Athandizeni Kusankha Mnzawo wa Muukwati Mwanzeru
KODI ana anu amadziŵa chimene ayenera kufunafuna mwa mnzawo wa muukwati ndi mmene angasankhire mwanzeru? Nkofunika kulingalira nkhaniyi ndi kuwathandiza kupanga chosankha chanzeru, popeza kuti zimenezi zidzakhala zofunika kaamba ka chimwemwe chawo chamtsogolo.
M’maiko amene chizolowezi chiri kuyendera limodzi kwa mnyamata ndi msungwana, pali chitsenderezo chomakulakula cha kupanga timagulu ta aŵiriaŵiri pamsinkhu waung’ono kwambiri. “Makolo a ana azaka 10 akundiuza kuti ali pachipsinjo chachikulu chakuti alole ana awo kukayenda ndi asungwana kapena anyamata,” anatero Dr. Ronald W. Taffel, dokotala wamaganizo m’New York. “Mwadzidzidzi makolo amadzipeza kukhala ali kuvutana pankhani zimene sanayembekezere kudzachita nazo kufikira [ana awo] atasinkhukirapo.”
Kodi zotulukapo zake zikakhala chiyani ngati mugonja ndi kulola achichepere anu kuyamba kukayenda ndi mabwenzi achisungwana kapena achinyamata iwo adakali aang’ono? The Journal of the American Medical Association inati: “Kuyendera limodzi kwa mnyamata ndi msungwana pausinkhu waung’ono ndiponso kwakaŵirikaŵiri kumachititsa kuyambika kwa [kugonana].” Inde, inu mwinamwake mwaŵerenga malipoti a “chiŵerengero chomakulakula cha asungwana ausinkhu wazaka 10 kufikira 14 akumabala ana.”
Chotero, kodi mungachitenji kuthandiza ana anu?
Aphunzitseni Kuyambira Pausinkhu Waung’ono
Makolo afunikira kukhomereza makhalidwe abwino Achikristu mwa ana awo ndi kuwathandiza kukulitsa amenewa. Ndipo afunikiranso kuwathandiza kupeza makhalidwe amenewa mwa mnzawo wa muukwati woyembekezeredwa. Pamene mwana wanu ayambitsa nkhani yokayenda ndi wina wosiyana naye ziŵalo, fotokozani kuti zimenezi sizimalingaliridwa moyenera monga kokathera nthaŵi kongocheza chabe kapena kaamba ka awo amene sanafikitse kapena ali kuchiyambiyambi kwa zaka zawo za 13-19. Mmalo mwake, mveketsani bwino kwa iwo kuti kukayenda ndi tsamwali wosiyana naye ziŵalo nkwa anthu achikulire mokwanira kotero kuti afunefune mwamphamvu munthu woti akwatirane naye.
Ana alibe chidziŵitso chopendera munthu, monga momwedi iwo eni ayenera kuvomerezera zimenezi. Msungwana wina Wachimwenye panthaŵi ina anafotokozera phungu wa maukwati kuti: “Makolo athu ali achikulire ndi anzeru kwambiri, ndipo samabwatikidwa mwamsanga monga momwe tingakhalire. . . . Nkofunika kwambiri kuti mwamuna wondikwatira akhale woyenerera. Ndingaphophonye mosavuta ngati ndinati ndimfunefune ndekha.” Achichepere angapinduledi ndi chithandizo cha achikulire!
Achichepere kaŵirikaŵiri amayerekezera anzawo a muukwati oyembekezeredwa mogwirizana ndi miyezo imene simathandizira konse kuti iwo adzakhala amuna okwatira kapena akazi okwatibwa abwino kapena ayi. Anyamata angakopedwe ndi nkhope yokongola ndi kaumbidwe kathupi kokongola—koma bwanji pambuyo pake? Matupi ndi nkhope zimasintha, ndipo pambuyo pake mosakaikira mnyamatayo adzafuna makhalidwe a mkazi wachidziwitso, kuphatikizapo luntha ndi kukhoza kusenza mathayo. Asungwana kaŵirikaŵiri amaika chisamaliro pa kukongola kwa mnyamatayo, kukhala wovala mokongola, ndi woseketsa mmalo mwa kukhala ndi makhalidwe ofunika kwambiri a kukhala wokoma mtima ndi kukonda Mulungu ndi anthu anzathu.
Chotero, kodi mungachitenji? Kodi mulekeranji kusonyeza ana anu anthu amene iwo amadziwa ndi amene ali ndi maukwati abwino. Mungatchule kuti ena a anthu amenewa anasankha, osati kwakukulukulu chiphadzuwa kapena chinthemanthema cha mumzinda, koma munthu amene anali ndi makhalidwe abwino ndi amenenso anali ndi zifuno, zikondwerero, ndi zolinga zimene iwo anali nazo.
Kodi mulekeranji kukambitsirana nkhanizi ndi ana anu? Pamene Ann anali wazaka 13 zakubadwa, amake anamfunsa za mikhalidwe imene anafuna mwa mwamuna. Iwo anakambitsirana zimenezi, ndipo Ann anapereka mpambo wa mikhalidwe imene angayembekezere. Umenewu sunali mpambo wopambanitsa. Unaphatikizapo yakuti iye ayenera kukhala mwamuna amene iye akalemekeza, ndipo zifuno ndi zikondwerero za mnyamatayo ziyenera kukhala zofanana ndi zake. Tsopano iye monga gogo wachimwemwe, Ann adakavomerezabe kuti ena atsatire chitsanzo chimenechi.
Kwa Mkristu, lamulo Labaibulo la kukwatira ‘kokha mwa ambuye’ nlofunika mwapadera. (1 Akorinto 7:39) Munthu yemwe ali “mwa Ambuye” ali uyo amene ali Mkristu wodzipatulira, wobatizidwa ndi amene ali wodzipereka kukhala ndi phande m’ntchito yofanana ndi imene Yesu anachita. Awo amene amanyalanyaza lamulo la kukwatira kokha mwa Ambuye limeneli kaŵirikaŵiri amakhala ndi zotulukapo zatsoka. Chotero tsimikizirani kusonyeza achichepere anu kufunika kwa kulingalira mnzawo wa muukwati kokha munthu amene amatsatira malamulo amakhalidwe abwino amaganizo ndi auzimu onga amene iwo amatsatira ndi amene motero adzakhala okhoza kuwathandiza kukhomereza mikhalidwe imeneyi mwa ana alionse amene angadzakhale nawo.
Akonzekeretseni Kudzasamalira Mavuto
Pamene mwatsimikizira kuti ana anu ngachikulire mokwanira kuyendera limodzi ndi asungwana kepana anyamata, khomerezani mwa iwo nzeru ya kuzoloŵerana ndi atsamwali awo m’malo apoyera, kukhala ndi phande limodzi m’zochita, zonga kupita kumakantini, mamyuziyamu, kosungira zinyama, kapena kumalo osonyezera zinthu zopangidwa mwaukatswiri, kumene kumawalola kulankhula ndi kufikira podziwana wina ndi mnzake popanda kudzilekanitsa ndi anthu ena. Athandizeni kumvetsetsa chifukwa chake zimenezi ziri zanzeru kwambiri koposa kuthera nthaŵi m’malo obisika m’galimoto yoimikidwa kapena m’malo mwina mmene mulibe anthu ena pafupi. Nkofunikanso, kuwaphunzitsa kuti pamene afika panyumba kuchokera kokayenda, nkoyenera kutsazikana ali pakhomo ndi kusalola munthu kulowa kusiyapo, ndithudi, ngati simunagone ndipo mulimo.
Chenjezani ana anu za zimene zingachitike. Mwachitsanzo, lipoti lina la panyuzi, likusimba za wophunzira amene anaitanira mnyamata woyenda naye kuchipinda chake pambuyo pa chakudya kuti akavine ndi kulankhula. Ngakhale kuti mnyamatayo anafuna kuti agone onse, msungwanayo sanamuumirize kuti adzipita. Mmalo mwake, pamene msungwanayo anatsutsa, mnyamatayo ankapepesa kaamba ka zochita zake, komano kenako ankayesanso kunyenga msungwanayo. Lipotilo limati: “Potsirizira pamene kunali mbandakucha mnyamatayo anamuumiriza” mwa kumgwirira chigololo. Nzachisoni chotani nanga!
Chotero tsimikizirani kuti ana anu akudziŵa mmene angachitire motsimikiza ngati aliyense angatchule za machitachita achisembwere. Iwo ayenera kuthaŵa mkhalidwewo monga momwe Yosefe wachichepereyo anathaŵira mkazi woumiriza wa Potifara. (Genesis 39:7-12) Iwo ayenera kudziŵa kuti pempho losalekeza lakuti, “Ngati undikonda,” kaŵirikaŵiri ndilo chida cha wonyengayo. Aliyense amene amachigwiritsira ntchito mwinamwake amatero mwakaŵirikaŵiri, ndiyeno amasiya mkhole wakewo napita kukagonjetsa watsopano. Mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi ayenera kudziŵa kuti kunena kuti, ayi motsimikiza ndilo yankho labwino kopambana kulingaliro lachisembwere.
Tsimikizirani kuphunzitsa mwana wanu wamkazi kupewa mikhalidwe mmene angagwiriridwe chigololo. Gogomezerani kufunika kwa kudziŵa bwino lomwe mnyamata amene angapite naye kokayenda ndi kuti inu, kholo lake, nanunso muzolowerane bwino lomwe ndi munthuyo. Ngati ana anu samakhala m’dera lapafupi ndi kwanu, pamenepo tsimikizirani kuti iwo akufunsa woyang’anira Wachikristu ponena za mnzawo wa muukwati wothekera. Kumbukirani, pali onyenga amene amadzinenera kukhala Akristu ndi amene amalowa mumpingo, monga momwedi zinaliri m’zaka za zana loyamba.—2 Petro 2:13-15, 17, 18.
Ndiponso, mufunikira kuphunzitsa ana anu aamuna kuti amuna enieni samavulaza anthu ena mwadala. Iwo amawachinjiriza ndi kuwatetezera. Amuna enieni ali ambuye, osati akapolo, a zisonkhezero zawo. Iwo ayenera kuchita ndi asungwana moyenera monga momwe akanachitira ndi amawo kapena alongo awo, mwaulemu ndi kulemekeza.—1 Timoteo 5:1, 2.
Musalole konse ana anu kuiŵala lamulo lamakhalidwe abwino lalikulu Labaibulo lakuti: “Mabwenzi oipa amaipitsa makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33, Revised Standard Version) Chotero, ana anu ayenera kuzindikira kufunika kwa kupewa mayanjano ndi aliyense amene samadzisungira bwino m’moyo. Kuyambira paukhanda wawo, muyenera kumveketsa kwa iwo kuti pamene kuli kwakuti ena sangawone zimene iwo akuchita, Mulungu nthaŵi zonse amawona, ndipo adzapatsa aliyense wa ife mogwirizana ndi zochita zathu.—Aroma 2:6.
Kudzisungira Bwino m’Dziko Lachisembwere
Ngakhale kuti olamulira adziko adandaula kuti iwo “samadziŵa mmene angaletsere azaka 13-19 osakwatirana kuyamba kugonana,” makolo Achikristu amadziŵa kuti zimenezo zingachitidwe. Mwa kukhomereza chikondi cha pa Mulungu ndi kukhomereza kulemekeza mowona mtima malamulo ake mwa ana awo, makolo angakonzekeretse ana awo kukaniza ziyeso za dziko lachisembwereli ndi kukhala ndi moyo wowongoka, wamakhalidwe abwino. Chimangidwe chachikulu cha Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri nchodabwitsa m’kumamatira kwawo kumiyezo yamakhalidwe apamwamba ya Mawu a Mulungu. Ngakhale New Catholic Encyclopedia imanena kuti ‘makhalidwe aukwati ndi azakugonana a kagulu kameneka ngolimba kwambiri.’—Voliyamu 7, tsamba 864.
Achichepere pakati pa Mboni za Yehova amene amadzisungira bwino mwamakhalidwe amadziŵa kuti akufunidwa ndi kuyamikiridwa osati kokha ndi makolo awo komanso ndi Akristu anzawo kuzungulira padziko lonse. Iwo moyenerera amadziwona kukhala ochita bwino chifukwa cha chikumbumtima chabwino, amakhala ndi mbali pamisonkhano yampingo, amakulitsa maluso a kuphunzitsa, ndipo amakhala ndi phande m’maphunziro Abaibulo. Iwo amachitira chitsanzo makhalidwe aumulungu, amasangalala ndi malingaliro abwino a kudzilemekeza, ndipo ali ndi chiyembekezo cha mtsogolo motsimikizirika m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.—1 Yohane 2:17; Chivumbulutso 21:3, 4.
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Bokosi patsamba 32]
Kodi Mudzakwatirana ndi Yani?
Bukhulo Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza limapereka malingaliro abwino kwambiri onena za mmene achichepere angazoloŵeranirane ndi munthu wina amene iwo ali ndi chikondwerero cha kukwatirana naye.a Limasonyeza kufunika kwa kudziŵa zikhoterero zabwino ndi zoipa za munthuyo, kuti iye kwenikweni ali wotani. Kodi mungatero motani?
Choyamba, mungayang’anitsitse munthuyo. Kodi iye amadzisungira motani? Kodi iye amachita motani ndi anthu ena? Kodi amalankhula motani ndi makolo ake kapena ziwalo zina zabanja? Zinthu zimenezi nzofunika chifukwa chakuti zimasonyeza mmene m’kupita kwanthaŵi mungadzachitidwire.
Kupyolera mwamakambitsirano amwamwaŵi, mungathe kudziŵa kaya ngati zikondwerero ndi zonulirapo zake ziri zofanana ndi zanu. Mungafunenso kudziwa mmene anthu ena amawonera munthu ameneyu.
Mudzafuna kudziŵa mtundu wa munthu amene iye ali, malingaliro ake, maganizo ake, ndi umunthu wake wamkati. Kodi amachita motani atapanikizidwa? Kodi mabwenzi ake ndani? Kodi banja lake nlotani, ndipo kodi amachitirana motani wina ndi mnzake?
Kugwirira ntchito limodzi kungakupatseni chidziŵitso chabwinopo chonena za mikhalidwe ya munthuyo. Lolani nthaŵi yakuti zizolowezi zake zosakondweretsa ziwonekere. Pamenepo, monga momwe bukhu labwino kwambiri limeneli limanenera ponena za achichepere amene agwiritsira ntchito uphungu wanzeru woterowo: “Maso awo pokhala atatseguka kwambiri, iwo angathe kuloŵa muukwati mwa chidaliro cha kukhala okhoza kuthetsa kusagwirizana kumene kungabuke. Kutomerana kwachipambano kwawakonzekeretsa kaamba ka ukwati wachipambano ndi wachimwemwe.”—Mitu 29-32.
[Mawu a M’munsi]
a Bukhu limeneli nlofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., ofalitsa magazini ano.
[Chithunzi patsamba 30]
Mawonekedwe akunja okongola angakhale ochititsa chidwi, koma makhalidwe abwino kwambiri amkati ngofunika koposerapo
[Chithunzi patsamba 31]
Kufikira podziŵana bwino m’malo apoyera nkwanzeru kwambiri koposa kuthera nthaŵi m’malo anokha obisika