Chidakwa m’Banja
“Uchidakwa ndimkhalidwe wa zidakwa . . . Ngakhale kuti munthu mmodzi ndiye angakhale chidakwa m’nyumba, banja lonse limavutika ndi uchidakwa wake.”—Dr. Vernon E. Johnson.
ALICE wazaka zisanu zakubadwa anagona pakama, mwendo wake ukupweteka kwambiri. Anayenera kukulungidwa bandeji mwendo wonse womwe unavulala dzana lake. Koma bandejiyo inamangidwa kwambiri kotero kuti mwendowo unayamba kutupa. Alice anapempha makolo ake kuti apite naye kwa dokotala, koma abambo ake anali ndi matsire amoŵa, choncho amayi ake anathedwa nzeru osadziŵa ndani anafunikira chisamaliro mwamsanga.
Patapita masiku angapo, mwendo wa Alice unazizira. Koma pamene chala chake chakumwendo chinayamba kutulutsa matsina akuda, mpamene makolo a Alice anathamangira naye kuchipatala. Bandejiyo itachotsedwa, nesi wina anakomoka ndi zimene anawona. Mwendo wa Alice unali ndi chironda chonyeka mwakuti sakanachitira mwina koma kuudula.
Zidakwa ndi Akapolo a Uchidakwa wa Ena
Tsoka la chochitikacho limaposa pa kudulidwa mwendo. Atate a Alice anali chidakwa. Chotero, iwo sanali kudera nkhaŵa ndipo sankapezekapo panyumba pamene anali ofunikira kwambiri kwa mwana wawo. “Uchidakwa umafuna kuti chidakwayo akankhire banja lake kumbuyo—ndi kuika moŵa ndi zofuna zake zonse patsogolo,” akutero phungu Toby Rice Drews.
Bwanji nanga za amake Alice? Nawonso anamangidwa ukapolo, osati ku moŵa, koma ku uchidakwa wa mwamuna wawo. Kwenikweni, mkaziyo amene iye sichidakwa amatangwanidwa kwambiri kuchita izi ndi izi kuyesayesa kuletsa kumwa kwa chidakwayo kapena kuyesa kupirira ndi zochita zake zosadziŵika.a Amakhala wotangwanidwa kwambiri ndi mavuto a chidakwayo mwakuti nayenso amaasonyeza mikhalidwe ya kumangidwa ukapolo kuuchidakwa—ngakhale kuti iye samamwa moŵa. Chifukwa cha chimenechi, kaŵirikaŵiri anthu onga amake Alice amatchedwa akapolo a uchidakwa wa ena.
Onse aŵiri chidakwa ndi woikidwa muukapoloyo amalamulidwa mosadziŵa ndi kenakake kapena winawake. Onse aŵiri amachititsidwa khungu ndi malingaliro onyalanyaza vuto lenilenilo. Onse aŵiri samakhala ndi mpata wakuganiza za ana awo. Onse aŵiri amakhala ogwiritsidwa mwala, popeza kuti monga momwe chidakwa sangalamulire kumwa kwake, woikidwa muukapoloyo sangalamulire chidakwayo, ndipo onse aŵiriwo sangalamulire chiyambukiro chimene uchidakwa udzakhala nacho pa ana awo.
Koma chithandizo chiripo kwa chidakwa ndi banja lake. Tidzapenda zimenezo m’nkhani zotsatirazi.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti zidakwa zotchulidwa m’nkhani zathuzi ndiamuma, njira zothandiza zoperekedwazo zimagwiranso ntchito kwa akazi.