Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 6/8 tsamba 12-13
  • Mapemphero Obwerezabwereza Kapena Ochokera Mumtima?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapemphero Obwerezabwereza Kapena Ochokera Mumtima?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Pemphero Limakhalira
  • Kodi Kristu Yesu Ananenanji?
  • Mmene Pemphero la Mtima Wonse Limathandizira
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • “Zopempha Zanu Zidziwike kwa Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 6/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Mapemphero Obwerezabwereza Kapena Ochokera Mumtima?

NDEGE yaikulu yonyamula anthu inali kuthamanga paliŵiro lalikulu pautali wa mamita 12,500 m’mwamba. Inkauluka pamwamba pa nyanja yozizira ya Pacific. Mwadzidzidzi, imodzi ya mainjini ake nkuleka kugwira ntchito. Ndiyeno, mainjini atatu enawo anachepa mphamvu. Kalanga ine, ndegeyo inazolika ilinkugwa paliŵiro la makilomita khumi m’mphindi ziŵiri! Koma mwamwaŵi wanji, pamene inafika pautali wa mamita 2,700 kuchokera pansi, ndegeyo inapezanso mphamvu nikatera bwino lomwe ku San Francisco. Wokweramo wina anafoya nati: “Ndipo ndapemphera ndi mtima wonse kuposa panthaŵi iriyonse m’moyo wanga.”

Panthaŵi za tsoka, ngozi, kapena chisoni chachikulu, anthu ambiri, ngakhale osapembedza, amapempha chithandizo kwa Wamphamvuyonse. Mosiyana nzimenezo, anthu opembedza amabwerezabwereza mapemphero m’matchalitchi ndi mu akachisi kapena m’nyumba. Mogwiritsira ntchito akolona, ambiri amapereka mapemphero otchedwa Pemphero la Ambuye ndi la Tikuwoneni Mariya. Ena amagwiritsira ntchito mabuku amapemphero. Mamiliyoni a anthu akum’maŵa amazungulitsa chipangizo chokhala ndi mapemphero mkati mwake monga njira yobwerezerabwerezera mapemphero mofulumira kwambiri.

Kodi munalingalirapo kuti, ‘Kodi tiyenera kupemphera motani? Kodi mapemphero ayenera kukhala obwerezabwereza kapena ochokera mumtima?’

Mmene Pemphero Limakhalira

Bwanji ngati atate ŵanu omwe mumawakonda kwambiri, okhala m’dziko lina, akulimbikitsani kumawaimbira foni nthaŵi iriyonse pamene mwafuna—popanda malipiro. Kodi simukawaimbira kaŵirikaŵiri? Kodi simukakhala wokondwa kupitiriza, ngakhaletu kulimbitsa unansi wanu wamtengo wapataliwo? Kodi simukalankhula za nkhaŵa zanu ndi kusonyeza chiyamikiro chanu pachithandizo chirichonse ndi chilimbikitso zimene anakupatsani m’moyo wanu wonse? Unansiwo wapakati pa inuyo ndi iwo, ukhoza kukhala wamtengo wapatali kwa inu, sitero kodi?

Pomalankhula nawo pafoni, mukhoza kumaŵatchulira nkhani zina mobwerezabwereza, koma simukanena nkhanizo mwakuŵerenga m’bukhu kapena mwakubwerezabwereza mawu oloŵeza, kodi mukatero? Chotero, ngakhale pemphero Lachikristu siliyenera kukhala lotero. Kwenikweni, Kristu Yesu ananena kuti mapemphero sayenera kukhala otero.

Kodi Kristu Yesu Ananenanji?

‘Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.’a (Mateyu 6:7) Matembenuzidwe ena amanena kuti: “M’mapemphero anu, musamabwebwete ngati akunja.” (The New English Bible) “Popemphera musachulukitse mawu opanda pake monga momwe Akunja amachitira.”—Revised Standard Version.

Anthu ena molakwa amatenga kuchulukitsa mawu kukhala kukangalika, kudziŵa kukamba bwino kukhala kudzipereka, kubwerezabwereza ndi kulankhula kwa nthaŵi yaitali kukhala kopezetsa yankho. Komabe, Mulungu samapima kufunika kwa pemphero ndi utali wake. Mwachidziŵikire, Yesu sanafune otsatira ake kupemphera mwanjira zolinganizidwa kale zosasintha kapena kubwereza mapemphero oloŵezedwa. Chotero, kodi akolona, mabuku amapemphero, kapena zipangizo zamapemphero ziri ndiphindu lanji lokhalitsa?

Atatha kunena zapamwambazi, Yesu anapereka pemphero lachitsanzo kwa ophunzira ake—Pemphero la Ambuye lotchukalo. (Mateyu 6:9-13) Koma kodi anafuna kuti iwo adzibwerezabwereza mawu enieniwo mmene aliri? Ayi. Tikuwona kuti ngakhale Yesu mwiniyo, sanagwiritsire ntchito mawu amodzimodziwo pamene analitchulanso koposa chaka chimodzi pambuyo pake. (Luka 11:2-4) Kodi pali cholembedwa chirichonse chosonyeza kuti Akristu oyambirira anachita zimenezo kapena kuti ankabwerezabwereza mapemphero ena? Ndithudi palibe.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingatchule mfundo yofanana kapena kupempha kwanthaŵi zambiri? Kutalitali, chifukwa chakuti Yesu anatinso: “Pemphanibe, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funanibe, ndipo mudzapeza.” (Mateyu 7:7, NW) Kaŵirikaŵiri kumakhala kofunika kwa ife kupempha chinthu chimodzimodzicho kwanthaŵi zambiri. Motero, Yehova amawona kufunitsitsa kwathu m’mapemphero athu ndi malingaliro athu amphamvu pankhaniyo.

Mwachitsanzo, m’zaka za zana lachisanu B.C.E., Nehemiya, mwamuna wopembedza anali mmodzi wa akapolo Achiyuda m’Babulo. Anali wopereka chikho kwa mfumu ya Peresiya. Pamene anauzidwa kuti abale ake, nzika za ku Yudeya, ankavutika, anapemphera “usana ndi usiku” kuti ziwakhalire bwino. (Nehemiya 1:6) Mapemphero ake anamvedwa. Yehova anachititsa wolamulira wachifundo wa Peresiya kulola Nehemiya kutenga ulendo wopita ku Yerusalemu kukawongola zinthu. Iye anachitadi zimenezo, nakondweretsa anthu ake ndi kusungitsa chikhulupiriro chawo.—Nehemiya 1:3–2:8.

Mmene Pemphero la Mtima Wonse Limathandizira

Ngakhale kuti ali Woposa m’Mphamvu m’chilengedwe chonse, Yehova akupempha “ana” ake kumfikira ndi mtima wonse. ‘Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,’ akutero Yakobo wophunzira wa Yesu. (Yakobo 4:8) Koma motani? Eya, tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu. (Yohane 14:6, 14) Ndiponso, monga momwe Paulo ananenera: ‘Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.’—Ahebri 11:6.

Amene ali ndi mavuto, ngakhale awo amene anachita machimo aakulu, akhoza kupempha ndi kulandira chithandizo ndi kukhululukidwa. Yesu anafotokoza zimenezi mwafanizo m’nthano yake ya mtsogoleri wachipembedzo yemwe, popemphera, anayamikira Mulungu kuti iye anali woyera kuposa ena; koma wamsonkho (m’masikuwo wowonedwa kukhala wonyansa ndi wochimwa kwambiri) anangoti: ‘Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.’ Ndithudi, pemphero losavuta, ndi la mtima wonse limenelo silinachokere m’bukhu. Ndipo Yesu anatsutsa wachipembedzo wonyengayo nati za winayo: ‘Wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.’—Luka 18:10-14.

Mikhalidwe yoipa yapadziko imachititsa anthu ambiri kuda nkhaŵa ndi kupsinjika. Ngakhale Akristu angade nkhaŵa ponena za kaimidwe kawo ndi Mulungu. Koma kupempha chithandizo kwa Yehova, nthaŵi zonse, kochokera mumtima kungadzetse mapindu odabwitsa. Paulo analemba kuti: ‘Musadere nkhaŵa konse, komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.’—Afilipi 4:6, 7.

Kupembedzera kumatanthauza kuchonderera kwa mtima wonse, kupempha chithandizo kwa Mulungu, kumuuza zakukhosi kwathu monga momwe mwana angachitire kwa kholo lake lachikondi ndi losamala. Mapemphero oterowo samachokera m’mabuku, ndiponso samakhala oloŵezedwa omabwerezedwabwerezedwa. Amachokera m’mitima yofuna chithandizo ndi yokhala ndi chikhulupiriro chenicheni mwa Yehova, “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.

[Mawu a M’munsi]

a Liwu lomasuliridwa ‘kubwerezabwereza’ (bat·ta·lo·geʹo) lagwiritsiridwa ntchito kamodzi kokha m’Baibulo ndipo limatanthauza “‘kubwebweta’ mwakuyesa kupeza chipambano m’pemphero mwakuchulukitsa mawu amodzimodzi.”—Theological Dictionary of the New Testament.

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

Zithunzithunzi za Albrecht Dürer/Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena