ali ndi ufulu wokulirapo. Koma kumbukirani: ‘Wolekerera mwanake osammeya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.’—Miyambo 13:24.

M’moyo wanu wonse mudzafunikira kutsatira malamulo ndi ziletso. Chotero nkukaniranji nthaŵi yausiku yoyenera kufika panyumba yosavutayo? Zowona, nthaŵi zausiku zoyenera kufika panyumba zingakhale zopambanitsa nthaŵi zina, ndipo nkhani yamtsogolo idzakuthandizani kuchita ndi mkhalidwewo. Komabe, mudzachita bwino kugwirizana ndi makolo anu ndi kuyesa kuwona zinthu mmene iwo amaziwonera. Miyambo 28:7 imati: ‘Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira.’ Mwina mkupita kwa nthaŵi mudzaiwona nkhaniyo mofanana ndi mkazi wina wachichepere yemwe anati: “Sindinali kumvetsa chifukwa chake amayi ndi atate ankanditetezera motero ndi kukwiya nane nditafika usiku kwambiri panyumba. Tsopano pokhala ndine kholo, ndimadziŵa chifukwa chake amayi ankakhala maso kundiyembekezera. Chifukwa chakuti ankandikonda!”

[Mawu a M’munsi]

a Maina asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 29]

Kaŵirikaŵiri achichepere amada kufika msanga panyumba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena