Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 7/8 tsamba 4-9
  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Panyumba?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Panyumba?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumene Amafuna Ana Aamuna Kapena Aakazi
  • Ntchito ya Mkazi Simatha Konse
  • Kupanda Ulemu—Vuto Ladziko Lonse
  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Lerolino?
    Galamukani!—1992
  • Kupatsa Ulemu Akazi m’Moyo Watsiku ndi Tsiku
    Galamukani!—1992
  • Kuchitira Nkhanza Akazi Ndi Vuto la Padziko Lonse
    Galamukani!—2008
  • Kodi Amuna Amamenyeranji Akazi?
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 7/8 tsamba 4-9

Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Panyumba?

“Mmodzi pambuyo pamnzake, akazi anafa imfa zomvetsa chisoni. . . . Ndipo ngakhale kuti imfa zawo zinasiyana, mikhalidwe yeniyeni imene zinachitikiramo sinasiyane: apolisi a ku Quebec [Canada] amanena kuti aliyense wa akaziwo anaphedwa ndi mwamuna wake kapena tsamwali wake wakale kapena watsopano. Onse pamodzi, akazi 21 mu Quebec aphedwa chaka chino [1990], mikhole ya chiwawa chomakulakula pakati pa amuna ndi akazi.”—Maclean’s, October 22, 1990.

CHIWAWA cha m’banja, chimene ena amachitcha “mbali yosakondweretsa ya moyo wa muukwati,” chachititsa kusweka kwa maukwati ambiri ndi kupangitsa ana kukula ndi malingaliro opotoka ponena za chimene chiyenera kukhala unansi wa mwamuna ndi mkazi muukwati. Ana samadziŵa kholo kwa limene ayenera kukhulupirika pamene akuyesayesa kudziŵa chifukwa chimene atate amamenyera amayi. (Nkwakamodzikamodzi, kufunsa kuti, kodi nchifukwa ninji amayi amakhala ankhanza kwa atate?) Kaŵirikaŵiri, chiwawa cha m’banja chimaphatikizapo ana amene amakula kukhala omenya akazi awo. Chitsanzo cha makolo awo chinawasiya ndi mavuto aakulu pa malingaliro ndiponso pa umunthu.

Bukhu la UN lakuti The World’s Women—1970-1990 limati: “Kuukira akazi kwa amuna m’mabanja awo kumalingaliridwa kukhala upandu wochepetsetsa umene sumachitiridwa lipoti kaŵirikaŵiri—mwapang’ono chifukwa chakuti chiwawa choterocho chimawonedwa kukhala vuto wamba lamakhalidwe, osati upandu.”

Kodi kuchitira nkhalwe akazi mu United States kuli koipa motani? Lipoti la Senate logwidwa mawu m’nkhani yapitayo limanena kuti: “Liwu lakuti ‘chiwawa cha m’banja’ lingamvekere lofeŵa, koma mkhalidwe umene limalongosola ngwokakala. Ziŵerengero zimapereka chithunzi choziziritsa m’nkhongono ponena za mmene kuliri kowopsa—ndithudi ngakhale kupha—kuchitira nkhanza mkazi. Akazi pakati pa 2,000 ndi 4,000 amafa chaka chiri chonse chifukwa cha nkhanza. . . . Mosiyana ndi maupandu ena, kuchitira nkhanza mkazi ndiko chiwawa ‘chosatha.’ Ndiko chiwopsezo cha nthaŵi zonse ndi kuvulaza kwakuthupi kobwerezabwereza.”

Magazini a World Health amanena kuti: “Kuchitira akazi chiwawa kumachitika m’dziko lirilonse ndi pakati pa anthu alionse, olemera kapena osauka. Malinga ndi miyambo yambiri, kumenya mkazi kumawonedwa kukhala koyenera kwa mwamuna. Kaŵirikaŵiri, kumenya kwa nthaŵi zonse ndi kugwiriridwa chigololo kwa akazi ndi asungwana kumalingaliridwa kukhala ‘nkhani zaumwini’ zimene sizimakhudza ena—kaya akuluakulu alamulo kapena akatswiri a zaumoyo.” Chiwawa cha m’banja chimenechi chingakhoze kufikira mosavuta kusukulu.

Izi zinasonyezedwa m’chimene chinachitika pasukulu yogonera komweko ya anyamata ndi asungwana ya ku Kenya mu July 1991. The New York Times inasimba kuti “asungwana apasukulu 71 anagwiriridwa chigololo ndi anyamata apasukulu ndipo ena 19 anafa m’chiwawa cha m’zipinda zawo zogona chimene chinasimbidwa kukhala . . . chinapitirizabe osaletsedwa ndi apolisi akumaloko kapena aphunzitsi.” Kodi tingati nchiyani chimene chimachititsa kufalikira kwa chiwawa pa akazi choterocho? “Tsoka limenelo linatsimikizira kufunafuna kukwezeka kwa amuna kumene kumalamulira moyo wa anthu a ku Kenya,” analemba motero Hilary Ng’Weno, mkonzi wamkulu wa The Weekly Review, nyuzipepala yoŵerengedwa koposa m’Kenya. “Mkhalidwe wa moyo wa akazi akwathuwa ndi asungwana ngwomvetsa chisoni. . . . Timalera anyamata athu mwa njira yosapatsa asungwana ulemu.”

Apa mpamene pali muzu wa vutolo kuzungulira dziko lonse—kaŵirikaŵiri anyamata pokula amaphunzitsidwa kuwona asungwana ndi akazi monga otsika, zolengedwa zogwiritsira ntchito. Akazi amawonedwa monga ofeŵa ndipo osavuta kuwalamulira. Chifukwa cha malingaliro oterowo nkwapafupi kusapatsa ulemu akazi ndi kufunafuna kukwezeka kwa amuna ndiponso nkwapafupi kugwirira chigololo munthu wodziŵana naye kapena wopita naye kocheza. Ndipo ponena zakugwirira chigololo, tisaiŵale kuti “kuukirako kumatha mphindi zochepa, koma chiyambukiro chake choipa chimakhala kwa moyo wonse.”—Senate Report.

Amuna ambiri, ngakhale kuti samachitira akazi chiwawa chapathupi, akhoza kunenedwa kukhala adani a akazi okakala. Mmalo mwakuchita chiwawa chapathupi, amagwiritsira ntchito kukakala kapena kubwanyula kwamalingaliro. M’bukhu lake lakuti Men Who Hate Women & the Women Who Love Them, Dr. Susan Forward amati: “Monga momwe anzawo [akazi] amawanenera, [amunaŵa] kaŵirikaŵiri anali okongola ndipo achikondi, koma mwadzidzidzi anali kusinthira kumkhalidwe wankhanza, wosuliza, ndi wotukwana. Mkhalidwe wawo unaphatikizapo mbali zambiri, kuyambira pa chiwopsezo chenicheni ndi zithupso kufikira pa ziwukiro zamachenjera kwambiri zampangidwe wakuneneza kapena kusuliza kochititsa manyazi. Uliwonse umene unali mpangidwewo, zotulukapo zinali zofanana. Mwamuna anapeza ulamuliro mwakutsendereza mkazi. Amuna ameneŵa anakananso kuvomereza thayo lirilonse la mmene ziukiro zawo zinachititsira anzawo kuvutika.”

Yasuko,a Mjapani wamba, yemwe tsopano wakhala zaka 15 muukwati wake, anasimbira mtola nkhani wa Galamukani! zochitika za banja lake kuti: “Atate kaŵirikaŵiri anali kumenya amayi ndi kuwavuta kwambiri. Anali kuwaponda ndi phazi ndi kuwakantha ndi nkhonya, kuwaduduluza mogwira tsitsi, ndipo ngakhale kuwaponya miyala. Mudziŵa chifukwa chake? Chifukwa chakuti amawafunsa za kusakhulupirika kwawo ndi mkazi wina. Mwawona nanga, molingana ndi mwambo Wachijapani, kumawonedwa kukhala koyenera kwa amuna ena kukhala ndi mkazi wachibwenzi. Mosiyana ndi akazi apanthaŵiyo, amayi sanamvane nazo zimenezo, ndipo anakana kuzivomereza. Pambuyo pazaka 16 muukwati ndi ana anayi, anakapeza chisudzulo. Abambo sanawasiire ndalama iriyonse yosungira ana.”

Komabe, ngakhale kumene kumenya kwa akazi kwachitiridwa lipoti kwa olamulira, zimenezo kaŵirikaŵiri sizinaletsa mwamuna wolipsayo kupha mwambanda mkazi wake. Nthaŵi zambiri, m’maiko onga United States, lamulo lakhala losakwanira kutetezera mkazi wothupsidwa ndi kuzunzidwa ndi mwamuna wake. “Mafufuzidwe ena anasonyeza kuti m’zochitika zoposa theka la imfa zonse za akazi ophedwa ndi amuna awo, apolisi anaitaniridwa kunyumba kasanu m’chaka chapitapo kudzafufuza madandaulo a chiwawa cha m’banja.” (Senate Report) M’zochitika zina zonkitsa, kuti adziwombole ku kuchitiridwa nkhanza kowonjezereka, mkazi amapha mwamuna wake.

Chiwawa cha m’banja, chimene kaŵirikaŵiri mkazi ndiye amakhala mkhole, chimachitika mwanjira zosiyanasiyana. Mu Indiya imfa zosimbidwa zotchedwa imfa za malowolo (amuna kupha akazi awo chifukwa chakusakhutira ndi malowolo amene banja la mkaziyo linapereka) zinawonjezereka kuchokera pa 2,209 mu 1988 kufika pa 4,835 mu 1990. Komabe, ziŵerengerozi sizingatengedwe kukhala zokwanira ndi zolondola, popeza kuti imfa zambiri za akazi zimanamiziridwa kukhala ngozi zapanyumba—kaŵirikaŵiri mwakuwatentha dala ndi palafini. Kuwonjezera pazimenezi pali kudzipha kwa akazi amene samathanso kupirira nkhanza za m’banja.

Kumene Amafuna Ana Aamuna Kapena Aakazi

Akazi amachitiridwa tsankho kuyambira pakubadwa ndipo ngakhale asanabadwe. Kodi ziri choncho motani? Mtola nkhani wa Galamukani! anafunsa Madhu wa ku Bombay, Indiya, yemwe anayankha kuti: “Pamene mwana wamwamuna abadwa m’banja Lachimwenye, pamakhala chisangalalo. Mavuto a nakubala atha. Tsopano makolowo ali ndi mwana amene adzawasamalira atakalamba. Mkhalidwe wawo wa ‘kusungika’ watsimikiziridwa. Koma ngati abala wamkazi, amawonedwa monga wolephera. Kuli ngati kuti wangobweretsa mtolo wina padziko. Makolo adzafunikira kudzapereka malowolo okwera mtengo kuti amkwatitse. Ndipo ngati amayiwo apitirizabe kubala ana aakazi, amalingaliridwa kukhala wolephera.”b

Magazini a Indian Express anasimba za asungwana mu India kuti: “Kukhala kwawo ndi moyo sikumalingaliridwa kukhala kofunika kwambiri m’kukhalako kwa banja.” Magazini amodzimodziwo amatchula kufufuza kochitidwa m’Bombay kumene “kunavumbula kuti pa miluza 8,000 yotaidwa mwakutchotsa mimba, pambuyo pakupima kudziŵa ngati ndimwamuna kapena mkazi, 7,999 anali akazi.”

Elisabeth Bumiller analemba kuti: “Mkhalidwe wa akazi ena a ku Indiya ngwoipa kwambiri kwakuti ngati kuvutika kwawo kungapatsidwe chisamaliro chonga chimene chimaperekedwa ku mkhalidwe wa mafuko ena aang’ono m’mbali zina zadziko, kudandaula kwawo kukhoza kumvedwa ndi mabungwe ochirikiza ufulu wa anthu.”—May You Be the Mother of a Hundred Sons.

Ntchito ya Mkazi Simatha Konse

Kaŵirikaŵiri kwanenedwa kuti ntchito ya mkazi siimatha konse. Mawuŵa amanena chowonadi chimene amuna ambiri amanyalanyaza. Mkazi amene ali ndi ana samakhala ndi mpata wa kukhala ndi ndandanda yokhazikika ya ntchito zake, yochokera 8 koloko m’maŵa mpaka 5 koloko madzulo, monga momwe kaŵirikaŵiri amachitira amuna. Ngati mwana alira usiku, kodi ndani amene mwachiwonekere adzamsamalira? Kodi ndani amasesa, kuchapa, ndi kusita? Kodi ndani amaphika ndi kupereka chakudya mwamuna ataŵeruka kuntchito? Kodi amene amatchotsa mbale pambuyo pachakudya ndi kukonzekeretsa ana kukagona ndani? Ndipo m’maiko ambiri, kuwonjezera pazonsezi, ndani amene amayembekezeredwa kukatunga madzi ndipo ngakhale kugwira ntchito m’munda ndi mwana kumbuyo? Kaŵirikaŵiri amakhala mayi. Ndandanda yake yantchito simangokhala yamaola 8 kapena 9 patsiku; kaŵirikaŵiri imakhala yamaola 12 mpaka 14 kapena kuposerapo. Komabe, samalandira malipiro a ovataimu—ndipo kaŵirikaŵiri samathokozedwa nkomwe!

Malinga nkunena kwa magazini a World Health, mu Ethiopia “akazi [ambiri] amayembekezeredwa kugwira ntchito kwa maola 16 mpaka 18 patsiku, [ndipo] mlingo wa malipiro awo umakhala wochepera kwambiri kotero kuti sangathe kudzipereza zokwanira iwo eni ndi mabanja awo. . . . Njala ili chochitika cha masiku onse; nthaŵi zambiri, [akazi okatolera ndi kunyamula nkhuni] amadya chakudya chimodzi chosakwanira patsiku ndipo kaŵirikaŵiri amanyamuka panyumba popanda kufisula.”

Siu, wobadwira ku Hong Kong, yemwe wakhala muukwati wake kwa zaka 20 tsopano, anati: “Molingana ndi khalidwe la Atchaina, amuna ngozoloŵera kululuza akazi, kumawawona monga othandiza apanyumba ndi obala ana kapena, mwanjira ina yonkitsa, monga mafano, zidole, kapena okhutiritsira chikhumbo chakugonana. Koma kwenikweni, chimene akazife timafuna ndicho kuchitiridwa monga zolengedwa zaluntha. Timafuna amuna kumatimvetsera pamene tilankhula osati kungochita zinthu monga zidole!”

Nkosadabwitsa pamene bukhu lakuti Men and Women limati: “Kulikonse, ngakhale kumene akazi amalemekezedwa kwambiri, ntchito za amuna zimawonedwa kukhala zoposa za akazi. Mosasamala kanthu za mmene chitaganya chimagaŵira malo ndi ntchito pakati pa amuna ndi akazi; za amuna mosakaikira zimaŵerengeredwa kwambiri m’chitaganya chonse.”

Chenicheni cha nkhaniyo nchakuti kaŵirikaŵiri ntchito ya mkazi m’banja simawonedwa kukhala yonunkha kanthu. Chifukwa chake, mawu oyambirira a bukhu lakuti The World’s Women—1970-1990 amati: “Mikhalidwe ya moyo wa akazi—ndi chithandizo chimene amapereka ku banja, chuma ndi zapanyumba—kaŵirikaŵiri zakhala zikunyalanyazidwa. Ziŵerengero zambiri zakhala zikuperekedwa mwa mawu osonyeza mikhalidwe ya amuna ndi chithandizo chimene amapereka, osati za akazi, kapena kusatchula kuti ndiamuna kapena akazi. . . . Ntchito zambiri zimene akazi amachita sizimalingaliridwa konse kukhala zothandiza chuma—ndipo sizimaŵerengeredwa konse.”

Mu 1934, wolemba nkhani wa ku North America Gerald W. Johnson anapereka malingaliro onena za akazi m’malo antchito kuti: “Kaŵirikaŵiri mkazi amapatsidwa ntchito ya mwamuna koma sinthaŵi zonse kupatsidwa malipiro amwamuna. Chifukwa nchakuti palibe ntchito yodziŵika iriyonse ya tsiku ndi tsiku imene singachitidwe bwinopo ndi amuna kuposa mkazi aliyense. Akatswiri osoka zovala ndi okonza zakumutu za akazi ali amuna . . . Akatswiri ophika ali amuna. . . . Ngakhake pompano ndiponso tsopano lino nzowona kuti wolemba ntchito aliyense ali wofunitsitsa kulipira mwamuna ndalama zochulukirapo kuposa mkazi pantchito imodzimodzi chifukwa chakuti amakhulupirira kuti mwamuna adzaichita bwinopo.” Komabe, ngakhale kuti ndemanga imeneyo ingakhale kukuza mawu ndi malovu, inasonyeza tsankho la m’nthaŵi ino, limene lidakali m’maganizo a amuna ambiri.

Kupanda Ulemu—Vuto Ladziko Lonse

Chitaganya chirichonse chakhala ndi kaimidwe kake kamaganizo, tsankho, ndi kusuliza ntchito ya mkazi m’chitaganya. Koma funso limene liyenera kuyankhidwa nlakuti, Kodi kaimidwe kamaganizo kameneka kamasonyeza ulemu kaamba ka kulemekezedwa kwa akazi? Kapena, kodi mmalomwake, kamasonyeza kulamulira akazi kochitidwa ndi amuna mkati mwa zaka mazana ambiri chifukwa cha nyonga ya amunawo yakuthupi? Ngati akazi akuchitiridwa monga akapolo kapena zinthu zogwiritsira ntchito, pamenepa ulikuti ulemu wawo kaamba ka kulemekezedwa kwawo? Kumlingo waukulu kapena waung’ono, zitaganya zochuluka zaluluza ntchito ya mkazi ndi kuchepetsa ulemu wake.

Chitsanzo chimodzi cha zambiri zochokera padziko lonse lapansi chikuchokera mu Afirika: “Akazi Achiyoruba [Nigeria] ayenera kuyesayesa kukhala mbuli zosadziŵa kanthu ndi achete pamaso pa amuna awo, ndipo pamene apereka chakudya, ayenera kugwadira amuna awo.” (Men and Women) M’mbali zina za dziko, kugonjera kopambanitsa kumeneku kungasonyezedwe m’njira zosiyanasiyana—kuyenda kwa mkazi mtunda wakutiwakuti pambuyo pamwamuna wake, kapena kuyenda pansi mwamuna wake atakwera pakavalo kapena pabulu, kapena pamene anyamula katundu mwamuna wake akuyenda chimanjamanja, kapena pamene amadyera payekha, ndi zina zotero.

M’bukhu lake lakuti The Japanese, Edwin Reischauer, amene anabadwira ndi kukulira m’Japani analemba kuti: “Kaimidwe kamaganizo ka kufunafuna kukwezeka kwa amuna nkowonekeratu m’Japani. . . . Muyezo wamakhalidwe abwino wokomera mbali imodzi, umene umapatsa ufulu amuna ndi kutsendereza akazi, udakali wofala. . . . Kwakukulukulu, akazi okwatiwa, amayembekezeredwa kukhala okhulupirika kuposa amuna.”

Mofanana ndi maiko ambiri, kuvutitsa akazi kulinso vuto m’Japani, makamaka m’tireni zoyenda pansi panthaka panthaŵi yopita kuntchito. Yasuko, yemwe amakhala ku Hino City, mu m’laga wa Tokyo, anauza mtola nkhani wa Galamukani! kuti: “Monga mkazi wachichepere, ndinkakwera tireni poyenda m’Tokyo. Kunali kochititsa manyazi kwambiri chifukwa chakuti amuna ena anapezerapo mwaŵi wakumatitsinatsina ndi kugwiragwira paliponse pamene anafuna. Kodi tikanatani akazife? Tinangopirira nazo. Koma zinali zochititsa manyazi. Panthaŵi yam’maŵa yopita kuntchito, panali tireni lapadera la akazi, choncho mwapang’ono ena anapeŵa kululuzidwako.”

Sue, amene kale anali kukhala ku Japani, anali ndi njira yake yakudziwonjola ku zochitika zimenezo. Iye anali kukuŵa kuti “Fuzakenai de kudasai!” ndiko kuti “Lekani kupusa koteroko!” Iye anati: “Zimenezo zinapangitsa anthu kuwona mwamsanga ndi kuleka. Palibe amene anafuna kuchititsidwa manyazi pamaso pa ena. Mwadzidzidzi panalibe mwamuna amene anandigwiragwira!”

Kusoŵeka kwa kulemekeza akazi m’banja kuli vuto lowonekeratu ladziko lonse. Koma bwanji ponena za ntchito ya akazi pantchito? Kodi amapatsidwa ulemu wokulirapo ndi kuyesedwa kanthu?

[Mawu a M’munsi]

a Ofunsidwawo anapempha kusatchulidwa maina. Chotero maina onse ogwiritsiridwa ntchito ngopeka.

b Amuna kaŵirikaŵiri amalingalira kuti mkaziyo ndiye ali ndi liŵongo lakubala ana aakazi. Iwo samalingalira konse lamulo lamajini lakubala. (Wonani bokosi, patsamba lino.)

[Bokosi patsamba 6]

Kodi Nchiyani Chimapangitsa Mwana Kukhala Mwamuna Kapena Mkazi?

“Kuti mwana adzakhala mwamuna kapena mkazi kumatsimikiziridwa pakutsagana kwa ubwamuna ndi dzira la mkazi, ndipo liri selo la ubwamuna wa atate limene limapangitsa. Dzira lirilonse, limene mkazi amatulutsa limakhala lalikazi mlingaliro lakuti limakhala ndi X, kapena kulomosomu yachikazi. Mwa mwamuna, theka lokha la maselo a ubwamuna ndilo limakhala ndi kulomosomu ya X, pamene theka linalo limakhala ndi Y, limene liri kulomosomu lachimuna.” Chotero ngati makulomosomu a X aŵiri atsagana, mwanayo adzakhala mkazi; ngati Y wachimuna atsagana ndi X wachikazi mwanayo adzakhala mwamuna. Chotero, kuti mkazi adzabala anyamata kapena asungwana kumadalira pa makulomosomu a ubwamuna wa mwamuna. (ABC’s of the Human Body, bukhu la Reader’s Digest) Kuli kosayenera kuti mwamuna aimbe mlandu mkazi wake chifukwa chakubala akazi okhaokha. Palibe amene ayenera kuimbidwa mlandu. Zangokhala lotale pakubala.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

Tsoka Lalikulu Kwambiri

M’bukhu lake lakuti Feminism Without Illusions, Elizabeth Fox-Genovese analemba kuti: “Pali chifukwa chomveka chokhulupiririra kuti amuna ambiri . . . mowonjezerekawonjezereka amayesa kugwiritsira ntchito nyonga [zawo] mumkhalidwe wina umene mwachiwonekere zimawapatsa mwaŵi—muunasi wawo ndi akazi. Ngati ndalondola m’lingaliro langa loyerekezera limeneli, pamenepo tikuyang’anizana ndi tsoka lalikulu kwambiri.” Ndipo tsoka lalikululo limaphatikizapo mamiliyoni a akazi amene amavutitsidwa tsiku ndi tsiku ndi amuna awo omenya, atate, kapena mwamuna wina aliyense—mwamuna amene amalephera “kukwaniritsa zofunika za kulingana ndi chiŵeruzo cholungama.”

“M’maboma makumi atatu [a United States], kukali kosaletsedwa ndi lamulo kwa amuna kugwirira chigololo akazi awo; ndipo zigawo khumi zokha ndizo ziri ndi malamulo akumanga anthu ochita chiwawa m’banja. . . . Akazi amene sangachitire mwina kusiyapo kuthaŵa amapezanso kuti kutero sindiko njira yabwino. . . . Chigawo chimodzi mwa zitatu za akazi 1 miliyoni omenyedwa amene amakafuna pothaŵira pamwamsanga chaka chirichonse samapapeza.”—Mawu oyamba a bukhu la Backlash—The Undeclared War Against American Women, lolembedwa ndi Susan Faludi.

[Chithunzi]

M’mamiliyoni ambiri, chiwawa cha m’banja chimawonedwa kukhala mbali yosakondweretsa ya moyo wa muukwati

[Chithunzi patsamba 7]

Mamiliyoni mazana ambiri amakhala m’malo popanda madzi a kumpopi, zimbudzi zamadzi, kapena magetsi m’nyumba zawo—ngati ali nayo nyumbayo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena