Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 9/8 tsamba 31
  • Achichepere Ena Samafuna Kukhala Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Ena Samafuna Kukhala Moyo
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kudzipha—Mliri Umene Ukuwononga Achinyamata
    Galamukani!—1998
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amatopa Nawo Moyo?
    Galamukani!—2001
  • Vuto Lapadziko Lonse
    Galamukani!—2001
  • Kudzipha—Mliri Wobisika
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 9/8 tsamba 31

Achichepere Ena Samafuna Kukhala Moyo

KUDZIPHA kochitidwa ndi achichepere kwakhala chikhoterero chochititsa mantha mu Indiya. Ofufuza m’dzikolo akuyerekezera kuti m’mphindi ziŵiri zirizonse munthu wina amayesa kudzipha, ndipo m’mphindi khumi zirizonse munthu wina amadzipha kumene.

Mkati mwa 1990 pafupifupi anthu 60,000 anadzipha mu Indiya, ndipo “pafupifupi theka la iwo anali a msinkhu wapakati pa zaka 18 ndi 35,” anatero magazini a India Today. Mikhole ina ya kudzipha njaing’ono monga ngati zaka khumi zakubadwa. Chiwerengero chenicheni cha anthu amene amadzipha mu Indiya nchosadziŵika chifukwa chakuti mabanja ambiri amachitira lipoti kudzipha kukhala ngozi kuchitira kuti apeŵe manyazi.

India Today ikunena kuti “anyamata ndi asungwana oposa 2,500 anadzipha chifukwa cha kusagwirizana m’nkhani za chibwenzi” mkati mwa 1990. Malinga nkunena kwa madokotala a nthenda ya maganizo, chifukwa china cha kuwonjezereka kwa odzipha pakati pa achichepere ndicho zitsenderezo za mpikisano ponena za mmene akuchitira kusukulu, kumene kumayamba adakali achichepere kwambiri.

Magaziniwo akuwonjezera kuti “madokotala anthenda za amaganizo akhulupirira kuti kusweka kwa mabanja apachibale kukuchititsa kwambiri nsautso ndi kusungulumwa zimene zingayambitse malingaliro akudzipha” mwa anawo. Dokotala wina wa nthenda za maganizo, Dr. S. G. Dastoor, anati: “Ngati kokha makolo anadera nkhaŵa kuthera nthaŵi yowonjezereka ndi ana awo ndi kupeza kuti chinali kuwavuta nchiyani, miyoyo yawo ikapulumutsidwa. Kaŵirikaŵiri ndimaganiza kuti ali makolo amene afunikira uphungu.”

Baibulo limalimbikitsa makolo Achikristu kuthera nthaŵi ndi ana awo ndi kukhomereza mwa iwo malamulo amakhalidwe abwino aumulungu. (Deuteronomo 6:4-9) Malemba amalangizanso makolo kusakwiitsa ana awo koma kuwalera iwo ‘m’chilango ndi kulamulira maganizo kwa Yehova.’—Aefeso 6:4.

Ndiponso, achichepere Achikristu angalake zitsenderezo zamakono mwakugwiritsira ntchito uphungu wanzeru wopezeka m’Baibulo pa Afilipi 4:6, 7, umene umati: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena